Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tengelani Citsanzo ca Atumiki Okhulupilika a Yehova

Tengelani Citsanzo ca Atumiki Okhulupilika a Yehova

“Kodi Yehova akufuna ciani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzicita cilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako.”—MIKA 6:8.

NYIMBO: 63, 43

1, 2. Kodi Davide anaonetsa bwanji kuti anali wokhulupilika kwa Mulungu? (Onani cithunzi pamwamba.)

SAULI ndi asilikali ake 3,000, anali kufunafuna Davide m’cipululu ca Yuda kuti amuphe. Koma usiku wina, Davide ndi anthu ake anapeza malo amene Sauli ndi asilikali ake anamangapo msasa. Iwo anali gone, conco Davide ndi Abisai anayenda mosamala pang’onopang’ono kudutsa asilikaliwo ndi kufika pamene panali Sauli. Ndiyeno Abisai anauza Davide capansipansi kuti: “Ndilole conde, ndimubaye ndi kumukhomelela pansi ndi mkondo kamodzi kokha, sindicita kubweleza kaŵili.” Koma Davide sanam’lole kuti aphe Sauli. Iye anauza Abisai kuti: “Ayi, usamuphe. Kodi ndani anatambasula dzanja lake ndi kupha wodzozedwa wa Yehova, n’kukhala wopanda mlandu?” Davide anapitiliza kunena kuti: “Kwa ine, n’zosatheka! Sindingacite zimenezi pamaso pa Yehova. Sindingatambasule dzanja langa ndi kukantha wodzozedwa wa Yehova.”—1 Samueli 26:8-12.

2 Davide anadziŵa zimene anayenela kucita kuti akhalebe wokhulupilika kwa Yehova. Iye anadziŵa kuti afunika kulemekeza Sauli, ndipo sanaganizileko zomucitila coipa ciliconse. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Mulungu ndiye anasankha Sauli kukhala mfumu ya Aisiraeli. Monga kale, Yehova amafunanso kuti atumiki ake onse akhale okhulupilika kwa iye ndi kuti azilemekeza anthu amene iye walola kuti azitsogolela.—Ŵelengani Mika 6:8.

3. Kodi Abisai anaonetsa bwanji kuti anali wokhulupilika kwa Davide?

3 Abisai anali kulemekeza Davide cifukwa anali kudziŵa kuti Davide anasankhidwa ndi Mulungu kuti akhale mfumu. Komabe, atakhala mfumu, Davide anacita macimo aakulu. Iye anagona ndi mkazi wa Uriya, kenako anauza Yowabu kuti aonesetse kuti Uriya waphedwa ku nkhondo. (2 Samueli 11:2-4, 14, 15; 1 Mbiri 2:16) Yowabu anali m’bale wa Abisai, conco n’kutheka kuti Abisai anamva zimene Davide anacita. Komabe, iye anapitilizabe kulemekeza Davide. Kuonjezela pamenepo, Abisai anali mkulu wa asilikali ndipo akanafuna akanadziika kukhala mfumu, koma sanacite zimenezo. M’malomwake, anali kutumikila Davide ndi kum’teteza kwa adani ake.—2 Samueli 10:10; 20:6; 21:15-17.

4. (a) Kodi Davide anaonetsa bwanji kuti anali wokhulupilika kwa Mulungu? (b) Tikambilana zitsanzo zina ziti?

4 Davide anali wokhulupilika kwa Yehova pa umoyo wake wonse. Pamene anali wacinyamata, iye anapha cimphona cochedwa Goliyati cimene cinali kutukwana Yehova ndi Aisiraeli. (1 Samueli 17:23, 26, 48-51) Ndipo Davide atakhala mfumu, mneneli wa Yehova Natani anam’patsa uphungu cifukwa ca macimo amene anacita. Iye anavomeleza mwamsanga macimo ake ndipo analapa. (2 Samueli 12:1-5, 13) Davide atakalamba, anapeleka zinthu zambili zamtengo wapatali zomangila kacisi wa Yehova. (1 Mbiri 29:1-5) Ngakhale kuti anacita macimo aakulu pa umoyo wake, iye anapitilizabe kukhala wokhulupilika kwa Mulungu. (Salimo 51:4, 10; 86:2) M’nkhani ino, tikambilana citsanzo ca Davide ndi ena amene anakhalako m’nthawi yake. Kukambilana zimenezi kutithandiza kudziŵa zimene tingacite kuti tikhale okhulupilika kwa Yehova kuposa kwa wina aliyense. Tikambilananso makhalidwe ena amene tiyenela kukhala nao kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova.

KODI MUDZAKHALABE WOKHULUPILIKA KWA YEHOVA?

5. Ndi mfundo yofunika iti imene tikuphunzila pa maganizo olakwika amene Abisai anali nao?

5 Pamene Abisai anafuna kupha Sauli, anali kufuna kuonetsa kukhulupilika kwake kwa Davide. Koma Davide anadziŵa kuti n’kulakwa kucitila coipa “wodzozedwa wa Yehova.” Ndiye cifukwa cake sanalole Abisai kupha mfumu. (1 Samueli 26:8-11) Apa tikuphunzilapo mfundo yofunika kwambili yakuti: Ngati pacitika zinazake ndipo tifuna kusankha kuti tikhala wokhulupilika kwa ndani, tiyenela kuganizila mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize.

Cofunika kwambili ndi kukhala wokhulupilika kwa Yehova kuposa kwa munthu wina aliyense

6. Ngakhale kuti timafuna kukhala okhulupilika kwa acibale athu ndi anzathu, n’cifukwa ciani tiyenela kusamala?

6 Anthufe timafuna kukhala okhulupilika kwa anthu amene timawakonda, monga anzathu kapena acibale athu. Koma cifukwa ca kupanda ungwilo, tikhoza kuona zinthu molakwika. (Yeremiya 17:9) Conco, ngati munthu amene timakonda wacita colakwa ndipo wacotsedwa mumpingo, tiyenela kukumbukila kuti cofunika kwambili ndi kukhala wokhulupilika kwa Yehova kuposa kwa wina aliyense.—Ŵelengani Mateyu 22:37.

7. Kodi mlongo wina anaonetsa bwanji kukhulupilika kwa Mulungu ngakhale panthawi zovuta?

7 Ngati wina m’banja lanu wacotsedwa mumpingo, mukhoza kukhala wokhulupilika kwa Yehova. Mwacitsanzo, tsiku lina, amai ake a Anne, amene anali ocotsedwa, anam’tumila foni ndi kukamba kuti akufuna kudzam’cezela. [1] (Onani mau akumapeto.) Iwo anakamba kuti ndi okhumudwa kwambili cifukwa cakuti onse m’banja lao sawakambitsa. Anne sanasangalale ndi zimenezo, ndipo anawalonjeza kuti adzawalembela kalata. Asanalembe kalatayo, Anne anasinkhasinkha mfundo za m’Baibulo. (1  Akorinto 5:11; 2 Yohane 9-11) Ndiyeno, m’kalatayo, iye mokoma mtima anawafotokozela kuti io ndi amene anakhumudwitsa banja lao cifukwa cakuti anacimwa ndipo sanalape. Anne anauza amai ake kuti angakhalenso osangalala kokha ngati abwelela kwa Yehova.—Yakobo 4:8.

8. Ndi makhalidwe ati amene angatithandize kukhala okhulupilika kwa Yehova?

8 Atumiki okhulupilika a Mulungu m’nthawi ya Davide analinso odzicepetsa, okoma mtima, ndiponso olimba mtima. Tiyeni tikambilane mmene makhalidwe amenewa angatithandizile kukhala okhulupilika kwa Yehova.

TIYENELA KUKHALA ODZICEPETSA

9. N’cifukwa ciani Abineri anafuna kupha Davide?

9 Mwana wa Sauli Yonatani, ndiponso mtsogoleli wa gulu lankhondo, Abineri, analipo pamene Davide anabweletsa mutu wa Goliyati kwa Mfumu Sauli. Yonatani anakhala bwenzi la Davide ndipo anakhalabe wokhulupilika kwa iye. (1 Samueli 17:57–18:3) Koma Abineri sanakhale bwenzi lake. Ndipo pambuyo pake, Abineri anathandiza Sauli, amene anafuna kupha Davide. (1 Samueli 26:1-5; Salimo 54:3) Onse aŵili, Yonatani ndi Abineri, anadziŵa kuti Mulungu anasankha Davide kuti akhale mfumu yotsatila ya Isiraeli. Koma Sauli atafa, Abineri sanakhale ku mbali ya Davide. M’malomwake, anafuna kuika Isi-boseti, mwana wa Sauli kukhala mfumu. Zioneka kuti panthawi ina Abineri analinso kufuna kukhala mfumu. Mwina ndiye cifukwa cake anagona ndi mdzakazi wa Mfumu Sauli. (2 Samueli 2:8-10; 3:6-11) N’cifukwa ciani Yonatani ndi Abineri anali kuona Davide mosiyana kwambili? Cifukwa cakuti Yonatani anali wokhulupilika kwa Yehova ndiponso anali wodzicepetsa. Koma Abineri anali wodzikuza ndi wosakhulupilika.

10. N’cifukwa ciani Abisalomu sanali wokhulupilika kwa Mulungu?

10 Abisalomu, mwana wa Mfumu Davide, sanali wokhulupilika kwa Mulungu cifukwa cakuti sanali wodzicepetsa. Iye anali kufuna kukhala mfumu. Conco, anatenga “galeta lokokedwa ndi mahachi, ndipo amuna 50 anali kuthamanga patsogolo pake.” (2 Samueli 15:1) Abisalomu anakopanso Aisiraeli ena kuti akhale kumbali yake. Anafika pofuna kupha atate ake, ngakhale kuti anadziŵa kuti Davide anasankhidwa ndi Yehova kuti akhale mfumu ya Aisiraeli.—2 Samueli 15:13, 14; 17:1-4.

11. Kodi zitsanzo za m’Baibulo za Abineri, Abisalomu, ndi Baruki zingatipindulitse bwanji?

11 Ngati munthu si wodzicepetsa ndipo afuna kukhala ndi ulamulilo, cimakhala covuta kuti akhalebe wokhulupilika kwa Mulungu. N’zoona kuti timakonda Yehova, ndipo sitifuna kukhala wodzikonda ndi woipa monga Abineri ndi Abisalomu. Koma tiyenela kusamala kuti tisayambe kukonda kwambili ndalama, kapena kufuna nchito yapamwamba. Kucita zimenezi kungasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Panthawi ina, Baruki mlembi wa Yeremiya, anali kufuna kukhala ndi zinthu zazikulu. Izi zinam’cititsa kuti asamasangalale potumikila Mulungu. Ndiyeno, Yehova anauza Baruki kuti: “Taona! Zimene ndamanga, ndikuzigwetsa, ndipo zimene ndabzala, ndikuzizula. Ndicita zimenezi m’dziko lonse. Koma iwe, ukufunafunabe zinthu zazikulu. Leka kuzifunafuna.” (Yeremiya 45:4, 5) Baruki anamvela Yehova. Ifenso tiyenela kumumvela cifukwa posacedwapa adzaononga dziko loipali.

Mukauza mkristu mnzanu kuti akapemphe thandizo kwa akulu, ndiye kuti mukucita zinthu mokoma mtima ndiponso ndinu wokhulupilika kwa Yehova

12. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti sitingakhale okhulupilika kwa Mulungu ngati ndife odzikonda?

12 M’bale wina wa ku Mexico, dzina lake Daniel, anafunika kusankha kuti adzakhala wokhulupilika kwa ndani. Anafuna kukwatila mtsikana amene sanali kutumikila Yehova. Daniel anati: “Ndinapitilizabe kutumila mtsikanayo mameseji ngakhale pamene ndinakhala mpainiya.” Ndiyeno anazindikila kuti anali kucita zinthu modzikonda. Iye sanali wokhulupilika kwa Yehova, ndipo anafunika kukhala wodzicepetsa. Conco, anauzako mkulu wofikapo za mtsikanayo. Daniel anafotokoza kuti: “Mkuluyo anandithandiza kuzindikila kuti ngati ndifuna kukhala wokhulupilika kwa Mulungu, ndiyenela kuleka kutumizila mtsikanayo mameseji. Pambuyo popeleka mapemphelo ambili uku ndikulila, ndinaleka kum’tumila mameseji. Patapita nthawi yocepa, ndiyamba kusangalala kwambili ndi utumiki.” Tsopano Daniel anakwatila mkazi amene amakonda Yehova, ndipo akutumikila monga woyang’anila dela.

KUKHALA WOKHULUPILIKA KWA MULUNGU KUMATITHANDIZA KUKHALA WOKOMA MTIMA

Ngati mwadziŵa kuti mnzanu wacita chimo lalikulu, kodi mudzakambilana naye ndi kuonetsetsa kuti walandila thandizo la akulu? (Onani ndime 14)

13. Davide atacimwa, kodi Natani anaonetsa bwanji kuti anali wokhulupilika kwa Mulungu ndiponso kwa Davide?

13 Tikakhala okhulupilika kwa Yehova, tidzakhalanso okhulupilika kwa ena ndipo tidzayesetsa kuwathandiza. Mneneli Natani anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova ndiponso kwa Davide. Pamene Davide anatenga mkazi wa munthu wina ndi kupha mwamuna wake, Yehova anatuma Natani kuti akam’patse uphungu. Natani anali wolimba mtima ndipo anamvela Yehova. Koma anacitanso zinthu mwanzelu mwa kukamba mokoma mtima ndi Davide. Iye anafuna kuti Davide azindikile kuti anacita macimo aakulu. Conco anauza Davide fanizo la munthu wolemela amene anaba kamwana ka nkhosa kamodzi kokha ka munthu wosauka. Davide atamva fanizolo, anakwiya kwambili ndi zimene munthu wolemelayo anacita. Kenako Natani anamuuza kuti: “Munthu ameneyo ndiwe!” Davide anazindikila kuti wacimwila Yehova.—2 Samueli 12:1-7, 13.

14. Mungaonetse bwanji kuti ndinu wokhulupilika kwa Yehova ndi kwa mnzanu kapena wacibale?

14 Inunso mungakhale wokhulupilika kwa Yehova ndi kwa ena mwa kukhala wokoma mtima. Mwacitsanzo, mungakhale ndi umboni wokwanila wakuti Mkristu wina wacita chimo lalikulu. Pamenepa, mwina mungafune kukhala wokhulupilika kwa iye makamaka ngati ndi mnzanu wapamtima kapena wacibale wanu. Koma mukudziŵanso kuti kukhala wokhulupilika kwa Yehova ndiye kofunika kwambili. Ngati zakhala conco, muyenela kumvela Yehova ndi kucita zinthu mokoma mtima kwa Mkristuyo monga mmene Natani anacitila. Muuzeni kuti akapemphe thandizo kwa akulu mwamsanga. Ngati sanacite zimenezo, inuyo mukauze akulu za colakwaco. Mukacita zimenezo, mudzaonetsa kuti ndinu wokhulupilika kwa Yehova. Komanso, ndiye kuti mwamucitila zinthu mokoma mtima cifukwa akulu adzamuthandiza kukhalanso paubwenzi wabwino ndi Yehova. Iwo adzamuongolela mwacikondi ndi mokoma mtima.—Ŵelengani Levitiko 5:1; Agalatiya 6:1.

TIMAFUNIKA KULIMBA MTIMA KUTI TIKHALE OKHULUPILIKA KWA MULUNGU

15, 16. N’cifukwa ciani Husai anafunika kulimba mtima kuti akhalebe wokhulupilika kwa Mulungu?

15 Husai anali mmodzi wa mabwenzi okhulupililka a Mfumu Davide. Pamene anthu anafuna kuika Abisalomu kukhala mfumu, Husai anafunika kulimba mtima kuti akhale wokhulupilika kwa Davide ndi kwa Mulungu. Iye anadziŵa kuti Abisalomu ndi asilikali ake aloŵa mu Yerusalemu ndipo Davide wathaŵa. (2 Samueli 15:13; 16:15) Koma kodi Husai anacita ciani? Kodi anasiya Davide n’kutsatila Abisalomu? Iyai. Ngakhale kuti Davide anali wokalamba ndipo anthu ambili anali kufuna kumupha, Husai anakhalabe wokhulupilika kwa iye cifukwa Yehova ndiye anasankha Davide kukhala mfumu. Conco, Husai anapita ku Phili la Maolivi kukakumana ndi Davide.—2 Samueli 15:30, 32.

16 Davide anauza Husai kuti abwelele ku Yerusalemu ndi kukadzionetsa monga bwenzi la Abisalomu, kuti akacititse Abisalomu kumvela malangizo ake osati a Ahitofeli. Husai anali wolimba mtima ndipo anaika moyo wake pangozi mwa kumvela Davide ndi kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Davide anapempha Yehova kuti athandize Husai, ndipo Iye anam’thandizadi. Abisalomu anamvela malangizo a Husai osati a Ahitofeli.—2 Samueli 15:31; 17:14.

17. N’cifukwa ciani tifunika kulimba mtima kuti tikhale okhulupilika?

17 Timafunika kulimba mtima kuti tikhale okhulupilika kwa Yehova ndi kumumvela m’malo momvela zilizonse zimene a m’banja lathu, anzathu a ku nchito, ndi akuluakulu a boma amatiuza kucita. Mwacitsanzo, Taro, amene akukhala ku Japan, anali kucita zimene angathe kuti akondweletse makolo ake kuyambila ali mwana. Iye anali kuwamvela ndi kukhala wokhulupilika kwa io osati cifukwa cakuti anali kufunika kucita zimenezi, koma cifukwa cowakonda. Koma pamene anayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova, makolo ake anamuuza kuti aleke. Zimenezi zinam’khumudwitsa kwambili, ndipo cinali covuta kwa iye kuwafotokozela kuti waganiza zoyamba kupezeka pamisonkhano. Taro anakamba kuti: “Iwo anakwiya kwambili cakuti kwa zaka zambili, anali kundiletsa kupita kukawacezela kunyumba. Ndinapempha Yehova kuti andithandize kukhala wolimba mtima kuti ndisasinthe maganizo anga. Tsopano, io anasintha ndipo ndimapita kukawacezela nthawi zambili.”—Ŵelengani Miyambo 29:25.

18. Mwapindula bwanji ndi nkhani ino?

18 Tiyeni tikhalebe okhulupilika kwa Yehova mofanana ndi Davide, Yonatani, Natani, ndi Husai. Tikatelo tidzakhala ndi umoyo wosangalala. Sitifuna kukhala monga Abineri ndi Abisalomu, amene sanali okhulupilika. N’zoona kuti ndife opanda ungwilo ndipo timalakwitsa. Koma tiyeni tionetse kuti cinthu cofunika kwambili pa umoyo wathu ndi kukhala okhulupilika kwa Yehova.

^ [1] (ndime 7) maina ena asinthidwa.