Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

““Dziko lapansi lidzapeleka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.”—SALIMO 67:6

Mungapeze Madalitso Osatha kwa Mlengi Wathu

Mungapeze Madalitso Osatha kwa Mlengi Wathu

Mulungu analonjeza mneneli Abulahamu kuti mmodzi mwa mbadwa zake adzabweletsa madalitso ku “mitundu yonse ya padziko lapansi.” (Genesis 22:18) Kodi amene anali kudzakhala mbadwayo ndani?

Zaka pafupi-pafupi 2,000 zapitazo, Mulungu anapatsa Yesu mphamvu yocita zozizwitsa zazikulu, ndipo iye ndiye anali mbadwayo ya Abulahamu. Zozizwitsazo zinaonetsa kuti lonjezo limene linapelekedwa kwa Abulahamu lidzakwanilitsidwa ku mitundu yonse ya anthu kupitila mwa Yesu.—Agalatiya 3:14.

Zozizwitsa zimene Yesu anacita, zinathandiza anthu kudziŵa kuti iye ndiye wosankhidwa na Mulungu kuti adalitse mitundu ya anthu. Ndipo zozizwitsazo, zinaonetsa mmene Mulungu adzam’seŵenzetsela podalitsa mitundu ya anthu kwamuyaya. Onani mmene zozizwitsa za Yesu zionetsela makhalidwe ake abwino.

Cikondi—Yesu anacilitsa odwala.

Panthawi ina, wakhate anacondelela Yesu kuti am’cilitse. Ndiyeno Yesu anakhudza munthuyo n’kumuuza kuti: “Ndikufuna!” Ndipo nthawi yomweyo khate lake linathelatu.—Maliko 1:40-42.

Kuwolowa manja—Yesu anadyetsa anjala.

Yesu sanali kufuna anthu kukhala na njala. Iye anadyetsa anthu masauzande mozizwitsa, mwa kuculukitsa mikate yoŵelengeka komanso tunsomba tocepa. Ndipo anacita izi osati kamodzi cabe. (Mateyu 14:17-21; 15:32-38) Atatsiliza kudya, onse anakhuta ndipo cakudya coculuka cinatsalako.

Cifundo Cacikulu—Yesu anaukitsa akufa.

‘Atagwidwa na cifundo,’ Yesu anaukitsa mwana wa mkazi wamasiye amene panthawiyo anali wacisoni kwambili, ndipo analibe aliyense wom’samalila.—Luka 7:12-15.