Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mbali ya buku la Yesaya yopezeka m’mipukutu ya Dead Sea Scrolls, ndipo pansi pake inamasulidwa mu Ciarabu. Uthenga wa m’Mawu a Mulungu sunasinthidwe mpaka pano

Kodi Mawu a Mulungu Anasinthidwa?

Kodi Mawu a Mulungu Anasinthidwa?

Anthu ena amaganiza kuti mwina Mawu a Mulungu anasinthidwa. Mneneli Yesaya anati mawu a Mulungu “adzakhala mpaka kalekale.” (Yesaya 40:8) Kodi tingatsimikize bwanji kuti malonjezo a Mulungu sanasinthidwe?

Mulungu ali na mphamvu yoteteza Mawu ake kuti asasinthidwe. Akatswili amakedzana okopolola Malemba pamanja, anali kucita kuŵelenga cilembo cimodzi-cimodzi pofuna kutsimikiza kuti palibe ciliconse cimene cawonjezeledwa, kusinthidwa, kapena kucotsedwamo m’malemba oyela. Ngakhale n’telo, popeza kuti munthu ni wopanda ungwilo, ena mwa akatswiliwo anali kulakwitsabe zina zocepa.

KODI TINGATSIMIKIZE BWANJI KUTI MALEMBA OYELA A MASIKU ANO AKALI NA UTHENGA WENI-WENIWO WA MULUNGU?

Mipukutu yamakedzana yofika masauzande ya Malemba Oyela ikalipo. Ngati mpukutu wina wapezeka na mbali yosiyanako, ngakhale pang’ono cabe, ungayelekezeledwe na mipukutu ina pofuna kudziŵa zoona. Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani yakuti, “Kodi Baibulo Linasinthidwa Kapena Kusokonezedwa?” pa jw.org ku Chichewa.

Mwacitsanzo, ganizilani za mipukutu yakale-kale yochedwa Dead Sea Scrolls imene anatulukila anthu amtundu wochedwa abeduwini, m’mapanga a pafupi na nyanja yochedwa Dead Sea mu 1947. Mipukutu yamakedzana imeneyi ni mbali ya Malemba Oyela, ndipo inalembedwa zaka zopitilila 2000 kumbuyoko. Akatswili anayelekezela mipukutu yamakedzana imeneyi na Malemba Oyela amene tili nawo masiku ano. Kodi anapeza zotani?

Akatswiliwo anapeza kuti Mawu a Mulungu amene tili nawo masiku ano ni ofanana na zolembedwa m’mipukutu yoyambilila. * Inde, kuyelekezela mosamala mipukutu yakale imeneyi, kwaonetsa kuti zimene timaŵelenga m’Malemba Oyela ulidi uthenga weni-weni wa Mulungu. Kukamba zoona, Mulungu wacita zonse zotheka kuteteza Malemba Oyela kuti akhalebe olondola mpaka masiku ano.

Conco, tiziŵelenga Mawu a Mulungu na cidalilo conse kuti ni oona, komanso olondola. Tili na mfundoyi m’maganizo, tiyeni lomba tione zimene tingaphunzile kwa aneneli ponena za Mulungu.

^ ndime 7 Malinga na buku lakuti The Complete Dead Sea Scrolls in English ya Geza Vermes, peji 16.