Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Khalani Wokhulupilika kwa Yehova

Khalani Wokhulupilika kwa Yehova

“Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndi pakati pa ana ako ndi ana anga mpaka kalekale.”—1 SAMUELI 20:42.

NYIMBO: 125, 62

1, 2. N’cifukwa ciani ubwenzi wa Davide ndi Yonatani ndi citsanzo cabwino ca kukhulupilika?

YONATANI ayenela kuti anacita cidwi kwambili ndi kulimba mtima kwa Davide, amene anali wacinyamata. Davide anali atapha cimphona cochedwa Goliyati, ndipo anapeleka “mutu wa Mfilisiti” ameneyu kwa Mfumu Sauli, atate ake a Yonatani. (1 Samueli 17:57) Ataona zimenezi, Yonatani sanakaikile kuti Mulungu ali ku mbali ya Davide. Kucokela nthawi imeneyo, Yonatani ndi Davide anakhala mabwenzi apamtima. Iwo anacita pangano lakuti adzakhalabe okhulupilika kwa wina ndi mnzake. (1 Samueli 18:1-3) Yonatani anakhalabe wokhulupilika kwa Davide kwa moyo wake wonse.

2 Yonatani anakhala wokhulupilika kwa Davide ngakhale kuti Yehova anasankha Davide m’malo mosankha iye kukhala mfumu yotsatila ya Aisiraeli. Ndipo pamene Sauli anafuna kupha Davide, Yonatani anadela nkhawa bwenzi lake limeneli. Yonatani anadziŵa kuti Davide anali m’cipululu ku Horesi. Cotelo, anapita kumeneko kukamulimbikitsa kuti apitilize kudalila Yehova. Iye anauza Davide kuti: “Usacite mantha, cifukwa dzanja la Sauli bambo anga silikupeza, moti iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala waciŵili kwa iwe.”—1 Samueli 23:16, 17.

3. N’ciani cinali cofunika kwambili kwa Yonatani kuposa kukhala wokhulupilika kwa Davide? Nanga tidziŵa bwanji zimenezi? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

3 Nthawi zambili, anthu okhulupilika timawakonda. Koma kodi timakonda Yonatani cabe cifukwa cakuti anali wokhulupilika kwa Davide? Iyai. Kukhala wokhulupilika kwa Mulungu cinali cinthu cofunika kwambili pa umoyo wa Yonatani. Ndiye cifukwa cake iye anali wokhulupilika kwa Davide ndipo sanali kumucitila nsanje ngakhale kuti Davide anali kudzakhala mfumu m’malo mwa iye. Yonatani analimbikitsa Davide kudalila Yehova. Iwo anakhalabe okhulupilika kwa Yehova ndi kwa wina ndi mnzake. Ndipo anasunga pangano lao lakuti: “Yehova akhale pakati pa iwe ndi ine, ndi pakati pa ana ako ndi ana anga mpaka kalekale.”—1 Samueli 20:42.

4. (a) N’ciani cingatithandize kukhaladi osangalala komanso okhutila? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?

4 Ifenso tiyenela kukhala okhulupilika kwa a m’banja lathu, mabwenzi athu, komanso kwa abale ndi alongo mumpingo. (1 Atesalonika 2:10, 11) Koma koposa zonse, tiyenela kukhala wokhulupilika kwa Yehova. Iye ndi amene anatipatsa moyo. (Chivumbulutso 4:11) Tikakhala okhulupilika kwa Yehova, timakhala osangalala ndi okhutila. Koma tidziŵa kuti tiyenela kukhala okhulupilika kwa iye ngakhale pa nthawi zovuta. M’nkhani ino, tikambilana mmene citsanzo ca Yonatani cingatithandizile kukhala okhulupilika kwa Yehova m’zocitika zinai izi: (1) pamene tiona kuti munthu winawake waudindo sacita zinthu mwacilungamo, (2) pamene tifunika kusankha woyenela kumvela, (3) pamene m’bale amene akutsogolela sakutimvetsetsa kapena akuticitila zinthu mopanda cilungamo, ndi (4) pamene taona kuti n’covuta kusunga pangano.

PAMENE TIONA KUTI MUNTHU WINAWAKE WAUDINDO SACITA ZINTHU MWACILUNGAMO

5. N’cifukwa ciani cinali covuta kwa Aisiraeli kukhala okhulupilika kwa Mulungu pamene Sauli anali mfumu?

5 Panthawi ina, Yonatani ndi Aisiraeli anakumana ndi mavuto. Mfumu Sauli, atate ake a Yonatani, anapandukila Mulungu. Izi zinacititsa kuti Yehova am’kane. (1 Samueli 15:17-23) Ngakhale n’conco, Mulungu analola Sauli kupitiliza kulamulila kwa zaka zambili. Conco, cinali covuta kwa anthu kukhala okhulupilika kwa Mulungu popeza mfumu imene inasankhidwa kuti ikhale “pampando wacifumu wa Yehova,” inali kucita zoipa.—1 Mbiri 29:23.

6. N’ciani cionetsa kuti Yonatani anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova?

6 Yonatani anali wokhulupilika kwa Yehova nthawi zonse. Ganizilani zimene Yonatani anacita Sauli atangoyamba kupandukila Mulungu. (1 Samueli 13:13, 14) Panthawi imeneyo, gulu lalikulu la Afilisiti ndi magaleta ankhondo 30,000, linabwela kuti limenyane ndi Aisiraeli. Sauli anali cabe ndi asilikali 600, ndipo iye ndi Yonatani ndiwo okha amene anali ndi zida za nkhondo. Koma Yonatani sanacite mantha. Iye anakumbukila mau a mneneli Samueli akuti: “Cifukwa ca dzina lake lalikulu, Yehova sadzasiya anthu ake.” (1 Samueli 12:22) Ndiyeno, Yonatani anauza msilikali wina kuti: “Palibe cimene cingalepheletse Yehova kupulumutsa anthu ake pogwilitsa nchito anthu ambili kapena ocepa.” Conco, iye ndi msilikaliyo anamenyana ndi gulu lankhondo la Afilisiti cakuti anapha pafupifupi afilisiti 20. Yonatani anakhulupilila Yehova ndipo Iye anamudalitsa. Yehova anacititsa civomezi moti Afilisiti anacita mantha. Kenako, io anayamba kumenyana okhaokha ndi kuphana mpaka Aisiraeli anawina nkhondoyo.—1 Samueli 13:5, 15, 22; 14:1, 2, 6, 14, 15, 20.

7. Kodi Yonatani anali kuwaona bwanji atate ake?

7 Ngakhale kuti Sauli anapitilizabe kusamvela Yehova, Yonatani anayesetsabe kuwamvela atate ake. Mwacitsanzo, io anamenyela pamodzi nkhondo kuti ateteze anthu a Yehova.—1 Samueli 31:1, 2.

8, 9. Kodi kulemekeza amene amatitsogolela kumaonetsa bwanji kuti ndife okhulupilika kwa Mulungu?

8 Mofanana ndi Yonatani, nafenso tingaonetse kuti ndife okhulupilika kwa Yehova mwa kuyesetsa kumvela malamulo a boma. Yehova walola “olamulila akuluakulu” amenewa kutilamulila, ndipo amafuna kuti tiziwalemekeza. (Ŵelengani Aroma 13:1, 2.) Ndiye cifukwa cake tiyenela kulemekeza akuluakulu a boma ngakhale kuti nthawi zina amacita zinthu mwacinyengo. Mulimonse mmene zingakhalile, tiyenela kulemekeza aliyense amene waloledwa ndi Yehova kuti azititsogolela.—1 Akorinto 11:3; Aheberi 13:17.

Njila imodzi imene tingaonetsele kuti ndife okhulupilika kwa Yehova ndi mwa kulemekeza mwamuna kapena mkazi wathu, ngakhale kuti satumikila Yehova (Onani ndime 9)

9 Mlongo Olga, amene amakhala ku South America, anaonetsa kuti ndi wokhulupilika kwa Yehova mwa kulemekeza mwamuna wake ngakhale kuti anali kumucitila zinthu mwankhanza. [1] (Onani mau a kumapeto.) Nthawi zina, mwamuna wakeyo sanali kukamba naye ndiponso anali kumuuza mau oipa cifukwa cakuti anali wa Mboni za Yehova. Anali kumuuzanso kuti adzamusiya ndi kutenga ana onse. Koma Olga sanali ‘kubwezela coipa pa coipa.’ Iye anayesetsa kukhala mkazi wabwino. Anali kum’phikila, kum’capila, ndi kusamalila acibale ena a mwamuna wakeyo. (Aroma 12:17) Ndipo nthawi zina anali kupitila pamodzi kukaceza kwa acibale ndi mabwenzi a mwamunayo. Mwacitsanzo, pamene apongozi ake aamuna anamwalila, iye anakonza zofunikila kuti apitile pamodzi ku mzinda kumene kunali malilo. Ndiyeno, pamene mwambo wa malilo unali kucitika m’chalichi, iye anayembekezela mwamuna wake panja. Patapita zaka zambili, mwamuna wa Olga anayamba kum’komelako mtima cifukwa cakuti Olga anali woleza mtima ndiponso anali kum’lemekeza nthawi zonse. Masiku ano, mwamunayo amam’limbikitsa kupita kumisonkhano ndipo amam’pelekeza. Nthawi zina amapezeka pamisonkhano.—1 Petulo 3:1.

PAMENE TIFUNIKA KUSANKHA WOYENELA KUMVELA

10. N’cifukwa ciani Yonatani anasankha kukhala wokhulupilika kwa Davide?

10 Sauli atakamba kuti adzapha Davide, Yonatani anafunika kupanga cosankha koma zinali zovuta. Iye anali kufuna kukhala wokhulupilika kwa atate ake, koma anali kufunanso kukhala wokhulupilika kwa Davide. Yonatani anadziŵa kuti Mulungu ali ndi Davide osati Sauli, conco anasankha kukhala wokhulupilika kwa Davide. Iye anacenjeza Davide kuti abisale, kenako anafotokozela Sauli cifukwa cake sayenela kupha Davide.—Ŵelengani 1 Samueli 19:1-6.

11, 12. Kodi kukonda Mulungu kumatithandiza bwanji kusankha kukhala wokhulupilika kwa iye?

11 Alice, amene amakhala ku Australia, anafunika kusankha kuti adzakhala wokhulupilika kwa ndani. Pamene anali kuphunzila Baibulo, anali kuuzako a m’banja lake zimene anali kuphunzila. Iye anawauzanso kuti waleka kukondwelela Krisimasi, ndipo anawafotokozela cifukwa cake. Poyamba, anthu a m’banja lakewo anakhumudwa, kenako anam’kwiila kwambili. Iwo anali kuona kuti iye sawaganizila. Ndiyeno amai ake anamuuza kuti safuna kumuonanso. Alice anati: “Ndinadabwa ndipo cinandiŵaŵa kwambili cifukwa ndimawakonda abale anga. Komabe, ndinaona kuti ndiyenela kukonda kwambili Yehova ndi Mwana wake. Cotelo, pamsonkhano wadela wotsatila, ndinabatizidwa.”—Mateyu 10:37.

12 Sitiyenela kukhala wokhulupilika kwambili ku zinthu zina monga timu ya maseŵela, sukulu, kapena dziko lathu, kuposa mmene timakhalila okhulupilika kwa Yehova. Mwacitsanzo, Henry anali kukonda kuseŵela chesi m’timu ya pa sukulu yake. Iye anali kufuna kuwina mphoto kuti achukitse sukuluyo. Koma popeza kuti anali kuseŵela chesi kumapeto kwa mlungu uliwonse, sanali kupeza nthawi yopita muutumiki ndi kumisonkhano. Henry anakamba kuti anali wokhulupilika kwambili ku sukuluyo kuposa kwa Mulungu. Conco, anasiya kuseŵela chesi moimila sukulu yake.—Mateyu 6:33.

13. Kodi kukhala wokhulupilika kwa Mulungu kungatithandize bwanji kulimbana ndi mavuto m’banja?

13 Nthawi zina zimakhala zovuta kukhala wokhulupilika kwa onse a m’banja panthawi imodzi. Mwacitsanzo, m’bale Ken anati: “Nthawi ndi nthawi, ndinali kufuna kumacezela amai anga amene ndi acikulile, ndipo ndinali kufuna kuti nthawi zina azikhala nafe. Koma amai ndi mkazi wanga sanali kugwilizana kwenikweni. Ndikacita zinthu zokondweletsa uyu, wina anali kukhumudwa.” Ken anasinkhasinkha zimene Baibulo limakamba ndipo anaona kuti pacocitika cimeneci, anafunika kukondweletsa mkazi wake ndi kukhala wokhulupilika kwa iye. Conco, anacita zinthu zimene zinasangalatsa mkazi wake. Ndiyeno, anafotokozela mkazi wake cifukwa cimene ayenela kukomela mtima apongozi ake. Ken anafotokozelanso amai ake cifukwa cimene ayenela kulemekezela mkazi wake.—Ŵelengani Genesis 2:24; 1 Akorinto 13:4, 5.

PAMENE M’BALE SAKUTIMVETSETSA KAPENA AKUTICITILA ZINTHU MOPANDA CILUNGAMO

14. Kodi Sauli anam’citila ciani Yonatani mopanda cilungamo?

14 Tingakhalenso okhulupilika kwa Yehova ngakhale kuti m’bale amene akutsogolela akuticitila zinthu mopanda cilungamo. Mfumu Sauli anasankhidwa ndi Yehova, koma anacitila mwana wake zinthu zoipa. Iye sanamvetse cifukwa cimene Yonatani anali kukondela Davide. Conco, pamene Yonatani anafuna kuthandiza Davide, Sauli anakwiya kwambili ndipo anamucititsa manyazi pamaso pa anthu ambili. Koma Yonatani anali kuwalemekezabe atate ake. Panthawi imodzimodziyo, anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova ndi kwa Davide, amene anasankhidwa ndi Yehova kukhala mfumu yotsatila ya Aisiraeli.—1 Samueli 20:30-41.

15. N’ciani cimene tiyenela kucita ngati m’bale waticitila zinthu mopanda cilungamo?

15 Masiku ano, abale amene amatsogolela m’mipingo yathu, amayesetsa kucitila aliyense cilungamo. Koma abale amenewa ndi opanda ungwilo. Pacifukwa cimeneci, nthawi zina io sangamvetsetse cifukwa cimene tacitila zinthu zinazake. (1 Samueli 1:13-17) Conco, ngati atiganizila molakwika kapena sanatimvetsetse, tiyeni tikhalebe okhulupilika kwa Yehova.

PAMENE TAONA KUTI N’ZOVUTA KUSUNGA PANGANO

16. Ndi pa zocitika ziti pamene tiyenela kukhala okhulupilika kwa Yehova ndi kupewa kudzikonda?

16 Sauli anali kufuna kuti Yonatani adzakhale mfumu yotsatila osati Davide. (1 Samueli 20:31) Koma Yonatani anali kukonda Yehova ndipo anali wokhulupilika kwa iye. Conco, Yonatani sanacite zinthu modzikonda, koma anakhala bwenzi la Davide ndi kusunga pangano. Munthu aliyense amene amakondadi Yehova ndipo amafuna kukhala wokhulupilika kwa iye, “akalumbila kucita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingalilo ake.” (Salimo 15:4) Popeza ndife okhulupilika kwa Yehova, tiyenela kusunga malonjezo athu. Mwacitsanzo, ngati tinacita pangano la bizinesi, tiyenela kucita zimene tinapangana ngakhale kuti zakhala zovuta. Ndipo ngati tikukumana ndi mavuto m’cikwati, tiyenela kuonetsa kuti timakonda Yehova mwa kukhalabe okhulupilika kwa mwamuna kapena mkazi wathu.—Ŵelengani Malaki 2:13-16.

Ngati tinacita pangano la bizinesi, tidzacita zimene tinapangana cifukwa ndife okhulupilika kwa Mulungu (Onani ndime 16)

17. Kodi nkhani ino yakuthandizani bwanji?

17 Monga Yonatani, ife timafuna kukhala okhulupilika kwa Mulungu ngakhale pamavuto. Conco, tiyeni tikhalebe okhulupilika kwa abale ndi alongo athu pamene atikhumudwitsa. Tikacita zimenezo, tidzasangalatsa mtima wa Yehova, ndipo tidzakhala osangalala kwambili. (Miyambo 27:11) Ndife otsimikiza kuti Yehova adzapitilizabe kuticitila zabwino ndi kutisamalila. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zimene tingaphunzile kwa anthu a m’nthawi ya Davide amene anali okhulupilika ndiponso amene sanali okhulupilika.

^ [1] (ndime 9) Maina ena asinthidwa.