Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 16

Cilikizani Coonadi Pankhani ya Akufa

Cilikizani Coonadi Pankhani ya Akufa

“Mmenemu ndi mmene timadziwila mawu ouzilidwa oona kapena abodza.”—1 YOH. 4:6.

NYIMBO 73 Tilimbitseni Mtima

ZA M’NKHANI INO *

M’malo motengako mbali m’miyambo yosakondweletsa Mulungu, yesetsani kutonthoza acibululu anu amene ataikilidwa wokondedwa wawo (Onani ndime 1-2) *

1-2. (a) Kodi Satana wasoceletsa bwanji anthu? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

SATANA ni “tate wake wa bodza,” ndipo wakhala akusoceletsa anthu kungoyambila nthawi ya Adamu na Hava. (Yoh. 8:44) Mabodza ake aphatikizapo ziphunzitso zonama ponena za imfa, komanso za kumene munthu amapita akamwalila. Ziphunzitso zimenezi zakhala maziko a zikhulupililo zambili na miyambo yake yofala. Mwa ici, abale na alongo ena amafunika “kumenya mwamphamvu nkhondo yacikhulupililo,” ngati munthu winawake m’banja lawo kapena m’dela lawo wamwalila.—Yuda 3.

2 Ngati mukakamizidwa kucitako miyambo imeneyi, n’ciani cingakuthandizeni kucilikiza coonadi ca m’Baibo ponena za akufa? (Aef. 6:11) Nanga mungacite ciani kuti mutonthoze na kulimbikitsa Mkhristu mnzanu, amene akukakamizidwa kutengako mbali m’miyambo yosakondweletsa Mulungu? Nkhani ino idzafotokoza malangizo amene Yehova watipatsa. Koma coyamba, tiyeni tikambilane zimene Baibo imakamba ponena za akufa.

COONADI PONENA ZA AKUFA

3. Kodi bodza loyamba linabweletsa mavuto anji?

3 Mulungu sanalenge anthu kuti azifa. Kuti anthu oyambilila Adamu na Hava akhale na moyo wosatha, anafunika kumvela lamulo losavuta limene Yehova anawapatsa lakuti: “Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa cabwino ndi coipa. Cifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Gen. 2:16, 17) Koma Satana anayambitsa mavuto. Kupitila mwa njoka, iye anauza Hava kuti: “Kufa simudzafa ayi.” N’zomvetsa cisoni kuti Hava anakhulupilila bodzalo na kudya cipatsoco. Pambuyo pake, mwamuna wake nayenso anadya cipatsoco. (Gen. 3:4, 6) Izi zinabweletsa ucimo komanso imfa kwa anthu.—Aroma 5:12.

4-5. Kodi Satana wapitiliza bwanji kusoceletsa anthu?

4 Mogwilizana na zimene Mulungu anakamba, Adamu na Hava anafadi. Koma Satana sanalekele pamenepo kukamba mabodza ponena za imfa. Patapita nthawi, iye anayamba kufalitsa mabodza ena. Limodzi mwa mabodzawo ni ciphunzitso cakuti munthu akafa, “mzimu” wake umacoka mwa iye na kupitiliza kukakhala na moyo kumalo a mizimu. Kuyambila kale-kale mpaka pano, anthu ambili-mbili asoceletsedwa na mabodza osiyana-siyana ozikidwa pa mfundo imeneyi.—1 Tim. 4:1.

5 N’cifukwa ciani anthu ambili asoceletsedwa? Satana amadziŵa mmene imfa imakhudzila anthu, ndipo amatengelapo mwayi kuti awasoceletse. Anthufe sitifuna kufa, cifukwa Mulungu anatilenga na mtima wofuna kukhala na moyo kwamuyaya. (Mlal. 3:11) Timaona kuti imfa ni mdani wathu.—1 Akor. 15:26.

6-7. (a) Kodi Satana wakwanitsa kubisa coonadi kwa anthu pankhani ya akufa? Fotokozani. (b) Kodi coonadi ca m’Baibo cimatithandiza bwanji kuti tisamaope akufa?

6 Mosasamala kanthu za mabodza a Satana, coonadi ponena za akufa sicinabisike. Ndipo tsopano, anthu ambili kuposa kale lonse amadziŵa zimene Baibo imaphunzitsa ponena za akufa, komanso za ciukililo. Ndipo amauzako ena zimenezi. (Mlal. 9:5, 10; Mac. 24:15) Kudziŵa coonadi cimeneci kumatitonthoza na kutithandiza kuti tisamaope kwambili imfa. Mwacitsanzo, sitiyopa akufa kapena kudela nkhawa kuti akuvutika. Timadziŵa kuti iwo sali na moyo kwinakwake, komanso kuti sangavulaze amoyo. Zili monga kuti ali m’tulo tofa nato. (Yoh. 11:11-14) Cinanso, tidziŵa kuti akufa sadziŵa utali wa nthawi imene akhala m’manda. Conco, ngakhale anthu amene anafa zaka mahandiledi ambili kumbuyoko, akakaukitsidwa adzangoona ngati kuti pangopita kanthawi kocepa kwambili kucokela pamene anafa.

7 Conco, tingaone kuti coonadi ponena za akufa n’cosacoloŵana, komanso n’cosavuta kumvetsetsa. N’cosiyana kwambili na mabodza a Satana, amene asoceletsa anthu ambili. Koma kuwonjezela pa kusoceletsa anthu, mabodza a Satana aipitsanso dzina la Mlengi wathu. Kuti timvetsetse kukula kwa mavuto amene Satana wabweletsa, tiyeni tikambilane mafunso aya: Kodi mabodza a Satana aipitsa bwanji dzina la Yehova? Kodi mabodzawa apangitsa bwanji anthu kuona kuti kukhulupilila nsembe ya dipo la Khristu kulibe phindu? Nanga awonjezela bwanji mavuto na cisoni pakati pa anthu?

MABODZA A SATANA AWONONGA ZAMBILI

8. Malinga ndi Yeremiya 19:5, kodi mabodza a Satana pankhani ya akufa amaipitsa bwanji dzina la Yehova?

8 Mabodza a Satana pankhani ya akufa amaipitsa dzina la Yehova. Mabodza amenewa aphatikizapo ciphunzitso conama cakuti akufa amazunzika ku moto wa helo. Ciphunzitso cimeneci cimaipitsa dzina la Mulungu! Motani? Cimapangitsa anthu kuona ngati kuti Mulungu ni wankhanza monga Mdyelekezi. Koma zoona zake n’zakuti Mulungu ni wacikondi. (1 Yoh. 4:8) Kodi mumamvela bwanji mukaganizila zimenezi? Nanga kuli bwanji Yehova? Kodi muganiza kuti iye amamvela bwanji? Cimamuŵaŵa kwambili, cifukwa amazonda khalidwe lililonse lankhanza.—Ŵelengani Yeremiya 19:5.

9. Kodi mabodza a Satana amakhudza bwanji mmene anthu amaonela nsembe ya dipo la Khristu yochulidwa pa Yohane 3:16; na Yohane 15:13?

9 Mabodza a Satana ponena za akufa amapangitsa anthu kuona kuti kukhulupilila nsembe ya dipo la Khristu kulibe phindu. (Mat. 20:28) Bodza lina la Satana n’lakuti anthu tili na mzimu wosakhoza kufa. Izi zikanakhala zoona, sembe ife tonse sitikufa. Ndipo Khristu sakanafunika kupeleka moyo wake monga dipo kuti tikapeze moyo wosatha. Koma kumbukilani kuti nsembe ya Khristu ndiyo njila yopambana imene Mulungu anaonetsela cikondi cake kwa anthu. (Ŵelengani Yohane 3:16; 15:13.) Ganizilani cabe mmene Yehova na Mwana wake amamvelela cifukwa ca ziphunzitso zosukulutsa mphatso ya mtengo wapatali imeneyi!

10. Kodi mabodza a Satana pankhani ya akufa awonjezela bwanji cisoni na mavuto kwa anthu?

10 Mabodza a Satana awonjezela cisoni na mavuto kwa anthu. Nthawi zina, makolo okhala na cisoni cifukwa cofedwa mwana wawo, amauzidwa kuti Mulungu watenga mwanayo kuti akakhale mngelo kumwamba. Bodza la Satana limeneli limangowonjezela cisoni cawo, osati kucicepetsa. Komanso, ciphunzitso cabodza ca moto wa ku helo cagwilitsidwa nchito monga cifukwa codzikhululukila pozunza anthu. Mwacitsanzo, anthu ena anawatentha na moto atawamangilila pa mtengo cifukwa cakuti anali kutsutsa ziphunzitso za chechi yawo. Buku lina lokamba za khoti yakale ya Katolika ku Spain linakamba kuti, ena mwa anthu amene anali kucita nkhanza zimenezi, anali kukhulupilila kuti pamene akutentha otsutsawo, ndiye kuti “akuwalaŵitsako moto wamuyaya wa ku helo,” n’colinga cakuti asanafe, alape kuti asapite ku helo. M’maiko ena, anthu amalambila mizimu ya makolo awo, pofuna kuwalemekeza kapena kupempha kuti awadalitse. Enanso amacita izi pofuna kukondweletsa mizimu ya makolowo kuti isawalange mwanjila inayake. Comvetsa cisoni n’cakuti mabodza a Satana amenewa sapatsa anthu citonthozo ceni-ceni. M’malomwake, amacititsa anthu kukhala na mantha komanso nkhawa.

MMENE TINGACILIKIZILE COONADI CA M’BAIBO

11. Kodi acibululu kapena mabwenzi angatikakamize bwanji kucita zinthu zosemphana na Mawu a Mulungu?

11 Kukonda Yehova komanso Mawu ake, kumatilimbikitsa kumumvela ngakhale pamene acibululu kapena mabwenzi akutikakamiza kucitako miyambo yosemphana na Malemba, yokhudzana ndi akufa. Iwo angakambe mawu otipangitsa kuti tidziimbe mlandu. Mwina angatinene kuti sitinali kum’konda munthu amene anamwalilayo, kapena kuti sitinali kumulemekeza. Mwinanso anganene kuti kukana kucitako mwambowo kungapangitse kuti womwalilayo avulaze amoyo mwanjila inayake. Zikakhala conco, kodi tingacilikize bwanji coonadi ca m’Baibo? Onani mmene mfundo za m’Baibo zotsatilazi zingakuthandizileni.

12. Chulani zikhulupililo na miyambo yokhudza akufa imene ni yosagwilizana na Malemba.

12 Tsimikizani mtima kupewa zikhulupililo na miyambo yosemphana na Malemba. (2 Akor. 6:17) M’dziko lina ku Caribbean, anthu ambili amakhulupilila kuti munthu akamwalila, “ciwanda” cake cimatsala. Iwo amati “ciwandaco” cimakhala pafupi, ndipo cingavulaze adani a munthu wakufayo. Buku lina linakambanso kuti “cipukuco” cingabweletse “mavuto aakulu m’mudzi.” Komanso m’maiko a mu Africa, kukacitika malilo, anthu amasonkha moto usiku wonse panyumba ya malilo. Cifukwa ciani? Amakamba kuti kucita izi kumapitikitsa mizimu yoipa. Pokhala atumiki a Yehova, sitikhulupilila mabodza kapena kutengako mbali m’miyambo iliyonse imene imacilikiza mabodza a Satana!—1 Akor. 10:21, 22.

Kufufuza mosamala mfundo za m’Baibo m’zofalitsa zathu, komanso kukambilana mwaulemu na abululu anu amene si Mboni, kudzakuthandizani kupewa mikangano (Onani ndime 13-14) *

13. Malinga n’zimene Yakobo 1:5 imakamba, n’ciani cimene muyenela kucita ngati simuli wotsimikiza zakuti mwambo winawake ni wogwilizana na Malemba kapena ayi?

13 Ngati simuli wotsimikiza ngati mwambo winawake ni wogwilizana na Malemba kapena ayi, pemphelani kwa Yehova. M’pempheni kuti akupatseni nzelu. (Ŵelengani Yakobo 1:5.) Kenako, citani zinthu mogwilizana na pemphelo lanu mwa kufufuza malangizo m’zofalitsa zathu. Mwinanso mungafunsile kwa akulu mumpingo. Iwo sadzakuuzani zocita, koma adzakufotokozelani mfundo za m’Baibo zogwilizana na nkhaniyo, monga zimene zafotokozedwa m’nkhani ino. Ngati mucita zimenezi, mudzaphunzitsa “mphamvu [zanu] za kuzindikila,” zimene zidzakuthandizani “kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.”—Aheb. 5:14.

14. Kodi tingapewe bwanji kukhumudwitsa anthu?

14 “Citani zonse ku ulemelelo wa Mulungu. Pewani kukhala okhumudwitsa.” (1 Akor. 10:31, 32) Pamene tisankha kuti titengeko mbali pa mwambo winawake, tiyenelanso kuganizila mmene cosankha cathu cingakhudzile cikumbumtima ca ena, maka-maka Akhristu anzathu. Tipewe kukhumudwitsa aliyense! (Maliko 9:42) Komanso, tipewe kukhumudwitsa osakhulupilila pa zifukwa zazing’ono. Cifukwa cakuti timawakonda, timakamba nawo mwaulemu. Ndipo izi zimapangitsa kuti Yehova alemekezeke. Timapewa kukangana nawo, kapena kunyoza miyambo yawo. Kumbukilani kuti cikondi n’camphamvu. Ngati tionetsa cikondi mwa kucita zinthu mowaganizila komanso mwaulemu, tingafewetse mitima yawo.

15-16. (a) N’cifukwa ciani n’cinthu canzelu kudziŵitsa ena zimene timakhulupilila? Fotokozani citsanzo. (b) Kodi mawu a Paulo pa Aroma 1:16 tingawaseŵenzetse bwanji?

15 Dzidziŵikitseni kwa anthu a m’dela lanu kuti ndimwe Mboni ya Yehova. (Yes. 43:10) Munthu wina akamwalila pa banja panu, acibululu komanso anthu ena angakhumudwe ngati mukana kutengako mbali pa mwambo winawake. Koma zimakhala zosavuta kweni-kweni ngati munawafotokozela pasadakhale zimene mumakhulupilila. M’bale Francisco, amene akhala ku Mozambique, analemba kuti: “Pamene ine na mkazi wanga, Carolina, tinaphunzila coonadi, tinawauzilatu acibululu athu kuti sitidzalambilanso anthu akufa. Cikhulupililo cathucinayesedwa pamene mkulu wake wa mkazi wanga anamwalila. Munthu akamwalila, pali mwambo wapadela umene anthu kuno amatsatila posambika mtembo. Akatsiliza kusambika mtembo, wacibululu wapafupi kwambili wa womwalilayo amafunika kugona pamene ataila madzi osambikila mtembowo kwa masiku atatu. Amati colinga ca mwambo umenewu ni kugoneka mzimu wa womwalilayo. Acibululu a mkazi wanga anafuna kuti iye acite mwambo umenewu.”

16 Kodi m’bale Francisco na mkazi wake anacita ciani? M’baleyo anati: “Popeza timakonda Yehova ndipo timafuna kumukondweletsa, tinakana kucita mwambo umenewo. Acibululu a mkazi wanga anakhumudwa kwambili. Anatinena kuti sitikulemekeza malemuyo. Anakambanso kuti sadzapondanso phazi pakhomo pathu kapena kutithandiza. Popeza kuti tinali titawauzilatu zimene timakhulupilila, sitinakambilanenso nawo za nkhaniyi pamene anali okwiya. Ena mwa iwo anayamba kutiikila kumbuyo. Anali kukamba kuti tinawafotokozela kale zimene timakhulupilila. M’kupita kwa nthawi, acibululuwo analeka kutikwiyila, ndipo tinayambanso kugwilizana. Pano tikamba, ena amabwela kunyumba kwathu kudzapempha mabuku ophunzilila Baibo.” Conco, sitiyenela kucita mantha kuteteza coonadi ponena za akufa.—Ŵelengani Aroma 1:16.

MUZITONTHOZA NA KULIMBIKITSA AMENE AFEDWA

Mabwenzi eni-eni amatonthoza na kulimbikitsa anzawo amene afedwa (Onani ndime 17-19) *

17. N’ciani cingatithandize kukhala bwenzi leni-leni kwa Mkhristu amene wafedwa?

17 Mkhristu mnzathu akafedwa, tifunika kuyesetsa kukhala “bwenzi lenileni . . . , m’bale amene anabadwila kuti [athandize] pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Kodi tingaonetse bwanji kuti ndife “bwenzi lenileni,” maka-maka ngati m’bale kapena mlongo wofedwa akukakamizidwa kucitako miyambo yosagwilizana na Malemba? Kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo zotsatilazi kungatithandize kutonthoza munthu amene wafedwa.

18. N’cifukwa ciani Yesu anagwetsa misozi? Nanga tingaphunzilepo ciani pa citsanzo cake?

18 “Lilani ndi anthu amene akulila.” (Aroma 12:15) Nthawi zina, tingasoŵe cokamba kuti titonthoze munthu amene ali na cisoni cacikulu. Zikakhala conco, kungolila naye kungakhale kotonthoza kwambili. Mwacitsanzo, pamene Lazaro bwenzi la Yesu anamwalila, Mariya, Marita, ndi anthu ena analila cifukwa ca imfa ya mlongosi wawo komanso bwenzi lawo. Patapita masiku anayi, Yesu anafika, ndipo nayenso “anagwetsa misozi,” olo kuti anali kudziŵa kuti posacedwa adzamuukitsa Lazaro. (Yoh. 11:17, 33-35) Kulila kwa Yesu kunaonetsa mmene Atate wake anamvelela pamene Lazaro anamwalila. Kunaonetsanso kuti Yesu anali kulikonda banja lija, ndipo mwacionekele izi zinatonthoza Mariya na Marita. Mofananamo, abale athu akaona kuti timawakonda na kuwadela nkhawa, amalimbikitsidwa. Amazindikila kuti sali okha, koma ali na mabwenzi ambili amene amawakonda na kuwathandiza.

19. Kodi tingaseŵenzetse bwanji malangizo a pa Mlaliki 3:7 potonthoza Mkhristu mnzathu amene wafedwa?

19 “Nthawi yokhala cete ndi nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) Njila ina imene tingatonthozele Mkhristu wofedwa ni kumumvetsela mwachelu. M’patseni mwayi wofotokoza momasuka mmene akumvelela, ndipo musakhumudwe ngati wayamba ‘kulankhula zopanda pake.’ (Yobu 6:2, 3) Kuphatikiza pa cisoni, iye angakhale wovutika maganizo kwambili cifukwa cakuti acibululu ake amene si Mboni akumukakamiza kucita miyambo yosayenela. Conco, pemphelani naye pamodzi. Pemphani “Wakumva pemphelo” kuti am’patse mphamvu na nzelu. (Sal. 65:2) Ngati n’zotheka, ŵelengani naye Baibo. Kapena ŵelengani naye nkhani yolimbikitsa ya m’zofalitsa zathu. Mwacitsanzo, mungamuŵelengele nkhani ya m’magazini athu yofotokoza mbili ya munthu winawake.

20. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

20 Ha! Ni mwayi waukulu cotani nanga kudziŵa coonadi ponena za akufa komanso za ciyembekezo cokondweletsa cimene onse ali m’manda acikumbutso ali naco! (Yoh. 5:28, 29) Conco, m’mawu na m’zocita zathu, tiyeni ticilikize molimba mtima coonadi ca m’Baibo, komanso tiziuzako ena coonadi cimeneci pa mpata uliwonse umene tapeza. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana za msampha wina umene Satana amaseŵenzetsa pofuna kusunga anthu mumdima wauzimu. Msampha umenewu ni wa kukhulupilila zamizimu. Tidzaphunzila cifukwa cake tifunika kupewa kucita zinthu zamizimu, kuphatikizapo zosangalatsa zogwilizana na zamizimu.

NYIMBO 24 Bwelani ku Phili la Yehova

^ ndime 5 Satana na ziŵanda zake amasoceletsa anthu mwa kugwilitsila nchito mabodza osiyana-siyana onena za akufa. Mabodza amenewa apangitsa kuti pakhale miyambo yambili yosemphana na Malemba. Nkhani ino idzakuthandizani kudziŵa zimene mungacite kuti mukhalebe okhulupilika kwa Yehova ngati anthu ena akukakamizani kucitako miyambo yotelo.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Pamene wacibululu wofedwa akulila, abale ake amene ni Mboni akumutonthoza.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Pambuyo pofufuza mfundo zokhudza miyambo ya malilo, mwaulemu m’bale akufotokozela abululu ake zimene amakhulupilila.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Akulu akutonthoza na kulimbikitsa m’bale amene watayikilidwa wokondedwa wake mu imfa.