Yehova Anamucha kuti “Bwenzi Langa”
“Iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga, iwe Yakobo amene ndakusankha, mbeu ya bwenzi langa Abulahamu.”—YESAYA 41:8.
1, 2. (a) Timadziŵa bwanji kuti anthu angakhale mabwenzi a Mulungu? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?
PAUMOYO wathu wonse, anthufe timafuna kukondedwa. Timafuna kukondedwa ndi mwamuna kapena mkazi wathu komanso kukhala ndi mabwenzi ena apamtima. Koma koposa zonse, timafuna kukondedwa ndi Yehova. Anthu ambili amakhulupilila kuti popeza kuti Mulungu saoneka ndipo ndi wamphamvuyonse, n’zosatheka kukhala naye pa ubwenzi weniweni. Koma zimenezi si zoona.
2 Baibulo limakamba kuti anthu ena anali mabwenzi a Mulungu. Conco, ife tiyenela kutengela citsanzo cao. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti kukhala paubwenzi ndi Mulungu ndiye colinga cacikulu cimene tingakhale naco pa umoyo wathu. Tsopano, tiyeni tikambilane citsanzo ca Abulahamu. (Ŵelengani Yakobo 2:23.) Kodi iye anakhala bwanji bwenzi la Mulungu? Abulahamu anakhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu cifukwa cakuti anali ndi cikhulupililo. Iye amachedwa “tate wa onse . . . okhala ndi cikhulupililo.” (Aroma 4:11) Pamene tikukambilana citsanzo cake, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndingatengele bwanji cikhulupililo ca Abulahamu kuti ndilimbitse ubwenzi wanga ndi Yehova?’
N’CIANI CINATHANDIZA ABULAHAMU KUKHALA BWENZI LA YEHOVA?
3, 4. (a) Ndi nthawi iti pamene cikhulupililo ca Abulahamu cinayesedwa kwambili? (b) N’cifukwa ciani Abulahamu anali wokonzeka kupeleka Isaki nsembe?
3 Yelekezelani kuti mukuona Abulahamu ali ndi zaka pafupifupi 125, ndipo akuyenda pang’onopang’ono kukwela phili. [1] (Onani mau akumapeto.) Mwana wake Isaki, amene ali ndi zaka pafupifupi 25, akumulondola. Isaki wanyamula nkhuni ndipo Abulahamu wanyamula mpeni ndi zoyatsila moto. Ulendowo uyenela kuti unali wovuta kwambili pa maulendo onse a Abulahamu. Koma osati cifukwa cakuti anali wokalamba. Iye anali akali ndi mphamvu. Unali ulendo wovuta cifukwa cakuti Yehova anamuuza kuti apeleke nsembe mwana wake.—Genesis 22:1-8.
Sikuti Abulahamu anamvela Mulungu m’cimbulimbuli, kapena kuti mosaganiza bwino
4 Mwina apa m’pamene cikhulupililo ca Abulahamu cinayesedwa kwambili. Anthu ena amakamba kuti pamene Mulungu anauza Abulahamu kupeleka mwana wake nsembe, anacita zinthu mwankhanza. Enanso amakamba kuti Abulahamu sanali kukonda mwana wake, ndiye cifukwa cake anali wokonzeka kumupeleka monga nsembe. Anthu amakamba zimenezi cifukwa cakuti alibe cikhulupililo. Iwo sadziŵa kuti cikhulupililo ceniceni n’ciani, kapena sadziŵa mmene cimagwilila nchito. (1 Akorinto 2:14-16) Koma sikuti Abulahamu anamvela Mulungu m’cimbulimbuli, kapena kuti mosaganiza bwino. Iye anamvela Mulungu cifukwa cakuti anali ndi cikhulupililo ceniceni. Iye anadziŵa kuti Yehova sangamulamule kucita zinthu zimene zingamukhumudwitse kwa moyo wake wonse. Abulahamu anadziŵa kuti ngati wamvela Yehova, Iye adzamudalitsa limodzi ndi mwana wake. N’ciani cinathandiza Abulahamu kukhala ndi cikhulupililo colimba? Iye anali kum’dziŵa bwino Mulungu ndipo anakumana ndi zinthu zimene zinalimbitsa cikhulupililo cake.
5. Kodi zioneka kuti Abulahamu anaphunzila bwanji za Yehova? Nanga zimene anaphunzila zinam’thandiza bwanji?
Yoswa 24:2) Nanga kodi Abulahamu anaphunzilila kuti za Yehova? Baibulo limaonetsa kuti Semu mwana wa Nowa, anali wacibale wa Abulahamu. Iye anamwalila pamene Abulahamu anali ndi zaka pafupifupi 150. Semu anali ndi cikhulupililo colimba, ndipo zioneka kuti anali kuuzako acibale ake za Yehova. Mwina, umu ndi mmene Abulahamu anaphunzilila za Yehova. Zimene Abulahamu anaphunzila, zinam’cititsa kukonda kwambili Yehova ndi kulimbitsa cikhulupililo cake.
5 Kuphunzila za Mulungu. Abulahamu anakulila mumzinda wa Uri. Anthu mumzindawo anali kulambila milungu yonama, ndipo ngakhale atate ake a Abulahamu anali kucita zimenezi. (6, 7. Kodi zimene zinacitikila Abulahamu zinalimbitsa bwanji cikhulupililo cake?
6 Zocitika pa umoyo wake. Kodi zocitika pa umoyo wa Abulahamu zinam’thandiza bwanji kulimbitsa cikhulupililo cake mwa Yehova? Anthu ambili amakamba kuti maganizo amakhudza mtima wa munthu. Abulahamu anakhudzidwa mtima ndi zimene anaphunzila zokhudza Yehova. Izi zinamulimbikitsa kulemekeza “Yehova Mulungu Wam’mwambamwamba, amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 14:22) Baibulo limakamba kuti ulemu umenewo ndiwo “kuopa Mulungu.” (Aheberi 5:7) Kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu, tiyenela kumuopa. (Salimo 25:14) Khalidwe limeneli ndi limene linalimbikitsa Abulahamu kumvela Yehova.
7 Mulungu anauza Abulahamu ndi Sara kuti asamuke mumzinda wa Uri ndi kukakhala ku dziko lacilendo. Iwo anali acikulile koma anafunika kusamuka ndi kukakhala m’misasa kwa umoyo wao wonse. Ngakhale kuti Abulahamu anadziŵa kuti adzakumana ndi mavuto ambili, anali wofunitsitsa kumvela Yehova. Cifukwa cakuti anali womvela, Mulungu anam’dalitsa ndi kum’teteza. Mwacitsanzo, maulendo angapo, Sara, mkazi wokongola wa Abulahamu, anatengedwa ndi Mfumu. Panthawiyo, Abulahamu akanaphedwa, koma mozizwitsa Yehova anawateteza onse aŵili. (Genesis 12:10-20; 20:2-7, 10-12, 17, 18) Zocitika zimenezi zinalimbitsa cikhulupililo ca Abulahamu.
8. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tim’dziŵe bwino Yehova ndi kum’mvela?
8 Kodi nafenso tingathe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova? Inde. Monga mmene Abulahamu anacitila, tiyenela kuphunzila za Yehova. Tikatelo, nafenso tidzamudziŵa bwino Mulungu, Danieli 12:4; Aroma 11:33) Baibulo limatiuza zambili zokhudza Mulungu “amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.” Zimene timaphunzila zimatithandiza kukonda Yehova ndi kum’lemekeza kwambili. Kucita zimenezi kumatilimbikitsa kumumvela. Tikamamvela Mulungu, iye amatiteteza ndi kutidalitsa ndipo zimenezi zimalimbitsa cikhulupililo cathu. Ngati titumikila Yehova mokwanila, tidzakhala okhutila, acimwemwe, komanso tidzakhala ndi mtendele wa m’maganizo. (Salimo 34:8; Miyambo 10:22) Pamene tikuphunzila zambili zokhudza Mulungu ndi kuona mmene akutithandizila, ubwenzi wathu ndi iye umalimba kwambili.
ndipo masiku ano tili ndi zinthu zambili zotithandiza kuposa zimene Abulahamu anali nazo. (ZIMENE ZINATHANDIZA ABULAHAMU KUKHALABE PA UBWENZI NDI MULUNGU
9, 10. (a) Kodi cofunika n’ciani kuti ubwenzi ukhale wolimba? (b) N’ciani cionetsa kuti Abulahamu analimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova ndi kuuona kukhala wamtengo wapatali?
9 Ubwenzi wolimba uli ngati cuma cam’tengo wapatali. Timafunika kuulimbitsa “nthawi zonse.” (Ŵelengani Miyambo 17:17.) Ubwenzi umenewu suli ngati mphika wodula wokongoletsela m’nyumba. Koma uli ngati maluŵa okongola amene amafuna madzi ndi cisamalilo kuti azioneka bwino. Abulahamu anaona ubwenzi wake ndi Yehova kukhala cinthu camtengo wapatali ndipo anali kuuteteza. Kodi anacita bwanji zimenezi?
Ubwenzi uli ngati maluŵa okongola amene amafuna madzi ndi cisamalilo kuti akule bwino
10 Abulahamu anali kuopa kwambili Mulungu ndi kumumvela. Mwacitsanzo, pamene anapita ku Kanani ndi banja lake pamodzi ndi atumiki ake, iye anapitiliza kudalila Yehova popanga zosankha zazikulu ndi zazing’ono. Kutatsala caka cimodzi kuti Isaki abadwe, Yehova anauza Abulahamu kuti acite mdulidwe wa amuna onse okhala m’nyumba yake. Panthawiyo, Abulahamu anali ndi zaka 99. Kodi Abulahamu anakaikila Yehova kapena kupeleka zifukwa zodzikhululukila n’colinga cakuti asacite zimene Mulungu anamuuza? Ayi. Iye anakhulupilila Yehova ndi kumumvela “tsiku lomwelo.”—Genesis 17:10-14, 23.
11. N’cifukwa ciani Abulahamu anada nkhawa atamva kuti Sodomu ndi Gomora adzaonongedwa? Nanga Yehova anam’thandiza bwanji?
11 Cifukwa cakuti Abulahamu anali kumvela Yehova ngakhale pa zinthu zing’onozing’ono, ubwenzi wake ndi Mulungu unalimba kwambili. Iye anali kuuza Yehova zilizonse ngakhale zinthu zimene zinali kumuvutitsa maganizo. Mwacitsanzo, pamene Yehova anakamba kuti adzaononga mizinda ya Sodomu ndi Gomora, Abulahamu anada nkhawa. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anali kuganiza kuti anthu abwino adzaonongedwa pamodzi ndi anthu oipa. Mwina anali kudela nkhawa wacibale wake Loti ndi banja lake amene anali kukhala ku Sodomu. Popeza kuti anali kukhulupilila Yehova, “Woweluza wa dziko lonse lapansi,” iye anamuuza nkhawa imene anali nayo. Yehova anacita zinthu moleza mtima ndi bwenzi lake Abulahamu, ndipo anam’thandiza kudziŵa kuti Iye ndi Mulungu wacifundo. Genesis 18:22-33.
Iye anauza Abulahamu kuti nthawi zonse akamapeleka ciweluzo, amafufuza anthu abwino ndi kuwapulumutsa.—12, 13. (a) Kodi zimene Abulahamu anaphunzila ndi zocitika pa umoyo wake zinamuthandiza bwanji panthawi ina? (b) N’ciani cimene cionetsa kuti Abulahamu anali kukhulupilila Yehova?
12 N’zoonekelatu kuti zinthu zimene Abulahamu anadziŵa zokhudza Mulungu ndiponso zimene zinacitika pa umoyo wake, zinamuthandiza kuti akhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Conco, pamene Yehova anauza Abulahamu kuti apeleke mwana wake nsembe, Abulahamu anadziŵa kuti nthawi zonse Yehova anali kumucitila zinthu moleza mtima, mwacifundo, mokhulupilika ndiponso anali kumuteteza. Abulahamu anadziŵa kuti Yehova sangasinthe mwadzidzidzi ndi kukhala wankhanza. N’cifukwa ciani tikunena zimenezi?
13 Asanasiye atumiki ake, Abulahamu anawauza kuti: “Inu tsalani pano ndi buluyu, ine ndi mwana wangayu tikupita uko kukalambila, tikupezani.” (Genesis 22:5) Kodi pamenepa Abulahamu anatanthauza ciani? Kodi anali kuwanamiza kuti adzabwelela ndi Isaki pamene akudziŵa kuti adzam’peleka nsembe? Iyai sanali kuwanamiza. Baibulo limakamba kuti Abulahamu anali kudziŵa kuti Yehova angathe kuukitsa Isaki kwa akufa. (Ŵelengani Aheberi 11:19.) Abulahamu anali kudziŵa kuti Yehova ndiye anamupatsa mphamvu zoti akhale ndi mwana ngakhale kuti iye ndi Sara anali okalamba kwambili. (Aheberi 11:11, 12, 18) Cotelo, anali kudziŵa kuti palibe cimene Yehova angalephele. Abulahamu sanali kudziŵa kuti cicitike n’ciani. Koma anali ndi cikhulupililo cakuti panthawi ina iliyonse, Yehova akhoza kuukitsa Isaki kuti malonjezo ake onse akwanilitsidwe. Ndiye cifukwa cake Abulahamu amachedwa “tate wa onse . . . okhala ndi cikhulupililo.”
Abulahamu anali ndi cikhulupililo cakuti panthawi ina iliyonse, Yehova akhoza kuukitsa Isaki kuti malonjezo ake onse akwanilitsidwe
14. Ndi mavuto otani amene mumakumana nao potumikila Yehova? Nanga citsanzo ca Abulahamu cingakuthandizeni bwanji?
14 Masiku ano, Yehova sangatipemphe kupeleka nsembe ana athu, koma amatipempha kuti tizimvela malamulo ake. Nthawi zina, sitingamvetse cifukwa cimene Mulungu watipatsila malamulo ena ake, kapena tingaone kuti malamulowo ndi ovuta kuwatsatila. Kodi nanunso mumamva conco? Ena amaona kuti nchito yolalikila ndi yovuta. Mwina, n’cifukwa cakuti ali ndi manyazi ndipo zimawavuta kukamba ndi anthu amene sadziŵa. Ena amaopa kukhala osiyana ndi anzawo kunchito kapena kusukulu. (Ekisodo 23:2; 1 Atesalonika 2:2) Ngati mwauzidwa kucita zinthu zimene muona kuti n’zovuta, muzikumbukila citsanzo ca Abulahamu pankhani ya cikhulupililo ndi kulimba mtima. Ngati tisinkhasinkha zitsanzo za amuna ndi akazi okhulupilika, tidzalimbikitsidwa kuwatsanzila ndi kuyandikila Bwenzi lathu, Yehova.—Aheberi 12:1, 2.
UBWENZI UMENE UMABWELETSA MADALITSO
15. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti Abulahamu sanadziimbepo mlandu cifukwa cokhala wokhulupilika kwa Yehova?
15 Kodi Abulahamu anadziimbapo mlandu cifukwa comvela malamulo a Yehova? Genesis 25:8) Pamene anali ndi zaka 175, Abulahamu anali kukhala wokhutila akaganizila za umoyo wake. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti nthawi zonse, anali kuona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndiwo cinthu cofunika kwambili. Komabe, pamene Baibulo limakamba kuti Abulahamu anali “wokalamba . . . ndi wokhutila,” sizitanthauza kuti iye anali kufuna kufa.
Baibulo limakamba kuti Abulahamu “anamwalila ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino, wautali ndi wokhutila.” (16. Ndi zinthu zina ziti zimene Abulahamu adzasangalala nazo m’Paladaiso?
16 Baibulo limakamba kuti Abulahamu “anali kuyembekezela mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.” (Aheberi 11:10) Abulahamu anali kukhulupilila kuti adzaona mzinda umenewo, umene ndi Ufumu wa Mulungu, ukulamulila dziko lonse lapansi. Ndipo n’zoona adzauonadi. Mwacionekele, Abulahamu adzasangalala kwambili m’paladaiso. Iye adzapitiliza kulimbitsa ubwenzi wake ndi Mulungu. Adzakondwela kudziŵa kuti kwa zaka zambili citsanzo cake cathandiza atumiki a Mulungu kukhala okhulupilika. M’paladaiso, iye adzadziŵa kuti nsembe ya pa phili la Moriya inaimila cinthu cacikulu kwambili. (Aheberi 11:19) Ndipo adzadziŵanso kuti anthu okhulupilika mamiliyoni ambili akaganizila mmene iye anamvelela pamene anali kufuna kupeleka mwana wake, amamvetsa mmene Yehova anamvelela pamene anapeleka Mwana wake, Yesu Kristu, kukhala dipo la anthu. (Yohane 3:16) Citsanzo ca Abulahamu cimatithandiza kuyamikila kwambili dipo, limene ndi njila yaikulu imene Mulungu anatisonyezela cikondi.
17. Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciani? Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?
17 Motelo, tiyeni tonse tiziyesetsa kutengela cikhulupililo ca Abulahamu. Mofanana ndi Abulahamu, tifunika kum’dziŵa bwino Mulungu ndi kumumvela. Pamene tipitiliza kuphunzila za Yehova ndi kumumvela, iye adzatidalitsa ndi kutiteteza. (Ŵelengani Aheberi 6:10-12.) Tikatelo, Yehova adzakhala Bwenzi lathu mpaka kalekale. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zitsanzo zitatu za anthu okhulupilika amene anakhala mabwenzi a Mulungu.
^ [1] (ndime 3) Poyamba, Abulahamu anali kuchedwa Abulamu, ndipo Sara anali kucedwa Sarai. Koma m’nkhani ino, tagwilitsila nchito maina amene Yehova anawapatsa.