Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kudziŵa Kulamulila Mtima Wathu

Kudziŵa Kulamulila Mtima Wathu

Baibo imaticenjeza kuti tifunika kupewa makhalidwe ovulaza, ndipo imatilimbikitsa kukhala na makhalidwe abwino.

MKWIYO

MFUNDO YA M’BAIBO: “Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.”—Miyambo 16:32.

TANTHAUZO LAKE: Kuyesetsa kulamulila mkwiyo wathu kumatipindulitsa. Ngakhale kuti nthawi zina tingakwiye pa zifukwa zomveka, mkwiyo wosalamulilika ni wowononga. Ofufuza masiku ano amakamba kuti munthu akakwiya, nthawi zambili amakamba, kapena kucita zinthu zimene pambuyo pake zingamuvutitse maganizo.

ZIMENE MUNGACITE: Phunzilani kulamulila mkwiyo wanu, usanayambe kukulamulilani. Ena amaganiza kuti munthu akakhala wamkwiyo wosalamulilika ndiye kuti ni wamphamvu. Koma m’ceni-ceni ni wopanda mphamvu. Baibo imati: “Munthu wosaugwila mtima ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa, n’kuusiya wopanda mpanda.” (Miyambo 25:28) Njila yabwino yolamulilila mkwiyo wanu ni kumvetsetsa bwino-bwino zimene zacitika, musanakambe kapena kucita ciliconse. Baibo imakamba kuti: “Kuzindikila kumacititsa munthu kubweza mkwiyo wake.” (Miyambo 19:11) Tingacite bwino kumvetsetsa mbali zonse za nkhaniyo. Zimenezi zingatithandize kubweza mkwiyo.

KUYAMIKILA

MFUNDO YA M’BAIBO: “Sonyezani kuti ndinu oyamikila.”—Akolose 3:15.

TANTHAUZO LAKE: Ena amati munthu woyamikila yekha ndiye angakhale wacimwemwe. Ngakhale anthu ena amene anakumanapo na mavuto akulu-akulu monga kufeledwa, amavomeleza zimenezi. Iwo amakamba kuti cothandiza ni kupewa kuganizila kwambili pa zimene anataikilidwa, koma kuika maganizo awo pa zimene ali nazo na kukhala oyamikila pa zimenezo.

ZIMENE MUNGACITE:Tsiku lililonse, lembani zinthu zimene mungakhalile woyamikila. Zinthuzi sikuti zifunika kukhala zikulu-zikulu. Khalani oyamikila ngakhale pa zinthu zing’ono-zing’ono monga kukongola kwa dzuŵa pamene ikutuluka, maceza abwino na anthu amene mumakonda, kapena kuyamikila cifukwa cokhala na moyo pa tsikulo. Kupeza nthawi yoganizila zinthu zimenezi na kukhala woyamikila, kungakuthandizeni kukhala wacimwemwe.

Zingakhale zopindulitsa kuganizila zifukwa zimene mumaŵakondela abululu anu na mabwenzi anu. Mukazindikila zimene mumakonda mwa anthu ena, auzeni zimenezo. Kaya mwacindunji, kuŵalembela kalata, imelo, kapena meseji. Mosakaikila, kucita izi kudzalimbitsa ubwenzi wanu na iwo, ndipo kudzakupangitsani kukhala na cimwemwe cobwela cifukwa ca kupatsa.—Machitidwe 20:35.

MFUNDO ZINA ZA M’BAIBO

Mungacite daunilodi Baibo yomvetsela m’citundu cimene mudziŵa. Mungaipeze mu vitundu 40 pa jw.org

PEWANI MIKANGANO.

“Ciyambi ca mkangano cili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo. Conco mkangano usanabuke, cokapo.”​—MIYAMBO 17:14.

PEWANI NKHAWA ZOSAFUNIKILA ZOKHUDZA ZA KUTSOGOLO.

“Musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.”​—MATEYU 6:34.

MUKAKWIYA, GANIZILANI MOSAMALA ZA NKHANIYO MUSANACITE CILICONSE.

“Kuganiza bwino kudzakuyang’anila, ndipo kuzindikila kudzakuteteza.”​—MIYAMBO 2:11.