Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 17

“Nakuchani Mabwenzi”

“Nakuchani Mabwenzi”

“Ndakuchani mabwenzi, cifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.”YOH. 15:15.

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi mumacita ciani kuti mupange ubwenzi wolimba na munthu wina?

NTHAWI zambili, cinthu coyamba cimene munthu amacita kuti apange ubwenzi wolimba na munthu wina ni kupatula nthawi yoceza naye. Akamaceza, kufotokozelana za mumtima, komanso zimene akumana nazo pa umoyo, amapanga ubwenzi. Koma kupanga ubwenzi wolimba na Yesu kungakhale kovutilapo. Cifukwa ciani?

2. Kodi coyamba cimene cimapangitsa kuti kukhala pa ubwenzi na Yesu kukhale kovutilapo n’citi?

2 Coyamba cimene cimapangitsa kuti kukhala pa ubwenzi na Yesu kukhale kovutilapo n’cakuti Yesu sitinamuonepo. Akhristu ambili m’nthawi ya atumwi, nawonso sanamuonepo Yesu. Olo zinali telo, mtumwi Petulo anati: “Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupilila mwa iye.” (1 Pet. 1:8) Cotelo, n’zotheka kupanga ubwenzi wolimba na Yesu ngakhale kuti sitinamuonepo.

3. Kodi caciŵili cimene cingapangitse kuti kukhala pa ubwenzi na Yesu kukhale kovutilapo n’citi?

3 Copinga caciŵili n’cakuti sitikwanitsa kukamba na Yesu. Pamene tipemphela, timangokamba na Yehova. N’zoona kuti timapemphela kupitila m’dzina la Yesu, koma sitikamba naye. Ndipo Yesu safuna kuti tizipemphela kwa iye. Cifukwa ciani? Cifukwa pemphelo ni mbali ya kulambila, ndipo Yehova yekha ndiye woyenela kumulambila. (Mat. 4:10) Ngakhale n’conco, n’zotheka ndithu kuonetsa kuti timam’konda Yesu.

4. Kodi copinga cacitatu n’citi? Nanga tikambilana ciani m’nkhani ino?

4 Copinga cacitatu n’cakuti Yesu amakhala kumwamba. Motelo, tilibe mwayi wokhala naye pamodzi. Ngakhale n’telo, n’zotheka kudziŵa zambili za Yesu. M’nkhani ino, tikambilana zinthu zinayi zimene tingacite kuti tipange ubwenzi na Yesu na kupitiliza kuulimbitsa. Koma coyamba, tiyeni tione cifukwa cake kupanga ubwenzi wolimba na Khristu n’kofunika kwambili.

N’CIFUKWA CIANI TIFUNIKA KUKHALA PA UBWENZI NA YESU?

5. N’cifukwa ciani tifunika kukhala mabwenzi a Yesu? (Onaninso bokosi lakuti “ Kukhala pa Ubwenzi na Yesu Kumatithandiza Kukhala pa Ubwenzi na Yehova,” komanso yakuti “ Kuona Udindo wa Yesu Moyenela.”)

5 Tifunika kukhala pa ubwenzi na Yesu kuti tikhale pa ubale wabwino na Yehova. N’cifukwa ciani takamba conco? Onani zifukwa ziŵili izi: Coyamba, Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Atateyo amakukondani, cifukwa munandikonda ine.” (Yoh. 16:27) Anakambanso kuti: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.” (Yoh. 14:6) Kuyesa kukhala bwenzi la Yehova popanda kupanga ubwenzi wolimba na Yesu kuli ngati kufuna kuloŵa m’nyumba osadzela pakhomo. Yesu anakamba mfundo yofanana na imeneyi pamene anati, “ine ndine khomo la nkhosa.” (Yoh. 10:7) Cifukwa caciŵili n’cakuti, Yesu anatengela bwino kwambili makhalidwe a Atate wake. Iye anauza ophunzila ake kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Conco, njila imodzi yofunika kwambili imene timadziŵila Yehova ni kuphunzila za umoyo wa Yesu. Pamene tiphunzila za Yesu, timayamba kum’konda kwambili. Ndipo tikayamba kum’konda kwambili, m’pamenenso timakonda kwambili Atate wake.

6. N’cifukwa cina citi cimene tiyenela kukhalila mabwenzi a Yesu? Fotokozani.

6 Tifunika kukhala pa ubwenzi na Yesu kuti mapemphelo athu ayankhidwe. Izi sizitanthauza kungokamba mwamwambo cabe mawu akuti “m’dzina la Yesu,” kumapeto kwa pemphelo. Tifunika kudziŵa mmene Yehova amaseŵenzetsela Yesu poyankha mapemphelo athu. Yesu anauza atumwi kuti: “Ciliconse cimene mudzapemphe m’dzina langa, ine ndidzacicita.” (Yoh. 14:13) N’zoona kuti Yehova ndiye amamvetsela na kuyankha mapemphelo athu. Koma anapatsa mphamvu Yesu yocita zimene Yehovayo walamula. (Mat. 28:18) Conco, Mulungu asanayankhe mapemphelo athu, amaona ngati ife timatsatila malangizo amene Yesu anatipatsa. Mwacitsanzo, Yesu anati: “Mukamakhululukila anthu macimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukilani. Koma ngati simukhululukila anthu macimo awo, Atate wanu sadzakukhululukilani macimo anu.” (Mat. 6:14, 15) Ndithudi, n’kofunika kwambili kuti tizicitila ena zinthu mokoma mtima monga mmene Yehova na Yesu amacitila na ife!

7. Ndani adzapindula na dipo la Yesu?

7 Anthu okhawo amene ali pa ubwenzi wolimba na Yesu ndiwo adzapindula na nsembe yake ya dipo. Tidziŵa bwanji zimenezi? Yesu anakamba kuti adzapeleka “moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake.” (Yoh. 15:13) Atumiki a Yehova okhulupilika amene anakhalako Yesu asanabwele padziko lapansi, adzafunika kuphunzila za iye kuti ayambe kum’konda. Amuna na akazi monga Sara, Abulahamu, Mose, komanso Rahabi adzaukitsidwa. Koma nawonso adzafunika kupanga ubwenzi na Yesu kuti akakhale na moyo wosatha.—Yoh. 17:3; Mac. 24:15; Aheb. 11:8-12, 24-26, 31.

8-9. Malinga na Yohane 15:4, 5, kodi kukhala mabwenzi a Yesu kumatipatsa mwayi wotani? Nanga n’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika?

8 Timakondwela kuseŵenzela pamodzi na Yesu pa nchito yophunzitsa na kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anali kugwila nchito yophunzitsa. Kungocokela pamene anabwelela kumwamba, iye monga mutu wa mpingo akupitiliza kutsogolela pa nchito yolalikila na kuphunzitsa. Yesu amaona na kuyamikila zonse zimene mumacita pothandiza anthu ambili mmene mungathele, kuti amudziŵe iye komanso kuti adziŵe Atate wake. Ndipo tingakwanitse kugwila nchitoyi kokha mothandizidwa na Yehova komanso Yesu.—Ŵelengani Yohane 15:4, 5.

9 Mawu a Mulungu amakamba momveka bwino kuti tifunika kukonda Yesu nthawi zonse kuti tikondweletse Yehova. Tiyeni lomba tikambilane zinthu zinayi zimene tingacite kuti tikhale mabwenzi a Yesu.

ZIMENE TINGACITE KUTI TIKHALE MABWENZI A YESU

Tingakhale pa ubwenzi na Yesu mwa (1) kumudziŵa bwino, (2) kuganiza na kucita zinthu monga iye, (3) kuthandiza abale ake, komanso (4) kucilikiza makonzedwe a gulu la Yehova (Onani ndime 10-14) *

10. Kodi coyamba cimene tiyenela kucita kuti tipange ubwenzi na Yesu n’ciani?

10 (1) Tifunika kum’dziŵa bwino Yesu. Kuti tim’dziŵe bwino Yesu, tiyenela kuŵelenga mabuku a m’Baibo a Mateyu, Maliko, Luka, na Yohane. Pamene tisinkha-sinkha nkhani za m’Baibo zokamba za umoyo wa Yesu, timayamba kum’konda na kum’lemekeza cifukwa ca mmene anali kucitila zinthu mokoma mtima ndi anthu. Mwacitsanzo, olo kuti anali Mbuye, ophunzila ake sanali kucita nawo zinthu monga akapolo. M’malomwake, anali kuwafotokozela maganizo ake na mmene anali kumvelela. (Yoh. 15:15) Iwo akakhala na cisoni, nayenso anali kumvela cisoni, ndiponso anali kulila nawo limodzi. (Yoh. 11:32-36) Ngakhale anthu otsutsa, anavomeleza kuti Yesu anali bwenzi la anthu amene analabadila uthenga wake. (Mat. 11:19) Ngati titengela citsanzo ca Yesu ca mmene anali kucitila zinthu na ophunzila ake, ubwenzi wathu na ena udzalimba. Tidzakhala acimwemwe, ndipo tidzayamba kum’konda kwambili Yesu na kum’lemekeza.

11. N’ciani caciŵili cimene tingacite kuti tikhale mabwenzi a Yesu? Nanga n’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika?

11 (2) Tiziganiza na kucita zinthu monga Yesu. Tikadziŵa bwino maganizo a Yesu na kutengela kaganizidwe kake, ubwenzi wathu na iye udzalimba kwambili. (1 Akor. 2:16) Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu? Onani mfundo iyi: Yesu anali kuganizila kwambili za mmene angathandizile ena m’malo modzikondweletsa iye mwini. (Mat. 20:28; Aroma 15:1-3) Cifukwa cokhala na maganizo amenewa, iye anali wodzimana komanso wa mtima wokhululuka. Sanali kukwiya msanga ena akam’nena. (Yoh. 1:46, 47) Ndipo sanali kuona munthu molakwika cifukwa cokumbukila zolakwa zimene anacita m’mbuyomo. (1 Tim. 1:12-14) Kuona anthu mmene Yesu anali kuwaonela n’kofunika cifukwa iye anati: “Mwakutelo, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Conco, dzifunseni kuti, “Kodi nimatengela citsanzo ca Yesu mwa kucita zonse zimene ningathe kuti nikhalebe pa mtendele na abale na alongo anga?”

12. Kodi cacitatu cimene tingacite kuti tikhale mabwenzi a Yesu n’ciani? Nanga tingacite bwanji zimenezo?

12 (3) Tizithandiza abale a Khristu. Yesu amaona kuti tikamacitila zabwino abale ake odzozedwa, ndiye kuti tikucitila iyeyo. (Mat. 25:34-40) Njila imodzi yaikulu imene timathandizila odzozedwa ni mwa kutengako mbali mokwanila pa nchito yolalikila za Ufumu na kuphunzitsa, imene Yesu analamula otsatila ake kuti azicita. (Mat. 28:19, 20; Mac. 10:42) Popanda thandizo la Akhristu a “nkhosa zina,” abale a Khristu sangakwanitse kugwila nchito yaikulu yolalikila imene ikucitika padziko lonse masiku ano. (Yoh. 10:16) Motelo, ngati ndimwe wa nkhosa zina, dziŵani kuti nthawi iliyonse imene mugwila nchitoyi, mumaonetsa kuti mumakonda odzozedwa komanso Yesu.

13. Kodi tingatsatile bwanji malangizo a Yesu a pa Luka 16:9?

13 Cina cimene tingacite kuti tikhale mabwenzi a Yehova na Yesu ni kupanga zopeleka zocilikizila nchito imene iwo akuitsogolela. (Ŵelengani Luka 16:9.) Mwacitsanzo, tingapange zopeleka zocilikizila nchito ya padziko lonse. Zopelekazi zimathandiza pa nchito zosiyana-siyana monga yolalikila uthenga wabwino ku madela akutali, kumanga na kukonzanso Nyumba za Ufumu na malo ena olambilila, komanso kuthandiza anthu okhudzidwa pakacitika ngozi zacilengedwe kapena matsoka ena. Tingapangenso zopeleka zothandizila pa mpingo wathu. Komanso, tingathandize anthu amene tidziŵa kuti ni osoŵa. (Miy. 19:17) Izi ndizo njila zimene tingathandizile abale a Khristu.

14. Malinga na Aefeso 4:15, 16, n’ciani cacinayi cimene tingacite kuti tikhale mabwenzi a Yesu?

14 (4) Tizicilikiza makonzedwe a gulu la Yehova. Timalimbitsa ubwenzi wathu na Yesu, mutu wa mpingo, mwa kucita zinthu mogwilizana na amuna amene anaikidwa kuti azititsogolela mwacikondi. (Ŵelengani Aefeso 4:15, 16.) Mwacitsanzo, tsopano tikucita zonse zotheka kuti Nyumba za Ufumu zonse zizigwilitsidwa nchito mokwanila. Pa cifukwa ici, mipingo ina anaiphatikiza pamodzi, ndipo magawo anasinthidwa. Izi zathandiza kupulumutsa ndalama zambili za gulu. Koma zacititsanso kuti ofalitsa ena asamukile ku mipingo ina. N’kutheka kuti ofalitsa okhulupilika amenewa anatumikila mu mpingo wawo kwa zaka zambili, ndipo anapanga ubwenzi wathithithi na abale na alongo mu mpingowo. Koma tsopano auzidwa kuti asamukile ku mpingo wina. Kukamba zoona, Yesu amakondwela kwambili akaona Akhristu okhulupilikawa akugonjela makonzedwe amenewa.

MUNGAKHALE BWENZI LA YESU KWAMUYAYA

15. Kodi ubwenzi wathu na Yesu udzakhala bwanji kutsogolo?

15 Akhristu odzozedwa na mzimu woyela ali na ciyembekezo cokakhala na Yesu kwamuyaya, komanso kukatumikila naye pamodzi mu Ufumu wa Mulungu. Iwo azikakhaladi naye Khristu, azikamuona, komanso kukambilana naye. (Yoh. 14:2, 3) Nawonso Akhristu amene ali na ciyembekezo codzakhala pa dziko lapansi, Yesu adzawasamalila mwacikondi. Olo kuti iwo sazikamuona Yesu, ubwenzi wawo na iye udzapitiliza kulimba, pamene akusangalala na moyo umene Yehova adzawapatsa kupitila mwa Yesu.—Yes. 9:6, 7.

16. Kodi kukhala mabwenzi a Yesu kuli na mapindu anji?

16 Yesu akutipempha kuti tikhale mabwenzi ake. Tikakhala mabwenzi ake, timapeza madalitso ambili. Mwacitsanzo, monga mabwenzi ake, iye amatikonda na kuticilikiza. Tili na mwayi wodzakhala na moyo wamuyaya. Koposa zonse, kukhala pa ubwenzi na Yesu kumatipatsa mwayi wamtengo wapatali kwambili, wokhala bwenzi la Atate wake, Yehova. Ndithudi, ni mwayi kukhala bwenzi la Yesu!

NYIMBO 17 ‘Nifuna’

^ ndime 5 Kwa zaka zingapo, atumwi anali na mwayi woceza na Yesu komanso kuseŵenza naye. Ndipo anakhala naye pa ubwenzi wabwino. Yesu amafuna kuti nafenso tikhale mabwenzi ake. Komabe, si copepuka kwa ife kukhala naye pa ubwenzi monga mmene zinalili kwa atumwi. M’nkhani ino, tikambilana zinthu zina zimene zimapangitsa kuti kucita izi kusakhale kopepuka. Tikambilananso zimene tingacite kuti tipange ubwenzi wolimba na iye, komanso kuti tipitilize kukhala mabwenzi ake.

^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: (1) Pa kulambila kwa pabanja, tingaŵelenge za umoyo wa Yesu na utumiki wake. (2) Mumpingo, tiyenela kuyesetsa kucitapo kanthu kuti tikhale pa mtendele na abale athu. (3) Tingathandize abale a Khristu mwa kutengako mbali mokwanila pa nchito yolalikila. (4) Akulu akapanga ciganizo cakuti aphatikize pamodzi mipingo, tifunika kugonjela.