NKHANI YA PACIKUTO | MASOMPHENYA A ZINTHU ZA KUMWAMBA
Masomphenya Oonetsa Amene Ali Kumwamba
Baibo imakamba za masomphenya ambili ocititsa cidwi, amene amatithandiza kudziŵa amene amakhala kumwamba. Tikupemphani kuti muŵelenge mosamalitsa nkhani yokamba za masomphenya amenewa. Ngakhale kuti zinthu zina za m’masomphenya amenewa n’zophiphilitsa cabe, zingakuthandizeni kudziŵa amene ali kumwamba ndi mmene zocita zawo zimakukhudzilani.
YEHOVA NDIYE WAMKULU KOPAMBANA
“Mpando wacifumu unaoneka uli pamalo ake kumwamba, wina atakhalapo. Wokhala pampandoyo, anali wooneka ngati mwala wa yasipi, ndi mwala wofiila wamtengo wapatali. Utawaleza wooneka ngati mwala wa emalodi unazungulila mpando wacifumuwo.”—Chivumbulutso 4:2, 3.
“Pamalo onse omuzungulila panali powala. Panali cinacake cooneka ngati utawaleza umene umaoneka mumtambo pa tsiku la mvula yamphamvu. Umu ndi mmene kuwala kozungulila pamalopo kunali kuonekela. Zinali kuoneka ngati ulemelelo wa Yehova.”—Ezekieli 1:27, 28.
M’masomphenya amenewa ofotokoza za ulemelelo wa Yehova, Mulungu Wam’mwambamwamba, amene mtumwi Yohane ndi Mneneli Ezekieli anaona, munali zinthu zimene tingakwanitse kuona. Zinthu monga miyala yonyezimila modabwitsa, utawaleza, ndi mpando wacifumu wokwezeka. Zinthu zimenezi zimaonetsa kuti malo amene Yehova amakhala ndi okongola, osangalatsa ndi amtendele.
Masomphenya amenewa onena za Mulungu, agwilizana na mau amene wamasalimo analemba akuti: “Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenela kutamandidwa kwambili. Iye ndi wocititsa mantha kuposa milungu ina yonse. Cifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake, koma Yehova ndiye anapanga kumwamba. Ulemu ndi ulemelelo zili pamaso pake. Mphamvu ndi kukongola zili m’nyumba yake yopatulika.”—Salimo 96:4-6.
Ngakhale kuti Yehova ndi Wamkulu Koposa, akutipempha kuti tizipemphela kwa iye ndipo akutitsimikizila kuti adzamvetsela mapemphelo athu. (Salimo 65:2) Mulungu amatikonda kwambili ndipo amatisamalila, cakuti zinapangitsa mtumwi Yohane kulemba kuti: “Mulungu ndiye cikondi.”—1 Yohane 4:8.
YESU ALI NA MULUNGU
“Koma iye [wophunzila wa Yesu Sitefano], pokhala wodzazidwa ndi mzimu woyela, anayang’anitsitsa kumwamba ndi kuona ulemelelo wa Mulungu ndi wa Yesu ataimilila kudzanja lamanja la Mulungu. Ndipo ananena kuti: ‘Taonani! Ndikuona kumwamba kotseguka, ndipo Mwana wa munthu waimilila kudzanja lamanja la Mulungu.’”—Machitidwe 7:55, 56.
Panthawi imene Sitefano anaona masomphenya amenewa anali kukamba ndi atsogoleli a Ciyuda. Apa n’kuti papita nthawi yocepa cabe kucokela pamene atsogoleli a Ciyudawo anasonkhezela anthu kupha Yesu. Masomphenya amenewa anaonetsa kuti Yesu anali wamoyo. Iye anali ataukitsidwa ndipo anapatsidwa ulemu. Ponena za nkhaniyi mtumwi Paulo analemba Aefeso 1:20, 21.
kuti: “[Yehova] anaukitsa [Yesu] kwa akufa ndi kumukhazika kudzanja lake lamanja m’malo akumwamba. Anamuika pamwambamwamba kuposa boma lililonse, ulamulilo uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse, ndi dzina lililonse lopelekedwa kwa wina aliyense, osati mu nthawi ino yokha, komanso imene ikubwelayo.”—Kuwonjezela pa kufotokoza za malo ake okwezeka, Malemba amaonetsa kuti Yesu, mofanana ndi Yehova, amatikonda kwambili. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anacilitsa odwala, olemala ndi kuukitsa akufa. Iye anaonetsa kuti amakonda kwambili Mulungu na anthu mwa kupeleka moyo wake monga nsembe. (Aefeso 2:4, 5) Popeza kuti Yesu ali ku dzanja la manja la Mulungu, posacedwa adzayamba kulamulila dziko lapansi ndipo adzapeleka madalitso osaneneka kwa anthu onse omvela.
ANGELO AMATUMIKILA MULUNGU
“Ine [mneneli Danieli] ndinapitiliza kuyang’ana kufikila pamene mipando yacifumu inaikidwa ndipo Wamasiku Ambili [Yehova] anakhala pa mpando wake wacifumu. . . . Panali atumiki okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikila nthawi zonse, ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimilila pamaso pake nthawi zonse.”—Danieli 7:9, 10.
M’masomphenya a kumwamba amenewa, Danieli anaona angelo ambili-mbili. Anali masomphenya owopsa kwambili. Angelo ni zolengedwa zauzimu zapamwamba kwambili, zanzelu, ndi zamphamvu. Pali angelo a udindo wosiyana-siyana. Ena mwa iwo ndi aserafi ndi akerubi. Baibo imachula angelo maulendo oposa 250.
Angelo si anthu amene anali kukhala padziko lapansi kale-kale. Mulungu analenga angelo kale-kale akalibe kulenga anthu. Pamene Mulungu anali kulenga dziko lapansi, angelo anali kuona ndipo anafuula ndi cisangalalo.—Yobu 38:4-7.
Njila imodzi imene angelo amatumikila Mulungu ndi kuthandiza pa nchito yofunika kwambili imene ikucitika padziko lapansi masiku ano, yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Masomphenya amene mtumwi Yohane anaona amapeleka umboni wakuti angelo amathandiza pa nchitoyi. Iye analemba kuti: “Ndinaona mngelo winanso akuuluka capafupi m’mlengalenga. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse.” (Chivumbulutso 14:6) Ngakhale kuti masiku ano angelo sakamba na anthu mmene anali kucitila kale, amatsogolela alaliki uthenga wabwino kuti apeze anthu a mtima wabwino.
SATANA AKUSOCELETSA ANTHU AMBILI
“Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli [Yesu Khiristu] ndi angelo ake anamenyana ndi cinjoka. Cinjokaco ndi angelo ake cinamenya nkhondo, koma sicinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. Conco cinjokaco cinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wochedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”—Chivumbulutso 12:7-9.
Panthawi inayake, kumwamba kunalibe mtendele. Anthu atalengedwa, mngelo wina anayamba kulaka-laka kuti anthu azimulambila. Conco, iye anapandukila Yehova n’kukhala Satana, kutanthauza kuti “Wotsutsa.” Angelo ena anagwilizana na Satana, ndipo anayamba kuchedwa ziwanda. Ziwanda n’zoipa kwambili. Zimatsutsa Yehova ndi kusonkhezela anthu ambili kusamvela malangizo ake.
Satana na ziwanda zake ali na makhalidwe oipa ndipo ndi ankhanza. Iwo ni adani a anthu ndipo acititsa mavuto ambili pa dziko lapansi. Mwacitsanzo, Satana anapaya ziŵeto za munthu wokhulupilika, Yobu, ndiponso atumiki ake. Anapayanso ana ake onse 10 mwa kucititsa “cimphepo” cimene cinagwetsa nyumba imene munali anawo. Pambuyo pake, Satana “anagwetsela Yobu zilonda zopweteka, kuyambila kuphazi mpaka kumutu.”—Yobu 1:7-19; 2:7.
Koma posacedwa, Satana adzawonongedwa. Kucokela pamene anaponyedwa pa dziko lapansi, iye wakhala akudziŵa kuti “wangotsala ndi kanthawi kocepa.” (Chivumbulutso 12:12) Ni nkhani yokondweletsa kwambili kudziŵa kuti Satana adzawonongedwa.
AMENE ACOKELA PA DZIKO LAPANSI
“Inu [Yesu] munagula anthu kuti atumikile Mulungu. Anthu ocokela mu fuko lililonse, cinenelo ciliconse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse. Ndipo munawasandutsa mafumu ndi ansembe a Mulungu wathu, moti adzakhala mafumu olamulila dziko lapansi.”—Chivumbulutso 5:9, 10.
Yesu anaukitsidwa ndi kukakhala na moyo wauzimu kumwamba. Ni mmenenso anthu ena adzacitila. Yesu anauza atumwi ake okhulupilika kuti: “Ndikupita kukakukonzelani malo. Ndiponso, . . . ndidzabwelanso kudzakutengelani kwathu, kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko.”—Yohane 14:2, 3.
Pali colinga cimene anthu ena amapitila kumwamba. Iwo pamodzi na Yesu adzapanga Boma la Mulungu limene lidzalamulila anthu padziko lonse lapansi na kuwadalitsa. Boma limeneli ndilo Ufumu umene Yesu anauza otsatila ake m’pemphelo lacitsanzo kuti aziupemphelela. Iye anawauza kupemphela kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.”—KODI AMENE ALI KUMWAMBA ADZACITA CIANI?
“Ine [mtumwi Yohane] ndinamva mawu ofuula kucokela kumpando wacifumu, akuti: ‘Taonani! Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu. . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.’”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Masomphenya a ulosi amenewa akamba za nthawi imene Ufumu wa Mulungu, wopangidwa na Yesu pamodzi na anthu amene adzaukitsidwila kumwamba, udzacotsapo ulamulilo wa Satana ndi kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso. Zinthu zonse zimene zipangitsa anthu kuvutika kwambili zidzasila. Imfa nayonso idzatha.
Nanga n’ciani cidzacitika kwa anthu ambili-mbili amene anafa ndipo sanapite kumwamba? Iwo adzaukitsidwa ndipo adzakhala na moyo wosatha m’paradaiso, pano padziko lapansi.—Luka 23:43.
Masomphenya amene taŵelengawa, aonetsa kuti Yehova Mulungu, Yesu Khiristu, angelo okhulupilika, ndi anthu amene anagulidwa pa dziko lapansi, onse amatikonda ndi kutifunila zabwino. Ngati mufuna kudziŵa zambili pa zimene iwo adzacita, kambani na Mboni za Yehova, kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.pr418.com, na kucita daunilodi buku la Zimene Baibo Ingatiphunzitse.