MFUNDO YOTHANDIZA PA KUŴELENGA KWANU
Muziphunzila Mfundo Zatsopano Mukamaŵelenga
Tikafuna kuyamba kuŵelenga, tingadzifunse kuti, ‘Kodi nidzaphunzila ciyani?’ Tingakhale na mfundo inayake imene tikuyembekezela kupeza m’nkhani imene tikuŵelenga. Koma tizikumbukila kuti pali mfundo zina zatsopano zimene Yehova angafune kutiphunzitsa m’nkhaniyo. Tingadziŵe bwanji zimene Yehova afuna kutiphunzitsa?
Muzipempha nzelu. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa zimene akufuna kuti muphunzile panthawiyo. (Yak. 1:5) Musakhale okhutila na mfundo zimene mudziŵa kale.—Miy. 3:5, 6.
Lolani mphamvu ya Mawu a Mulungu kugwila nchito pa moyo wanu. “Mawu a Mulungu ndi amoyo.” (Aheb. 4:12) Conco, nthawi zonse tikamaŵelenga Baibo, imatiphunzitsa mfundo zatsopano komanso kutithandiza m’njila zosiyana-siyana. Koma izi zingatheke kokha ngati timavomeleza kuti pali mfundo inayake imene Mulungu afuna kutiphunzitsa.
Muziyamikila zonse zimene Yehova amatiphunzitsa. Cakudya cauzimu cimene Yehova amatipatsa cili monga “phwando la zakudya zabwino kwambili.” (Yes. 25:6) Musapewe “zakudya,” kapena kuti nkhani, zimene muona kuti simudzasangalala nazo. Mukatelo mudzapindula kwambili, ndipo mudzapeza cimwemwe pamene mukuŵelenga!