Tsoka Likagwa
NGATI tsoka linakugwelamponi, ndiye kuti mungamvetse mmene ena anamvelela tsoka litaŵagwela. Iwo amakhala odabwa kwambili, sakhulupilila, amavutika maganizo, nkhawa, komanso kucita mantha. Ambili amene anapulumuka tsoka, amavutika maganizo komanso kulefuka. Ndipo amakhala alibe cifuno copitiliza kukhala na moyo.
Ngati zinthu zanu zonse zinawonongeka pa tsoka, mwina mungaone kuti umoyo wafika posapililika. Mungayambe kuona kuti moyo wanu ulibe phindu. Komabe, Baibo imafotokoza kuti moyo wanu ni wofunika, ndipo mungakhale na zifukwa zabwino zoyembekezela tsogolo labwino.
KUDZIŴA COONADI CA M’BAIBO KUMAPANGITSA MOYO KUKHALA WAPHINDU
Mlaliki 7:8 imati: “Mapeto a cinthu amakhala bwino kuposa ciyambi cake.” Tsoka likangocitika kumene, zingaoneke monga kuti umoyo wanu sudzakhalanso bwino. Koma mukalimbikila kukonzanso zinthu pang’ono-pang’ono, umoyo wanu udzakhalanso bwino.
Baibo imakambilatu za nthawi pamene ‘sikudzamvekanso kulila kokweza mawu kapena kulila kwacisoni.’ (Yesaya 65:19) Izi zidzacitika dziko lapansi likadzakonzedwa kukhala paradaiso mu Ufumu wa Mulungu. (Salimo 37:11, 29) Masoka adzakhala zinthu zakale. Zinthu zonse zotivutitsa maganizo, komanso zotibweletsela cisoni zidzafafanizika m’maganizo mwathu kwamuyaya. Izi zidzacitikadi, cifukwa Mulungu Wamphamvuzonse anatilonjeza kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukilidwanso ndipo sizidzabwelanso mumtima.”—Yesaya 65:17.
Tangoganizilani cabe, Mlengi wathu wakonza zakuti ‘mukhale ndi ciyembekezo, komanso tsogolo labwino.’ Ndithudi, udzakhala umoyo wabwino kwambili mu ulamulilo wangwilo wa Mulungu. (Yeremiya 29:11) Kodi kudziŵa zimenezi kungakuthandizeni kuona moyo wanu kukhala wofunika? Sally, amene tam’chula m’nkhani yoyamba, anati: “Kuganizila zinthu zosangalatsa zimene Ufumu wa Mulungu udzaticitila kutsogolo, kungakuthandizeni kuiŵala mavuto akumbuyo, na kupilila amene mukukumana nawo pali pano.”
Kodi na imwe simungakonde kuphunzila zambili zimene Ufumu wa Mulungu udzacitila anthu posacedwa? Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuona kuti, mosasamala kanthu za tsoka limene linakucitikilani, moyo wanu ni wofunika ngakhale pali pano, pamene mukuyembekezela mwacidwi tsogolo lopanda tsoka lililonse. Ndipo Baibo ili na malangizo amene angakuthandizeni kupilila zovuta zimene tsoka linakubweletselani. Onani zitsanzo zocepa cabe pa peji yotsatila.