Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kufuna-funa Coonadi

Kufuna-funa Coonadi

Kudziŵa coonadi kungapulumutse moyo wathu. Mwacitsanzo, ganizilani mmene anthu apindulila cifukwa codziŵa coonadi pa funso lakuti, Kodi matenda oyambukila amafalikila bwanji?

Kwa zaka masauzande, palibe amene anali kudziŵa bwino mmene matenda amafalikilila. Ndipo milili ya matenda oyambukila inapha anthu mamiliyoni ambili pa nthawiyo. M’kupita kwa nthawi, asayansi anadziŵa zoona. Iwo anapeza kuti nthawi zambili matenda anali kubwela cifukwa ca tuzilombo toyambitsa matenda, monga mabakitiliya kapena mavailasi. Kudziŵa coonadi pa nkhaniyi kwathandiza anthu kupewa matenda ena ambili, komanso kucilitsa matenda ambili. Izi zathandiza kuti anthu ofika m’mabiliyoni akhale na umoyo wathanzi, komanso moyo wotalikilapo.

Kodi muganiza kuti mungapindule bwanji ngati mwadziŵa mayankho a zoona pa mafunso aya?

  • Kodi Mulungu n’ndani?

  • Kodi Yesu Khristu n’ndani?

  • Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani?

  • Kodi kutsogolo kuli ciani?

Anthu ofika mamiliyoni apeza mayankho pa mafunso amenewa, ndipo izi zaŵathandiza kukhala umoyo waphindu. Na imwe mungapindule ngati mwadziŵa mayankho ake.

KODI N’ZOTHEKADI KUPEZA COONADI?

Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi n’zothekadi kudziŵa coonadi pa nkhani ina yake?’ N’zosadabwitsa kufunsa funso limeneli cifukwa masiku ano n’zovuta kudziŵa zoona pa nkhani zambili. Cifukwa ciani?

Anthu ambili cimawavuta kukhulupilila zokamba za maboma, amalonda, kapena ofalitsa nkhani. Zili conco cifukwa pamene nkhani zina zofalitsidwa zimakhala zoona, zina zimakhala maganizo cabe a anthu, zina zimakhala zopotoza pang’ono, pamene zina zimakhala mabodza amkunkhuniza. Cifukwa ca kusakhulupililana kwa anthu na kuculuka kwa mabodza, anthu ambili amalephela kugwilizana ngakhale pa mfundo zeni-zeni, kapenanso pa mapindu ake.

Ngakhale n’conco, n’zotheka kupeza mayankho a zoona pa mafunso ofunika kwambili mu umoyo. Motani? Mwa kucita zimene mumacita nthawi zonse pofuna kupeza mayankho pa mafunso ena amene mumakhala nawo pa umoyo wa tsiku na tsiku.

TONSE TIMAFUNA-FUNA COONADI

M’njila ina, tingati mumasakila coonadi tsiku na tsiku. Ganizilani za mayi wina dzina lake Jessica. Iye anati: “Mwana wanga wamkazi amadwala kwambili akadya nshaŵa, cakuti ngakhale m’zakudya mukhale gawo locepa la nshaŵa, akhoza kufa.” Conco, Jessica amafunika kutsimikiza kuti m’zakudya zimene afuna kugula mulibe mbali iliyonse ya nshaŵa. Iye anati: “Coyamba, nimaŵelenga mosamala mawu ofotokoza zimene anasakaniza kuti apange zakudyazo. Ndiyeno nimapitiliza kufufuza, ngakhale kutuma foni ku kampani yopanga zakudyazo kuti atsimikizile ngati sizinasakanizike na nshaŵa mwangozi popanga. Nimafufuzanso kwa ena odalilika kuti atsimikizile ngati kampaniyo imayesetsa kutsatila malangizo popanga zakudya.”

Mwina mafunso amene mumakhala nawo tsiku na tsiku si okhudza nkhani yaikulu monga mmene zinalili kwa Jessica. Koma mofanana na Jessica, mungacite zotsatilazi kuti mupeze mayankho pa mafunso amene muli nawo:

  • Dziŵani zeni-zeni.

  • Fufuzani.

  • Tsimikizani kuti magwelo anu ni odalilika.

Njila imeneyi ingakuthandizeninso kupeza mayankho a zoona pa mafunso ofunika kwambili mu umoyo. Motani?

BUKU LAPADELA LA COONADI

Pofuna-funa mayankho pa mafunso ofunika kwambili mu umoyo, Jessica anaseŵenzetsa njila yofanana na imene amaseŵenzetsa pofufuza zakudya zoyenelela malinga na vuto la mwana wake. Iye anati: “Kuŵelenga Baibo mosamala na kulimbikila kufufuza, zinanithandiza kupeza mayankho a zoona.” Mofanana na Jessica, anthu ofika m’mamiliyoni adziŵa zimene Baibo imakamba pa mafunso otsatilawa:

  • N’cifukwa ciani tili na moyo?

  • N’ciani cimacitika munthu akafa?

  • N’cifukwa ciani pa dzikoli pali mavuto?

  • Kodi Mulungu akucita ciani kuti acotsepo mavuto onse?

  • Kodi tingacite ciani kuti tikhale na banja lacimwemwe?

Mungapeze mayankho a zoona pa mafunso amenewa ndi ena, mwa kuŵelenga Baibo na kufufuza pa webusaiti ya www.pr418.com.