NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA April 2020

Magazini ino ili na nkhani zophunzila kuyambila pa June 1–July 5, 2020.

Kuukila kwa Mdani Wocokela Kumpoto!

Nkhani yophunzila 14: Wiki ya June 1-7, 2020. Kodi pali zifukwa zinayi ziti zomveka bwino zimene zionetsa kuti tifunika kusintha kamvedwe kathu ka ulosi wa m’macaputa 1 na 2 a buku la Yoweli?

Kodi Mumawaona Bwanji Anthu a mu Gawo Lanu?

Nkhani yophunzila 15: Wiki ya June 8-14, 2020. Onani mmene tingatsatilile citsanzo ca Yesu na mtumwi Paulo mwa kuganizila zikhulupililo za anthu amene timawalalikila, zinthu zimene amacita nazo cidwi, komanso kuwaona kuti angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu.

Amvetseleni, Adziŵeni Bwino, Aonetseni Cifundo

Nkhani yophunzila 16: Wiki ya June 15-21, 2020. Mwacikondi, Yehova anathandiza Yona, Eliya, Hagara, na Loti. Onani mmene tingatsatilile citsanzo ca Yehova pocita zinthu na ena.

“Nakuchani Mabwenzi”

Nkhani yophunzila 17: Wiki ya June 22-28, 2020. Kupanga ubwenzi na Yesu na kuulimbitsa kumakhala kovutilapo. Olo n’telo, n’zotheka kukhala naye pa ubwenzi.

“Nathamanga Panjilayo Mpaka pa Mapeto”

Nkhani yophunzila 18: Wiki ya June 29–July 5, 2020. Nciani cimene tonsefe tingacite kuti tipambane mpikisano wokalandila moyo, olo kuti tikuvutika na ukalamba kapena matenda ena ofooketsa thupi?