NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA April 2019

Magazini ino ili na nkhani zophunzila wiki ya June 3-30, 2019.

Kodi Mumakwanilitsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?

Kodi tingacite ciani kuti tizilalikila mogwila mtima, komanso kuti tizipeza cimwemwe pa nchitoyi?

Tengelani Yesu Kuti Mukhalebe na Mtendele wa Mumtima

Zinthu zitatu zimene Yesu anacita zingatithandize kukhalabe na mtendele wamumtima ngakhale pamene takumana na mavuto aakulu.

Cilikizani Coonadi Pankhani ya Akufa

Tingapewe bwanji kutengako mbali pa miyambo yosagwilizana na malemba yokhudza akufa?

Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Kukaniza Mizimu Yoipa

N’zinthu ziti zimene tingacite kuti tisacoseletsedwe na Satana komanso ziwanda zake?

MBILI YANGA

Tinapeza “Ngale . . . Yamtengo Wapatali”

Ŵelengani nkhani yonena za umoyo wokhutilitsa wa m’bale Winston na mlongo Pamela Payne, a ku Australia.

Kodi Mudziŵa?

M’nthawi yamakedzana, kodi munthu anali kupeza bwanji ngalawa akafuna kuyenda ulendo wapanyanja?