Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MAFUNSO OCOKELA KWA AŴELENGI. . .

Kodi Akhristu Ayenela Kukondwelela Khrisimasi?

Kodi Akhristu Ayenela Kukondwelela Khrisimasi?

Anthu mamiliyoni padziko lonse amakhulupilila kuti Khrisimasi ni mwambo wokondwelela tsiku la kubadwa kwa Yesu Khristu. Komabe, kodi munaganizilapo ngati Akhristu a m’nthawi ya atumwi, amene anali anzake a Yesu anali kukondwelela Khrisimasi? Kodi mudziŵa zimene Baibo ikamba pankhani ya masiku akubadwa? Kudziŵa mayankho a mafunso amenewa kungatithandize kudziŵa ngati Akhristu ayenela kukondwelela Khrisimasi kapena ayi.

Coyamba, Baibo siichula za cikondwelelo ca tsiku la kubadwa la Yesu kapena la mlambili aliyense wokhulupilika wa Mulungu. Malemba amakamba cabe za anthu aŵili amene anakondwelela masiku awo akubadwa. Onse sanali olambila Yehova, Mulungu wa Baibo. Ndipo pa zikondwelo zawo za masiku akubadwa panacitika zinthu zoipa kwambili. (Genesis 40:20; Maliko 6:21) Buku yochedwa Encyclopædia Britannica, inakamba kuti Akhristu oyambilila anali kutsutsa “miyambo yacikunja yokondwelela tsiku lakubadwa.”

Kodi Yesu anabadwa pa tsiku liti?

Baibo siikamba mwacindunji tsiku limene Yesu anabadwa. Buku yochedwa Cyclopedia imene McClintock na Strong analemba imati: “Tsiku limene Khristu anabadwa silipezeka mu Cipangano Catsopano kapena kwina kulikonse.” Kukamba zoona, ngati Yesu anali kufuna kuti otsatila ake azikondwelela tsiku lake la kubadwa, akanaonetsetsa kuti iwo adziŵa bwino-bwino tsiku limene iye anabadwa.

Caciŵili, Baibo siikamba kuti Yesu kapena wophunzila wake aliyense anali kukondwelela Khrisimasi. Buku yochedwa New Catholic Encyclopedia, inakamba kuti kukondwelela Khrisimasi kunachulidwa koyamba “mu kalenda ya zaka yaciroma yokonzedwa ndi Philocalus. Kalenda imeneyo ionetsa zocitika zoyambila mu 336 [C.E.].” Mwacionekele, apa n’kuti Baibo yonse italembedwa kale, ndipo patapita zaka zambili kucokela pamene Yesu anali padziko lapansi. Mpake kuti McClintock na Strong anati: “Kukondwelela Khrisimasi sikunacokele kwa Mulungu, ndipo sikucokela m’Malemba a Cipangano Catsopano.” *

Ni cocitika citi cimene Yesu anauza ophunzila ake kukumbukila?

Monga Mphunzitsi Waluso, Yesu anapatsa otsatila ake malangizo omveka bwino a zimene anayenela kucita. Malangizo amenewa ali m’Baibo. Koma iye sanawauze zakuti azikondwelela Khrisimasi. Mwacitsanzo, tica wa kusukulu safuna kuti ana ake a sukulu azipitilila zinthu zimene anawalangiza. Nayenso Yesu safuna kuti otsatila ake ‘azipitilila zinthu zolembedwa’ m’Malemba Oyela.—1 Akorinto 4:6.

Komabe, pali cocitika cimodzi capadela cimene Akhristu oyambilila anali kucidziŵa bwino—Cikumbutso ca imfa ya Yesu. Yesu anauza ophunzila ake mwacindunji kuti azicita mwambo umenewu ndipo anawaonetsa mmene ayenela kucitila. Malangizo acindunji amenewa, kuphatikizapo tsiku la imfa yake, zinalembedwa m’Baibo.—Luka 22:19; 1 Akorinto 11:25.

Monga mmene taonela, Khrisimasi ni kukondwelela tsiku la kubadwa, ndipo Akhristu oyambilila sanali kucita mwambo wacikunja umenewu. Kuwonjezela apo, Baibo siikamba kuti Yesu kapena munthu wina aliyense anali kukondwelela Khrisimasi. Cifukwa ca mfundo zimenezi, Akhristu ofika m’mamiliyoni zungulile dziko lonse aona kuti sayenela kukondwelela Khrisimasi.

^ par. 6 Kuti mudziŵe kumene miyambo yambili ya pa Khrisimasi inacokela, onani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi . . . Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Tiyenera Kudziwa pa Nkhani ya Khirisimasi?” mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2014. Ili pa intaneti pa www.pr418.com.