Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi kutalikitsa moyo wa maselo a munthu ndiye cinsinsi cokhalila na moyo wautali?

Kufuna-funa Moyo Wautali

Kufuna-funa Moyo Wautali

“Ndaona nchito imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azigwila. Ciliconse iye anacipanga cokongola ndiponso pa nthawi yake. Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”Mlaliki 3:10, 11.

MAWU akale-kale a Mfumu Solomo amenewa, aonetsa bwino mmene anthu amamvelela ponena za moyo. Mwina cifukwa cakuti moyo ni waufupi ndipo imfa ni yosapeweka, anthu akhala akufunitsitsa kukhala na moyo wautali. Ndipo kwa zaka zambili, akhala akufuna-funa njila yotalikitsila moyo.

Mwacitsanzo, ganizilani za Gilgamesh mfumu ya ku Sumeri. Nthano zambili za umoyo wake zinalembedwa. Ndipo nthano ina yopezeka m’buku la nthano za Gilgamesh, imafotokoza kuti iye anaika moyo wake pangozi pofuna kupeza njila yothaŵila imfa, koma analephela.

Wasayansi wakale m’cipinda cake ca zasayansi

Ca m’ma 300 B.C.E., asayansi a ku China anayesa kupanga msanganizo wa mankhwala, ndipo anthu anali kukhulupilila kuti mankhwala amenewo angatalikitse moyo. Iwo anasakaniza mankhwala a mercury na mankhwala ena ake ochedwa arsenic. Akuti mankhwala amenewo anapha mafumu ambili a ku China. Pakati pa zaka za m’ma 500 C.E. na 1500 C.E., asayansi ena ku Europe anayesa kupanga golide waufa wakuti azisungunuka munthu akameza. Anaganiza kuti cifukwa golide siicita nguwe, mphamvu yake imeneyo ingatalikitse moyo wa munthu.

Masiku ano, asayansi ena odziŵa za maselo komanso odziŵa za majini, akuyesa-yesa kupeza cimene cimayambitsa ukalamba. Zoyesa-yesa za asayansi zionetsa kuti anthu akali na ciyembekezo, cakuti adzapeza ndithu njila yopewela ukalamba na imfa. Koma kodi zotulukapo za kafuku-fuku wawo zakhala zotani?

MULUNGU “ANAPATSA ANTHU MTIMA WOFUNA KUKHALA NDI MOYO MPAKA KALEKALE.”—MLALIKI 3:10, 11

KUYESA-YESA KUPEZA COYAMBITSA UKALAMBA

Asayansi odziŵa za maselo a munthu, amapeleka zifukwa zosiyana-siyana zopitilila 300 pa za cifukwa cake timakalamba na kufa. M’zaka zapita, asayansi akwanitsa kutalikitsa moyo wa maselo a nyama komanso anthu. Kaamba ka ici, anthu olemela apeleka ndalama kwa asayansi kuti apeze “cifukwa cake timafa.” Kodi iwo acita zotani pa kafuku-fuku wawo?

Kuyesa Kutalikitsa Moyo. Akatswili ena a thupi la munthu amakhulupilila kuti ukalamba kweni-kweni umayambila m’majini athu. Majini amenewa ni omanga ku mapeto kwake monga nthambo za nsapato. Mapeto omanga amenewa amachedwa telomeres. Iwo amateteza malangizo opangitsa kuti maselo atsopano azipangika. Pamene maselo atsopano akupangika, nawonso mapeto omanga a telomeres amafupika. Pothela pake maselo atsopano amaleka kupangika, ndico cimakhala ciyambi ca ukalamba.

Mu 2009, Elizabeth Blackburn anapatsidwa mphoto pa nchito yake ya sayansi. Iye na anzake anapeza puloteni inayake m’thupi la munthu, yochedwa enzyme. Iwo anati puloteni imeneyi imacedwetsa kufupika kwa ma telomeres, cifukwa kufupika kwake n’kumene kumapangitsa ukalamba. Koma iwo anavomeleza kuti ma telomeres “satalikitsa moyo mozizwitsa, ndipo sangatalikitse moyo kupitilila pa zaka zimene anthu amayembekezeka kukhala na moyo masiku ano.”

Kukonzanso maselo, ni njila ina yopewela ukalamba. Maselo athu akakalamba kwambili cakuti n’kulephela kuculukana, iwo amayamba kutumiza mauthenga olakwika ku maselo oyandikana nawo, amene amagwebana na matenda. Izi zingapangitse munthu kuvimba, kumvela kuŵaŵa kosalekeza, komanso matenda ena. Caposacedwa, asayansi ku France anayesa kukonzanso maselo otengedwa kwa okalamba, ndipo okalamba ena anali na zaka zopitilila 100. Pulofesa Jean-Marc Lemaître, amene anali mtsogoleli pa kafuku-fuku ameneyo anati zimene anapeza zinaonetsa kuti “n’zotheka kuletsa ukalamba” m’maselo.

KODI SAYANSI INGATALIKITSEDI MOYO WATHU?

Olo kuti pali njila zambili zoletsela ukalamba, asayansi ambili amavomeleza kuti sitingakhale na moyo wautali kuposa pa zaka zimene timakhala na moyo masiku ano. N’zoona kuti kuyambila m’zaka za m’ma 1800, zaka zimene anthu amayembekezeledwa kukhala na moyo zawonjezekako. Koma kweni-kweni, izi zatheka cifukwa cakuti anthu amakhala aukhondo, komanso cifukwa ca njila zina zopewela matenda opatsilana, komanso akatemela ocinjiliza anthu ku matenda. Asayansi ena oona za majini, amati anthu sangakhale na moyo kupitilila pa zaka zimene amayembekezeledwa kukhala.

Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, wolemba Baibo Mose anakamba kuti: “Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70, ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadela amakwana zaka 80. Koma ngakhale zili conco, amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka. Pakuti masiku amene timakhala ndi moyo amatha mwamsanga ndipo timacoka mofulumila.” (Salimo 90:10) Ngakhale kuti anthu ayesa-yesa kutalikitsa moyo, kweni-kweni timakhala na moyo monga mmene Mose anafotokozela.

Koma zolengedwa zina monga fulu, komanso mtundu wina wa nkhono za m’madzi, zingakhale na moyo kupitilila zaka 200. Ndipo mitengo ina monga mtengo wa malambe, ingakhale na moyo kwa zaka masauzande. Tikaganizila kuculuka kwa zaka zimene zolengedwa izi zimakhala na moyo komanso zolengedwa zina, tingadzifunse kuti, ‘Kodi moyo ni uno cabe umene ulipo wokhala na moyo zaka 70 kapena 80?’