Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga

Pamene Yesu anali kuyambitsa Mgonelo wa Ambuye, kodi ophunzila 70 aja omwe anawatuma kuti akalalikile anali kuti? Kodi iwo anali atasiya kukhala ophunzila ake?

N’zoona kuti ophunzila 70 aja sanalipo pamene Yesu anayambitsa Mgonelo wa Ambuye. Koma izi siziyenela kutipangitsa kuganiza kuti Yesu sanawayanje. Tiyenelanso kupewa kuganiza kuti kusapezekapo kwawo kuonetsa kuti iwo anasiya kukhala ophunzila ake. Yesu anali kungofuna kukhala na atumwi ake pa cocitikaco.

Atumwi 12 komanso anthu ena aja 70, onse anali ophunzila ake. Pa ophunzila ambili amene anali nawo, Yesu anasankhapo anthu 12 amene anawacha kuti atumwi. (Luka 6:12-16) lye anali mu mzinda wa Galileya pomwe “anasonkhanitsa atumwi 12” na kuwatumiza “kuti azikalalikila za Ufumu wa Mulungu ndiponso kucilitsa anthu.” (Luka 9:1-6) Kenako ali mu Yudeya, Yesu “anasankha anthu ena 70 n’kuwatumiza aŵili-aŵili.” (Luka 9:51; 10:1) Conco, Yesu anali na ophunzila amene anali kulalikila za iye ku madela osiyana-siyana.

Ayuda amene anakhala ophunzila a Yesu, anali kucita Mwambo wa Pasika caka ciliconse, ndipo mwacionekele anali kucita zimenezi pamodzi na mabanja awo. (Eks. 12:6-11, 17-20) Atatsala pang’ono kuphedwa, Yesu na atumwi ake anapita ku Yerusalemu. Pocita Cikondwelelo ca Pasika, iye sanaitane ophunzila ake onse ocokela ku Yudeya, Galileya, komanso a ku Pereya. N’zoonekelatu kuti Yesu anali kufuna kukhala na atumwi ake okha pa mwambowu. Iye anawauza kuti: “Ndakhala ndikulakalaka kwambili kuti ndidye Pasika uyu limodzi ndi inu ndisanayambe kuzunzika.”​—Luka 22:15.

Anali na cifukwa comveka cocitila zimenezi. Posakhalitsa, Yesu anali kudzafa monga ‘Mwanawankhosa wa Mulungu amene anali kudzacotsa ucimo wa dziko.’ (Yoh. 1:29) Iye anali kudzafela ku Yerusalemu kumene anthu anali kupelekela nsembe kwa Mulungu. Mwanawankhosa yemwe Aisiraeli anali kudya pa Mwambo wa Pasika, unali kuwakumbutsa pamene Yehova anawamasula ku Iguputo. Koma nsembe imene Yesu anali kudzapeleka, inali kudzacita zambili kuposa pamenepa. Inali kudzamasula mtundu wonse wa anthu ku ucimo na imfa. (1 Akor. 5:7, 8) Nsembe imene iye anapeleka, inacititsa kuti atumwi ake 12 akhale maziko a mpingo wa Cikhristu. (Aef. 2:20-22) N’zocititsa cidwi kuti mzinda woyela wa Yerusalemu uli na “miyala yomangila maziko yokwana 12 ndipo pamiyalayo panalembedwa maina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa.” (Chiv. 21:10-14) Atumwi okhulupilika anali kudzacita mbali yofunika pokwanilitsa cifunilo ca Mulungu. Conco, m’pomveka kuti Yesu anali kufuna kukhala nawo pa mwambo wothela wa Pasika, komanso pa mwambo umene anali kudzayambitsa pambuyo pake wa Mgonelo wa Ambuye.

Ophunzila 70 aja na ophunzila ena sanali nawo pa mwambowu. Ngakhale n’telo, ophunzila onse amene anakhalabe okhulupilika, anali kudzapindula na mwambo wa Mgonelo wa Ambuye umene Yesu anayambitsa. M’kupita kwa nthawi, ophunzila onse amene anakhala Akhristu odzozedwa, analoŵa mu pangano la Ufumu limene Yesu anachulila atumwi ake usiku pomwe anayambitsa mwambowu.​—Luka 22:29, 30.