Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Thanzi Labwino

Thanzi Labwino

Ngakhale kuti Baibo si buku la zacipatala, ili na malangizo amene angatithandize kukhala na umoyo wathanzi. Onani mfundo za m’Baibo izi zimene zingakuthandizeni kukhala na thanzi labwino la kuthupi.

SAMALILANI THUPI LANU

MFUNDO YA M’BAIBO: “Palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” —Aefeso 5:29.

TANTHAUZO LAKE: Mfundo ya m’Baibo imeneyi, itilimbikitsa kucita zimene tingathe pofuna kusamalila thanzi lathu. Kafuku-fuku wina anaonetsa kuti matenda ambili amene anthu amadwala, amabwela cifukwa ca zimene amasankha kucita. Conco, kupanga zosankha mwanzelu kungakuthandizeni kukhala na thanzi labwino.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Zakudya. Sankhani kudya zakudya zopatsa thanzi komanso muzimwa madzi okwanila.

  • Maseŵela Olimbitsa Thupi. Maseŵela amenewa angakuthandizeni kukhala na thanzi labwino, mosasamala kanthu za msinkhu wanu. Mungapindule olo kuti ndimwe olemala kapena mudwala matenda okhalitsa. Anthu okukondani komanso madokotala, angakuthandizeni kucita maseŵela olimbitsa thupi. Koma kuti izi zitheke zidalila imwe.

  • Muzigona Mokwanila. Kusagona mokwanila kwa nthawi yaitali kungapangitse munthu kudwala matenda aakulu. Anthu ambili amasankha kucita zinthu zina pa nthawi imene afunika kugona. Izi zimaŵalepheletsa kugona mokwanila. Ngati mugona mokwanila, ndiye kuti mudzakhala na thanzi labwino.

LEKANI ZIZOLOŴEZI ZOIPA

MFUNDO YA M’BAIBO: “Tiyeni tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi kapena mzimu.”—2 Akorinto 7:1.

TANTHAUZO LAKE: Timakhala na thanzi labwino pamene tipewa zinthu zowononga thupi lathu, monga fodya. Zinthuzi n’zimene kaŵili-kaŵili zimabweletsa matenda na imfa.

ZIMENE MUNGACITE: Sankhani deti imene mufuna kuti mukaleke kukoka fodya, ndipo ikani cizindikilo pa detiyo pa kalenda yanu. Tsikulo lisanafike, tayani fodya, totsalila twa ndudu tumene ena amati tumashiki, komanso zonse zokhudzana ndi cizoloŵezi cowononga cimeneci. Pewani kupezeka kumalo kumene ena amakoka fodya. Ndiyeno uzani anzanu amene angakucilikizeni pa cosankha canu.

MFUNDO ZINA ZA M’BAIBO

Kuti mukhale na Baibo yanu, mungaonane na wa Mboni za Yehova wa m’dela lanu

CITANI ZINTHU MOSAMALA KUTI MUPEWE NGOZI.

“Ukamanga nyumba yatsopano uzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopela kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kucokela padengapo.”​——DEUTERONOMO 22:8.

LAMULILANI MKWIYO WANU.

“Wosafulumila kukwiya n’ngozindikila zinthu kwambili, koma wokwiya msanga amalimbikitsa ucitsilu.”​—MIYAMBO 14:29.

PEWANI KUDYA KWAMBILI.

“Usakhale pakati pa anthu . . . odya nyama mosusuka.”​—MIYAMBO 23:20.