Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nanga N’ndani Amapangitsa Mavuto?

Nanga N’ndani Amapangitsa Mavuto?

Ngati Mulungu si ndiye amapangitsa mavuto, nanga n’ndani amapangitsa kuti pakhale njala yosatha, kuphana mwankhanza pa nkhondo, matenda olemalika, komanso masoka a zacilengedwe? Mau a Mulungu, Baibo, amafotokoza zinthu zitatu zimene zimapangitsa anthu kuvutika:

  1. Dyela, Umbombo, Cidani. “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.” (Mlaliki 8:9) Nthawi zambili anthu amavutika cifukwa cakuti anthu opanda ungwilo, adyela, kapena ankhanza amacitila anzawo zinthu zopanda cilungamo.

  2. Nthawi ya Tsoka na Zinthu Zosayembekezeleka. Anthu amavutika cifukwa ‘nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka zimawagwela.’ (Mlaliki 9:11) Izi zitanthauza kuti anthu angapezeke m’ngozi mwatsoka cabe. Nthawi zina, n’cifukwa cocita zinthu mosasamala, kapena molakwitsa.

  3. Wolamulila Woipa wa Dzikoli. Baibo imaonetsa bwino-bwino amene amapangitsa mavuto ambili a anthu. Imati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) “Woipayo” ni Satana Mdyelekezi, colengedwa cauzimu camphamvu, amene paciyambi anali mngelo wa Mulungu, koma “sanakhazikike m’coonadi.” (Yohane 8:44) Zolengedwa zina zauzimu zinagwilizana na Satana kupandukila Mulungu, n’colinga cofuna kukhutilitsa zilako-lako zawo zadyela, ndipo zinakhala ziwanda. (Genesis 6:1-5) Kucokela pamene Satana na ziwanda zake anapanduka, iwo ali na cisonkhezelo coipa komanso camphamvu pa zocitika za m’dzikoli. Izi zionekela bwino maka-maka masiku ano. Pali pano, Mdyelekezi ni wokwiya kwambili. Iye “akusoceletsa dziko lonse lapansi,” ndipo zotulukapo zake ni ‘matsoka pa dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 12:9, 12) Ndithudi, Satana ni wolamulila wankhanza. Amakondwela kwambili kuona anthu akuvutika. Conco, Satana ndiye amapangitsa anthu kuvutika, osati Mulungu.

GANIZILANI IZI: Munthu wouma mtima komanso wankhanza ndiye amene angapangitse anthu osalakwa kuvutika. Mosiyana na Satana, Baibo imati: “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8.) Mogwilizana na khalidwe lake lacikondi, “Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.”—Yobu 34:10.

Koma mungafunse kuti, ‘Kodi Mulungu Wamphamvu zonse adzalola ulamulilo woipa wa Satana mpaka liti?’ Monga mmene taonela, Mulungu amadana na zinthu zoipa, ndipo cimamuŵaŵa kwambili akaona kuti tivutika. Kuwonjezela apo, Mau ake amati: ‘M’tulileni nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Mulungu amatikonda, komanso ali na mphamvu zocotsapo mavuto onse na kupanda cilungamo, monga mmene nkhani yotsatila idzafotokozela. *

^ Kuti mudziŵe zambili za cifukwa cimene Mulungu walolela mavuto, onani phunzilo 26 m’buku yakuti, Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! yopangiwa na Mboni za Yehova ndipo mungaicite daunilodi mahala pa webusaiti ya www.pr418.com.