Tengelani Citsanzo ca Mabwenzi Apamtima a Yehova
“Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa.”—SALIMO 25:14.
1-3. (a) N’cifukwa ciani sitiyenela kukaikila zoti tingakhale mabwenzi a Mulungu? (b) Tikambilana za ndani m’nkhani ino?
M’BAIBULO, Abulahamu amachedwa bwenzi la Mulungu katatu. (2 Mbiri 20:7, Buku Lopatulika; Yesaya 41:8; Yakobo 2:23) Ndiye yekha amene amachulidwa mwacindunji m’Baibulo kuti anali bwenzi la Mulungu. Koma kodi zimenezi zitanthauza kuti Abulahamu ndiye yekha amene anakhalapo bwenzi la Yehova? Iyai. Baibulo limaonetsa kuti aliyense angathe kukhala bwenzi la Mulungu.
2 M’Baibulo, muli zitsanzo zambili za amuna ndi akazi okhulupilika amene anali kuopa Yehova ndi kum’khulupilila, ndipo anakhala mabwenzi ake apamtima. (Ŵelengani Salimo 25:14.) Iwo ndi mbali ya ‘mtambo waukulu wa mboni’ umene Paulo anachula. Anthu onsewa anali mabwenzi a Mulungu.—Aheberi 12:1.
3 Tiyeni tikambilane za mabwenzi ena atatu a Yehova amene amachulidwa m’Baibulo. (1) Rute, mkazi wamasiye wokhulupilika wa ku Mowabu, (2) Hezekiya, Mfumu yokhulupilika ya Yuda, ndi (3) Mariya, mai wodzicepetsa wa
Yesu. Kodi tingaphunzile ciani tikaona zimene zinawathandiza kukhala mabwenzi a Mulungu?ANAONETSA CIKONDI CENICENI
4, 5. Kodi Rute anafunika kupanga cosankha cotani? Nanga n’cifukwa ciani kusankha zimenezo kunali kovuta? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
4 Naomi ndi azipongozi ake, Rute ndi Olipa, anali kuyenda ulendo wautali kucokela ku Mowabu kupita ku Isiraeli. Mkati mwa ulendowo, Olipa anasankha kubwelela kwao ku Mowabu. Komabe, Naomi anali wofunitsitsa kupita kwao ku Isiraeli. Nanga kodi Rute anasankha kucita ciani? Apa, Rute anafunika kusankha mwanzelu ngakhale kuti zinali zovuta. Kodi iye akanasankha kubwelela kwao ku Mowabu kumene kunali acibale ake, kapena kupita ndi Naomi m’pongozi wake ku Betelehemu?—Rute 1:1-8, 14.
5 Acibale a Rute anali kukhala ku Mowabu. Rute akanafuna, akanabwelela, ndipo mwacionekele acibale akewo akanamusamalila. Iye anali kuwadziŵa bwino anthu a ku Mowabu. Anali kudziŵanso cinenelo ndi cikhalidwe cao. Naomi anali kudziŵa kuti umoyo wa ku Betelehemu udzakhala wosiyana kwambili ndi umene Rute anazoloŵela. Ndipo Naomi anali kuda nkhawa kuti sadzapeza mwamuna woti akwatile Rute kapena nyumba yoti azikhalamo. Conco, Naomi anauza Rute kuti abwelele ku Mowabu. Monga mmene tafotokozela, Olipa ‘anabwelela kwa anthu a kwao ndi kwa milungu yake.’ (Rute 1:9-15) Koma Rute sanabwelele kwao kumene kunali milungu yonama.
6. (a) Ndi cosankha ca nzelu citi cimene Rute anapanga? (b) N’cifukwa ciani Boazi anakamba kuti Rute anathaŵila m’mapiko mwa Yehova ndi kupezamo citetezo?
6 Zioneka kuti Rute anaphunzila za Yehova kucokela kwa mwamuna wake kapena kwa Naomi. Iye anaphunzila kuti Yehova sali monga milungu yonama ya ku Mowabu. Rute anali kukonda Yehova ndipo anadziŵa kuti iye ndiye Mulungu woyenela kum’konda ndi kum’lambila. Conco, Rute anasankha mwanzelu. Iye anauza Naomi kuti: “Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Timakhudzidwa mtima tikaganizila mmene Rute anali kukondela Naomi. Koma timacita cidwi kwambili tikaganizila mmene iye anali kukondela Yehova. Boazi nayenso anacita cidwi ndi zimenezi. Ndiye cifukwa cake anayamikila Rute cifukwa ‘cothawila m’mapiko mwa Yehova ndi kupezamo citetezo.’ (Ŵelengani Rute 2:12.) Mau amene Boazi anakamba angatikumbutse za citetezo cimene mwana wa mbalame amapeza akakhala m’mapiko a mai ake. (Salimo 36:7; 91:1-4) Mofananamo, Yehova anateteza Rute ndipo anamudalitsa cifukwa ca cikhulupililo cake. Rute sanadziimbepo mlandu cifukwa ca cosankha cimene anapanga.
7. N’ciani cingathandize anthu amene amawayawaya kudzipeleka kwa Yehova?
7 Anthu ambili amaphunzila za Yehova koma safuna kuthaŵila kwa iye. Iwo amawayawaya kudzipeleka ndi kubatizidwa. Ngati inunso simunadzipeleke, ganizilani cimene cikukulepheletsani. Musaiŵale kuti munthu aliyense ali ndi mulungu amene amam’tumikila. (Yoswa 24:15) Koma cinthu canzelu ndi kutumikila Mulungu woona. Mukadzipeleka kwa Yehova, mudzaonetsa kuti mumakhulupilila kuti iye ndi malo anu othaŵilapo. Ndipo iye adzakuthandizani kuti mupitilize kum’tumikila ngakhale mukumane ndi mavuto otani. Izi n’zimene Mulungu anacitila Rute.
“ANAPITILIZA KUMAMATILA YEHOVA”
8. Kodi Hezekiya anakulila m’banja lotani?
8 Hezekiya anakulila m’banja losiyana kwambili ndi la Rute. Hezekiya anali mbali ya mtundu wodzipeleka kwa Mulungu. Koma Aisiraeli ena anakhala osakhulupilika. Mfumu Ahazi, atate ake a Hezekiya, anali munthu woipa. Iye sanalemekeze kacisi wa Mulungu, ndipo analimbikitsa anthu kuti azilambila milungu ina. Ahazi anafika poocha abale a Hezekiya ali a moyo ndi kuwapeleka nsembe ku milungu yonama. Hezekiya anakulila m’banja loipa kwambili!—2 Mafumu 16:2-4, 10-17; 2 Mbiri 28:1-3.
9, 10. (a) N’cifukwa ciani cinali capafupi kuti Hezekiya akwiile Mulungu? (b) N’cifukwa ciani sitiyenela kukwiila Mulungu? (c) Nanga n’cifukwa ciani sitiyenela kuganiza kuti banja limene tinakulilamo likhoza kuticititsa kukhala munthu woipa kapena wabwino?
9 Ahazi anapeleka citsanzo coipa kwa mwana wake Hezekiya. Izi zikanacititsa kuti Hezekiya akwiile Yehova. Masiku ano, anthu amene amakumana ndi mavuto aang’ono poyelekezela ndi a Hezekiya, ‘amakwiila Yehova’ kapena gulu lake. (Miyambo 19:3) Ena amaona kuti ngati anakulila m’banja loipa ndiye kuti basi naonso adzayamba kucita zinthu zoipa kapena kutengela zocita za makolo ao. (Ezekieli 18:2, 3) Koma kodi zimenezo n’zoona?
10 Umoyo wa Hezekiya uonetsa kuti maganizo amenewo si oona. Palibe cifukwa comveka cokwiila Yehova. Iye sacititsa anthu kukumana ndi mavuto. (Yobu 34:10) N’zoona kuti makolo akhoza kuphunzitsa ana ao zinthu zabwino kapena zoipa. (Miyambo 22:6; Akolose 3:21) Koma zimenezi sizitanthauza kuti zocita za banja lathu n’zimene zingaticititse kukhala munthu wabwino kapena woipa. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti Yehova anatilenga ndi ufulu wodzisankhila zocita. Zimenezi zitanthauza kuti tikhoza kusankha kucita zabwino kapena zoipa. (Deuteronomo 30:19) Kodi Hezekiya anagwilitsila nchito bwanji ufulu umenewo?
11. N’ciani cinacititsa kuti Hezekiya akhale mfumu yabwino ya Yuda?
11 Ngakhale kuti atate a Hezekiya anali mmodzi wa mafumu oipa kwambili a Yuda, Hezekiya anakhala mmodzi wa mafumu abwino kwambili. (Ŵelengani 2 Mafumu 18:5, 6.) Iye sanatsatile citsanzo coipa ca atate ake. M’malomwake, anasankha kumvela aneneli a Yehova monga Yesaya, Mika, ndi Hoseya. Hezekiya anamvetsela mwachelu malangizo ndi uphungu umene aneneliwo anam’patsa. Zimenezi zinam’limbikitsa kukonza zinthu zimene atate ake anaononga. Iye anayeletsa kacisi, anapempha Mulungu kuti akhululukile anthu ake, ndiponso anaononga mafano onse amene anali m’dzikolo. (2 Mbiri 29:1-11, 18-24; 31:1) Patapita nthawi, pamene mfumu ya Asuri, Senakeribu inafuna kuononga Yerusalemu, Hezekiya anacita zinthu molimba mtima ndiponso mwa cikhulupililo. Iye anali kukhulupilila kuti Yehova adzawateteza ndipo analimbikitsa anthu ake. (2 Mbiri 32:7, 8) Panthawi ina, Hezekiya anacita zinthu modzikuza koma Yehova atamuongolela, anadzicepetsa. (2 Mbiri 32:24-26) Kukamba zoona, Hezekiya ndi citsanzo cabwino cimene tiyenela kutengela. Iye sanatengele khalidwe loipa la atate ake. M’malomwake, anaonetsa kuti anali bwenzi la Yehova.
12. Mofanana ndi Hezekiya, kodi anthu ambili masiku ano aonetsa bwanji kuti ndi mabwenzi a Yehova?
12 M’dzikoli anthu ndi ankhanza ndipo alibe cikondi, ndiponso ana ambili saleledwa ndi makolo acikondi. (2 Timoteyo 3:1-5) Ngakhale kuti Akristu ambili masiku ano anakulila m’mabanja acitsanzo coipa, io asankha kukhala paubwenzi wabwino ndi Yehova. Mofanana ndi Hezekiya, io amaonetsa kuti banja la munthu silingamucititse kukhala munthu wabwino kapena woipa. Mulungu watipatsa ufulu wodzisankhila zocita, ndipo tikhoza kusankha kum’tumikila ndi kum’lemekeza monga mmene Hezekiya anacitila.
“NDINETU KAPOLO WA YEHOVA!”
13, 14. N’cifukwa ciani udindo umene Mariya anapatsidwa unaoneka wovuta kwambili? Koma kodi Mariya anayankha ciani kwa Gabirieli?
13 Patapita zaka zambili Hezekiya atamwalila, mtsikana wina wodzicepetsa dzina lake Mariya, anali paubwenzi wapadela ndi Yehova. Iye anapatsidwa udindo wapadela. Anayenela kukhala ndi pakati, kubeleka Mwana wa Mulungu, ndi kumulela. Yehova anali kum’konda Mariya ndi kum’khulupilila. Ndiye cifukwa cake anamupatsa mwai wapadela umenewu. Koma kodi Mariya anamva bwanji atauzidwa za udindo umenewo?
14 Nthawi zambili timakamba za mwai umene Mariya anapatsidwa. Koma kodi ndi zinthu ziti zimene ayenela kuti anada nazo nkhawa? Mwacitsanzo, mngelo Gabirieli anauza Mariya kuti adzakhala ndi pakati popanda kugona ndi mwamuna aliyense. Koma mngeloyo sanafotokozele banja la Mariya ndi anzake za mmene Mariya adzakhalila ndi pakati. Mwina Mariya anadela nkhawa kuti, ‘kodi anthu akadziŵa kuti ndili ndi pakati adzandiona bwanji? Nanga ndidzam’fotokozela bwanji Yosefe kuti asaganize zoti ndinayenda ndi mwamuna wina?’ Kuonjezela pamenepo, ayenela kuti Luka 1:26-38.
anali kudela nkhawa za udindo waukulu wolela Mwana wa Mulungu. Sitidziŵa zinthu zonse zimene Mariya anali kuda nazo nkhawa, koma tidziŵa zimene anayankha Gabirieli. Iye anati: “Ndinetu kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zicitike ndithu kwa ine.”—15. N’cifukwa ciani cikhulupililo ca Mariya cinali capadela?
15 Mariya anali ndi cikhulupililo capadela kwambili. Iye anali wokonzeka kucita ciliconse cimene anauzidwa monga mmene kapolo amacitila. Iye anali kukhulupilila kuti Yehova adzamusamalila ndi kum’teteza. N’ciani cinacititsa Mariya kukhala ndi cikhulupililo colimba? Sitibadwa ndi cikhulupililo. Koma tingakhale ndi cikhulupililo ngati tiyesetsa kucita zinthu zimene zingatithandize kukhala naco, ndi kupempha Mulungu kuti adalitse khama lathu. (Agalatiya 5:22; Aefeso 2:8) Mariya anali kucita khama kuti alimbitse cikhulupililo cake. Tidziŵa bwanji zimenezi? Tiyeni tikambilane mmene anali kucitila pomvetsela ndi zimene anali kukamba.
16. N’ciani cionetsa kuti Mariya anali mmvetseli wabwino?
16 Mariya anali kumvetsela mosamala. Baibulo limakamba kuti tikhale ‘ofulumila kumva, odekha polankhula.’ (Yakobo 1:19) Mariya anali mmvetseli wabwino. Baibulo limaonetsa kuti anali kumvetsela mosamala zinthu zimene anali kumva, makamaka zinthu zokhudza Yehova. Iye anali kupeza nthawi yosinkhasinkha zinthu zofunika zimenezo. Mwacitsanzo, Yesu atabadwa, Mariya anamvetsela uthenga umene abusa anamuuza wocokela kwa mngelo. Pa nthawi inanso, Yesu ali ndi zaka 12, Mariya anali kumvetsela pamene Yesu anali kukamba zinthu zodabwitsa. Pa zocitika zonsezi, Mariya anamvetsela ndi kusunga zimene anamva, kenako anayamba kuzisinkhasinkha.—Ŵelengani Luka 2:16-19, 49, 51.
17. Tiphunzila ciani zokhudza Mariya tikaona zimene anali kukamba?
17 Zimene Mariya anali kukamba. M’Baibulo muli mau ocepa amene Mariya anakamba. Pa Luka 1:46-55, ndi pamene pali mau ake ambili. Mau akewo aonetsa kuti Mariya anali kudziŵa bwino Malemba Aciheberi. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa mau a Mariya ndi ofanana ndi mau amene Hana, mai wa Samueli, anakamba m’pemphelo lake. (1 Samueli 2:1-10) Pokamba mauwo, Mariya ayenela kuti anagwila Mau a m’Malemba pafupifupi nthawi 20. N’zoonekelatu kuti iye anali kukonda kuuza ena coonadi cimene anaphunzila kwa Bwenzi lake lapamtima, Yehova.
18. Tingatengele bwanji cikhulupililo ca Mariya?
18 Mofanana ndi Mariya, nthawi zina Yehova angatipatse udindo umene tingaone kuti ndi wovuta. Zikatelo, tiyenela kutengela citsanzo ca Mariya mwa kuvomela udindowo modzicepetsa, ndi kudalila Yehova kuti atithandize. Tingatengelenso cikhulupililo ca Mariya mwa kumvetsela mosamala kwambili kwa Yehova, ndi kusinkhasinkha zinthu zimene taphunzila zokhuza iye ndi zolinga zake. Tikacita zimenezo, tidzakhala osangalala pouza ena zimene taphunzila.—Salimo 77:11, 12; Luka 8:18; Aroma 10:15.
19. Kodi tingayembekezele ciani ngati titengela zitsanzo za m’Baibulo za anthu a cikhulupililo?
19 Taona kuti Rute, Hezekiya, ndi Mariya anali mabwenzi a Yehova mofanana ndi Abulahamu. Iwo anali mbali ya ‘mtambo waukulu wa mboni’ zimene zinali ndi mwai wokhala mabwenzi a Mulungu. Tiyeni tipitilize kutengela cikhulupililo colimba ca anthu amenewa. (Aheberi 6:11, 12) Ngati ticita zimenezo, tingayembekezele mphoto yokhala mabwenzi a Yehova kwa muyaya.