Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mungasangalale na Madalitso Osatha Ocokela kwa Mulungu Wacikondi

Mungasangalale na Madalitso Osatha Ocokela kwa Mulungu Wacikondi
  • Kodi mumalakalaka kukhala m’dziko limene mulibe nkhondo, ciwawa, na mikangano?

  • Kodi mumalakalaka kukhala m’dziko lopanda matenda, mavuto, kapena imfa?

  • Kodi mumalakalaka kukhala wopanda nkhawa?

  • Kodi mumalakalaka kukhala m’dziko lopanda matsoka a zacilengedwe?

Mulungu wathu wacikondi, amene analenga dziko lapansi lokongolali, analonjeza kuti adzadalitsa mtundu wa anthu powapatsa moyo wosatha, komanso wacimwemwe m’dziko lamtendele. Amenewa si maloto cabe.

M’nkhani zotsatila, tikulimbikitsani kuganizila izi:

  • Mmene Mlengi wathu amaonela anthu

  • Zimene Mawu a Mulungu amatiuza

  • Zimene aneneli anakamba ponena za madalitso amene Mulungu analonjeza

  • Zimene tingacite kuti tikhale acimwemwe palipano, na kuti Mulungu akatipatse madalitso osatha kutsogolo

Tiyeni tiyambe na kuona mmene Mlengi wathu amakondela anthu