Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Palibe Angathaŵe Imfa

Palibe Angathaŵe Imfa

GANIZILANI kuti mutamba filimu ya munthu wina wake wochuka, mwina katswili woimba nyimbo amene mumakonda. Filimuyo iyamba na kuonetsa munthuyo ali mwana, akuphunzila nyimbo, komanso kuyeseza kwake mobweleza-bweleza. Ndiyeno muona katswiliyo akuimba m’malo osiyana-siyana, akuyenda m’maiko ambili, ndipo akuchuka pa dziko lonse. Posapita nthawi, munthuyo afika m’zaka zaukalamba, ndipo pamene filimuyo ikutha iye amwalila.

Cocitika ici sicopeka, ndipo cionetsa zimene zimacitikadi. Kaya munthuyo akhale woimba, wasayansi, wocita maseŵela othamanga, kapena munthu wina aliyense wochuka, mapeto ake akanakhala cimodzi-modzi. Munthuyo anacita zinthu zambili zabwino. Koma ganizilani za kuculuka kwa zimene akanacita sembe sanakalambe na kumwalila.

Inde, imfa ni yoipa kwambili. Ndipo tonse tsiku lina tidzafa ndithu. (Mlaliki 9:5) Olo tiyesetse bwanji, sitingathaŵe ukalamba na imfa. Ndipo mwina tingafe mwadzidzidzi pa ngozi, kapena kumwalila cifukwa ca matenda. Monga mmene Baibo imakambila, tili monga nkhungu “yongoonekela kanthawi kenako n’kuzimililika.”—Yakobo 4:14.

Kwa ena moyo umaoneka monga ulibe phindu, cakuti amayendela mfundo yakuti “tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.” (1 Akorinto 15:32) Anthu amakhala umoyo umenewo cifukwa amadziŵa kuti tsiku lina adzafa, ndipo alibe ciyembekezo ca kutsogolo. Mukakumana na vuto lalikulu, mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi moyo ni uno cabe umene ulipo?’ Nanga mungapeze kuti yankho pa funso imeneyi?

Ambili amaganiza kuti sayansi ingapeleke yankho. Kupita patsogolo kwa sayansi komanso za mankhwala kumathandizadi kutalikitsa moyo pang’ono. Ndipo asayansi ena akuyesa-yesa kupezanso njila zina zotalikitsila moyo. Koma pa zonse zimene asayansi ayesa kucita, mafunso awa sayankhidwa: N’cifukwa ciani timakalamba na kumwalila? Kodi pali ciyembekezo cakuti imfa monga mdani wathu adzagonjetsedwa? Nkhani zotsatila zidzayankha mafunso amenewa, kuphatikizapo funso lakuti: Kodi moyo ni uno cabe umene ulipo?