Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 14

Kodi Mumakwanilitsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?

Kodi Mumakwanilitsa Mbali Zonse za Utumiki Wanu?

“Gwila nchito ya mlaliki, ndipo ukwanilitse mbali zonse za utumiki wako.”—2 TIM. 4:5.

NYIMBO 57 Tilalikile kwa Anthu a Makhalidwe Onse

ZA M’NKHANI INO *

Yesu ataukitsidwa, anakumana na ophunzila ake na kuwalamula kuti “pitani mukaphunzitse anthu” (Onani ndime 1)

1. Kodi atumiki onse a Mulungu amafuna kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani? (Onani cithunzi pacikuto.)

KHRISTU YESU analamula otsatila ake kuti, “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.” (Mat. 28:19) Atumiki a Mulungu onse okhulupilika, amafuna kudziŵa mmene ‘angakwanilitsile mbali zonse za utumiki’ wawo umenewu. (2 Tim. 4:5) Zili conco cifukwa nchitoyi ni yofunika kwambili, ni yokhutilitsa, komanso ifunika kugwilidwa mwamsanga kuposa nchito ina iliyonse imene tingacite. Koma nthawi zina, zingakhale zovuta kuthela nthawi yoculuka muulaliki monga mmene tifunila.

2. Ni mavuto ati amene timakumana nawo pamene tiyesetsa kukwanilitsa mbali zonse za utumiki wathu?

2 Pali zinthu zina zofunika zimene zimafuna nthawi na mphamvu zathu. Mwacitsanzo, timafunika kugwila nchito ya maola ambili patsiku n’colinga cakuti tipeze zofunikila muumoyo wathu, komanso za banja lathu. Tingakhalenso na maudindo ena a m’banja. Komanso, timakumana na zovuta zina monga matenda, kuvutika maganizo, kapena zopweteka zobwela cifukwa ca ukalamba. Kodi tingacite ciani kuti tikwanilitse mbali zonse za utumiki wathu, ngakhale kuti timakumana na mavuto amenewa?

3. Kodi mawu a Yesu pa Mateyu 13:23 amaonetsa ciani ponena za utumiki wathu?

3 Ngati zinthu muumoyo wathu sizitilola kuthela nthawi yoculuka potumikila Yehova, sitiyenela kugwa mphwayi. Sikuti tonse tingathele nthawi na mphamvu zoculuka mofanana pa nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Yesu anali kuidziŵa bwino mfundo imeneyi. (Ŵelengani Mateyu 13:23) Ndipo Yehova amayamikila kwambili zilizonse zimene timacita pom’tumikila malinga ngati timacita zonse zimene tingathe. (Aheb. 6:10-12) Ngakhale n’telo, mwina tingaone kuti malinga na mmene zinthu zilili muumoyo wathu, tingathe kuwonjezela zocita pautumiki wathu. M’nkhani ino, tidzakambilana zimene tingacite kuti tiziika nchito yolalikila patsogolo muumoyo wathu. Kuwonjezela apo, tidzakambilana mmene tingakhalile na umoyo wosalila zambili, komanso zimene tingacite kuti tikulitse luso lathu pa nchito yolalikila na kuphunzitsa. Koma kodi kukwanilitsa mbali zonse za utumiki wathu kumatanthauza ciani?

4. Kodi kukwanilitsa mbali zonse za utumiki wathu kumatanthauza ciani?

4 Mwacidule, kukwanilitsa mbali zonse za utumiki wathu, kumatanthauza kucita zilizonse zimene tingathe pa nchito yolalikila na kuphunzitsa. Koma izi sizitanthauza cabe kuthela nthawi yoculuka muulaliki. Yehova amaona kuti colinga cathu pom’tumikila ndiye cofunika kwambili. Timacita utumiki wathu na mtima wonse cifukwa cokonda Yehova ndi anthu. * (Maliko 12:30, 31; Akol. 3:23) Kutumikila Mulungu na moyo wathu wonse kumatanthauza kudzipeleka kwathunthu, kapena kuti kugwilitsila nchito mphamvu zathu zonse pom’tumikila. Ngati timayamikila mwayi umene tili nawo wogwila nchito yolalikila, tidzayesetsa kulalikila uthenga wabwino kwa anthu ambili mmene tingathele.

5-6. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti ngakhale munthu amene amakhala na zocita zambili angaike patsogolo nchito yolalikila.

5 Tiyelekezele kuti pali mnyamata wina amene amakonda nchito ya uphunzitsi. Iye amakonda kuphunzitsa pa mpata uliwonse umene wapeza. M’kupita kwa nthawi, akupeza nchito yophunzitsa pa sukulu inayake ya pulaiveti kumapeto kwa wiki iliyonse. Komabe, poona kuti ndalama zimene amapeza sizikwanila kusamalila zosoŵa zake zonse, analoŵa nchito yogulitsa m’shopu. Iye amagwila nchitoyi kuyambila pa Mande mpaka pa Cisanu. Olo kuti amathela nthawi yoculuka m’shopu, nchito imene amakonda kwambili ni ya uphunzitsi. Ndipo amafunitsitsa kukulitsa luso lake pa nchitoyi. Amafunanso kuti nchito yake yaikulu ikakhale ya uphunzitsi. Cotelo, mnyamatayu akapeza mpata uliwonse, ngakhale wocepa cabe, amayesetsa kuugwilitsila nchito pophunzitsa.

6 Mofananamo, n’kutheka kuti simupeza nthawi yokwanila yolalikila monga mmene mumafunila. Komabe, mumaikonda kwambili nchito yolalikila. Ndipo mumayesetsa kukulitsa luso lanu lolalikila kuti muzifika anthu pa mtima na uthenga wabwino. Kodi mungacite ciani kuti muikebe patsogolo nchito yolalikila, olo kuti mumakhala na zocita zambili zofuna nthawi?

ZIMENE TINGACITE KUTI TIZIIKA PATSOGOLO NCHITO YOLALIKILA

7-8. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pankhani ya mmene timaonela nchito yolalikila?

7 Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca mmene tiyenela kuonela nchito yolalikila. Iye anaika nchito yolalikila za Ufumu wa Mulungu patsogolo muumoyo wake. (Yoh. 4:34, 35) Anayenda m’madela ambili n’colinga cakuti akalalikile anthu oculuka mmene angathele. Nthawi zonse, anali kusakila mipata yolalikila anthu kunyumba zawo, komanso kumalo ena opezeka anthu ambili. Nchito yolalikila ndiyo inali yofunika kwambili muumoyo wa Yesu.

8 Nafenso tingatengele citsanzo ca Khristu mwa kuyesetsa kupeza mipata yolalikila uthenga wabwino kwa anthu, nthawi iliyonse komanso kulikonse. Timalolela kudzimana zinthu zina muumoyo wathu, n’colinga cakuti tigwile nchito yolalikila. (Maliko 6:31-34; 1 Pet. 2:21) Akhristu ena mumpingo amatumikila monga apainiya apadela, anthawi zonse, kapena othandiza. Ena aphunzila citundu cina. Enanso asamukila kumadela kumene kuli alaliki ocepa. Koma nchito yaikulu yolalikila, imagwilidwa na abale na alongo a pampingo amene amayesetsa kucita zonse zimene angathe pa nchitoyi. Mulimonsemo, Yehova satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse. Iye amafuna kuti tizikondwela na utumiki wathu, pamene tilengeza “uthenga wabwino waulemelelo . .wocokela kwa Mulungu wacimwemwe.”—1 Tim. 1:11; Deut. 30:11.

9. (a) Kodi Paulo anaonetsa bwanji kuti anali kuika nchito yolalikila patsogolo ngakhale pamene anali kugwilanso nchito ya kuthupi? (b) Kodi Machitidwe 28:16, 30, 31 ionetsa kuti Paulo anali kuiona bwanji nchito yolalikila?

9 Mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cabwino pankhani yoika patsogolo nchito yolalikila. Pamene anali ku Korinto, mkati mwa ulendo wake waciŵili waumishonale, ndalama zinam’thela moti kwa kanthawi, anali kugwila nchito yopanga matenti. Komabe, iye sanaone kuti nchito yopanga matenti ndiyo inali yofunika kwambili. Anali kugwila nchitoyo kuti imucilikize pa utumiki wake, komanso kuti anthu a ku Korinto amvetsele uthenga wabwino popanda “kutayilapo ndalama.” (2 Akor. 11:7) Ngakhale kuti Paulo anali kugwilanso nchito yakuthupi, anaikabe patsogolo nchito yolalikila, ndipo anali kulalikila pa Sabata iliyonse. Atathandizidwa mwakuthupi, iye anawonjezela zocita muulaliki. Baibo imati “anatanganidwa kwambili ndi nchito yolalikila mawu a Mulungu. Paulo anali kucitila umboni kwa Ayuda ndi kuwatsimikizila kuti Yesu ndiyedi Khristu.” (Mac. 18:3-5; 2 Akor. 11:9) Panthawi inanso, pamene anali mkaidi wosacoka panyumba kwa zaka ziŵili ku Roma, iye anali kulalikila anthu obwela kudzamuona komanso kulemba makalata. (Ŵelengani Machitidwe 28:16, 30, 31) Paulo anatsimikiza mtima kusalola ciliconse kumulepheletsa kuika patsogolo utumiki wake. Iye analemba kuti: “Popeza tili ndi utumiki umenewu. . . , sitikubwelela m’mbuyo.” (2 Akor. 4:1) Mofanana na Paulo, nafenso tingathe kuika patsogolo nchito ya Ufumu, ngakhale kuti mwina timathela nthawi yoculuka pa nchito yathu yakuthupi.

Pali zambili zimene tingacite kuti tikwanilitse mbali zonse za utumiki wathu (Onani ndime 10-11)

10-11. Tingacite ciani kuti tikwanilitse mbali zonse za utumiki wathu ngakhale pamene tikudwala?

10 Ngati sitikwanitsa kulalikila kunyumba na nyumba cifukwa ca ukalamba kapena matenda, tikhoza kumalalikila m’njila zina. Akhristu a m’nthawi ya atumwi anali kulalikila kulikonse kumene apeza anthu. Iwo anali kulalikila coonadi kwa anthu pa mpata uliwonse umene apeza. Anali kucita ulaliki wa kunyumba na nyumba, wapoyela, komanso wamwayi. Inde, iwo anali kulalikila kulikonse kumene ‘anapeza’ anthu. (Mac. 17:17; 20:20) Ngati sitikwanitsa kuyenda kwa nthawi yaitali muulaliki cifukwa ca thanzi lofooka, tingakhale pamalo ena ake popita anthu ambili na kumalalikila anthu odutsa m’njila. Kapena tingacite ulaliki wamwayi, wa makalata, kapena wa pafoni. Ofalitsa ambili amene sakwanitsa kucita ulaliki wa kunyumba na nyumba cifukwa ca matenda kapena mavuto ena, amakondwela kulalikila m’njila zimenezi.

11 Ngakhale pamene mudwala, mungathe kukwanilitsa mbali zonse za utumiki wanu. Ganizilaninso citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anati: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afil. 4:13) Paulendo wina waumishonale, Paulo anadwala, ndipo anafunikila mphamvu zimenezi zocokela kwa Mulungu. Iye anafotokozela Akhristu a ku Galatiya kuti mwayi woyamba wolengeza uthenga wabwino kwa iwo, anaupeza ‘cifukwa cakuti anali kudwala.’ (Agal. 4:13) Mofananamo, pamene tikudwala, tingakhale na mwayi wolengeza uthenga wabwino kwa ena, monga madokotala, manesi, komanso anthu ena ogwila nchito kucipatala. Ambili mwa anthu amenewa amakhala ku nchito pamene timafika pa nyumba zawo kuti tiwalalikile.

ZIMENE TINGACITE KUTI TIKHALE NA UMOYO WOSALILA ZAMBILI

12. Kodi kukhala na diso “lolunjika pa cinthu cimodzi” kumatanthauza ciani?

12 Yesu anati: “Nyale ya thupi ndi diso. Cotelo ngati diso lako lili lolunjika pa cinthu cimodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala.” (Mat. 6:22) Kodi anatanthauza ciani pamene anakamba mawu amenewa? Anatanthauza kuti tifunika kukhala na umoyo wosalila zambili, kapena kuti kusumika maganizo athu pa cinthu cimodzi kapena pa colinga cimodzi, popanda kucenjenekewa na zinthu zina. Yesu anapeleka citsanzo cabwino pankhaniyi mwa kuika maganizo ake onse pa utumiki wake. Ndipo analangiza otsatila ake kuti ayenela kusumika maganizo awo pa kutumikila Yehova, komanso pa Ufumu wake. Timatengela citsanzo ca Yesu mwa kuona nchito yolalikila kukhala yofunika kwambili, komanso “kufunafuna ufumu coyamba ndi cilungamo [ca Mulungu].”—Mat. 6:33.

13. N’ciani cingatithandize kuti tisumike maganizo athu pa nchito yolalikila?

13 N’ciani cingatithandize kuti tisumike maganizo athu pa nchito yolalikila? Cimodzi cimene cingatithandize ni kukhala na umoyo wosalila zambili, n’colinga cakuti tizithela nthawi yoculuka pothandiza ena kudziŵa Yehova na kum’konda. * Mwacitsanzo, kodi tingacepetseko maola ogwila nchito yathu ya kuthupi kuti tizithela nthawi yoculuka muulaliki mkati mwa wiki? Kodi tingacepetseko zosangalatsa zimene zimatidyela nthawi?

14. Ni masinthidwe otani amene banja lina linapanga kuti lizithela nthawi yoculuka muulaliki?

14 Izi n’zimene mkulu wina wa mumpingo, dzina lake Elias, na mkazi wake anacita. Iye anati: “Sitikanakwanitsa kuyamba upainiya nthawi yomweyo. Koma panali zinthu zina zimene tikanacita kuti tizithela nthawi yoculuka muulaliki. Tinayamba mwa kusinthako zinthu zina muumoyo wathu. Mwacitsanzo, tinacepetsako zogula-gula, tinaleka kucita zosangalatsa zimene zinali kutidyela nthawi, komanso tinapempha abwana athu kuti aticepetseleko nthawi yoseŵenza. Zotulukapo zake zinali zakuti, tinayamba kucitako ulaliki wa m’madzulo. Tinayambanso kutsogoza maphunzilo ambili a Baibo, ndiponso kutengako mbali muulaliki wa mkati mwa wiki, masiku aŵili pa mwezi. Zinali zokondweletsa kwambili!”

MMENE TINGAKULITSILE LUSO LATHU PA KULALIKILA NA KUPHUNZITSA

Kuseŵenzetsa mfundo zimene timaphunzila pamsonkhano wa mkati mwa wiki kudzatithandiza kunola luso lathu muulaliki (Onani ndime 15-16)) *

15-16. Malinga ndi 1 Timoteyo 4:13, 15, kodi tingapitilize bwanji kukulitsa luso lathu monga alaliki? (Onani danga lakuti “ Zolinga Zotithandiza Kukwanilitsa Mbali Zonse za Utumiki Wathu.”)

15 Cinanso cofunikila kuti tikwanilitse mbali zonse za utumiki wathu, ni kukulitsa luso lathu pa nchito yolalikila. Anthu ena pa nchito zawo, amapitiliza kulandila maphunzilo ena ake, n’colinga cakuti akulitse luso na kudziŵa bwino nchito zawo. N’cimodzi-modzinso kwa ife alaliki a Ufumu. Tifunika kupitiliza kuphunzila kuti tikulitse luso lathu pa nchito yolalikila.—Miy. 1:5; ŵelengani 1 Timoteyo 4:13, 15.

16 Koma kodi tingakulitse bwanji luso lathu pa nchito yolalikila? Tingacite zimenezi mwa kumvetsela mosamala malangizo amene timalandila pa Msonkhano wa Umoyo na Utumiki. Pa msonkhano umenewu, timaphunzila mfundo zofunika kwambili zotithandiza kunola luso lathu muulaliki. Mwacitsanzo, cheyamani akamapeleka uphungu kwa okamba nkhani za m’sukulu, tingatengepo mfundo zimene zingatithandize muulaliki. Ndiyeno, ulendo wotsatila polalikila kwa munthu uthenga wabwino, tingakagwilitsile nchito mfundozo. Tingapemphenso malangizo kwa woyang’anila kagulu kathu ka ulaliki, kapenanso kuyenda naye muulaliki. Tingayendenso muulaliki na wofalitsa waluso, mpainiya, kapena woyang’anila dela. Kucita izi kudzatithandiza kudziŵa moseŵenzetsela zida za mu Thuboksi yathu. Tikatelo, tidzapeza cimwemwe coculuka panchito yathu yolalikila na kuphunzitsa.

17. Kodi tidzapindula bwanji ngati tiyesetsa kukwanilitsa mbali zonse za utumiki wathu?

17 Ndife odala kuti Yehova watilola kukhala “anchito anzake.” (1 Akor. 3:9) Mukamayesetsa ‘kutsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili n’ziti,’ na kuika patsogolo utumiki, ‘mudzatumikila Yehova mokondwela.’ (Afil. 1:10; Sal. 100:2) Ndipo pokhala mtumiki wa Mulungu, musakayikile zakuti iye adzakupatsani mphamvu zofunikila kuti mukwanilitse utumiki wanu, mosasamala kanthu za mavuto amene muli nawo kapena zopinga. (2 Akor. 4:1, 7; 6:4) Kaya zinthu muumoyo wanu zimakulolani kucita zambili pa nchito yolalikila kapena ayi, ngati mumacita utumiki wanu na mtima wonse, ‘mudzakhala na cifukwa cosangalalila.’ (Agal. 6:4) Pamene mukwanilitsa mbali zonse za utumiki wanu, mumaonetsa kuti mumakonda Yehova komanso anthu anzanu. Baibo imati: ‘Tikatelo tidzadzipulumutsa tekha komanso anthu otimvela.’—1 Tim. 4:16.

NYIMBO 58 Kusakila Anthu Okonda Mtendele

^ ndime 5 Tinapatsidwa nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu na kupanga ophunzila. M’nkhani ino, tidzakambilana mmene tingakwanilitsile mbali zonse za utumiki wathu, ngakhale pamene tikumana na mavuto ambili muumoyo wathu. Tidzakambilananso zimene tingacite kuti tizilalikila mogwila mtima, komanso kuti tizipeza cimwemwe pa nchitoyi.

^ ndime 4 MAWU OFOTOKOZEDWA: Utumiki wathu umaphatikizapo mbali zosiyana-siyana, monga kulalikila na kuphunzitsa, kumanga malo olambilila na kuwakonza, komanso kugwila nchito yopeleka thandizo pakagwa masoka a zacilengedwe.—2 Akor. 5:18, 19; 8:4.

^ ndime 13 Onani mfundo 7 za m’bokosi yakuti, “Zimene Mungacite Kuti Mukhale na Umoyo Wosafuna Zambili,” mu Nsanja ya Mlonda ya July 2016, peji 10.

^ ndime 62 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Mlongo akucita citsanzo ca ulaliki ca ulendo wobwelelako pa msonkhano wa mkati mwa wiki. Ndiyeno, pamene cheyamani apeleka uphungu, iye akulemba mfundo zofunikila m’kabuku kakuti Kuphunzitsa. Ndipo kumapeto kwa wiki, pamene ali muulaliki, akuseŵenzetsa mfundozo.