Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Pitilizani Kutumikila Yehova Mwacimwemwe

Pitilizani Kutumikila Yehova Mwacimwemwe

KUMBUKILANI tsiku limene munasangalala kwambili pa umoyo wanu. Kodi linali tsiku limene munaloŵa m’banja? Kodi ndi tsiku limene mwana wanu woyamba anabadwa? Kapena linali tsiku limene munabatizidwa? Mwacionekele, tsiku la ubatizo linali lofunika kwambili ndi losangalatsa pa umoyo wanu. Ndipo patsikulo, abale ndi alongo anu anali okondwa kwambili poona kuti mumakonda Mulungu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse, ndi mphamvu zanu zonse.—Maliko 12:30.

Mosakaikila, kucokela pamene munabatizidwa, mwapeza cimwemwe cacikulu potumikila Yehova. Komabe, ofalitsa ena sakhalanso ndi cimwemwe potumikila Mulungu. N’ciani cacititsa zimenezi? Kodi ndi zinthu ziti zimene zimatilimbikitsa kupitiliza kutumikila Yehova mwacimwemwe?

CIFUKWA CAKE ENA SATUMIKILANSO MWACIMWEMWE

Uthenga wa Ufumu umatipatsa cimwemwe coculuka. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti Yehova walonjeza kuti posacedwapa, Ufumu wake udzaononga dziko loipali ndi kubweletsa dziko latsopano. Lemba la Zefaniya 1:14 limati: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwela mofulumila kwambili.” Ngati tiona kuti tsikulo likucedwa, cimwemwe cathu potumikila Yehova cingacepe. Zimenezi zingapangitse kuti tibwelele m’mbuyo potumikila Mulungu.—Miyambo 13:12.

Tikamaceza ndi abale ndi alongo, timalimbikitsidwa kupitiliza kutumikila Yehova mwacimwemwe. Makhalidwe abwino a anthu a Yehova ayenela kuti anatikopa kuti tiyambe kulambila Mulungu ndi kum’tumikila mwacimwemwe. (1 Petulo 2:12) Komabe, kodi cingacitike n’ciani ngati m’bale kapena mlongo anapatsidwa cilango cifukwa cosamvela malamulo a Mulungu? Zimenezi zingacititse ena mumpingo kukhumudwa ndi kusiya kutumikila Mulungu mwacimwemwe.

Kukonda zinthu zakuthupi kungatilepheletse kutumikila Mulungu mwacimwemwe. Zili conco cifukwa cakuti dziko la Satanali limatikopa kuti tizigula zinthu zosafunikila kwenikweni. Conco, tizikumbukila mau a Yesu akuti: “Kapolo sangatumikile ambuye aŵili, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupilika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikila Mulungu ndi Cuma nthawi imodzi.” (Mateyu 6:24) Ndithudi, n’zosatheka kutumikila Yehova mwacimwemwe kwinaku tikufunafuna zinthu za m’dzikoli.

TUMIKILANI YEHOVA MWACIMWEMWE

Kutumikila Yehova si kolemetsa kwa anthu amene amamukonda. (1 Yohane 5:3) Kumbukilani mau a Yesu akuti: “Bwelani kwa ine nonsenu ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzilani kwa ine, cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Kukhala Mkristu woona kumatipatsa cimwemwe. Tili ndi zifukwa zambili zokhalila acimwemwe potumikila Yehova. Tsopano, tiyeni tikambilane zifukwa zitatu mwa zifukwa zimenezo.—Habakuku 3:18.

Timatumikila Mulungu wacimwemwe, amene anatipatsa moyo. (Machitidwe 17:28; 1 Timoteyo 1:11) Ife tonse timadziŵa kuti tili ndi udindo wotumikila Mulungu cifukwa ndi Mlengi wathu. Conco, tiyeni tipitilizebe kum’tumikila mwacimwemwe mosasamala kanthu kuti takhala m’coonadi kwa zaka zingati.

Héctor amakhalabe wacimwemwe cifukwa coganizila madalitso a Ufumu ndiponso cifukwa cokhala wacangu mu utumiki

Ganizilani za Héctor, amene anatumikila Yehova kwa zaka 40 monga woyang’anila dela. Ngakhale kuti ndi wokalamba, iye akusangalalabe potumikila Yehova. (Salimo 92:12-14) Kudwala kwa mkazi wake kwacititsa kuti asamacite zambili potumikila Mulungu. Ngakhale n’telo, Héctor akutumikilabe mwacimwemwe. Iye anati: “Cimandiŵaŵa kuona mkazi wanga akudwaladwala, ndipo ndimavutika pom’samalila. Koma sindilola kuti zimenezi zindilande cimwemwe canga potumikila Mulungu woona. Kudziŵa kuti ndili ndi moyo cifukwa ca Yehova, amene analenga munthu n’colinga, kumandicititsa kum’konda kwambili ndi kum’tumikila ndi mtima wonse. Ndimayesetsa kukhala wacangu pa nchito yolalikila, ndiponso ndimaganizila za madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweletsa. Kucita zimenezi kwandithandiza kukhalabe wacimwemwe.”

Timatha kukhala acimwemwe cifukwa cakuti Yehova watipatsa nsembe ya dipo. Zoonadi, “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asaonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ndithudi, macimo athu angakhululukidwe ndipo tingakhale ndi moyo wosatha ngati timakhulupilila dipo limene Mulungu anatipatsa mwacikondi. Ici ndi cifukwa cacikulu cimene timakhalila oyamikila. Ndipo kuyamikila dipo limeneli, kumatilimbikitsa kutumikila Yehova mwacimwemwe.

Jesús anasintha umoyo wake ndipo anatumikila Yehova mwacimwemwe kwa zaka zambili

M’bale wina dzina lake Jesús, amene anali kukhala ku Mexico anati: “Ndinakhala kapolo wa nchito yanga, ndipo nthawi zina ndinali kuseŵenza maola ambilimbili ngakhale sanandiuze kutelo. Ndinali kucita zimenezi kuti ndipeze ndalama zambili. Kenako, ndinaphunzila za Yehova ndi kuti anapeleka Mwana wake wokondedwa cifukwa ca anthu, ndipo ndinayamba kufuna kum’tumikila. Conco, ndinadzipeleka kwa Yehova. Pambuyo poseŵenza kwa zaka 28 pa kampani, ndinasankha zosiya nchito ndi kuyamba utumiki wa nthawi zonse.” Apa mpamene Jesús anayambila kutumikila Yehova mwacimwemwe.

Tili ndi makhalidwe abwino amene amaticititsa kukhala acimwemwe. Kodi mukumbukila mmene umoyo wanu unalili musanadziŵe Yehova? Mtumwi Paulo anakumbutsa Akristu a ku Roma kuti poyamba anali “akapolo a ucimo,” koma anakhala “akapolo a cilungamo.” Cifukwa cakuti anali ndi makhalidwe abwino, anali kuyembekezela kudzakhala ndi moyo wosatha. (Aroma 6:17-22) Popeza kuti timatsatila miyezo ya Yehova, timapewa mavuto amene amabwela cifukwa ca makhalidwe oipa. Izi zimaticititsa kukhala acimwemwe.

“Ngati pali zaka zosangalatsa kwambili pa umoyo wanga, ndi zaka zimene ndakhala ndikutumikila Yehova.”​—Jaime

Ganizilani citsanzo ca Jaime amene anali wankhonya. Iye analinso kukhulupilila kuti kulibe Mulungu ndi kuti zinthu zinacita kusandulika. Jaime anayamba kupezeka pa misonkhano yacikristu, ndipo anacita cidwi ndi cikondi cimene Akristu oona ali naco. Kuti asinthe umoyo wake wakale, Jaime anapempha Yehova kuti am’thandize kukhala ndi cikhulupililo mwa Iye. Jaime anati: “Pang’ono ndi pang’ono, ndinadziŵa kuti kuli Tate wacikondi ndiponso Mulungu wacifundo. Kutsatila miyezo yolungama ya Yehova kwanditeteza. Zikanakhala kuti sindinasinthe umoyo wanga, ndikanaphedwa monga anzanga ena amene anali ankhonya. Ngati pali zaka zosangalatsa kwambili pa umoyo wanga, ndi zaka zimene ndakhala ndikutumikila Yehova.”

MUSATOPE

Kodi tifunika kucita ciani pamene tikuyembekezela kuonongedwa kwa dziko loipali? Kumbukilani kuti tikucita cifunilo ca Mulungu, ndipo tikuyembekezela mwacidwi moyo wosatha. “Conco tisaleke kucita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.” (Galatians 6:8, 9) Mothandizidwa ndi Yehova, tiyeni tipitilize kupilila ndi kucita khama kuti tikhale ndi makhalidwe abwino amene adzatithandiza kupulumuka “cisautso cacikulu.” Ndiponso tisaleke kutumikila Yehova mwacimwemwe.—Chivumbulutso 7:9, 13, 14; Yakobo 1:2-4.

Ndife otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa cifukwa ca kupilila kwathu popeza akudziŵa nchito imene tikucita ndi cikondi cimene tili naco pa iye, ndiponso pa dzina lake. Tikapitiliza kum’tumikila mwacimwemwe, tidzafanana ndi wamasalimo Davide amene anati: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. Conco moyo wanga ukukondwela, ndipo ndidzakhala wosangalala. Komanso ndidzakhala wotetezeka.”—Salimo 16:8, 9.