Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Pali Ciyembekezo Cakuti Akufa Adzauka?

Kodi Pali Ciyembekezo Cakuti Akufa Adzauka?

Imfa imakhudza aliyense wa ife. Koma kodi imfa ndiye mapeto a zonse? Kodi akufa basi anaiŵalika? Kodi pali ciyembekezo cakuti akufa adzauka?

ONANI ZIMENE BAIBO IMAKAMBA:

AKUFA SANAIŴALIKE

“Onse ali m’manda acikumbutso . . . adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.

Inde, Mulungu adzaukitsa onse amene akuwambukila.

AKUFA ADZAUKA PA DZIKO LAPANSI

“Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.

Anthu ofika m’mabiliyoni adzaukitsidwa ali na ciyembekezo codzakhala na moyo wamuyaya, komanso wamtendele woculuka.

TINGAKHULUPILILEDI KUTI AKUFA ADZAUKA

“[Mulungu] amawelenga nyenyezi zonse, ndipo zonsezo amazichula mayina ake.”—Salimo 147:4.

Popeza Mulungu amatha kuchula nyenyezi iliyonse na dzina lake, si nkhani kwa iye kukumbukila anthu amene afuna kudzawaukitsa.