Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacita Zotani?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzacita Zotani?

Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kupemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele. Iye anadziŵa kuti zoipa zimene zimacitika padziko lapansi si cifunilo ca Mulungu. Ndipo Ufumu wa Mulungu cabe ndiye boma limene lingacotsepo mavuto amenewa. Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita zotani?

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU WACITA KALE

M’nkhani yapita, taona cizindikilo cimene Yesu anapeleka. Cizindikilo cimeneci ni umboni wooneka bwino wakuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba, ndipo Yesu Khristu ndiye Mfumu yake.

Baibo imatiuza kuti Yesu atangotenga mphamvu za Ufumu, anacotsa Satana na ziŵanda zake kumwamba. Zocita zawo tsopano zimakhudza cabe dziko lapansi. Ndipo cimeneci n’cimodzi mwa zifukwa zopangitsa kuti zinthu ziziipila-ipila kucokela mu 1914.—Chivumbulutso 12:7, 9.

Ngakhale kuti zinthu m’dzikoli zikuipila-ipila, Yesu monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu wacita zinthu zothandiza anthu kuzungulila dziko lonse. Cifukwa ca nchito ya padziko lonse yophunzitsa anthu Baibo, ambili aphunzila kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo mu umoyo wawo wa tsiku na tsiku. (Yesaya 2:2-4) Anthu ofika m’mamiliyoni aphunzila kuona nchito moyenela, mmene angakhalile na banja lacimwemwe, komanso kukondwela na zinthu zakuthupi popanda kukhala akapolo a zinthuzo. Anthu amenewa akuphunzila zimene angacite kuti zinthu ziziwayendela bwino, ndipo asintha na kukhala anthu amene Mulungu afuna kuti akakhale nzika za Ufumu wake.

NANGA KUTSOGOLO UFUMU WA MULUNGU UDZACITA ZOTANI?

Ngakhale kuti Yesu akulamulila kumwamba, maboma a anthu akali kulamulila padziko lapansi. Komabe, Mulungu anauza Yesu kuti: “Pita ukagonjetse anthu pakati pa adani ako.” (Salimo 110:2) Posacedwa, Yesu adzawononga kothelatu onse otsutsa ndipo adzabweletsa mpumulo kwa amene amamvela Mulungu.

Posacedwa, Ufumu wa Mulungu udzacitapo kanthu mwa

  • Kuwononga cipembedzo conyenga. Zipembedzo zimene zimaphunzitsa mabodza ponena za Mulungu, komanso kupangitsa anthu kukhala pa mavuto zidzawonongedwa. Baibo imafotokoza kuti zipembedzo zonyenga zili monga hule. Ndipo kuwonongedwa kwake kudzadabwitsa ambili.—Chivumbulutso 17:15, 16.

  • Kuthetsa ulamulilo wa anthu. Ufumu wa Mulungu udzacitapo kanthu na kuthetsa maulamulilo onse a anthu.—Chivumbulutso 19:15, 17, 18

  • Kucotsapo anthu oipa. Nanga bwanji za anthu okonda kucita zoipa, ndipo amakana kumvela Mulungu? Baibo imati: “Koma oipa adzacotsedwa padziko lapansi.”—Miyambo 2:22.

  • Kucotsapo Satana na ziŵanda. Satana na ziŵanda zake ‘sadzasoceletsanso mitundu ya anthu.’—Chivumbulutso 20:3, 10.

Kodi pambuyo pa zonsezi zinthu zidzakhala bwanji kwa anthu amene amavomeleza Ufumu wa Mulungu?

ZIMENE UFUMU WA MULUNGU UDZACITILA ANTHU

Monga Mfumu kumwamba, Yesu adzakwanitsa kucita zambili kuposa munthu wina aliyense wolamulila. Iye adzalamulila pamodzi ndi a 144,000 monga omuthandiza, amene anasankhidwa pakati pa anthu. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3) Adzaonetsetsa kuti cifunilo ca Mulungu cacitika pansi pano. Kodi n’ciani cimene Ufumu wa Mulungu udzacitila anthu padziko lapansi?

  • Udzacotsapo matenda na imfa. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala,’” ndipo “imfa sidzakhalaponso.”—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4.

  • Udzabweletsa bata na mtendele weni-weni. “Mtendele wa ana ako udzakhala woculuka,” ndipo “aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.”—Yesaya 54:13; Mika 4:4.

  • Udzapatsa anthu nchito zokhutilitsa. “Anthu anga osankhidwa mwapadela adzapindula mokwanila ndi nchito ya manja awo. Sadzagwila nchito pacabe.”—Yesaya 65:22, 23.

  • Udzathetsa mavuto azacilengedwe. “Cipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dela lacipululu lidzakondwa ndipo lidzacita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”—Yesaya 35:1.

  • Udzaphunzitsa anthu zimene afunika kucita kuti akakhale kwamuyaya. “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

Mulungu afuna kuti mukakondwele na madalitso amenewa. (Yesaya 48:18) Nkhani yokonkhapo idzafotokoza zimene mungacite palipano kuti mukhale na ciyembekezo ca tsogolo labwino limeneli.