Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 15

Tengelani Yesu Kuti Mukhalebe na Mtendele wa Mumtima

Tengelani Yesu Kuti Mukhalebe na Mtendele wa Mumtima

“Mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.”—AFIL. 4:7.

NYIMBO 113 Mtendele Wathu

ZA M’NKHANI INO *

1-2. N’cifukwa ciani Yesu anasautsika mtima?

PATSIKU lotsiliza la moyo wake pano padziko lapansi, Yesu anasautsika mtima. Anali atatsala pang’ono kuphedwa mwankhanza ndi anthu oipa. Koma iye sanali kuda nkhawa cabe cifukwa cakuti anali pafupi kuphedwa. Popeza kuti Yesu anali kuwakonda kwambili Atate wake, sanafune kucita zinthu zowakhumudwitsa. Iye anadziŵa kuti ngati akhalabe wokhulupilika pa mayeselo aakulu amenewo, adzathandiza kuyeletsa dzina la Yehova na kulikweza. Komanso, Yesu anali kukonda anthu, ndipo anali kudziŵa kuti ciyembekezo cathu cokakhala na moyo wosatha, cinadalila pa kukhala kwake wokhulupilika mpaka imfa.

2 Olo kuti panthawiyo Yesu anali wopanikizika maganizo kwambili, anakhalabe na mtendele wa mumtima. Ndiye cifukwa cake anauza atumwi ake kuti: “Ndikupatsani mtendele wanga.” (Yoh. 14:27) Iye anali na “mtendele wa Mulungu.” Uwu ni mtendele wa mumtima umene munthu amakhala nawo cifukwa cokhala pa ubwenzi wolimba na Yehova. Mtendele umenewu unathandiza Yesu kukhazika mtima pansi.—Afil. 4:6, 7.

3. Kodi m’nkhani ino tidzakambilana ciani?

3 Palibe aliyense wa ife amene adzakumana na mavuto aakulu ngati amene Yesu anakumana nawo. Ngakhale n’telo, aliyense amene amatsatila Yesu, adzakumana na mayeselo muumoyo wake. (Mat. 16:24, 25; Yoh. 15:20) Ndipo mofanana na Yesu, timakhala na nkhawa nthawi zina. Tingacite ciani kuti tisamakhale na nkhawa yopitilila malile imene ingatilande mtendele wa mumtima? Tiyeni tikambilane zinthu zitatu zimene Yesu anacita pautumiki wake wa padziko lapansi. Kenako, tidzaona mmene tingatsatilile citsanzo cake pamene takumana na mavuto.

YESU ANALI KUPEMPHELA KAŴILI-KAŴILI

Kupemphela kumatithandiza kukhalabe na mtendele wamumtima (Onani ndime 4-7)

4. Mogwilizana na mfundo ya pa 1 Atesalonika 5:17, chulani zitsanzo zoonetsa kuti Yesu anapemphela mobweleza-bweleza patsiku lothela la moyo wake padziko lapansi?

4 Ŵelengani 1 Atesalonika 5:17. Patsiku lothela la moyo wake padziko lapansi, Yesu anapemphela mobweleza-bweleza. Mwacitsanzo, pamene anali kuyambitsa mwambo wokumbukila imfa yake, anapemphelela mkate na vinyo. (1 Akor. 11:23-25) Ndipo asanacoke pamalo amene anacitila Pasika, anapemphela pamodzi na ophunzila ake. (Yoh. 17:1-26) Komanso, Yesu na ophunzila ake atafika pamalo ochedwa Getsemane usiku wa tsiku limenelo, anapemphela mobweleza-bweleza. (Mat. 26:36-39, 42, 44) Ngakhale mawu omaliza amene iye anakamba atatsala pang’ono kufa, anali pemphelo. (Luka 23:46) Yesu anali kupemphela kwa Yehova pa ciliconse cimene cinacitika pa tsiku lothela la moyo wake padziko lapansi.

5. N’cifukwa ciani atumwi sanalimbe mtima pamene anakumana na mayeselo?

5 N’ciani cinathandiza Yesu kupilila mayeselo? Cinthu cimodzi cimene cinam’thandiza n’cakuti anadalila kwambili Atate wake mwa kupemphela kaŵili-kaŵili. Koma atumwi sanalimbikile kupemphela usikuwo. Zotulukapo zake zinali zakuti iwo sanalimbe mtima pamene nthawi ya mayeselo inafika. (Mat. 26:40, 41, 43, 45, 56) Pamene takumana na mayeselo, tingakhale okhulupilika ngati titengela citsanzo ca Yesu mwa ‘kupemphela mosalekeza.’ Kodi tingapemphe ciani?

6. Kodi cikhulupililo cingatithandize bwanji kukhalabe na mtendele wa mumtima?

6 Tingapemphe Yehova kuti ‘atiwonjezele cikhulupililo.’ (Luka 17:5; Yoh. 14:1) Tifunika kukhala na cikhulupililo cifukwa Satana amayesa aliyense amene amatsatila Yesu. (Luka 22:31) Kodi cikhulupililo cingatithandize bwanji kukhalabe na mtendele wamumtima ngakhale pamene tikumana na mavuto motsatizana-tsatizana? Ngati tacita zonse zimene tingathe kuti tithane na vuto linalake, cikhulupililo cidzatithandiza kuti tisamangodela nkhawa za mavutowo. M’malomwake, tidzasiya zonse m’manja mwa Yehova. Timakhala na mtendele wa mumtima, cifukwa timadziŵa kuti iye ndiye adziŵa bwino njila yothetsela mavuto athu.—1 Pet. 5:6, 7.

7. Tiphunzilapo ciani pa zimene m’bale Robert anakamba?

7 Pemphelo limatithandiza kukhalabe na mtendele wa m’maganizo, olo tikumane na mayeselo otani. Ganizilani citsanzo ca mkulu wina wokhulupilika, dzina lake Robert, amene ali na zaka za m’ma 80. Iye anati: “Malangizo a pa Afilipi 4:6, 7 anithandiza kupilila mayeselo ambili muumoyo wanga. N’nakumana na mavuto azacuma. Komanso, panthawi ina n’natsitsidwa pa ukulu.” N’ciani cathandiza m’bale Robert kukhalabe na mtendele wamumtima? Iye anati: “Nikangoyamba kukhala na nkhawa, nimapemphela nthawi yomweyo. Nimaona kuti ngati nipemphela kaŵili-kaŵili komanso mwakhama, m’pamene nimakhala na mtendele woculuka wamumtima.”

YESU ANALI KULALIKILA MOKANGALIKA

Kulalikila kumatithandiza kukhalabe na mtendele wamumtima (Onani ndime 8-10)

8. Malinga n’zimene Yohane 8:29 ikamba, n’ciani cina cimene cinathandiza Yesu kukhala na mtendele wamumtima?

8 Ŵelengani Yohane 8:29. Ngakhale pamene anali kuzunzidwa, Yesu anakhalabe na mtendele wamumtima cifukwa anali kudziŵa kuti anali kucita zinthu zokondweletsa Atate ake. Iye anakhalabe womvela, ngakhale pamene zinali zovuta kutelo. Yesu anali kuwakonda Atate ake, ndipo anali kuona kuti cofunika kwambili muumoyo wake ni kutumikila Yehova. Iye asanabwele padziko lapansi, anali “mmisili waluso” wa Mulungu. (Miy. 8:30) Ndipo pamene anali padziko, anali kuphunzitsa anthu za Atate ake mokangalika. (Mat. 6:9; Yoh. 5:17) Nchito imeneyi, inali kumubweletsela cimwemwe coculuka.—Yoh. 4:34-36.

9. Kodi kulalikila mokangalika kumatithandiza bwanji kukhalabe na mtendele wamumtima?

9 Tingatengele citsanzo ca Yesu mwa kumvela Yehova komanso ‘kukhala ndi zocita zambili nthawi zonse mu nchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) ‘Kutangwanika kwambili’ na nchito yolalikila kumatithandiza kuti tiziona mavuto athu moyenelela. (Mac. 18:5) Mwacitsanzo, anthu amene timawalalikila, nthawi zambili amakhala na mavuto aakulu kuposa amene ife tili nawo. Koma akaphunzila za Yehova na kuyamba kum’konda komanso kumvela malamulo ake, umoyo wawo umasintha ndipo amakhala na cimwemwe coculuka. Tikaona zimenezi, cikhulupililo cathu cakuti Yehova adzatisamalila, cimalimba. Cikhulupililo cimeneci n’cimene cimatithandiza kukhalabe na mtendele wamumtima. Mlongo wina amene wakhala akuvutika maganizo kwa nthawi yaitali komanso kudziona ngati wacabe-cabe, anadzionela yekha kuti kutangwanika na nchito yolalikila n’kothandiza. Iye anati: “Nikamalalikila mokangalika, nkhawa zimacepa, komanso nimakhala wacimwemwe kwambili. Niona kuti zimakhala conco cifukwa nikakhala muulaliki, m’pamene nimadzimva kuti nili pafupi kwambili na Yehova.”

10. Kodi mwaphunzilapo ciani pa zimene mlongo Brenda anakamba?

10 Ganizilani citsanzo ca mlongo wina, dzina lake Brenda. Iye na mwana wake wamkazi, ali na matenda aakulu, owononga minyewa ya muubongo (multiple sclerosis). Mlongo Brenda amayenda pa njinga ya olemala, ndipo nthawi zambili amakhala wofooka. Akakhalako na mphamvu, amacita ulaliki wa kunyumba ndi nyumba. Koma nthawi zambili amacita ulaliki wa m’makalata. Iye anati: “Pamene n’nazindikila kuti matenda anga sadzatha m’dongosolo lino la zinthu, n’nasumika maganizo anga onse pa nchito yolalikila. Ndipo nchito yolalikila imanithandiza kuti nisamangoganizila za mavuto anga. M’malomwake, nimaika maganizo anga pa kuthandiza anthu amene nimawalalikila m’gawo la mpingo wathu. Kuwonjezela apo, nchitoyi imanithandiza kuti nthawi zonse niziganizila za ciyembekezo cathu ca tsogolo labwino.”

YESU ANALANDILA THANDIZO KUCOKELA KWA MABWENZI AKE

Kugwilizana na mabwenzi abwino kumatithandiza kukhalabe na mtendele wamumtima (Onani ndime 11-15)

11-13. (a) Kodi atumwi ndi anthu ena anaonetsa bwanji kuti anali mabwenzi eni-eni a Yesu? (b) Kodi Yesu anamvela bwanji cifukwa ca thandizo limene mabwenzi ake anam’patsa?

11 Pa nthawi yonse imene Yesu anacita utumiki wake pano padziko lapansi, atumwi ake okhulupilika anacita zinthu zoonetsa kuti analidi mabwenzi ake eni-eni. Iwo anali mabwenzi abwino, monga mmene Baibo imakambila kuti: “Pali bwenzi limene limamatilila kuposa m’bale wako.” (Miy. 18:24) Yesu anali kuona mabwenzi otelewa kukhala ofunika kwambili. Pamene anali kucita utumiki wake padzikoli, panalibe ngakhale mmodzi wa abale ake a mimba imodzi amene anakhulupilila mwa iye. (Yoh. 7:3-5) Ndipo panthawi ina, abululu ake anafika poganiza kuti iye wacita misala. (Maliko 3:21) Koma mosiyana na zimenezi, atumwi anakhalabe okhulupilika kwa Yesu. Ndipo pa usiku wakuti maŵa adzaphedwa, iye anawauza kuti: “Inu mwakhalabe ndi ine m’mayeselo anga.”—Luka 22:28.

12 Nthawi zina, atumwi anali kucita zinthu zom’khumudwitsa Yesu. Koma iye sanali kuyang’ana kwambili pa zolakwa zawo. M’malomwake, anali kuyang’ana pa cikhulupililo cimene anali naco mwa iye. (Mat. 26:40; Maliko 10:13, 14; Yoh. 6:66-69) Usiku wakuti maŵa adzaphedwa, Yesu anauza atumwi ake okhulupilika kuti: “Ndakuchani mabwenzi, cifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.” (Yoh. 15:15) Mosakayikila, mabwenzi ake amenewa anamulimbikitsa kwambili. Ndipo cifukwa ca thandizo lawo pa nchito yolalikila, Yesu anakondwela kwambili.—Luka 10:17, 21.

13 Kuwonjezela pa atumwi, Yesu analinso na mabwenzi ena, amuna ndi akazi, amene anali kum’thandiza pa nchito yolalikila komanso m’njila zina. Ena anali kumuitanila ku nyumba zawo kuti akadye nawo cakudya. (Luka 10:38-42; Yoh. 12:1, 2) Ena anali kuyenda naye na kum’tumikila pogwilitsa nchito cuma cawo. (Luka 8:3) Yesu anali na mabwenzi abwino cifukwa nayenso anali bwenzi labwino. Iye anali kuwacitila zabwino, ndipo sanali kuyembekezela kuti iwo acite zinthu zimene sakanakwanitsa. Olo kuti Yesu anali wangwilo, anayamikila thandizo limene mabwenzi ake opanda ungwilo anali kum’patsa. Ndipo mosakayikila, iwo anam’thandiza kukhalabe na mtendele wamumtima.

14-15. Kodi tiyenela kucita ciani kuti tipeze mabwenzi abwino? Nanga mabwenzi otelo angatithandize bwanji?

14 Nafenso tikakhala na mabwenzi abwino, angatithandize kukhalabe okhulupilika kwa Yehova. Ndipo cofunika kwambili kuti tipeze mabwenzi abwino ni kuyamba ndife kukhala bwenzi labwino kwa ena. (Mat. 7:12) Mwacitsanzo, Baibo imatilimbikitsa kukhala odzipeleka pothandiza ena, maka-maka “osowa.” (Aef. 4:28) Kodi pali aliyense mumpingo mwanu amene muona kuti afunikila thandizo lanu? Kodi mungadzipeleke kuthandiza m’bale kapena mlongo amene sakwanitsa kuyenda cifukwa ca matenda kapena ukalamba mwa kukam’gulilako zinthu kumsika? Kodi mungapatseko cakudya banja limene likusoŵa ndalama zogulila cakudya? Nanga bwanji ngati mumadziŵa moseŵenzetsela webusaiti ya jw.org® kapena JW Library®? Kodi mungathandizeko ena mumpingo mwanu kudziŵa moseŵenzetsela zida zimenezi? Tikamayesetsa kuthandiza ena, tidzakhala na cimwemwe.—Mac. 20:35.

15 Mabwenzi athu amatithandiza tikakumana na mavuto, ndipo izi zimatithandiza kukhalabe na mtendele wamumtima. Iwo angatilimbikitse mwa kumvetsela moleza mtima pamene tifotokoza mavuto athu. Izi n’zimene Elihu anacita pamene Yobu anali kufotokoza mavuto ake. (Yobu 32:4) Komabe, sitiyenela kuyembekezela anzathu kutisankhila zocita. Ngakhale n’telo, tifunika kulabadila malangizo awo ocokela m’Baibo. (Miy. 15:22) Mofanana na Mfumu Davide, imene inadzicepetsa mwa kulandila thandizo locokela kwa mabwenzi ake, ifenso tifunika kuonetsa kudzicepetsa mwa kulandila thandizo limene mabwenzi athu angatipatse tikakumana na mavuto. (2 Sam. 17:27-29) Kukamba zoona, mabwenzi otelo ni mphatso yocokela kwa Yehova.—Yak. 1:17.

ZIMENE TINGACITE KUTI TIKHALEBE NA MTENDELE WAMUMTIMA

16. Malinga ndi Afilipi 4:6, 7, kodi tingapeze bwanji mtendele wamumtima? Fotokozani.

16 Ŵelengani Afilipi 4:6, 7. Yehova anakamba kuti tingalandile mtendele wamumtima wocokela kwa iye kupitila “mwa Khristu Yesu.” N’cifukwa ciani zili telo? Cifukwa cakuti tingakhale na mtendele wokhalitsa wamumtima ndi wam’maganizo, kokha ngati tikhulupilila mwa Yesu, komanso kumvetsetsa udindo umene ali nawo pokwanilitsa cifunilo ca Mulungu. Mwacitsanzo, kupitila mu nsembe ya dipo la Yesu, macimo athu onse amakhululukidwa. (1 Yoh. 2:12) Kodi si zolimbikitsa kwambili zimenezi? Cinanso, pokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzacotsapo mavuto onse amene Satana na dziko lake atibweletsela. (Yes. 65:17; 1 Yoh. 3:8; Chiv. 21:3, 4) Kodi si ciyembekezo cokondweletsa cimeneci? Komanso, olo kuti Yesu anatipatsa nchito yovuta, sanatisiye tekha. Amaticilikiza pamene tigwila nchitoyi m’masiku otsiliza ano ovuta. (Mat. 28:19, 20) Kuzindikila mfundo imeneyi kumatithandiza kukhala olimba mtima kwambili. Conco, zinthu zitatu izi—cilimbikitso, ciyembekezo, na kulimba mtima—ni zina mwa zinthu zofunika kwambili zimene zimatithandiza kukhala na mtendele wamumtima.

17. (a) Kodi Mkhristu angacite ciani kuti akhalebe na mtendele wamumtima? (b) Malinga n’zimene Yesu anakamba pa Yohane 16:33, kodi tidzakwanitsa kucita ciani tikakumana na mayeselo?

17 Malinga n’zimene takambilana, kodi mungacite ciani kuti mukhalebe na mtendele wamumtima pamene mukumana na mavuto aakulu? Muyenela kucita zimene Yesu anacita. Coyamba, limbikilani kupemphela. Caciŵili, mvelani Yehova komanso muzilalikila mokangalika, ngakhale pamene zili zovuta kutelo. Ndipo cacitatu, landilani thandizo locokela kwa mabwenzi anu, pamene mukumana na mavuto. Mukatelo, mtendele wa Mulungu udzateteza mitima yanu na maganizo anu. Ndipo mofanana ndi Yesu, mudzagonjetsa mayeselo aliwonse amene mungakumane nawo.—Ŵelengani Yohane 16:33.

NYIMBO 41 Mvelani Pemphelo Langa Conde

^ ndime 5 Tonsefe timakumana na mavuto amene angatilande mtendele wa mumtima. M’nkhani ino, tidzakambilana zinthu zitatu zimene Yesu anacita kuti akhalebe na mtendele wa mumtima. Ifenso ngati ticita zimenezo, tingathe kukhalabe na mtendele wa mumtima, ngakhale kuti timakumana na mavuto aakulu.