Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mdani Wathu Imfa, Adzagonjetsedwa Bwanji?

Kodi Mdani Wathu Imfa, Adzagonjetsedwa Bwanji?

NGAKHALE kuti kusamvela kwa makolo athu oyambilila Adamu na Hava, kunapangitsa kuti tonse tikhale ocimwa komanso kuti tizimwalila, izi sizinasinthe colinga ca Mulungu cokhudza anthu. Kupitila m’Mawu ake Baibo, Mulungu mobweleza-bweleza amagogomeza kuti colinga cake sicinasinthe.

  • “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” Salimo 37:29.

  • “Iye adzameza imfa kwamuyaya ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.”Yesaya 25:8.

  • “Imfa nayonso, monga mdani womalizila, idzawonongedwa.”1 Akorinto 15:26.

  • “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”Chivumbulutso 21:4.

Kodi Mulungu “adzameza imfa” kapena ‘kuiwononga’ motani? Monga taonela, Baibo imakamba momveka bwino kuti ‘olungama adzakhala kwamuyaya.’ Koma imakambanso kuti “palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amacita zabwino zokhazokha.” (Mlaliki 7:20) Koma pofuna kugonjetsa imfa, kodi Mulungu adzangonyalanyaza miyezo yake na kulola anthu ocimwa kukapeza moyo wosatha? Kutali-tali! Iye amasunga miyezo yake yapamwamba, sadzacita zimenezo, cifukwa “Mulungu . . . sanganame.” (Tito 1:2) Nanga kodi Mulungu adzacita ciani kuti akwanilitse colinga cake cimene analengela anthu?

MULUNGU “ADZAMEZA IMFA KWAMUYAYA.”—YESAYA 25:8

KUGONJETSA IMFA MWA KULIPILA DIPO

Yehova Mulungu anapanga makonzedwe acikondi kuti awombole anthu ku imfa mwa kulipila dipo. Dipo ni malipilo okwanila pa mtengo wa cinthu cimene cawonongedwa, kapena malipilo opelekedwa kuwombola munthu kapena cinthu cina cake. Popeza kuti anthu onse ni ocimwa ndipo cilango cawo ni imfa, Baibo imakamba mosapita mbali kuti: “Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola m’bale wake, kapena kumupelekela dipo kwa Mulungu, (ndipo malipilo owombolela moyo wawo ndi amtengo wapatali, moti munthu sangathe kuwapeleka mpaka kalekale).”—Salimo 49:7, 8.

Munthu wopanda ungwilo akamwalila, ndiye kuti walandila cilango ca macimo ake. Koma sangadziwombole kapena kulandila cilango pa macimo a munthu wina. (Aroma 6:7) Conco panafunika munthu wangwilo kuti apeleke moyo wake, osati cifukwa ca macimo ake, koma kaamba ka macimo athu.—Aheberi 10:1-4.

Amenewa ndiye makonzedwe amene Mulungu anapanga. Anatumiza Mwana wake Yesu, kucoka kumwamba na kudzabadwa pa dziko lapansi monga munthu wangwilo. (1 Petulo 2:22) Yesu anati anabwela “kudzapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.” (Maliko 10:45) Iye anafa kuti agonjetse imfa mdani wathu, kutiwombola kuti tikakhale na moyo wosatha.—Yohane 3:16.

KODI IMFA IDZAGONJETSEDWA LITI?

Masiku ano, tikukhala mu “nthawi . . . yovuta,” ndipo zikukwanilitsa ulosi wa m’Baibo. Izi zionetsa kuti tili mu “masiku otsiliza” a dongosolo lino loipa la zinthu. (2 Timoteyo 3:1) Masiku otsiliza amenewa, adzatha “m’tsiku laciweluzo ndi ciwonongeko ca anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:3, 7) Koma anthu amene amakonda Mulungu adzapulumuka ciwonongeko cimeneco, ndipo adzalandila dalitso la “moyo wosatha.”—Mateyu 25:46.

Yesu anabwela “kudzapeleka moyo wake dipo kuwombola anthu ambili.”—Maliko 10:45

Anthu ena mamiliyoni adzalandila moyo wosatha akadzaukitsidwa. Pamene Yesu anayenda ku mzinda wa Naini, anaonetsa kuti zidzatheka anthu akufa kuukitsidwa. Kumeneko, mwana mmodzi yekha wamwamuna, wa mkazi wamasiye anamwalila. Yesu ‘anamvelela cifundo’ mkaziyo, ndipo anaukitsa mwanayo. (Luka 7:11-15) Komanso, mtumwi Paulo anati: “Ndili ndi ciyembekezo mwa Mulungu, . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” Ciyembekezo cotsimikizika cimeneci, ni umboni wamphamvu wa cikondi ca Mulungu kwa anthu.—Machitidwe 24:15.

Anthu ofika mabiliyoni angayembekezele mwacidwi kukhala na moyo kwamuyaya. Baibo imati: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Pa nthawi imeneyo, anthu amenewo adzakhala okondwa, komanso olimbikitsidwa na mawu amene mtumwi Paulo analemba pafupi-fupi zaka 2,000 zapitazo akuti: “Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti?” (1 Akorinto 15:55) Inde, pa nthawiyo, imfa mdani wathu wankhanza adzagonjetsedwa!