Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 38

NYIMBO 25 Cuma Capadela

Kodi Mumamvela Macenjezo?

Kodi Mumamvela Macenjezo?

“Mmodzi adzatengedwa koma winayo adzasiyidwa.”​—MAT. 24:40.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Tikambilane mafanizo atatu amene Yesu anakamba, ndipo tione mmene amagwilizanila na ciweluzo cimene cidzacitika kumapeto a dongosolo lino la zinthu.

1. Kodi Yesu adzacita ciyani posacedwa?

 TIKUKHALA m’nthawi ya mapeto imene kudzacitika zinthu zikulu-zikulu! Posacedwa, Yesu adzaweluza anthu onse pa dziko lapansi. Iye anafotokoza zimene zidzacitike ciweluzoco cikadzayandikila. Anatelo mwa kuuza ophunzila ake “cizindikilo” ca kukhalapo kwake kosaoneka, komanso “ca cimalizilo ca nthawi ino.” (Mat. 24:3) Cizindikilo cimeneci cinalembedwa pa Mateyo caputala 24 na 25, Maliko caputala 13, komanso pa Luka caputala 21.

2. Tikambilane ciyani m’nkhani ino? Kodi kukambilana zimenezi kudzatithandiza bwanji?

2 Yesu anaseŵenzetsa mafanizo atatu potithandiza kukonzekela zocitikazo. Mafanizo amenewa ni: (1) fanizo la nkhosa na mbuzi, (2) fanizo la anamwali ocenjela na anamwali opusa, komanso (3) fanizo la matalente. Fanizo lililonse lidzatithandiza kumvetsa kuti Yesu adzaweluza munthu aliyense potengela zimene munthuyo amacita. Pokambilana mafanizowa, tione zimene tiphunzilapo na mmene tingazigwilitsile nchito. Tiyeni tiyambe mwa kukambilana fanizo la nkhosa na mbuzi.

FANIZO LA NKHOSA NA MBUZI

3. Ni liti pamene Yesu adzaweluza anthu?

3 M’fanizo la nkhosa na mbuzi, Yesu anafotokoza kuti adzaweluza anthu potengela zimene anthuwo anacita atamva uthenga wabwino. Ananenanso kuti adzawaweluza potengela zimene anthuwo anacita pothandiza abale ake odzozedwa. (Mat. 25:31-46) Yesu adzapeleka ciweluzo cimeneci mkati mwa “cisautso cacikulu,” Aramagedo itatsala pang’ono kucitika. (Mat. 24:21) M’busa amalekanitsa nkhosa na mbuzi. Mofananamo, Yesu adzalekanitsa anthu amene amathandiza odzozedwa mokhulupilika na aja amene sawathandiza.

4. Malinga na Yesaya 11:3, 4, n’ciyani cimatipangitsa kukhulupilila kuti Yesu adzaweluza mwacilungamo? (Onaninso pa cikuto.)

4 Ulosi wa m’Baibo umaonetsa kuti popeza Yesu anasankhidwa na Yehova kuti akhale woweluza, iye adzaweluza mwacilungamo (Ŵelengani Yesaya 11:3, 4.) Yesu amaona zimene anthu amacita, makhalidwe awo, komanso zokamba zawo. Amaonanso mmene anthuwo amacitila zinthu na abale ake odzozedwa. (Mat. 12:36, 37; 25:40) Adziŵa amene amathandiza abale ake odzozedwa pa nchito yawo. a Kugwila nchito yolalikila ni njila imodzi imene anthu amene ali monga nkhosa amathandizila abale a Khristu. Amene amathandiza pa nchito imeneyi adzaweluzidwa kuti ni “olungama.” Iwo adzakhala na ciyembekezo codzakhala na ‘moyo wosatha’ padziko lapansi (Mat. 25:46; Chiv. 7:16, 17) Imeneyi ni mphoto yosangalatsa kwambili kwa onse amene adzakhalabe okhulupilika! Anthu amene adzakhalabe okhulupilika pa cisautso cacikulu komanso pambuyo pake, maina awo adzalembedwa “mʼbuku la moyo.”​—Chiv. 20:15.

Posacedwa m’tsogolo, Yesu adzaweluza anthu poonetsa kuti ena anacita zinthu monga nkhosa kapena monga mbuzi (Onani ndime 4)


5. Kodi fanizo la nkhosa na mbuzi litiphunzitsa ciyani? Nanga ndani amapindula na fanizoli?

5 Khalanibe okhulupilika. Fanizo la nkhosa na mbuzi limakhudza kwambili anthu amene ali na ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha padziko lapansi. Anthuwo amaonetsa cikhulupililo cawo mwa kuthandiza abale a Yesu pa nchito yolalikila. Amaonetsanso cikhulupililo cawo mwa kutsatila mokhulupilika malangizo ocokela ku kagulu kocepa ka abale odzozedwa amene Yesu anasankha. (Mat. 24:45) Koma mfundo za m’fanizoli zimagwilanso nchito kwa anthu amene ali na ciyembekezo cokakhala kumwamba. N’cifukwa ciyani tikunena conco? Cifukwa Yesu amaona zocita zawo, makhalidwe awo, na zokamba zawo. Conco nawonso ayenela kukhalabe okhulupilika. Ndiye cifukwa cake Yesu anakamba mafanizo ena aŵili okhala na macenjezo opita kwa odzozedwa. Mafanizo amenewa nawonso amapezeka pa Mateyo caputala 25. Lomba, tiyeni tikambilane fanizo la anamwali ocenjela na anamwali opusa.

FANIZO LA ANAMWALI OCENJELA NA ANAMWALI OPUSA

6. Kodi anamwali 5 anaonetsa bwanji kuti anali ocenjela? (Mateyo 25:6-10)

6 Mu fanizo la anamwali, Yesu anakamba za anamwali 10 amene anapita kukacingamila mkwati. (Mat. 25:1-4) Onse anali kuyembekezela kupita na mkwati ku phwando la ukwati. Yesu anakamba kuti anamwali 5 anali “ocenjela,” koma anamwali ena 5 anali “opusa.” Anamwali ocenjela anali okonzeka ndipo anakhalabe chelu. Anali okonzeka kuyembekezela mpaka mkwati atafika, ngakhale kuti anali kudzafika usiku kwambili. Conco anamwaliwo anabwela na nyale kuti aziunikila mu mdima. Anatenganso mafuta owonjezela, pokonzekela kuti mwina mkwati angacedwe kufika. Motelo iwo anali okonzeka kusungabe nyale zawo zili zoyaka. (Ŵelengani Mateyo 25:6-10.) Pamene mkwati anafika, anamwali ocenjela analoŵa naye limodzi m’nyumba imene munali phwando la ukwati. Mofananamo, Akhristu odzozedwa amene adzakhalabe chelu komanso okhulupilika mpaka kubwela kwa Khristu, adzalandila mphoto yawo. Iwo adzaloŵa mu Ufumu wa kumwamba pamodzi na mkwati, Yesu. b (Chiv. 7:1-3) Nanga bwanji za anamwali opusa?

7. N’ciyani cinacitikila anamwali 5 opusa? Nanga n’cifukwa ciyani?

7 Mosiyana na anamwali ocenjela, anamwali 5 opusa aja sanali okonzeka pamene mkwati anafika. Nyale zawo zinali pafupi kuzima, ndipo iwo sanabweletse mafuta owonjezela. Atadziŵa kuti mkwati watsala pang’ono kufika, anapita kukagula mafuta. Mkwati atafika, iwo anali asanabweleko kokagula mafutako. Pa nthawi imeneyo, “anamwali amene anali okonzekawo analoŵa naye mʼnyumba imene munali phwando laukwati ndipo citseko cinatsekedwa.” (Mat. 25:10) Pambuyo pake anamwali opusa aja anafika, ndipo anafuna kuloŵa m’nyumba imene munali phwando la ukwati. Koma mkwati anaŵauza kuti: “Sinikudziŵani.” (Mat. 25:11, 12) Anamwali amenewa sanali okonzeka kuyembekezela mpaka mkwati atafika. Kodi odzozedwa aphunzilapo ciyani?

8-9. Kodi odzozedwa aphunzilapo ciyani pa fanizo la anamwali? (Onaninso cithunzi.)

8 Khalanibe chelu komanso okonzeka. Yesu sanali kunena kuti padzakhala magulu aŵili a odzozedwa. Sanatanthauze kuti odzozedwa ena adzakhala okonzeka kuyembekeza mpaka mapeto, ndipo ena sadzakhala okonzeka. M’malomwake, anali kufotokoza zimene zidzacitikile odzozedwa ngati sadzakhala okonzeka kupilila mokhulupilika mpaka mapeto. Ngati sadzakhala okonzeka sadzalandila mphoto yawo. (Yoh. 14:3, 4) Imeneyi ni cenjezo yofunika kumaikumbukila! Kaya ciyembekezo cathu ni cokakhala kumwamba kapena codzakhala padziko lapansi, tonse tiyenela kutengapo phunzilo pa fanizo la anamwali. Aliyense wa ife ayenela kukhalabe maso komanso wokonzeka kupilila mpaka mapeto.​—Mat. 24:13.

9 Yesu anakamba fanizo la anamwali poonetsa kufunika kokhala chelu komanso okonzeka. Pambuyo pofotokoza fanizo limeneli, Yesu anakambanso fanizo la matalente. Fanizo la matalente limatiphunzitsa kufunika kocita zinthu mwakhama.

M’pofunika kuti aliyense wa ife amvele cenjezo lopezeka m’fanizo la anamwali, mwa kukhalabe maso komanso okonzeka kupilila mpaka mapeto (Onani ndime 8-9)


FANIZO LA MATALENTE

10. Kodi akapolo aŵili anaonetsa bwanji kuti anali okhulupilika? (Mateyo 25:19-23)

10 Mu fanizo la matalente, Yesu anafotokoza za akapolo aŵili amene anali okhulupilika kwa mbuye wawo, komanso mmodzi amene sanali wokhulupilika. (Mat. 25:14-18) Akapolo aŵili okhulupilika anagwila nchito mwakhama kuti awonjezele cuma ca mbuye wawo. Pamene mbuye wawo anali kucoka kupita ku dziko lina anawapatsa matalente, kapena kuti ndalama zambili. Akapolo okhulupilika aŵili aja, anagwila nchito mwakhama ndipo anaseŵenzetsa ndalamazo mwanzelu. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Mbuye wawo atabwelako, akapolowo anali atawonjezela ndalama imene anawasiyila kuwilikiza kaŵili. Mbuye wawo anawayamikila kwambili akapolo aŵiliwo. Ndipo akapolowo ‘anasangalala pamodzi na . . . mbuye wawo.’ (Ŵelengani Mateyo 25:19-23.) Nanga bwanji ponena za kapolo wacitatu uja? Kodi anacita ciyani na ndalama imene mbuye wake anamupatsa?

11. N’ciyani cinacitikila kapolo waulesi? Ndipo n’cifukwa ciyani?

11 Kapolo wacitatu analandila talente imodzi, koma anali “waulesi.” Mbuye wake anali kuyembekezela kuti kapoloyu adzaseŵenzetsa ndalamayo mwanzelu. Koma iye anakumba pansi n’kubisa ndalamayo. Pamene mbuye wake anabwelako, kapoloyu analibe ndalama ina yowonjezela yoti amupatse. Kapoloyu sanacite zinthu mwanzelu. M’malo mopepesa kuti analephela kuwonjezela cuma ca mbuye wake, kapoloyu anayamba kunena mbuye wake kuti anali “munthu wovuta.” Mbuye wake sanasangalale naye. Kuwonjezela apo, anamulanda talente imene anamupatsa, na kum’cotsa m’nyumba ya mbuye wake.​—Mat. 25:24, 26-30.

12. Kodi akapolo aŵili okhulupilika aimila ndani masiku ano?

12 Akapolo aŵili okhulupilika aimila Akhristu odzozedwa. Mbuye wawo, amene ni Yesu, amawaitana kuti ‘asangalale pamodzi’ naye. Iwo amaukitsidwa pa kuuka koyamba, ndipo amalandila mphoto yawo kumwamba. (Mat. 25:21, 23; Chiv. 20:5b) Kumbali ina, citsanzo coipa ca kapolo waulesi ni cenjezo kwa odzozedwa. Motani?

13-14. Kodi odzozedwa aphunzilapo ciyani pa fanizo la matalente? (Onaninso cithunzi.)

13 Muzicita zinthu mwakhama. Monga zilili na fanizo la anamwali, mu fanizo la matalente, Yesu sanali kukamba kuti odzozedwa adzakhala aulesi. M’malomwake, anali kufotokoza zimene zingacitike ngati iwo asiya kucita zinthu mwakhama. Angalephele ‘kukhalabe okhulupilika, nʼcolinga coti apitilizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha.’ Ndipo sangaloledwe kukaloŵa mu Ufumu wa kumwamba.​—2 Pet. 1:10.

14 Mafanizo amene Yesu anakamba a anamwali komanso matalente, aonetsa bwino kuti Akhristu onse odzozedwa ayenela kukhala okonzeka komanso achelu. Mafanizowa amaphunzitsanso odzozedwa kuti azicita zinthu mwakhama. Kodi Yesu anakambanso cina cimene cili ngati cenjezo kwa odzozedwa? Inde anatelo! Timapeza cenjezo limeneli m’mawu ake a pa Mateyo 24:40, 41.

Yesu afuna kuti odzozedwa azigwila nchito mwakhama mpaka mapeto (Onani ndime 13-14) d


KODI NDANI “ADZATENGEDWA”?

15-16. Kodi Mateyo 24:40, 41 ithandiza bwanji odzozedwa kuona kufunika kokhalabe maso?

15 Asanakambe mafanizo atatu amenewa, Yesu anafotokoza ciweluzo cothela cimene cidzaonetsa odzozedwa amene adzakhala ovomelezedwa. Anakamba za amuna aŵili amene akugwila nchito m’munda, komanso akazi aŵili amene akupela pa mphelo. M’zocitika zonse ziŵili, anthuwo akuoneka kuti akugwila nchito yofanana. Koma Yesu anakamba kuti “mmodzi adzatengedwa koma winayo adzasiyidwa.” (Ŵelengani Mateyu 24:40, 41.) Conco analimbikitsa otsatila ake kuti: “Khalani maso cifukwa simukudziŵa tsiku limene Mbuye wanu adzabwela.” (Mat. 24:42) Yesu anakamba mawu ofanana na amenewa pambuyo pofotokoza fanizo la anamwali. (Mat. 25:13) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti cenjezo lakuti “mmodzi adzatengedwa koma winayo adzasiyidwa,” limakhudzanso odzozedwa? Zikuoneka conco. Anthu okhawo amene anadzozedwadi na Yehova na kukhalabe okhulupilika, ni amene “adzatengedwa” na Yesu kukakhala mu Ufumu wa kumwamba.​—Yoh. 14:3.

16 Khalanibe maso. Odzozedwa amene sadzakhalabe maso mwauzimu, sadzasonkhanitsidwa pamodzi na “osankhidwa ake.” (Mat. 24:31) Ndipo anthu onse a Mulungu amene ali na ciyembekezo codzakhala na moyo padziko lapansi, nawonso ayenela kumvela cenjezo la Yesu na kukhalabe maso komanso okhulupilika.

17. N’cifukwa ciyani sitiyenela kukhumudwa Yehova akadzoza munthu m’masiku athu ano?

17 Popeza tafika pomudziŵa bwino Yehova, sitikayikila kuti iye amacita zinthu mwacilungamo. Conco sitikhumudwa Yehova akasankha kudzoza anthu ena okhulupilika m’masiku athu ano. c Timakumbukila zimene Yesu anakamba m’fanizo la munda wa mpesa, zokhudza anthu amene anayamba kugwila nchito ca m’ma 5 koloko madzulo. (Mat. 20:1-16) Anthu amene anayamba kugwila nchito m’munda wa mpesa ca m’madzulo analandila malipilo ofanana ndendende na aja amene anayamba kugwila nchito m’maŵa. Mofananamo, zilibe kanthu kuti munthu anadzozedwa liti, iye adzalandila mphoto ya kumwamba akakhalabe wokhulupilika.

MUZIMVELA MACENJEZO

18-19. Taphunzila ciyani m’nkhani ino?

18 Kodi taphunzila ciyani m’nkhani ino? Mu fanizo la nkhosa na mbuzi, taphunzila kuti anthu amene ali na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya padziko lapansi, afunika kukhalabe okhulupilika kwa Yehova. Ayenela kutelo palipano, komanso pa nthawi ya cisautso cacikulu cimene cikubwela. Pa nthawi imeneyo, Yesu adzaweluza anthu okhulupilika kuti ni oyenela ‘kulandila moyo wosatha.’​—Mat. 25:46.

19 Taphunzilanso mafanizo aŵili amene apeleka macenjezo kwa odzozedwa. Mu fanizo la anamwali ocenjela komanso opusa limene Yesu anakamba, anamwali 5 anacita zinthu mwanzelu. Iwo anali okonzeka ndipo anakhalabe chelu. Anali okonzeka kuyembekezela mpaka mkwati atafika. Koma anamwali opusa sanali okonzeka. Conco mkwati sanawalole kuti aloŵe m’nyumba imene munali phwando la ukwati wake. Nafenso tiyenela kukhala okonzeka kuyembekezela mpaka pamene Yesu adzawononge dongosolo lino la zinthu. Tiyenela kuyembekezelabe kaya zitenge nthawi yaitali motani. Takambilananso fanizo la matalente limene Yesu anafotokoza. Mu fanizoli, akapolo aŵili okhulupilika anacita zinthu mwakhama. Anagwila nchito molimbika poseŵenzela mbuye wawo, ndipo iye anakondwela nawo. Koma kapolo waulesi uja anakanidwa. Tiphunzilapo ciyani? Tiyenela kukhala okangalika potumikila Yehova mpaka mapeto. Pothela pake, taphunzilanso zimene zingathandize odzozedwa kukhalabe maso kuti ‘akatengedwe’ na Yesu kukalandila mphoto yawo kumwamba. Odzozedwa amayembekezela mwacidwi “kusonkhanitsidwa” na Yesu kumwamba. Pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, iwo adzakhala mkwatibwi wa Yesu, pa ukwati wa Mwanawankhosa.​—2 Ates. 2:1; Chiv. 19:9.

20. Kodi Yehova adzawacitila ciyani anthu amene amamvela macenjezo ake?

20 Ngakhale kuti tsiku la ciweluzo likuyandikila, sitiyenela kucita mantha. Tikakhalabe okhulupilika, Atate wathu wacikondi wa kumwamba adzatipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti tidzathe “kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (2 Akor. 4:7; Luka 21:36) Kaya ciyembekezo cathu n’cokakhala kumwamba kapena codzakhala padziko lapansi, tidzakondweletsa Atate wathu ngati timamvela macenjezo opezeka m’mafanizo amene Yesu anakamba. Mwa cisomo ca Yehova, maina athu adzakhala atalembedwa “m’buku” la moyo.​—Dan. 12:1; Chiv. 3:5.

NYIMBO 26 Munacitila Ine

a Onani nkhani yakuti “Kodi Tidziŵapo Ciyani za Mmene Yehova Adzaweluzile Anthu M’tsogolo?” mu Nsanja ya Mlonda ya May 2024.

b Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani nkhani yakuti “Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?” mu Nsanja ya Mlonda ya March 15, 2015.

d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo wodzozedwa akuphunzila Baibo na mtsikana amene anapeza mu utumiki.