Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | KODI TINGAPEZE KUTI CITONTHOZO?

Mmene Mulungu Amatitonthozela

Mmene Mulungu Amatitonthozela

Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Yehova * “ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Motelo, Baibulo imatitsimikizila kuti Mulungu angakwanitse kuthandiza munthu aliyense. Ndipo Atate wathu wakumwamba sangalephele kutithandiza ngakhale titakumana na vuto lalikulu kwambili.

Koma ngati tifuna kuti Mulungu atitonthoze, tifunika kucita cinthu cina. Kodi dokota angatithandize bwanji ngati sitinapite kukamuuza vuto lathu? Mneneli Amosi anafunsa kuti: “Kodi anthu aŵili amayenda pamodzi asanapangane ndi kukumana mogwilizana ndi pangano lawolo?” (Amosi 3:3) N’cifukwa cake Malemba amatilimbikitsa kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8.

Tingadziŵe bwanji kuti Mulungu angatiyandikile na kutithandiza? Coyamba, amatiuza mobweleza-bweleza kuti amafuna kutithandiza. ( Onani bokosi m’nkhani ino.) Caciŵili, tili na umboni wotsimikizilika wa anthu amene Mulungu anawatonthoza, a m’nthawi yathu ndi a m’nthawi yakale.

Mofanana ndi anthu ambili amene amafuna thandizo la Mulungu, Mfumu Davide anali kukumana ndi mavuto kaŵili-kaŵili. Nthawi ina, iye anapempha Yehova kuti: “Imvani mawu anga ocondelela pamene ndikufuulila inu kuti mundithandize.” Kodi Mulungu anamuyankha? Inde. Davide anakambanso kuti: “Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwela.”—Salimo 28:2, 7.

MBALI YA YESU POTONTHOZA ONSE OLILA

Mulungu anasankha Yesu kuti agwile nchito yotonthoza anthu. Zina mwa nchito zimene Mulungu anapatsa Yesu ndi ‘kumanga zilonda za anthu osweka mtima’ ndi ‘kutonthoza anthu onse olila.’ (Yesaya 61:1, 2) Monga mmene malemba anakambila, Yesu anathandiza kwambili anthu amene anali “kugwila nchito yolemetsa ndi olemedwa.”—Mateyu 11:28-30.

Yesu anatonthoza anthu mwa kuwapatsa malangizo anzelu, kucita nawo zinthu mokoma mtima, ndipo nthawi zina anali kucilitsa odwala awo. Tsiku lina, wakhate anapempha Yesu kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeletsa.” Atagwidwa cifundo, Yesu anayankha wakhateyo kuti: “Ndikufuna. Khala woyela.” (Maliko 1:40, 41) Wakhateyo anacila.

Masiku ano, kulibe Mwana wa Mulungu kuti atitonthoze mwacindunji. Koma Atate wake, Yehova, “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse,” amathandizabe anthu amene afunika thandizo. (2 Akorinto 1:3) Onani njila zinayi zikulu-zikulu zimene Mulungu amaseŵenzetsa potonthoza anthu.

  • Baibulo. “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa ciyembekezo cifukwa Malembawa amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.

  • Mzimu Woyela wa Mulungu. Patapita nthawi yocepa kucokela pamene Yesu anaphedwa, mpingo wonse wacikhiristu unaloŵa m’nyengo yamtendele. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti “unali kuyenda moopa Yehova ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyela.” (Machitidwe 9:31) Mzimu woyela, umene ni mphamvu ya Mulungu yogwila nchito, ni wamphamvu kwambili. Mulungu angauseŵenzetse kutonthoza aliyense amene ali na vuto lililonse.

  • Pemphelo. Baibulo imatiuza kuti, “musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7.

  • Akhiristu Anzathu ndi anthu amene angatitonthoze tikakumana na mavuto. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti anzake ‘anamuthandiza na kumulimbikitsa . . . m’kusoŵa kwake konse ndi m’masautso ake onse.’—Akolose 4:11; 1 Atesalonika 3:7.

Koma mwina mungafunse kuti ‘Kodi zimenezi zimathandiza bwanji?’ Tiyeni tione zitsanzo za anthu amene anakumana na mavuto amene tawachula kuciyambi kwa nkhani ino. Molingana ndi anthu amenewa, mukhoza kuona kuti Mulungu amakwanilitsa lonjezo lolimbikitsa ili: “Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu.”—Yesaya 66:13.

^ par. 3 Baibulo imakamba kuti dzina la Mulungu ni Yehova.