NKHANI YOPHUNZILA 37
NYIMBO 118 “Tiwonjezeleni Cikhulupililo”
Kalata Yotithandiza Kupilila Mpaka Mapeto
“Zinthu zimene tinkadalila poyamba tazigwila mwamphamvu mpaka mapeto.”—AHEB. 3:14.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Tidzakambilana mfundo za m’kalata yopita kwa Aheberi zimene zidzatithandiza kupilila mokhulupilika mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.
1-2. (a) Kodi zinthu zinali motani mu Yudeya pomwe Paulo analembela kalata Aheberi? (b) N’cifukwa ciyani tinganene kuti kalatayi inalidi ya pa nthawi yake?
PAMBUYO pa imfa ya Yesu, Akhristu a Ciheberi amene anali kukhala ku Yerusalemu komanso ku Yudeya anakumana na mavuto ambili. Mpingo wa Cikhristu umene unali utangokhazikitsidwa kumene unayamba kuzunzidwa moopsa. (Mac. 8:1) Ndiyeno patapita zaka ngati 20, otsatila a Khristu anali kukumana na mavuto azacuma komanso njala yaikulu. (Mac. 11:27-30) Ca m’ma 61 C.E., Akhristu anali pamtendele. Koma anali kudzakumana na mavuto m’tsogolo. Pa nthawi imeneyo, iwo analandila kalata youzilidwa yocokela kwa mtumwi Paulo. Ndipo kalata imeneyo inalidi ya pa nthawi yake.
2 Kalata yopita kwa Aheberi inalidi ya panthawi yake, cifukwa mtendele umene Akhristuwo anali nawo unali wosakhalitsa. Paulo anapeleka malangizo amene anali kudzathandiza Akhristuwo kupilila cisautso cimene cinali kubwela. Kuwonongedwa kwa dongosolo la Ciyuda kumene Yesu anakambilatu, kunali kutatsala pang’ono kucitika. (Luka 21:20) N’zoona kuti Paulo komanso Akhristu a ku Yudeya, sanali kudziŵa nthawi yeniyeni pomwe ciwonongekoco cinali kudzafika. Komabe, Akhristuwo akanaseŵenzetsa nthawi yotsalayo podzikonzekeletsa mwa kukulitsa makhalidwe monga cikhulupililo komanso kupilila.—Aheb. 10:25; 12:1, 2.
3. N’cifukwa ciyani Akhristu masiku ano ayenela kukhala na cidwi coŵelenga buku la Aheberi?
3 Tikuyembekezela kukumana na cisautso cacikulu kuposa cimene Akhristu a Ciheberi anakumana naco. (Mat. 24:21; Chiv. 16:14, 16) Conco, tiyeni tikambilaneko ena mwa malangizo amene Yehova anapeleka kwa Akhristuwo. Malangizo amenewo angatithandize nafenso.
“TIKHALE AAKULU MWAUZIMU”
4. Ni zovuta ziti zimene Akhristu a Ciyuda anakumana nazo? (Onaninso cithunzi.)
4 Ayuda amene anakhala Akhristu anayenela kupanga masinthidwe aakulu, koma kucita zimenezi kunali kovuta. Pa nthawi ina, Ayuda anali mtundu wa anthu a Yehova osankhidwa. Kwa zaka zambili, mzinda wa Yerusalemu unali wofunika kwambili. Mafumu amene anali kuimilako Yehova anali kulamulila kucokela ku mzinda umenewu. Kulambila koyela nakonso kunali kucitikila pa kacisi wa ku Yerusalemu. Ayuda onse okhulupilika anali kutsatila Cilamulo ca Mose, komanso malamulo onse amene atsogoleli awo acipembedzo anali kuwaphunzitsa. Malamulowo anali okhudza zinthu monga cakudya, mdulidwe, komanso mmene anayenela kucitila zinthu na anthu omwe sanali Ayuda. Komabe, pambuyo pa imfa ya Yesu, Yehova analeka kulandila nsembe zimene Ayuda anali kupeleka pa kacisi. Conco, cinali covuta kuti Ayuda amene anazoloŵela kutsatila Cilamulowo asinthe njila ya kalambilidwe. (Aheb. 10:1, 4, 10) Ngakhale Akhristu aakulu kuuzimu monga mtumwi Petulo, anavutika kuzoloŵela masinthidwe amenewa. (Mac. 10:9-14; Agal. 2:11-14) Cifukwa ca zimene anayamba kukhulupilila, Akhristu anayamba kutsutsidwa na atsogoleli acipembedzo ca Ciyuda.
5. Kodi Akhristu anafunika kusamala na ciyani?
5 Akhristu a Ciheberi amenewo anali kutsutsidwa na magulu aŵili a anthu. Gulu loyamba linali la atsogoleli acipembedzo ca Ciyuda amene anali kuona Akhristuwo monga anthu ampatuko. Gulu laciŵili linali la Akhristu anzawo amene anali kuwalimbikitsa kuti apitilize kutsatila mfundo zina za m’Cilamulo ca Mose. N’kutheka kuti anali kuwalimbikitsa kucita zimenezo pofuna kupewa kuzunzidwa. (Agal. 6:12) N’ciyani cikanathandiza Akhristu okhulupilika kumamatilabe ku coonadi?
6. Kodi Paulo analimbikitsa okhulupilila anzake kucita ciyani? (Aheberi 5:14–6:1)
6 M’kalata yake yopita kwa Akhristu a Ciheberi, Paulo analimbikitsa okhulupilila anzake kuti azifufuza mozama m’Mawu a Mulungu. (Ŵelengani Aheberi 5:14–6:1.) Anaseŵenzetsa Malemba a Ciheberi pofotokozela abale ake kuti kalambilidwe ka Cikhristu kanali kopambana poyelekezela na kalambilidwe ka Ciyuda. a Analimbikitsa Akhristuwo kukulitsa cidziŵitso cawo ca m’Malemba na kumvetsa mfundo za coonadi. Kucita zimenezi kunali kudzawathandiza kuti asasoceletsedwe na ziphunzitso zabodza.
7. Ni zinthu ziti zimayesa cikhulupililo cathu masiku ano?
7 Masiku anonso, pali anthu amene amalimbikitsa maganizo otsutsana na mfundo zolungama za Yehova. Anthu ena otsutsa amati ife a Mboni za Yehova ndife okhalila cifukwa timatsatila zimene Baibo imakamba pa nkhani ya kugonana. Amanenanso kuti ndife osalolela komanso kuti ndife ankhanza. Maganizo a anthu a m’dzikoli masiku ano akutalikilana kwambili na maganizo a Yehova. (Miy. 17:15) Conco, m’pofunika kwambili kuti tizindikile maganizo olakwika amene otsutsa amalimbikitsa na kuwakaniza. Ndipo sitiyenela kulola kuti otsutsa atilefule kapena kutisoceletsa.—Aheb. 13:9.
8. N’ciyani cingatithandize kupitiliza kukula kuuzimu?
8 Paulo analimbikitsa Akhristu a Ciheberi kuti apitilize kukula kuuzimu. Nafenso tingacite bwino kutsatila malangizo amenewo. Izi zitanthauza kuti tiyenela kudziŵa mfundo za coonadi mozama na kutsatila kaganizidwe ka Yehova. Tiyenela kupitiliza kucita zimenezi, ngakhale pambuyo pa kudzipatulila na kubatizika. Mosasamala kanthu za nthawi imene takhala m’coonadi, tonse tiyenela kupitiliza kuŵelenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse. (Sal. 1:2) Kukhala na pulogilamu yabwino yocita phunzilo la munthu mwini, kudzatithandiza kulimbitsa khalidwe la cikhulupililo limene Paulo anagogomeza kwambili m’kalata yake yopita kwa Aheberi.—Aheb. 11:1, 6.
TIKHALE NA “CIKHULUPILILO COMWE CINGATITHANDIZE KUDZAPEZA MOYO”
9. N’cifukwa ciyani Akhristu a Ciheberi anafunika kukhala na cikhulupililo colimba?
9 Akhristu a Ciheberi anafunika kukhala na cikhulupililo colimba kuti adzapulumuke cisautso comwe cinali kudzacitika mu Yudeya. (Aheb. 10:37-39) Yesu anacenjeza otsatila ake kuti akadzaona magulu ankhondo atazungulila Yerusalemu adzathaŵile kumapili. Malangizo amenewo anali kupita kwa Akhristu onse, kaya anali kukhala mkati mwa mzindawo kapena m’madela a kumidzi. (Luka 21:20-24) M’masiku akale, anthu okhala m’madela a kumidzi akaukilidwa na gulu lankhondo, nthawi zambili anali kuthaŵila mu mzinda wokhala na mpanda kuti apeze citetezo. Malangizo akuti athaŵile ku mapili, m’malo mokhalabe mu mzinda wa Yerusalemu womwe unali na mpanda, anaoneka kukhala osathandiza. Conco, munthu anafunika kukhala na cikhulupililo colimba kuti atsatile malangizowo.
10. Kodi kukhala na cikhulupililo colimba kukanathandiza Akhristuwo kucita ciyani? (Aheberi 13:17)
10 Akhristu a Ciheberi anafunikilanso kukhulupilila anthu amene Yesu anali kuseŵenzetsa potsogolela mpingo. N’kutheka kuti amene anali kutsogolela anapeleka malangizo a mmene Akhristuwo akanacokela mu mzindawo, komanso nthawi imene anayenela kucoka. (Ŵelengani Aheberi 13:17.) Mawu a Cigiriki amene anawaseŵenzetsa pa Aheberi 13:17 akuti “muzimvela,” amakamba za munthu amene amakhala wokonzeka kumvela cifukwa amakhulupilila amene akupeleka malangizowo. Izi zitanthauza kumvela mocokela pansi pa mtima, osati cabe cifukwa munthu amene akupeleka malangizowo ali na udindo wocita zimenezo. Conco, Akhristu a Ciheberiwo anafunika kukulitsa cikhulupililo cawo mwa akulu amene anali kuwatsogolela cisautso cisanafike. Ngati Akhristuwo anamvela malangizo ocokela kwa akulu pa nthawi ya mtendele, zikanakhala zosavuta kuwamvela pa nthawi ya cisautso.
11. N’cifukwa ciyani masiku ano Akhristu ayenela kukhala na cikhulupililo colimba?
11 Monga mmene zinalili na Akhristu a Ciheberi, nafenso tifunika kukhala na cikhulupililo colimba. Izi zili conco cifukwa tikukhala m’nthawi imene anthu ambili sakhulupilila kuti mapeto a dongosolo lino la zinthu ayandikila. Iwo amafika ngakhale ponyoza anthu amene amakhulupilila zimenezi. (2 Pet. 3:3, 4) Ngakhale kuti Baibo imachulako zinthu zina zimene zidzacitika pa cisautso cacikulu, pali zambili zimene sitidziŵa zokhudza cocitikaco. Tiyenela kukhala na cikhulupililo colimba cakuti mapeto a dongosolo lino la zinthu adzafika pa nthawi imene Yehova anaika. Tiyenelanso kukhulupilila kuti iye adzatisamalila pa nthawiyo.—Hab. 2:3.
12. N’ciyani cingatithandize kukapulumuka cisautso cacikulu?
12 Tiyenelanso kulimbitsa cikhulupililo cathu cakuti Yehova akuseŵenzetsa “kapolo wokhulupilika ndiponso wanzelu” potitsogolela masiku ano. (Mat. 24:45) N’kutheka kuti Akhristu a Ciheberi analandila malangizo owathandiza kupulumuka pomwe Aroma anazungulila mzinda wa Yerusalemu. Nafenso tingadzalandile malangizo otithandiza kupulumuka pa cisautso cacikulu. Ino ndiyo nthawi yolimbitsa cikhulupililo komanso cidalilo cathu m’malangizo amene timalandila kucokela kwa amene akutsogolela m’gulu la Yehova. Ngati zimativuta kutsatila malangizo a amene akutsogolela palipano, cidzakhalanso covuta kuwamvela pa nthawi ya cisautso cacikulu.
13. N’cifukwa ciyani uphungu wa pa Aheberi 13:5 unali wothandiza?
13 Pomwe anali kuyembekezela kuti athaŵe, Akhristu a Ciheberiwo anafunika kukhala na umoyo wosalila zambili. Iwo anafunika kutsatila uphungu umene anapatsidwa wakuti “musamakonde ndalama.” (Ŵelengani Aheberi 13:5.) Ena a iwo anali atakumanapo kale na mavuto azacuma komanso njala yaikulu. (Aheb. 10:32-34) Ngakhale kuti pa nthawi ina iwo anali okonzeka kupilila zovuta kaamba ka uthenga wabwino, n’kutheka kuti ena a iwo anayamba kuona kuti kukhala na zinthu zambili za kuthupi n’kumene kukanawateteza. Koma ndalama sizinakakwanitsa kuwateteza ku ciwonongeko cimene cinali kubwela. (Yak. 5:3) Ndipo cikanakhala covuta kuti anthu amene anali na cuma cambili athaŵe n’kusiya nyumba zawo komanso katundu wawo.
14. Kodi kukhala na cikhulupililo colimba kudzatithandiza kuti tiziziona bwanji zinthu zakuthupi palipano?
14 Kukhala na cikhulupililo colimba cakuti mapeto a dzikoli afika posacedwa, kudzatithandiza kupewa kukondetsetsa cuma. Pa nthawiyo anthu adzatayila, “siliva wawo . . . m’misewu.” Adzatelo cifukwa adzazindikila kuti “siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku limene Yehova adzasonyeze mkwiyo wake waukulu.” (Ezek. 7:19) M’malo mothela nthawi yathu kufunafuna ndalama zambili, tiyenela kupanga zisankho zimene zidzatithandiza kukhala umoyo wosalila zambili, kwinaku tikutumikila Yehova. Izi zitanthauza kuti tiyenela kupewa nkhongole zosafunikila. Tizipewanso kuseŵenzetsa nthawi yathu yoculuka kusamalila katundu amene tili naye kale. Kuwonjezela apo, tizisamala kuti tisamaone cuma kukhala cinthu cofunika kwambili pa umoyo wathu. (Mat. 6:19, 24) Pamene tikuyandikila mapeto a dongosolo lino la zinthu, cikhulupililo cathu cidzayesedwa pa nkhani yokondetsetsa zinthu zakuthupi komanso pa nkhani zina.
“MUKUFUNIKA KUKHALA OPILILA”
15. N’cifukwa ciyani Akhristu a Ciheberi anafunika kukhala opilila?
15 Akhristu a Ciheberi anafunika kupilila zinthu zoyesa cikhulupililo cawo pomwe zinthu zinali kuipilaipila mu Yudeya. (Aheb. 10:36) Ngakhale kuti ena mwa Akhristuwo anakumanapo na cizunzo, ambili a iwo anakhala Akhristu pa nthawi yomwe kunali mtendele. Paulo ananena kuti, ngakhale kuti Akhristuwo anapilila zinthu zambili zoyesa cikhulupililo cawo, iwo sanakumane na mavuto monga amene Yesu anakumana nawo, moti mpaka kuphedwa. (Aheb. 12:4) Koma pamene Cikhristu cinayamba kufalikila, Ayuda otsutsa anayamba kuwacitila nkhanza kwambili Akhristu. Zaka zingapo Paulo asanalembe kalata yopita kwa Aheberi, gulu la anthu linamuukila ku Yerusalemu. Ayuda oposa 40 “anakonza ciwembu nʼkulumbila pocita kudzitembelela kuti saadya kapena kumwa ciliconse mpaka atapha Paulo.” (Mac. 22:22; 23:12-14) Ngakhale kuti Akhristuwo anali kudzakumana na cidani komanso kuzunzidwa, iwo sanali kufunika kusiya kusonkhana pamodzi kuti alambile. Anafunikanso kupitiliza kulalikila uthenga wabwino, komanso kusungabe cikhulupililo cawo cili colimba.
16. Kodi kalata yopita kwa Aheberi ingatithandize bwanji kuona mazunzo moyenela? (Aheberi 12:7)
16 N’ciyani cinali kudzathandiza Akhristu a Ciheberiwo kupilila pamene anali kuzunzidwa? Paulo anafuna kuthandiza Akhristuwo kuganizila mapindu amene akanapeza akapilila cizunzo. Conco, anawafotokozela kuti Akhristu akakumana na zinthu zoyesa cikhulupililo cawo, Mulungu angaseŵenzetse nthawi ya mayeselowo kuwaphunzitsa zinazake. (Ŵelengani Aheberi 12:7.) Pa nthawiyo, iye angawathandize kukulitsa makhalidwe abwino a Cikhristu. Kuganizila mapindu amene akanapeza akapilila cizunzo, kukanathandiza Akhristuwo kupilila mosavuta.—Aheb. 12:11.
17. Kodi Paulo anali kudziŵa ciyani pa nkhani ya kupilila mazunzo?
17 Paulo analimbikitsa Akhristu a Ciheberi kukhala olimba mtima komanso kuti asalefuke pokumana na zinthu zoyesa cikhulupililo cawo. Iye anali pamalo abwino owalimbikitsa pa nkhani yopilila. Zinali conco cifukwa asanakhale Mkhristu, iye anali kuzunza Akhristu. Conco anali kumvetsa cizunzo cimene iwo anali kukumana naco. Anali kudziŵanso zimene munthu angacite kuti apilile cizunzo. Anali kudziŵa zimenezi cifukwa anakumana na mazunzo osiyana-siyana atakhala Mkhristu. (2 Akor. 11:23-25) Cotelo, Paulo anali woyeneleladi kuŵauza zoyenela kucita kuti apilile. Anakumbutsa Akhristuwo kuti sanafunike kudzidalila kuti apilile mayeselo, koma anafunika kudalila Yehova. Conco Paulo molimba mtima anakamba kuti: “Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa.”—Aheb. 13:6.
18. N’ciyani cidzacitikila aliyense wa ife m’tsogolo? Nanga tingakonzekele bwanji?
18 Ena mwa abale athu akupilila mazunzo palipano. Tingawathandize mwa kuwapemphelela, ndipo nthawi zina mwa kuwapatsa zimene akufunikila pa umoyo. (Aheb. 10:33) Baibo imakamba mosapita m’mbali kuti “onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipeleka kwa Mulungu mogwilizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.” (2 Tim. 3:12) Podziŵa zimenezi, tonse tiyenela kukhala okonzeka kuti tingakumane na mazunzo nthawi ina iliyonse. Conco tiyeni tipitilize kudalila kwambili Yehova palipano. Ticite zimenezi tili na cikhulupililo cakuti iye adzatithandiza kupilila mavuto alionse amene angabwele. Pamapeto pake, iye adzapatsa alambili ake mpumulo.—2 Ates. 1:7, 8.
19. Tingacite ciyani kuti tikonzekele cisautso cacikulu cimene cikubwela? (Onaninso cithunzi.)
19 Mosakayikila, kalata imene Paulo analembela Aheberi inawathandiza kukonzekela cisautso cimene cinali kubwela. Paulo analimbikitsa abale ake kuti aziŵelenga kwambili Malemba na kuwamvetsa. Kucita zimenezi kukanawathandiza kuzindikila na kukaniza ziphunzitso zimene zikanafooketsa cikhulupililo cawo. Anawalimbikitsanso kuti alimbitse cikhulupililo cawo. Kucita zimenezi kukanawathandiza kuti azitsatila mosavuta malangizo ocokela kwa Yesu, komanso kwa amene anali kutsogolela mu mpingo. Anawathandiza kuti aziona mazunzo awo moyenela kuti athe kupilila, komanso kuti aziona nthawi ya mazunzo ngati mwayi wolola Atate wawo wacikondi kuwaphunzitsa. Nafenso tiyenela kuseŵenzetsa malangizo ouzilidwa amenewo. Tikatelo tidzatha kupilila mokhulupilika mpaka mapeto.—Aheb. 3:14.
NYIMBO 126 Khalani Maso, Cilimikani, Khalani Amphamvu
a M’caputala coyambilila cokha ca buku la Aheberi, Paulo anagwila mawu Malemba a Ciheberi maulendo 7 poonetsa kuti kalambilidwe ka Cikhristu kanali kopambana kuposa ka Ciyuda.—Aheb. 1:5-13.