Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 17

Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Kukaniza Mizimu Yoipa

Lolani Kuti Yehova Akuthandizeni Kukaniza Mizimu Yoipa

‘Tikulimbana . . . ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.’—AEF. 6:12.

NYIMBO 55 Musaŵayope!

ZA M’NKHANI INO *

1. Mogwilizana na Aefeso 6:10-13, ni njila imodzi iti yapadela kwambili imene Yehova amaonetsela kuti amatikonda? Fotokozani.

NJILA imodzi yapadela kwambili imene Yehova amaonetsela cikondi cake kwa ife atumiki ake, ni mwa kutithandiza kulimbana na adani athu. Adani athu aakulu ni Satana na ziŵanda. Yehova amaticenjeza za adani amenewa, ndipo amatipatsa zonse zofunikila kuti tisagonje polimbana nawo. (Ŵelengani Aefeso 6:10-13) Ngati tidalila Yehova na mtima wonse komanso kulola kuti atithandize, tingathe kum’kaniza Mdyelekezi. Ndipo tingakhale na cidalilo monga ca mtumwi Paulo. Iye analemba kuti: “Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?”—Aroma 8:31.

2. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

2 Pokhala Akhristu oona, sititaya nthawi yathu kukambilana kwambili za Satana na ziŵanda zake. M’malomwake, timaika kwambili maganizo athu pa kutumikila Yehova na kuphunzila za iye. (Sal. 25:5) Ngakhale n’conco, tiyenela kudziŵa zimene Satana amacita pofuna kusoceletsa anthu. Cifukwa ciani? Cifukwa zingatithandize kudziŵa mmene tingapewele kusoceletsedwa na macenjela ake. (2 Akor. 2:11) M’nkhani ino, tidzakambilana njila yaikulu imene Satana na ziŵanda zake amaseŵenzetsa pofuna kusoceletsa anthu. Tidzakambilananso zimene tingacite kuti asatisoceletse.

MMENE MIZIMU YOIPA IMASOCELETSELA ANTHU

3-4. (a) Kodi zamizimu n’ciani? (b) Kodi kukhulupilila zamizimu n’kofala motani?

3 Njila yaikulu imene Satana na ziŵanda zake amaseŵenzetsa pofuna kusoceletsa anthu ni zamizimu. Anthu amene amacita zamizimu amakamba kuti angakwanitse kucita zinthu zimene mwacibadwa munthu sangathe kucita kapena kudziŵa. Mwacitsanzo, ena amakamba kuti angakwanitse kudziŵa zakutsogolo mwa kuwombeza kapena kupenda nyenyezi. Ena amacita zinthu zoonetsa ngati kuti akukamba na anthu akufa. Enanso amacita za ufiti, zamatsenga, komanso amayesa kulodza ena. *

4 Kodi kukhulupilila zamizimu n’kofala motani? Kufufuza kwina kumene kunacitika m’maiko 18 a ku Latin America na ku Caribbean, kunaonetsa kuti pafupi-fupi munthu mmodzi mwa anthu atatu alionse kumeneko amakhulupilila zamatsenga, zaumfiti, kapena zanyanga. Ndipo pa kufufuza kumeneko anapezanso kuti anthu oculuka mofananamo amakhulupilila kuti n’zotheka kukamba na mizimu. Kufufuza kwina kunacitika m’maiko 18 a mu Africa. Ndipo pa avaleji, anthu opitilila 50 pesenti mwa anthu amene anafunsidwa anakamba kuti amakhulupilila zaumfiti. Komabe, mosasamala kanthu za kumene timakhala, tonsefe tifunika kudziteteza ku zamizimu. Tisaiŵale kuti Satana amafunitsitsa ‘kusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.’—Chiv. 12:9.

5. Kodi Yehova amaliona bwanji khalidwe locita zamizimu?

5 Yehova ni “Mulungu wacoonadi.” (Sal. 31:5) Kodi iye amaliona bwanji khalidwe locita zamizimu? Amadana nalo kwambili. Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto, wolosela, wocita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsila kwa wolankhula ndi mizimu, wolosela zam’tsogolo kapena aliyense wofunsila kwa akufa. Pakuti aliyense wocita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova.” (Deut. 18:10-12) N’zoona kuti Akhristu sali pansi pa Cilamulo cimene Yehova anapatsa Aisiraeli. Koma tidziŵa kuti maganizo ake pankhani ya zamizimu sanasinthe.—Mal. 3:6.

6. (a) Kodi Satana amaseŵenzetsa bwanji zamizimu pofuna kusoceletsa anthu? (b) Malinga ndi Mlaliki 9:5, n’ciani cimacitika ngati munthu wafa?

6 Yehova amaticenjeza kuti tiyenela kupewa zamizimu, cifukwa adziŵa kuti ni msampha umene Satana amaseŵenzetsa pofuna kusoceletsa anthu. Satana amaseŵenzetsa zamizimu pofalitsa mabodza, monga lakuti munthu akafa, cinacake cimapitiliza kukhala na moyo kumalo a mizimu. (Ŵelengani Mlaliki 9:5.) Iye amaseŵenzetsanso zamizimu pocititsa anthu kukhala mwamantha na kuleka kutumikila Yehova. Satana amafuna kuti anthu azidalila mizimu yoipa m’malo modalila Yehova.

ZIMENE TINGACITE KUTI TIKANIZE MIZIMU YOIPA

7. Kodi Yehova amatiuza ciani?

7 Monga takambilapo kale, Yehova amatiuza zimene tiyenela kucita kuti tipewe kusoceletsedwa na Satana, komanso ziŵanda zake. Lomba, tiyeni tikambilane zinthu zina zimene tingacite kuti tisagonje polimbana na Satana komanso ziŵanda.

8. (a) Ni njila yaikulu iti imene tingapewele kusoceletsedwa na mizimu yoipa? (b) Kodi Salimo 146:4 imavumbula bwanji bodza la Satana ponena za akufa?

8 Muziŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha. Iyi ndiyo njila yaikulu imene tingapewele kusoceletsedwa na mabodza a Satana na ziwanda zake. Mawu a Mulungu amavumbula mabodza amene Satana amafalitsa. (Aef. 6:17) Mwacitsanzo, amavumbula bodza lakuti akufa angathe kukamba ndi anthu a moyo. (Ŵelengani Salimo 146:4.) Cinanso, Mawu a Mulungu amakamba kuti Yehova yekha ndiye amakwanitsa kukamba zoona ponena za kutsogolo. (Yes. 45:21; 46:10) Conco, ngati timaŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha nthawi zonse, tidzapewa kukhulupilila mabodza a ziŵanda, ndipo tidzayamba kudana nawo.

9. N’zinthu monga ziti zokhudzana na zamizimu zimene timapewa?

9 Pewani kucita ciliconse cokhudzana na zamizimu. Pokhala Akhristu oona, timapewa kucita zamizimu za mtundu uliwonse. Mwacitsanzo, timapewa kufunsila kwa anthu olankhula na mizimu, kapena kuyesa kukamba na akufa m’njila iliyonse. Ndipo monga tinakambila m’nkhani yapita, timapewa kutengako mbali m’miyambo ya malilo yozikidwa pa cikhulupililo cakuti munthu akafa amakhalabe na moyo kwinakwake. Komanso, sitifunsila kwa olosela zakutsogolo kapena kwa openda nyenyezi n’colinga cakuti tidziŵe zakutsogolo. (Yes. 8:19) Timadziŵa kuti kucita zimenezi n’koopsa kwambili, ndipo kungatigwetsele m’manja mwa Satana na ziŵanda zake.

Tengelani citsanzo ca Akhristu a m’nthawi ya atumwi mwa kutaya ciliconse cogwilizana na zamatsenga, komanso kupewa zosangalatsa zokhudzana na zamizimu (Onani ndime 10-12)

10-11. (a) Kodi anthu ena a m’nthawi ya atumwi anacita ciani ataphunzila coonadi? (b) Malinga ndi 1 Akorinto 10:21, n’cifukwa ciani tiyenela kutengela citsanzo ca Akhristu a m’nthawi ya atumwi? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cawo?

10 Tayani ciliconse cogwilizana na zamatsenga. M’nthawi ya atumwi, anthu ena a ku Efeso anali kucita zamizimu. Koma ataphunzila coonadi, anacitapo kanthu molimba mtima kuti adule mgwilizano uliwonse na ziŵanda. Baibo imati: “Ambili ndithu amene anali kucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.” (Mac. 19:19) Anthu amenewo anatsimikiza mtima kukaniza mizimu yoipa. Mabuku awo a zamatsenga anali a ndalama zambili. Ndipo akanafuna akanapatsa ena mabukuwo kapena kuwagulitsa. Koma anawatentha. Zinalibe kanthu kuti mabukuwo anali a ndalama zingati, iwo anaona kuti cofunika kwambili ni kukondweletsa Yehova.

11 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Akhristu a m’nthawi ya atumwi amenewo? Tingacite bwino kutaya kanthu kalikonse kamene tingakhale nako kogwilizana na zamatsenga. Izi zingaphatikizepo mphinjili, zithumwa, kapena zinthu zina zimene anthu amavala pofuna kudziteteza ku mizimu yoipa.—Ŵelengani 1 Akorinto 10:21.

12. Ni mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa pankhani ya zosangalatsa zimene timakonda?

12 Sankhani mosamala zosangalatsa. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nimaŵelenga mabuku, magazini, kapena nkhani za pa intaneti zogwilizana na zamatsenga? Nanga bwanji ponena za nyimbo zimene nimamvetsela, mafilimu na mapulogilamu a pa TV amene nimatamba, kapena maseŵela a pa kompyuta amene nimacita? Kodi zosangalatsa zimene nimakonda n’zogwilizana na zamizimu? Kodi zimaonetsa zinthu monga vipuku, ziŵanda, kapena zamatsenga? Kodi zimaonetsa kuti kucita zamizimu, kulodza anthu ena kapena kuwatembelela kulibe vuto?’ Sikuti nthano zonse kapena zosangalatsa zonse zimene zimaoneka zodabwitsa zimakhala zokhudzana na zamizimu. Ngakhale n’telo, posankha zosangalatsa, tiyenela kuyesetsa kusankha zimene zidzatithandiza kupewelatu ciliconse cimene Yehova amazonda. Timafuna kucita zilizonse zimene tingathe kuti tikhalebe na cikumbumtima coyela pamaso pa Mulungu.—Mac. 24:16. *

13. Kodi tiyenela kupewa kucita ciani?

13 Pewani kusimba nkhani zokhudza zocita za ziŵanda. Pambali imeneyi, tiyenela kutengela citsanzo ca Yesu. (1 Pet. 2:21) Asanabwele padziko lapansi, Yesu anali kumwamba, ndipo anali kudziŵa zambili zokhudza Satana na ziŵanda zake. Koma atabwela padziko lapansi, sanali kusimba zimene mizimu yoipayo inacita. Yesu anali kukonda kuuza anthu za Yehova, osati za Satana. Nafenso tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kupewa kufalitsa nkhani zokhudza ziŵanda. M’malomwake, mwa zokamba zathu, tiyenela kuonetsa kuti ‘mtima wathu ni wogalamuka cifukwa ca nkhani yosangalatsa,’ imene ni coonadi.—Sal. 45:1.

Palibe cifukwa coopela mizimu yoipa. Yehova, Yesu, komanso angelo ni amphamvu kwambili kuposa Satana na ziŵanda zake (Onani ndime 14-15) *

14-15. (a) N’cifukwa ciani sitiyenela kuyopa mizimu yoipa? (b) Kodi pali umboni wotani woonetsa kuti Yehova amateteza atumiki ake?

14 Musamaope mizimu yoipa. Popeza tikhala m’dziko loipa, nthawi iliyonse matsoka angatigwele. Tingacite ngozi, kudwala, kapena kufa mosayembekezeleka. Zaconco zikacitika, sitiyenela kuganiza kuti mizimu yoipa ni imene yapangitsa. Baibo imati: “Nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka” zingagwele aliyense wa ife.” (Mlal. 9:11) Sitiyenela kuopa mizimu yoipa cifukwa Yehova waonetsa kuti ni wamphamvu kwambili kuposa ziŵanda. Mwacitsanzo, Mulungu sanalole Satana kupha Yobu. (Yobu 2:6) Ndipo m’nthawi ya Mose, Yehova anaonetsa kuti anali wamphamvu kwambili kuposa ansembe ocita zamatsenga a ku Iguputo. (Eks. 8:18; 9:11) Komanso panthawi ina, Yesu atapita kumwamba, Yehova anam’patsa mphamvu pa mizimu yoipa, moti anaponya Satana na ziŵanda zake padziko lapansi kucokela kumwamba. Posacedwapa, Yesu adzawaponya kuphompho, ndipo sadzakwanitsa kusoceletsa munthu aliyense.—Chiv. 12:9; 20:2, 3.

15 Pali maumboni ambili oonetsa kuti Yehova amateteza atumiki ake masiku ano. Ganizilani izi: Timalalikila na kuphunzitsa anthu coonadi padziko lonse lapansi. (Mat. 28:19, 20) Pamene tilalikila, timavumbula nchito zoipa za Mdyelekezi. Satana akanakhala na mphamvu yocita ciliconse, sembe anailetsa kale nchito yolalikila. Koma sangakwanitse. Cotelo, sitiyenela kuyopa mizimu yoipa. Tidziŵa kuti “maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Ngati tikhala okhulupilika kwa Yehova, ziŵanda sizingakwanitse kucita ciliconse cimene cingatilepheletse kukapeza moyo wosatha.

MADALITSO AMENE TINGAPEZE NGATI TILOLA YEHOVA KUTITHANDIZA

16-17. Fotokozani citsanzo coonetsa kuti pamafunika kulimba mtima kuti tikanize mizimu yoipa.

16 Kukhala wolimba mtima n’kofunika kwambili kuti tikanize mizimu yoipa, maka-maka pamene mabwenzi athu komanso acibululu akutitsutsa. Yehova amadalitsa anthu amene amaonetsa kulimba mtima. Ganizilani citsanzo ca mlongo Erica wa ku Ghana. Mlongoyu anayamba kuphunzila Baibo ali na zaka 21. Popeza kuti anali mwana wa sing’anga, anthu anayembekezela kuti iye adzacitako mwambo wa zamizimu umene unali kuphatikizapo kudya nyama yopelekedwa nsembe kwa mizimu ya makolo. Pamene Erica anakana, am’banja lake anakamba kuti iye wanyoza mizimu. Iwo anali kukhulupilila kuti cifukwa ca zimene iye anacita, mizimuyo idzawadwalitsa misala na matenda ena aakulu.

17 Makolo ake ndi abululu ake ena anayesa kum’kakamiza kuti aciteko mwambowo, koma Erica anakana. Anakanabe ngakhale atamuopseza kum’cotsa panyumba. Atam’cotsa, abale na alongo ena anam’lola kukakhala kumanyumba kwawo. Apa tingati Yehova anadalitsa Erica mwa kum’patsa banja latsopano, kutanthauza olambila anzake amene ali monga abululu ake akuthupi. (Maliko 10:29, 30) Ngakhale kuti abululu ake anam’kana mpaka kufika pomushokela zovala na zinthu zina, Erica anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Iye anabatizika, ndipo pano tikamba ni mpainiya wanthawi zonse. Iye sayopa ziŵanda. Pokamba za abululu ake, Erica anati: “Tsiku lililonse, nimapemphela kuti abululu anga nawonso am’dziŵe Yehova, na kuti adzakhale na ufulu umene umabwela cifukwa cotumikila Mulungu wathu wacikondi.”

18. Ni madalitso anji amene timalandila ngati tidalila Yehova?

18 Sikuti tonsefe tidzakumana na mayeselo ngati amenewa. Komabe, tonsefe tiyenela kukaniza mizimu yoipa na kudalila Yehova. Tikatelo, tidzalandila madalitso ambili, ndipo tidzapewa kusoceletsedwa na mabodza a Satana. Komanso, sitidzaleka kutumikila Yehova cifukwa coopa ziŵanda. Ndipo koposa zonse, tidzalimbitsa ubwenzi wathu na Yehova. Wophunzila wa Yesu, Yakobo analemba kuti: “Gonjelani Mulungu, koma tsutsani Mdyelekezi ndipo adzakuthawani. Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—Yak. 4:7, 8.

NYIMBO 150 Funani Cipulumutso ca Mulungu

^ ndime 5 Mwacikondi, Yehova amatiuza kuti tifunika kupewa mizimu yoipa, cifukwa ingatisoceletse. Kodi mizimu yoipa imawasoceletsa bwanji anthu? Nanga n’zinthu ziti zimene tingacite kuti isatisoceletse? M’nkhani ino, tidzakambilana mmene Yehova amatithandizila kuti tipewe kusoceletsedwa na mizimu yoipa.

^ ndime 3 MAWU OFOTOKOZEDWA: Zamizimu ni zikhulupililo komanso zinthu zina zimene anthu amacita mogwilizana na ziŵanda. Zimaphatikizapo cikhulupililo cakuti munthu akafa, mzimu wake umapitiliza kukhala na moyo kwinakwake komanso umakamba ndi anthu amoyo, maka-maka kupitila mwa munthu wolankhula na mizimu. Zamizimu zimaphatikizaponso zinthu monga umfiti na kuwombeza. Komanso zimaphatikizapo kucita zinthu zamatsenga, monga kutembelela ena, kuwalodza kapena kuvumula (kufumbulula) munthu amene walodzedwa. Koma zamizimu siziphatikizapo maseŵela odabwitsa amene ena amacita cifukwa ca luso lawo kuti akondweletse anthu.

^ ndime 12 Akulu alibe mphamvu yoikila ena malamulo pankhani yosankha zosangalatsa. M’malomwake, Mkhristu aliyense ayenela kuseŵenzetsa cikumbumtima cake cophunzitsidwa Baibo posankha zoŵelenga, zotamba, kapena maseŵela amene afuna kucita. Mitu ya mabanja yanzelu imaonetsetsa kuti zosangalatsa zimene mabanja awo amacita n’zogwilizana na mfundo za m’Baibo.—Onani nkhani ya pa jw.org® yakuti, “Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina?” Pitani ku Chichewa, pambali yakuti ZOKHUDZA IFEYO > MAFUNSO OFUNSIDWA KAWILIKAWILI.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Yesu, Mfumu yathu yamphamvu yakumwamba, akutsogolela gulu lankhondo la angelo.