Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 16

Amvetseleni, Adziŵeni Bwino, Aonetseni Cifundo

Amvetseleni, Adziŵeni Bwino, Aonetseni Cifundo

“Lekani kuweluza poona maonekedwe akunja, koma muziweluza ndi ciweluzo colungama.”—YOH. 7:24.

NYIMBO 101 Tisunge Umodzi Wathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi Baibo imafotokoza mfundo yolimbikitsa iti ponena za Yehova?

KODI mungakondwele ngati anthu amakuweluzani potengela mtundu wa khungu lanu, maonekedwe a nkhope yanu, kapena potengela kuti ndinu woyonda kapena wonenepa? Mwacidziŵikile, simungakondwele. Conco, n’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti Yehova satiweluza potengela maonekedwe athu! Mwacitsanzo, pamene Samueli anaona ana a Jese, sanakwanitse kuona zimene Yehova anaona. Yehova anali atauza Samueli kuti mmodzi wa ana a Jese adzakhala mfumu ya Isiraeli. Koma kodi ni mwana uti ameneyo? Samueli ataona Eliyabu, mwana woyamba wa Jese, anati: “Mosakayikila wodzozedwa wake waonekela pamaso pa Yehova.” Eliyabu anali wocititsa kaso m’maonekedwe, moti Samueli anaganiza kuti ndiye asankhidwe kukhala mfumu. “Koma Yehova anauza Samueli kuti: ‘Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake, pakuti ine ndamukana ameneyu.’” Kodi tiphunzilapo ciani? Malinga n’zimene Yehova anakamba, tiphunzilapo kuti: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”—1 Sam. 16:1, 6, 7.

2. Malinga na Yohane 7:24, n’cifukwa ciani sitiyenela kuweluza munthu potengela maonekedwe ake? Fotokozani citsanzo.

2 Pokhala anthu opanda ungwilo, tonsefe tili na cizoloŵezi coweluza ena potengela maonekedwe awo. (Ŵelengani Yohane 7:24.) Koma vuto n’lakuti sitingadziŵe zambili za munthu poona cabe maonekedwe ake. Mwacitsanzo, ngakhale dokotala wanzelu kwambili komanso wodziŵa bwino nchito yake sangadziŵe zambili poona cabe mmene wodwala akuonekela. Amafunika kumvetsela mwachelu kuti adziŵe matenda amene munthuyo anadwalapo, mmene vuto lake likum’khudzila, kapena mmene akumvelela pa nthawiyo. Dokotalayo angafunenso kuti wodwalayo akamutenge ekiselo (X-ray) kuti adziŵe mmene m’thupi mwake mulili. Popanda kucita izi, angamupatse mankhwala olakwika. Nafenso n’cimodzi-modzi. Sitingawadziŵe bwino abale na alongo athu poona cabe maonekedwe awo. Tifunika kuyesetsa kudziŵa bwino umunthu wawo wamkati. Koma popeza sitidziŵa zamumtima, sitingadziŵe munthu monga mmene Yehova amamudziŵila. Ngakhale n’conco, tingacite zonse zotheka potengela citsanzo ca Yehova. Motani?

3. Kodi zitsanzo za m’Baibo zimene tikambilane m’nkhani ino zitithandiza bwanji kutengela citsanzo ca Yehova?

3 Kodi Yehova amacita nawo zinthu motani olambila ake? Amawamvetsela. Iye amaganizila mmene zinthu zilili mu umoyo wawo, komanso zimene anakumana nazo m’mbuyomu. Kuwonjezela apo, amawaonetsa cifundo. Tiyeni tsopano tikambilane mmene Yehova anacitila zimenezi kwa Yona, Eliya, Hagara, na Loti. Pokambilana zimenezi, onani mmene tingatsatilile citsanzo cake pocita zinthu na abale na alongo athu.

MUZIWAMVETSELA MWACHELU

4. N’cifukwa ciani tingaganize kuti Yona anali munthu wosadalilika kapena wosakhulupilika?

4 M’kaonedwe kathu kaumunthu, tingaganize kuti Yona anali munthu wosadalilika, kapenanso wosakhulupilika. Yehova anamupatsa lamulo lacindunji lakuti akalengeze uthenga waciweluzo ku Nineve. M’malo momvela lamulo limenelo, Yona anakwela combo copita ku dziko lina, “kuthawa Yehova.” (Yona 1:1-3) Kodi mukanakhala imwe sembe munam’patsanso mwayi wina womvela lamulo limeneli? Mwina ayi. Koma Yehova anaona kuti Yona anafunika kum’patsanso mwayi wina.—Yona 3:1, 2.

5. Kodi mwaphunzila ciani za Yona pa mawu ake olembedwa pa Yona 2:1, 2, 9?

5 Pemphelo limene Yona anapeleka limaonetsa bwino kuti anali munthu wotani. (Ŵelengani Yona 2:1, 2, 9.) Mosakayikila, Yona anapemphela kambili-mbili kwa Yehova. Koma pemphelo limene anapeleka ali m’mimba mwa cinsomba, limatithandiza kudziŵa kuti m’ceni-ceni iye anali munthu wabwino, olo kuti anathaŵa utumiki wake. Mawu amene anakamba m’pemphelolo aonetsa kuti anali wodzicepetsa, woyamikila, komanso wofunitsitsa kumvela Yehova. Mpake kuti Yehova sanayang’ane kwambili pa zolakwa zake, koma anayankha pemphelo lake na kupitiliza kum’seŵenzetsa monga mneneli.

Kumvetsetsa mmene zinthu zilili, kudzatithandiza kumvelela ena cifundo kwambili (Onani ndime 6) *

6. N’cifukwa ciani tifunika kumvetsela mwachelu?

6 Kuti timvetsele mwachelu kwa ena, tifunika kukhala odzicepetsa komanso oleza mtima. Kucita zimenezi n’kofunika pa zifukwa zitatu. Coyamba, tidzapewa kuweluza ena molakwika. Caciŵili, tidzakwanitsa kudziŵa mmene m’bale wathu akumvelela komanso zolinga zake, ndipo izi zidzatilimbikitsa kucita naye zinthu mwacifundo kwambili. Cacitatu, tikapatsa mpata m’bale wathu kuti afotokoze za mumtima mwake, tingamuthandize kudzidziŵa bwino. Zili conco cifukwa nthawi zina anthufe sitidziŵa cimene cikutivutitsa mumtima mpaka titafotokozelako ena mmene tikumvelela. (Miy. 20:5) Mkulu wina ku Asia anati: “Nikumbukila kuti tsiku lina n’nafulumila kukamba nisanamvetsetse mmene zinthu zinalili. N’napatsa uphungu mlongo wina kuti afunika kumakamba ndemanga zogwila mtima pamisonkhano. Pambuyo pake, n’namvela kuti mlongoyo amaŵelenga movutikila, ndipo amafunika kuyesetsa kwambili kuti akwanitse kupelekako ndemanga.” Ndithudi, n’kofunika kwambili kuti akulu ‘azimvetsetsa’ mmene zinthu zilili asanapeleke uphungu.—Miy. 18:13.

7. Tiphunzilapo ciani tikaganizila mmene Yehova anacitila zinthu na Eliya?

7 Abale na alongo athu ena zimawavuta kufotokoza mmene akumvelela cifukwa ca mmene anakulila, cikhalidwe cawo, kapena cifukwa ca cibadwa cawo. Kodi tingawathandize bwanji kukhala omasuka? Kumbukilani mmene Yehova anacitila zinthu na Eliya pamene anali kuthaŵa Yezebeli. Panatenga masiku ambili kuti Eliya amasuke kufotokozela Atate wake wakumwamba mmene anali kumvelela. Yehova anamumvetsela mwachelu. Kenako anamulimbikitsa na kum’patsa nchito yofunika kwambili. (1 Maf. 19:1-18) Pangatenge nthawi yaitali kuti abale na alongo athu ayambe kutidalila moti n’kukamba nafe momasuka. Koma akamasuka, m’pamene tingadziŵe bwino mmene akumvelela. Ngati tikhala oleza mtima monga Yehova, iwo angayambe kutidalila. Ndipo akafuna kutifotokozela za mumtima mwawo, tiyenela kumvetsela mwachelu.

ADZIŴENI BWINO ABALE NA ALONGO ANU

8. Malinga na Genesis 16:7-13, kodi Yehova anam’thandiza bwanji Hagara?

8 Hagara, mdzakazi wa Sarai, anacita zinthu mopanda nzelu pamene anakhala mkazi wa Abulamu. Hagara atakhala na pakati, anayamba kupeputsa Sarai, amene panthawiyo analibe mwana. Ubale wa Sarai na Hagara unasokonezeka, ndipo zinthu zinafika poipa moti Hagara anathaŵa panyumbapo. (Gen. 16:4-6) M’kaonedwe kathu kaumunthu, tingaganize kuti Hagara anali mkazi wonyada, wofunikadi kulangidwa. Koma Yehova sanamuone mwanjila imeneyi. Iye anatumiza mngelo wake kwa Hagara. Atam’peza, anamuthandiza kuti asinthe khalidwe lake, komanso anam’dalitsa. Hagara anazindikila kuti Yehova anali kumuyang’anila, ndiponso kuti anali kudziŵa bwino mmene zinthu zinalili mu umoyo wake. Iye anakhudzika kwambili na zimenezi, cakuti anafika pokamba kuti Yehova ni “Mulungu amene amaona ciliconse.”—Ŵelengani Genesis 16:7-13.

9. N’cifukwa ciani Mulungu anacita zinthu mokoma mtima na Hagara?

9 Kodi n’ciani cimene Yehova anaona mwa Hagara? Iye anali kudziŵa bwino za umoyo wake, kuphatikizapo mavuto onse amene anapitamo. (Miy. 15:3) Hagara anali Mwiguputo, ndipo anali kukhala pa nyumba ya Abulamu, Mheberi. Conco, n’kutheka kuti anali kudziona ngati mlendo wosafunikila. N’kuthekanso kuti anali kuyewa kwawo komanso abululu ŵake. Kuwonjezela apo, iye sanali mkazi yekhayo wa Abulamu. Zinali conco cifukwa pa nthawi inayake kumbuyoko, anthu ena okhulupilika anali kukwatila akazi angapo. Koma izi sizinali zogwilizana na cifunilo ca Yehova ca poyamba. (Mat. 19:4-6) Telo n’zosadabwitsa kuti cipali cinali kubweletsa mavuto aakulu m’banja, monga nsanje na cidani. Yehova anadziŵa kuti zimene Hagara anacita, zopeputsa Sarai, zinali zolakwika. Ngakhale n’telo, iye anacita zinthu mokoma mtima na Hagara cifukwa anadziŵa bwino mmene anali kumvelela, komanso mmene zinthu zinalili pa umoyo wake.

Yesetsani kuwadziŵa bwino abale na alongo anu (Onani ndime 10-12) *

10. Tingacite ciani kuti tiwadziŵe bwino abale na alongo athu?

10 Tingatengele citsanzo ca Yehova mwa kuyesetsa kuwamvetsetsa abale na alongo athu. Adziŵeni bwino abale na alongo anu. Muzicezako nawo misonkhano ikalibe kuyamba komanso ikatha, muziyenda nawo mu ulaliki, ndipo ngati n’zotheka mungawaitanileko ku cakudya. Mukatelo, mungazindikile kuti mlongo uja amene mumamuona ngati si waubwenzi, kweni-kweni ni wamanyazi cabe, ndipo m’bale wa ndalama zambili uja si wokonda cuma, koma kweni-kweni ni wowoloŵa manja. Kapenanso mungazindikile kuti banja limene limakonda kubwela mocedwa ku misonkhano likukumana na citsutso. (Yobu 6:29) N’zoona kuti sitiyenela ‘kulowelela nkhani za eni.’ (1 Tim. 5:13) Komabe, ni bwino kuwadziŵa bwino abale na alongo athu, komanso kudziŵa zimene akukumana nazo. Tikatelo, tidzatha kuwamvetsetsa.

11. N’cifukwa ciani akulu afunika kuzidziŵa bwino nkhosa?

11 Akulu maka-maka afunika kudziŵa bwino abale na alongo awo mu mpingo. Ganizilani citsanzo ca m’bale wina, dzina lake Artur, amene anali woyang’anila dela. Iye na mkulu wina anapita kukacezela mlongo amene anali kuoneka wamanyazi komanso wosamasuka. Artur anati: “Mlongoyo anatiuza kuti mwamuna wake anamwalila pasanapite nthawi yaitali kucokela pamene anakwatilana. Olo kuti anali kukumana na mavuto, anakwanitsa kuphunzitsa ana ake aŵili coonadi mpaka kukhala Akhristu olimba mwauzimu. Pamene tinapita kukakamba naye n’kuti maso ake ayamba kufa, ndiponso anali kudwala matenda ovutika maganizo. Ngakhale n’telo, cikondi cake pa Yehova na cikhulupililo cake mwa iye zinali zolimba. Tinazindikila kuti panali zambili zofunika kuphunzila pa citsanzo cabwino ca mlongoyo.” (Afil. 2:3) Woyang’anila dela ameneyu anatengela citsanzo ca Yehova. Yehova amadziŵa bwino nkhosa zake. Amadziŵanso mavuto amene zikupitamo. (Eks. 3:7) Akulu amene amadziŵa bwino nkhosa, amakwanitsa kuzisamalila bwino.

12. Kodi mlongo Yip Yee anapindula bwanji cifukwa coyesetsa kudziŵa bwino mlongo wina wa mumpingo mwawo?

12 Mukayesetsa kum’dziŵa bwino m’bale kapena mlongo amene zocita zake sizikukondweletsani, mudzakwanitsa kumumvetsetsa. Ganizilani citsanzo ici: Mlongo Yip Yee, wa ku Asia anati: “Mlongo wina mu mpingo mwathu anali kukonda kulankhula mokweza mawu kwambili. N’nali kumuona ngati wopanda ulemu. Koma titaseŵenzelako pamodzi muulaliki, ananiuza kuti kale anali kuthandiza amayi ake kugulitsa nsomba kumsika. Kumeneko, anali kulankhula mokweza poitanila makasitoma.” Yip Yee anakambanso kuti: “N’naphunzilapo kuti nifunika kuwadziŵa bwino abale na alongo kuti niziwamvetsetsa.” Pamafunika khama kuti tiwadziŵe bwino abale athu. Ndipo tikayesetsa kufutukula mtima wathu potsatila malangizo a m’Baibo, ndiye kuti tikutengela Yehova amene amakonda “anthu, kaya akhale a mtundu wotani.”—1 Tim. 2:3, 4; 2 Akor. 6:11-13.

AONETSENI CIFUNDO

13. Malinga na Genesis 19:15, 16, n’ciani cimene angelo anacita pamene Loti anali kuzengeleza? Ndipo n’cifukwa ciani?

13 Pa nthawi yovuta kwambili mu umoyo wake, Loti anazengeleza kutsatila malangizo a Yehova. Angelo aŵili anabwela kwa iye na kumuuza kuti atuluke mu Sodomu pamodzi na banja lake. N’cifukwa ciani anamuuza kuti atuluke? Angelowo anati: “Malo ano tiwawononga.” (Gen. 19:12, 13) Pofika m’maŵa tsiku lotsatila, Loti na banja lake anali asanacoke mu Sodomu. Angelo aja anamucenjezanso Loti kaciŵili. Koma “iye anali kuzengeleza.” Mwina tingaone kuti Loti anali munthu wonyalanyaza, kapena wosamvela kumene. Koma Yehova sanaleke kum’thandiza. “Mwa cifundo ca Yehova pa iye,” angelowo anacita kugwila dzanja Loti, mkazi wake, ndi ana ake aŵili, n’kuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda.—Ŵelengani Genesis 19:15, 16.

14. Kodi n’kutheka kuti Yehova anacitila cifundo Loti pa zifukwa ziti?

14 Payenela kukhala zifukwa zingapo zimene zinapangitsa Yehova kum’citila cifundo Loti. Mwina iye anali kuzengeleza kucoka mu Sodomu cifukwa coopa anthu okhala kunja kwa mzindawo. Palinso zina zimene ziyenela kuti zinali kum’detsa nkhawa. Mwacionekele, Loti anamvapo za mafumu aŵili amene anagwela m’maenje aphula, m’cigwa capafupi na mzindawo. (Gen. 14:8-12) Popeza anali na mkazi komanso ana, ayenela kuti anadela nkhawa banja lake. Kuwonjezela apo, iye anali wolemela. Conco, n’kutheka kuti anali na nyumba yabwino mu Sodomu. (Gen. 13:5, 6) Koma zonsezi sizinali zifukwa zomveka zopangitsa Loti kuzengeleza kulabadila mwamsanga cenjezo la Yehova. Ngakhale n’conco, Yehova sanayang’ane kwambili pa colakwa ca Loti, koma anamuona kuti anali “munthu wolungama.”—2 Pet. 2:7, 8.

Ngati timvetsela ena akamakamba nafe, tingadziŵe mmene tingawaonetsele cifundo (Onani ndime 15-16) *

15. M’malo moweluza munthu pa zimene wacita, kodi tiyenela kucita ciani?

15 M’malo mofulumila kuweluza munthu pa zimene wacita, yesetsani kumvetsetsa mmene akumvelela. Izi n’zimene mlongo Veronica wa ku Europe anacita. Iye anati: “Mlongo wina nthawi zonse anali kukhala wosakondwela. Anali kukonda kukhala payekha. Nthawi zina, n’nali kuyopa kukamba naye. Koma mumtima n’nati, ‘Kodi nikanakhala ine, sembe nimvela bwanji? Sembe nilaka-laka kukhala na bwenzi.’ Cotelo, n’naganiza zomufunsa mmene anali kumvelela. Ndipo iye anamasuka kunifotokozela za mumtima mwake. Tsopano nimamudziŵa bwino kwambili.”

16. N’cifukwa ciani tiyenela kupemphela kwa Yehova kuti atithandize kukhala na mtima womvelela ena cifundo?

16 Yehova yekha ndiye amatimvetsetsa mokwanila. (Miy. 15:11) Conco, mupempheni kuti akuthandizeni kuona abale na alongo anu mmene iye amawaonela, ndiponso kudziŵa mmene mungaonetsele cifundo kwa iwo. Pemphelo linathandiza mlongo wina dzina lake Anzhela kukhala womvelela ena cifundo kwambili. Mumpingo mwawo munali mlongo wina wovuta kugwilizana naye. Anzhela anati: “Cinali capafupi kungomuuza mosapita m’mbali kuti ni wovuta, na kuleka kugwilizana naye. Koma n’napempha Yehova kuti anithandize kumudziŵa bwino.” Kodi Yehova anayankha pemphelo lake? Anzhela anati: “Tsiku lina, tinayendela limodzi mu ulaliki, ndipo pambuyo pake tinaceza kwa maawazi angapo. N’nali kumumvetsela mokoma mtima. Lomba nimam’konda kwambili, ndipo niziyesetsa kum’limbikitsa.”

17. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciani?

17 Simuyenela kucita kusankha abale na alongo ofunika kuwaonetsa cifundo cacikulu. Mofanana na Yona, Eliya, Hagara, na Loti, abale athu onse amakumana na mavuto. Nthawi zina, mavutowo amakhala odzibweletsela okha. Koma kukamba zoona, tonsefe tinakumanapo na mavuto odzibweletsela tekha. Telo m’pomveka kuti Yehova amatilangiza kuti tizimvelelana cifundo. (1 Pet. 3:8) Ngati timvela Yehova, timalimbitsa mgwilizano wocititsa cidwi wa banja lathu la padziko lonse, lokhala ndi anthu a mitundu yosiyana-siyana. Conco, pocita zinthu na abale na alongo athu, tiyeni tiziyesetsa kuwamvetsela, kuwadziŵa bwino, na kuwaonetsa cifundo.

NYIMBO 87 Bwelani Mutsitsimulidwe!

^ ndime 5 Ife anthu opanda ungwilo, timathamangila kuweluza ena na kukayikila zolinga zawo. Koma Yehova “amaona mmene mtima ulili.” (1 Sam. 16:7) M’nkhani ino, tikambilana mmene iye anaonetsela cikondi pothandiza Yona, Eliya, Hagara, komanso Loti. Nkhaniyi itithandiza kudziŵa mmene tingatsatilile citsanzo ca Yehova pocita zinthu na abale na alongo athu.

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wacikulile wakhumudwa na m’bale wacinyamata amene wabwela mocedwa ku misonkhano. Koma pambuyo pake wamvela kuti m’baleyo anacedwa cifukwa anapezeka m’ngozi.

^ ndime 54 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Poyamba, woyang’anila kagulu anali kuona kuti mlongo wina m’kagulu kake ni wamisulo komanso wosafuna kugwilizana na ena. Koma pambuyo pake anazindikila kuti mlongoyo ni wamanyazi cabe, ndipo samasuka akakhala ndi anthu osawadziŵa bwino.

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene mlongo anaona mlongo wina ku Nyumba ya Ufumu, anaganiza kuti ni wosaganizila ena komanso wokwiya-kwiya. Koma atapatula nthawi yoceza naye kuti amudziŵe bwino, anazindikila kuti mlongoyo ni wabwino-bwino.