Pamene Umoyo Wafika Posapililika
Mwacitsanzo, Sally * wa ku America, katundu wake wambili unawongedwa na cimphepo ca camkuntho cochedwa hurricane. Iye anafotokoza kuti: “N’nali kuona kuti siningakwanitse kupilila vuto limeneli.”
Nanga bwanji munthu amene mumam’konda akamwalila? Janice wa ku Australia anakamba kuti: “Ana anga aŵili aamuna atamwalila, ninamva kupweteka kwambili mumtima. N’nalibe na mphamvu ndipo n’nathedwa nzelu. N’nacondelela Mulungu kuti: ‘Conde, siningakwanitse kupilila, vuto ili lanikulila msinkhu! Lekani kuti nife cabe. Sinifuna kuti maŵa nikakhalenso na moyo.’”
Koma kwa Daniel, cinamuŵaŵa kwambili atadziŵa kuti mkazi wake sanali kuyenda bwino. Iye anati: “Pamene mkazi wanga anaulula kuti anali kucita zaciwelewele, zinali monga kuti wanilasa na mpeni kumtima. Ndipo kwa miyezi ingapo, nthawi zambili n’nali kumva kupweteka kumeneku.”
Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda idzafotokoza mmene moyo ungakhalile waphindu ngakhale pamene
Koma coyamba, kodi tingapilile motani tsoka likatigwela?
^ Maina ena m’nkhanizi asinthidwa.