Mmene Tingaonetsele Cikondi kwa Anthu Anzathu
Popeza kuti tonsefe kholo lathu loyamba ni Adamu, ndife banja limodzi. Ngakhale kuti a m’banja amafunika kukondana na kulemekezana, masiku ano n’zovuta kuti anthu a m’banja limodzi azikondana. Ndipo izi si zimene Mulungu wathu wacikondi amafuna.
ZIMENE MALEMBA OYELA AMAKAMBA PONENA ZA CIKONDI
“Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”—LEVITIKO 19:18.
“Pitilizani kukonda adani anu.”—MATEYU 5:44.
ZIMENE KUKONDA ANTHU ANZATHU KUMATANTHAUZA
Onani mmene Mulungu amafotokozela khalidwe lacikondi m’Mawu ake pa 1 Akorinto 13:4-7:
“Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima.”
Ganizilani izi: Kodi mumamvela bwanji ngati ena acita nanu zinthu moleza mtima komanso mokoma mtima, ndipo sacita nanu zinthu mwaukali mukalakwitsa zina zake?
“Cikondi sicicita nsanje.”
Ganizilani izi: Kodi mumamvela bwanji ngati ena amakukaikilani, kapena kukucitilani kaduka?
Cikondi “sicisamala zofuna zake zokha.”
Ganizilani izi: Kodi mumamvela bwanji ngati ena amalemekeza maganizo anu, ndipo saumilila maganizo awo?
Cikondi “sicisunga zifukwa.”
Ganizilani izi: Mulungu ni wokonzeka kukhululukila aliyense wolapa amene anam’lakwila. Malemba amatiuza kuti: “Iye sadzakhalila kutiimba mlandu nthawi zonse cifukwa ca zolakwa zathu, kapena kutisungila mkwiyo.” (Salimo 103:9) Timakondwela ngati munthu amene tinam’khumudwitsa watikhululukila. Conco, tiyenela kukhala okonzeka kukhululukila ena akatikhumudwitsa.—Salimo 86:5.
Cikondi “sicikondwela ndi zosalungama.”
Ganizilani izi: Zoipa zikaticitikila, sitingakonde kuti ena azikondwela pamene tivutika. Conco, sitiyenela kukondwela ngati ena akukumana na mavuto ngakhale kuti anaticitilapo zoipa.
Kuti tipeze madalitso a Mulungu, tifunika kukonda ena m’njila zimenezi, mosasamala kanthu za msinkhu, dziko, kapena cipembedzo cawo. Tingacite zimenezi mwa kuthandiza amene afunikila thandizo.