Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 15

Kodi Mumawaona Bwanji Anthu a mu Gawo Lanu?

Kodi Mumawaona Bwanji Anthu a mu Gawo Lanu?

“Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola.”—YOH. 4:35.

NYIMBO 64 Timasangalala Kuthandizila pa Nchito Yokolola

ZIMENE TIKAMBILANE *

1-2. Kodi Yesu anatanthauza ciani pamene anakamba mawu a pa Yohane 4:35, 36?

TSIKU lina, Yesu anali kuyenda kudutsa m’minda. Ndipo mwacidziŵikile minda imeneyo inali ya balele womela kumene. (Yoh. 4:3-6) Kunali kutatsala miyezi pafupi-fupi inayi kuti baleleyo ace. Conco, ophunzila ake ayenela kuti anadabwa pamene Yesu anawauza kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Ŵelengani Yohane 4:35, 36.) Kodi iye anatanthauza ciani?

2 N’zoonekelatu kuti apa Yesu anali kukamba za kusonkhanitsa anthu osati mbewu. Ganizilani zimene zinacitika iye asanakambe zimenezi. Yesu anali atangolalikila mayi wacisamariya, olo kuti Ayuda sanali kugwilizana na Asamariya. Mayiyo anamvetsela. Pamene Yesu anali kukamba kuti m’minda “mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola,” gulu la Asamariya amene anamva za iye kwa mkazi wacisamariya uja linali m’njila kubwela kwa Yesu kuti lidzaphunzile zambili. (Yoh. 4:9, 39-42) Ponena za cocitika cimeneci, buku lina lofotokoza Baibo linati: “Cifukwa cofunitsitsa kumvetsela uthenga wa Yesu, anthuwo . . . anali monga mbewu zakuca, zofunika kukolola.”

Kodi tiyenela kucita ciani ngati taona kuti m’minda yathu “mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola”? (Onani ndime 3)

3. Kodi kuona anthu mmene Yesu anali kuwaonela kudzakuthandizani bwanji pa ulaliki wanu?

3 Nanga bwanji inu? Kodi anthu amene mumawalalikila uthenga wabwino mumawaona bwanji? Kodi mumawaona monga mbewu zakuca zofunika kukolola? Kuona anthu mwa njila imeneyi, kudzakuthandizani m’njila zitatu. Coyamba, kudzakulimbikitsani kulalikila mwacangu. Nthawi yokolola ni yocepa. Motelo, tifunika kuigwilitsila nchito mwanzelu. Caciŵili, mudzakondwela poona kuti anthu akulabadila uthenga wabwino. Baibo imakamba kuti ‘anthu amasangalala pa nthawi yokolola.’ (Yes. 9:3) Ndipo cacitatu, mudzayamba kuona kuti munthu aliyense amene mwakumana naye angasinthe n’kukhala wophunzila wa Yesu. Conco, mudzayesetsa kusintha ulaliki wanu kuti ugwilizane na zimene amakonda.

4. Kodi m’nkhani ino tiphunzila ciani kwa Mtumwi Paulo?

4 N’kutheka kuti ophunzila ena a Yesu anali kuona kuti Asamariya sangakhale ophunzila ake. Koma iye sanali kuwaona mwanjila imeneyi. Anali kuwaona kuti angasinthe n’kukhala ophunzila ake. Nafenso tiyenela kuona anthu a m’gawo lathu kuti angasinthe n’kukhala ophunzila a Khristu. Mtumwi Paulo ni citsanzo cabwino cimene tiyenela kutengela. Kodi tingaphunzile ciani kwa iye? M’nkhani ino, tiphunzila (1) mmene iye anadziŵila zikhulupililo za anthu amene anali kuwalalikila, (2) mmene anadziŵila zinthu zimene zikanawacititsa cidwi, komanso (3) mmene anaonetsela kuti anali kuwaona kuti angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu.

KODI AMAKHULUPILILA ZOTANI?

5. N’cifukwa ciani Paulo anali kuwadziŵa bwino anthu amene anali kuwalalikila m’sunagoge?

5 Nthawi zambili, Paulo anali kulalikila m’masunagoge a Ayuda. Mwacitsanzo, m’sunagoge wa ku Tesalonika, Paulo “kwa masabata atatu anakambilana [na Ayuda] mfundo za m’Malemba.” (Mac. 17:1, 2) Mwacionekele, iye anali kukhala womasuka kulalikila m’sunagoge. Paulo anali Myuda. (Mac. 26:4, 5) Ndipo anali kuwadziŵa bwino Ayuda, moti anakwanitsa kuwalalikila mopanda mantha.—Afil. 3:4, 5.

6. Kodi anthu amene Paulo anali kuwalalikila pamsika wa ku Atene anasiyana bwanji ndi a ku sunagoge?

6 Paulo atathamangitsidwa ndi anthu otsutsa ku Tesalonika komanso ku Bereya, anakafika ku Atene. Ali kumeneko, anayambanso “kukambilana ndi Ayuda ndi anthu ena opembedza Mulungu” m’sunagoge. (Mac. 17:17) Koma pamene Paulo anali kulalikila pamsika, omvetsela ake anali osiyana ndi a ku sunagoge. Panali akatswili a nzelu za anthu, komanso anthu ena amene sanali Ayuda. Anthuwo anali kuona uthenga wa Paulo monga “ciphunzitso catsopano.” Iwo anamuuza kuti: “Zimene ukufotokozazi ndi zinthu zacilendo m’makutu mwathu.”—Mac. 17:18-20.

7. Malinga na Machitidwe 17:22, 23, kodi Paulo anasintha bwanji kalalikidwe kake?

7 Ŵelengani Machitidwe 17:22, 23. Polalikila kwa anthu a ku Atene amene sanali Ayuda, Paulo sanakambe nawo mofanana ndi mmene anakambila kwa Ayuda m’sunagoge. N’zoonekelatu kuti iye anadzifunsa kuti, ‘Kodi anthu a ku Atene amenewa amakhulupilila ciani? Iye anali kuyang’ana mosamala zinthu za kumeneko, ndiponso kuyesetsa kudziŵa miyambo yawo ya cipembedzo. Kenako, iye anaganizila mfundo za coonadi ca m’Baibo zimene anthuwo akanatha kuzikhulupilila mosavuta. Katswili wina wa Baibo anati: “Pokhala Mkhristu waciyuda, Paulo anali kudziŵa kuti Agiriki acikunja sanali kulambila Mulungu ‘woona’ wa Ayuda komanso Akhristu. Olo n’telo, Paulo anayesetsa kuwathandiza kuona kuti iye anali kulalikila za Mulungu amene m’ceni-ceni sanali wacilendo kwa Atene.” Motelo, Paulo anasintha ulaliki wake. Anauza anthu a ku Atene kuti uthenga wake ni wocokela kwa “Mulungu Wosadziwika,” amene iwo anali kumulambila. Ngakhale kuti anthu amenewo sanali kudziŵa Malemba, Paulo anali kuwaonabe kuti angasinthe n’kukhala Akhristu. Anali kuwaona monga mbewu zakuca zofunika kukolola, ndipo anasintha kalalikidwe kake ka uthenga wabwino.

Potengela citsanzo ca mtumwi Paulo, muzikhala chelu, muzisintha ulaliki wanu, ndiponso muziona kuti anthu angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu (Onani ndime 8, 12, 18) *

8. (a) Kodi mungadziŵe bwanji zimene anthu m’gawo lanu amakhulupilila? (b) Kodi mungakambe ciani ngati munthu wakuuzani kuti ali na cipembedzo cake?

8 Mofanana na Paulo, muzikhala chelu. Muziyang’ana na kuganizila mosamala zinthu zimene zingakuthandizeni kudziŵa zomwe anthu a m’gawo lanu amakhulupilila. Kodi mwininyumba anaikongoletsa bwanji nyumba yake? Kodi dzina lake, kavalidwe na kudzikonza kwake, kapena mmene amakambila zionetsa kuti ni wacipembedzo citi? Mwina iye angakuuzeni mwacindunji kuti ali na cipembedzo cake. Mpainiya wapadela wina, dzina lake Flutura, akauzidwa zimenezi amakamba kuti: “Colinga canga sikukukakamizani kuti muyambe kukhulupilila zimene ine nimakhulupilila. Koma nabwela kuti tikambilane za . . . ”

9. Pokambilana na munthu amene ali na cipembedzo cake, kodi mwina mungagwilizane naye pa mfundo ziti?

9 Kodi mungakambilane nkhani zotani na munthu amene ali na cipembedzo cake? Yesani kupeza mfundo zimene mungagwilizane naye. N’kutheka kuti nayenso amalambila Mulungu mmodzi cabe, kapena amakhulupilila kuti Yesu ni Mpulumutsi wa anthu. Kapenanso mwina munthuyo amakhulupilila kuti tikukhala m’masiku otsiliza ndipo zoipa zidzatha posacedwa. Mukapeza mfundo imene nayenso amaikhulupilila, kambilanani naye uthenga wa m’Baibo wogwilizana na mfundoyo m’njila imene ingam’kope cidwi.

10. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

10 Dziŵani kuti anthu ena sakhulupilila zonse zimene amaphunzila ku cipembedzo cawo. Conco, ngakhale pambuyo pozindikila cipembedzo ca munthu, yesetsani kufufuza kuti mudziŵe zimene iye mwini amakhulupilila. Mpainiya wapadela wina ku Australia, dzina lake David anati: “Masiku ano, anthu ambili amaphatikiza ziphunzitso za anthu na zimene amaphunzila ku cipembedzo cawo.” Mlongo wina ku Albania, dzina lake Donalta anati: “Anthu ena amene timawalalikila amakamba kuti ali na cipembedzo, koma pakapita nthawi amavomeleza kuti m’ceni-ceni sakhulupilila kuti kuli Mulungu.” Ndipo m’bale wina ku Argentina, amene ni mmishonale anakamba kuti anthu ena amene amanena kuti amakhulupilila Utatu, angakhale kuti sakhulupililadi zakuti Atate, Mwana, komanso mzimu woyela ni Mulungu mmodzi. Iye anakambanso kuti: “Kudziŵa kuti anthu ena sakhulupilila zonse zimene cipembedzo cawo cimaphunzitsa, kumanithandiza kupeza mosavuta mfundo zimene ningawilizane nawo.” Conco, yesetsani kufufuza kuti mudziŵe zeni-zeni zimene anthu amakhulupilila. Mukatelo, ndiye kuti mofanana na Paulo mungakhale “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.”—1 Akor. 9:19-23.

KODI AMACITA CIDWI NA ZINTHU ZITI?

11. Malinga na Machitidwe 14:14-17, kodi Paulo analalikila bwanji uthenga wake mokopa kwa anthu a ku Lusitara?

11 Ŵelengani Machitidwe 14:14-17. Paulo anali kuganizila zinthu zimene zikanacititsa cidwi omvetsela ake. Ndiyeno, anali kusintha ulaliki wake. Mwacitsanzo, khamu la anthu limene anakamba nalo ku Lusitara linali kudziŵako pang’ono cabe Malemba, kapena silinali kuwadziŵa n’komwe. Conco, Paulo anakamba nawo mfundo zimene akanazimvetsetsa. Anakamba za kuculuka kwa zokolola komanso mwayi wosangalala na moyo. Ndipo anaseŵenzetsa mawu na zitsanzo zimene iwo akanazimvetsetsa mosavuta.

12. Kodi mungadziŵe bwanji zimene munthu angacite nazo cidwi? Nanga mungasinthe bwanji ulaliki wanu kuti ugwilizane na zimene amakonda?

12 Seŵenzetsani luso la kuzindikila kuti mudziŵe nkhani zimene anthu a m’gawo lanu angacite nazo cidwi, ndiyeno sinthani ulaliki wanu kuti ugwilizane na zimene amakonda. Kodi mungadziŵe bwanji zimene munthu angacite nazo cidwi mukamufikila kuti mumulalikile kapena mukafika pakhomo pake? Monga takambila, khalani chelu. Mwacitsanzo, mwina mungam’peze akulima, kuŵelenga buku, kukonza njinga kapena motoka, kapenanso kucita zinthu zina. Ngati m’poyenela, mungaloŵele ku zimene iye akucita kuti muyambe kukambilana naye. (Yoh. 4:7) Ngakhale zovala zimene munthu wavala zingatithandize kudziŵa zinazake zokhudza munthuyo, monga dziko lake, nchito imene amagwila, kapena timu ya maseŵela imene amakonda. M’bale wina dzina lake Gustavo anati: “N’nayamba kukambilana na mnyamata wina wa zaka 19, amene anavala tisheti yokhala na cithunzi ca woimba winawake wochuka. N’namufunsa za cithunzico, ndipo iye ananiuza cifukwa cake anali kumukonda woimbayo. Zimene tinakambilanazo zinapangitsa kuti niyambe kuphunzila naye Baibo. Ndipo pano tikamba, iye ni mmodzi wa abale athu.”

13. Mungakambe bwanji m’njila yokopa cidwi popempha munthu kuti muziphunzila naye Baibo?

13 Popempha munthu kuti muziphunzila naye Baibo, kambani naye m’njila yakuti aone kuti kuphunzila Baibo ni kwabwino. M’thandizeni kuona mmene adzapindulila akayamba kuphunzila Baibo. (Yoh. 4:13-15) Mwacitsanzo, tsiku lina pamene mlongo wina dzina lake Poppy anali mu ulaliki, mayi wina wacidwi anamupempha kuti aloŵe m’nyumba yake. Ali m’nyumbamo, mlongoyo anaona satifiketi kucipupa yoonetsa kuti mayiyo ni pulofesa wa za maphunzilo. Conco, pokambilana naye, mlongoyo anagogomeza mfundo yakuti nafenso timaphunzitsa anthu kupitila m’pulogilamu ya phunzilo la Baibo komanso misonkhano. Mayiyo anavomela kuphunzila Baibo. Ndipo tsiku lotsatila, anapezeka pa msonkhano wa mpingo. Patapita nthawi yocepa, anapezekanso pa msonkhano wadela. Pambuyo pa caka cimodzi, anabatizika. Ndiye dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu amene nimacitako maulendo obwelelako amacita cidwi na zinthu zotani? Kodi ningawafotokozele bwanji za phunzilo la Baibo m’njila yokopa cidwi?’

14. Kodi mungagwilizanitse bwanji phunzilo la Baibo na wophunzila aliyense?

14 Mukayamba kuphunzila Baibo na munthu, konzekelani bwino phunzilo lililonse palokha. Ganizilani za umoyo wa wophunzilayo na wa banja lake, komanso zimene amacita nazo cidwi. Pamene mukonzekela, onani malemba amene mudzaŵelenga, mavidiyo amene mudzamutambitsa na zitsanzo zimene mudzakamba pofotokoza mfundo za coonadi ca m’Baibo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi n’ciani maka-maka cingamukope cidwi wophunzilayu na kumufika pa mtima?’ (Miy. 16:23) Ku Albania, mayi wina amene anali kuphunzila na mlongo wina dzina lake Flora anakamba motsimikiza kuti: “Siningakhulupilile zakuti akufa adzauka.” Mlongo Flora sanamukakamize mayiyo kukhulupilila ciphunzitso cimeneci. Iye anati: “N’nazindikila kuti coyamba afunika kudziŵa bwino Mulungu amene analonjeza za kuuka kwa akufa.” Kuyambila nthawiyo, pa phunzilo lililonse mlongo Flora anali kugogomeza za cikondi ca Yehova, nzelu, komanso mphamvu zake. Patapita nthawi, wophunzilayo anayamba kukhulupilila zakuti akufa adzauka. Lomba iye ni Mboni ya Yehova yokangalika.

MUZIWAONA KUTI ANGASITHE N’KUKHALA OPHUNZILA A YESU

15. Malinga na Machitidwe 17:16-18, ni makhalidwe ati a anthu a ku Atene amene sanam’kondweletse Paulo? Nanga n’cifukwa ciani iye sanaleke kuwalalikila?

15 Ŵelengani Machitidwe 17:16-18. Paulo sanaleke kulalikila anthu a ku Atene olo kuti ambili mu mzindawo anali kupembedza mafano, kucita zaciwelewele, na kukhulupilila nzelu za anthu. Komanso iye sanaleke kuwalalikila ngakhale kuti anali kumunyoza. Paja nayenso Paulo asanakhale Mkhristu anali “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wacipongwe.” (1 Tim. 1:13) Yesu anaona kuti Paulo angasinthe n’kukhala wophunzila wake. Mofananamo, Paulo nayenso anali kukhulupilila kuti anthu a ku Atene angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu. Ndipo izi n’zimenedi ena mwa iwo anacita.—Mac. 9:13-15; 17:34.

16-17. N’ciani cionetsa kuti anthu a mtundu uliwonse angakhale ophunzila a Khristu? Fotokozani citsanzo.

16 M’nthawi ya atumwi, anthu a mitundu yosiyana-siyana anasintha n’kukhala ophunzila a Yesu. Mwacitsanzo, pamene Paulo analembela kalata Akhristu a mu mzinda wa Korinto ku Girisi, anakamba kuti ena mumpingowo asanakhale Akhristu, anali zigaŵenga ndiponso anali na makhalidwe otayilila. Kenako anati: “Ena mwa inu munali otelo. Koma mwasambitsidwa kukhala oyela.” (1 Akor. 6:9-11) Mukanakhala imwe, kodi sembe muona kuti anthuwo angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu?

17 Masiku ano, anthu ambili akusintha makhalidwe awo n’colinga cakuti akhale ophunzila a Yesu. Mwacitsanzo, ku Australia, mpainiya wapadela wina dzina lake Yukina anadzionela yekha kuti zoonadi anthu a mtundu uliwonse angalabadile uthenga wa m’Baibo. Tsiku lina anaona mtsikana pa malo ena ake ocitila bizinesi. Mtsikanayo anali na zidindo pa khungu pake, ndiponso anavala vovala vacintemwende (vikulu-vikulu). Iye anati: “Poyamba n’nadodoma, koma pambuyo pake n’nayamba kumulalikila. N’nazindikila kuti anali na cidwi kwambili na uthenga wa m’Baibo, cakuti zina mwa zidindo za pa khungu lake zinali mavesi a m’buku la Masalimo!” Mtsikanayo anayamba kuphunzila Baibo komanso kupezeka pa misonkhano. *

18. N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kuweluza anthu?

18 Yesu anakamba kuti m’mindamo mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola. Kodi anakamba izi poganiza kuti anthu ambili adzamutsatila? Iyai. Malemba anali atakambilatu kuti ni anthu ocepa cabe amene adzamukhulupilila. (Yoh. 12:37, 38) Komanso, Yesu anali kukwanitsa kudziŵa za mumtima mwa munthu. Conco, anali kudziŵa kuti ambili sadzalabadila uthenga wake. (Mat. 9:4) Ngakhale kuti iye anaika kwambili maganizo ake pa anthu ocepa amene anamukhulupilila, analalikilabe mokangalika kwa anthu onse. Mosiyana na Yesu, ife sitikwanitsa kudziŵa zimene zili m’mitima ya anthu. Cotelo, tiyenela kupewelatu kuweluza anthu a m’gawo lathu kapena munthu aliyense. M’malomwake, tiyenela kuona kuti anthu angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu. Mmishonale wina ku Burkina Faso, dzina lake Marc anati: “Anthu amene nimaona kuti angapite patsogolo, nthawi zambili amaleka kuphunzila Baibo. Koma amene nimaganiza kuti sangapite patsogolo ni amene amapita patsogolo kwambili. Motelo, naphunzilapo kuti ni bwino kulola mzimu wa Yehova kutitsogolela.”

19. Kodi tiyenela kuwaona bwanji anthu a m’gawo lathu?

19 Poyamba, tingaganize kuti m’gawo lathu mulibe anthu ambili acidwi, amene ali ngati mbewu zakuca zofunika kukolola. Koma kumbukilani zimene Yesu anauza ophunzila ake. Iye anati m’mindamo mwayela kale, kutanthauza kuti ni mofunika kukolola. Anthu angasinthe n’kukhala ophunzila a Khristu. Yehova amaona anthu amenewa monga “zinthu zamtengo wapatali.” (Hag. 2:7) Ngati na ise timaona anthu mmene Yehova na Yesu amawaonela, tidzayetsetsa kuwadziŵa bwino, komanso kudziŵa zimene amacita nazo cidwi. Sitidzawaona ngati alendo, koma tidzawaona monga abale na alongo athu am’tsogolo.

NYIMBO 57 Tilalikile kwa Anthu a Makhalidwe Onse

^ ndime 5 Kodi mmene timaonela anthu a m’gawo lathu zimakhudza bwanji mmene timagwilila nchito yathu yolalikila na kuphunzitsa? M’nkhani ino, tikambilana mmene Yesu na mtumwi Paulo anali kuonela anthu amene anali kumvetsela uthenga wawo. Tikambilananso mmene tingatsatilile citsanzo cawo mwa kuganizila zimene anthu a m’gawo lathu amakhulupilila na zimene amakonda, komanso mwa kuwaona kuti angasinthe na kukhala ophunzila a Yesu.

^ ndime 17 M’nkhani zakuti “Baibo Imasintha Anthu,” muli zitsanzo zambili zoonetsa mmene anthu amasinthila umoyo wawo. Nkhanizi zinali kupezeka mu Nsanja ya Mlonda, koma zinaleka kutuluka m’magazini mu 2017. Lomba zimafalitsidwa pa jw.org®. Onani ku Chichewa pa ZOKHUDZA IFEYO > ZOCHITIKA PA MOYO WA A MBONI ZA YEHOVA.

^ ndime 57 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pamene m’bale na mkazi wake alalikila ku nyumba na nyumba, aona (1) pa nyumba posamalidwa bwino komanso pokongoletsedwa na maluŵa; (2) pa nyumba pamene pali ana aang’ono; (3) pa nyumba posasamalidwa bwino kunja na mkati momwe; komanso (4) pa nyumba ya anthu opembedza. Kodi ni pa nyumba iti pamene muona kuti mungapeze munthu amene angakhale wophunzila wa Yesu mosavuta?