NSANJA YA MLONDA Na. 2 2019 | Kodi Moyo Ukali na Phindu kwa Ine?
Kodi pali cocitika cimene cinakuvutitsani kwambili maganizo, cakuti munayamba kukaikila ngati moyo uli na phindu?
Pamene Umoyo Wafika Posapililika
Moyo ni waphindu mosasamala kanthu za vuto lililonse lalikulu limene tingakumane nalo.
Tsoka Likagwa
Baibo imapeleka citsogozo cofunikila, cimene cingakuthandizeni kupilila mavuto obwela cifukwa ca tsoka.
Munthu Wokondedwa Akamwalila
Onani njila 5 zimene zingakuthandizeni kupilila imfa ya munthu amene mumam’konda.
Pamene Mnzanu wa m’Cikwati Sayenda Bwino
Ambili amene mnzawo wa m’cikwati sanali kuyenda bwino, apeza citonthozo m’Malemba.
Pamene Mwadwala Matenda Aakulu
Dziŵani mmene ena anakwanitsila kupilila pamene anadwala matenda aakulu.
Mukafika Pakuti Simufunanso Kukhala na Moyo
Kodi munavutikapo kwambili maganizo cakuti munafuna kudzipha? Nanga kodi mungapeze kuti thandizo?
Inde, Moyo Ukali na Phindu kwa Imwe!
Ngakhale kuti ena sangamvetsetse bwino-bwino kukula kwa vuto limene mwakumana nalo, dziŵani kuti Mulungu amakudelani nkhawa ndipo amafuna kukuthandizani.
Iye “Amakudelani Nkhawa”
Mavesi a m’Baibo amenewa angakutonthozeni na kukulimbitsani.