Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 18

“Nathamanga Panjilayo Mpaka pa Mapeto”

“Nathamanga Panjilayo Mpaka pa Mapeto”

“Ndathamanga panjilayo mpaka pa mapeto pake.”—2 TIM. 4:7.

NYIMBO 129 Tidzapilila Mosalekeza

ZIMENE TIKAMBILANE *

1. Kodi tonsefe tiyenela kucita ciani?

KODI mungakonde kuthamanga pa mpikisano wovuta, pamene mudziŵa kuti ndimwe wodwala kapena wolema? Mwacionekele simungakonde. Ngakhale n’conco, mtumwi Paulo anakamba kuti Akhristu onse oona ali pa mpikisano wothamanga. (Aheb. 12:1) Ndipo tonse, kaya ndife acicepele kapena acikulile, amphamvu kapena ofooka, tifunika kuthamanga mopilila mpaka ku mapeto kuti tikalandile mphoto imene Yehova anatilonjeza.—Mat. 24:13.

2. Malinga na 2 Timoteyo 4:7, 8, n’cifukwa ciani Paulo anali na ufulu wolankhula?

2 Pa nkhani yothamanga pa mpikisano, Paulo anali na ufulu wolankhula cifukwa ‘anathamanga panjilayo mpaka pa mapeto pake.’ (Ŵelengani 2 Timoteyo 4:7, 8.) Koma kodi mpikisano wothamanga umene Paulo anakamba ni wotani maka-maka?

KODI TIKUTHAMANGA PA MPIKISANO WOTANI?

3. Kodi mpikisano wothamanga umene Paulo anakamba ni wotani?

3 Nthawi zina, Paulo pophunzitsa Akhristu mfundo zofunika, anali kufotokoza zinthu zimene zinali kucitika pa maseŵela ku Girisi wakale. (1 Akor. 9:25-27; 2 Tim. 2:5) Kangapo konse, iye anayelekezela umoyo wacikhristu na mpikisano wothamanga. (1 Akor. 9:24; Agal. 2:2; Afil. 2:16) Munthu amayamba kuthamanga pa ‘mpikisanowu’ akadzipatulila kwa Yehova na kubatizika. (1 Pet. 3:21) Ndipo Yehova akam’patsa mphoto ya moyo wosatha, ndiye kuti wafika pa mzele wotsiliza.—Mat. 25:31-34, 46; 2 Tim. 4:8.

4. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

4 Kodi pali kufanana kotani pakati pa kucita mpikisano wothamanga msenga wautali na kukhala umoyo wacikhristu? Pali mbali zambili zofanana. Koma tiyeni tikambilaneko mbali zitatu. Coyamba, tifunika kuthamanga pa njila yoyenela; caciŵili, tifunika kusumika maganizo athu pa mzele wotsiliza; ndipo cacitatu, tifunika kuthamanga mopilila ngakhale pamene tikukumana na mavuto.

THAMANGANI PA NJILA YOYENELA

Tonse tifunika kupitiliza kuthamanga pa njila yopita kumoyo (Onani ndime 5-7) *

5. Kodi tiyenela kuthamanga pa njila iti? Nanga n’cifukwa ciani?

5 Kuti munthu wothamanga pa mpikisano weni-weni alandile mphoto, amafunika kuthamanga pa njila imene okonza mpikisano akhazikitsa. Mofananamo, kuti tikalandile mphoto ya moyo wosatha, tifunika kuyenda pa njila ya coonadi. (Mac. 20:24; 1 Pet. 2:21) Komabe, Satana na otsatila ake amafuna kuti tileke kuyenda pa njila imeneyi. Amafuna kuti tipitilize “kuthamanga nawo limodzi m’cithaphwi ca makhalidwe oipa.” (1 Pet. 4:4) Iwo amatinyodola cifukwa coyenda pa njila ya coonadi. Amakamba kuti njila imene iwo akuyendamo ndiyo yabwino, yopatsa ufulu. Koma limenelo ni bodza.—2 Pet. 2:19.

6. Kodi mwaphunzilapo ciani pa citsanzo ca Brian?

6 Anthu amene asankha kuyenda m’njila imene anthu a m’dzikoli amayendamo, posapita nthawi amazindikila kuti njila imene asankha sikuwathandiza kukhala na ufulu, koma ikuwacititsa kukhala akapolo. (Aroma 6:16) Ganizilani za Brian. Makolo ake anamuphunzitsa kuyenda m’njila ya coonadi. Koma iye atafika pa msinkhu waunyamata, anayamba kuona ngati kuti kutumikila Mulungu kunali kum’manitsa mwayi wosangalala. Conco anaganiza zoyamba kuthamanga pamodzi ndi anthu a m’dzikoli, amene amatsatila mfundo za Satana. Brian anati: “Sin’nazindikile kuti zinthu zimene n’nali kuona ngati ndiye ufulu zidzaniloŵetsa mu ukapolo wa zilakolako zoipa. M’kupita kwa nthawi, n’nayamba kuseŵenzetsa amkolabongo, kumwa moŵa mwaucidakwa, komanso kucita zaciwelewele. Ndipo m’kupita kwa zaka, n’nayamba kuseŵenzetsa amkolabongo amphamvu kwambili, cakuti n’nakhala kapolo wa zinthu zimenezo. . . . N’nayambanso kugulitsa amkolabongowo kuti nizipeza ndalama zonithandiza pa zocita zangazo.” Koma patapita nthawi, Brian anayamba kucita zinthu mogwilizana na miyezo ya Yehova. Iye anatembenuka n’kuyamba kuyenda m’njila yabwino, moti mu 2001 anabatizika. Tsopano Brian ali na cimwemwe ceni-ceni cifukwa akuyenda pa njila ya coonadi. *

7. Malinga na Mateyu 7:13, 14, kodi pali njila ziŵili ziti zimene tingayendemo pa mpikisano wathu wothamanga?

7 Apa tingaone kuti kusankha njila yoyenela n’kofunika kwambili. Satana amafuna kuti tonse ticoke pa njila yopapatiza ‘yoloŵela ku moyo,’ n’kuyamba kuthamanga m’njila yaikulu ndi yotakasuka imene anthu ambili m’dzikoli akuthamangamo. Anthu ambili amaona kuti njila imeneyi ndiyo yabwino komanso yosavuta kuyendamo. Koma m’ceni-ceni, njilayi ni yopita “kuciwonongeko.” (Ŵelengani Mateyu 7:13, 14.) Kuti tisapatuke pa njila yoyenela, tifunika kudalila Yehova na kumumvela.

YANG’ANANIBE PA MPHOTO, PEWANI KUDZIPUNTHWITSA KAPENA KUPUNTHWITSA ENA

Tifunika kuyang’anabe pa mphoto na kupewa kupunthwitsa ena (Onani ndime 8-12) *

8. Kodi munthu wothamanga pa mpikisano amacita ciani akagwa?

8 Munthu amene ali pa mpikisano wothamanga msenga wautali, amayang’ana patsogolo kuti asapunthwe n’kugwa. Komabe, nthawi zina anzake othamanga naye angamupunthwitse, kapena iyemwini angaponde m’dzenje n’kugwa. Koma olo agwe, amauka n’kupitiliza kuthamanga. Saganizila kwambili za cimene camugwetsa. Mtima wake wonse umakhala pa kuyesetsa kuti akafike pa mzele wothela. Komanso amaika maganizo ake onse pa mphoto imene akuyembekezela kukalandila.

9. Kodi tiyenela kucita ciani tikapunthwa?

9 Pamene tili pa mpikisano wathu wothamanga, tingapunthwe nthawi zambili. Tingalakwitse m’zokamba kapena m’zocita zathu. Mwinanso anzathu othamanga nawo angacite zinthu zina zimene zingatikhumudwitse. Zaconco zikacitika, sitiyenela kudabwa. Paja tonse ndise opanda ungwilo, ndipo tikuthamanga pa njila imodzi yopapatiza yopita ku moyo. Conco kukwesana kapena kukolana miyendo n’kosapeweka. Paulo anakamba kuti nthawi zina tingacite zinthu zimene zingapangitse wina kukhala na “cifukwa codandaulila” za ife. (Akol. 3:13) Koma m’malo mwakuti tizingoganizila zimene zatikhumudwitsazo, tingacite bwino kupitiliza kuyang’ana pa mphoto imene ili patsogolo pathu. Tikapunthwa n’kugwa, tiyenela kuukilila n’kupitiliza kuthamanga. Koma tikakhumudwa n’kuleka kutumikila Yehova, sitingakafike pa mzele wotsiliza, ndiponso sitingakalandile mphoto. Kuwonjezela apo, tingakhale copinga kwa ena amene akuyesetsa kuthamanga pa njila yopapatiza yopita ku moyo.

10. Tingapewe bwanji kukhala “copunthwitsa” kwa ena?

10 Njila ina imene tingapewele kukhala “copunthwitsa” kwa anzathu othamanga nawo pa mpikisanowu, ni mwa kukhala ololela ngati m’poyenela, m’malo mongoumilila maganizo athu. (Aroma 14:13, 19-21; 1 Akor. 8:9, 13) Pambali imeneyi, timasiyana ndi anthu othamanga pa mpikisano weni-weni. Iwo amapikisana na othamanga anzawo, ndipo aliyense amayesetsa kuthamanga mwamphamvu n’colinga cakuti akalandile mphoto ni iyeyo. Othamangawo amangoganizila za iwo okha basi, moti ena amacita kukankha anzawo kuti akhale patsogolo ndiwo. Koma ife sitipikisana na Akhristu anzathu. (Agal. 5:26; 6:4) M’malomwake, colinga cathu ni kuthandiza anthu ambili mmene tingathele, kuti tonse tikwanitse kuthamanga mpaka kukafika pa mzele wotsiliza na kukalandila mphoto ya moyo. Motelo, timayesetsa kutsatila malangizo ouzilidwa a Paulo akuti, “musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.”—Afil. 2:4.

11. Kodi ocita mpikisano wothamanga amaganizila kwambili za ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

11 Kuwonjezela pa kuyang’ana patsogolo, ocita mpikisano wothamanga weni-weni amaganizila kwambili za kufika pa mzele wotsiliza. Olo kuti mzelewo sauona, amayelekezela m’maganizo mwawo kuti afika pa mzelewo ndipo akulandila mphoto. Kuganizila kwambili za mphotoyo kumawalimbikitsa kupitiliza kuthamanga mwamphamvu.

12. Kodi Yehova mokoma mtima anatilonjeza ciani?

12 Pampikisano wathu wothamanga, mokoma mtima Yehova analonjeza kuti ngati tithamanga mopilila mpaka ku mapeto, adzatipatsa mphoto ya moyo wosatha, kaya kumwamba kapena m’paradaiso pano padziko lapansi. Mphoto imeneyi ni yotsimikizilika. Baibo imafotokoza mmene moyo umenewo udzakhalila, n’colinga cakuti tizitha kuganizila mmene tidzasangalalila panthawiyo. Ngati tipitiliza kuganizila pa mphoto imene Yehova anatilonjeza, sitidzalola ciliconse kutipunthwitsa.

PITILIZANI KUTHAMANGA OLO MUKUMANE NA MAVUTO

Tiyenela kupitiliza kuthamanga pa mpikisano wopita ku moyo olo tikukumana na mavuto (Onani ndime 13-20) *

13. Kodi ife tili na mwayi wotani umene anthu ocita mpikisano wothamanga weni-weni alibe?

13 Ocita mpikisano wothamanga ku Girisi anali kulimbana na zopinga, monga kulema komanso kuphweteka kwa thupi. Kuti zinthu ziwayendele bwino, anali kungodalila mphamvu zawo na mapulakatisi amene anali kucita. Mofanana na ocita mpikisano wothamanga amenewo, nafenso timaphunzitsidwa mmene tingathamangile pa mpikisano wathu wokalandila moyo. Koma ife tili na mwayi umene ocita mpikisano wothamanga weni-weni alibe. Tingapeze mphamvu kucokela kwa Yehova, gwelo la mphamvu zopanda malile. Yehova analonjeza kuti ngati tim’dalila, adzatiphunzitsa na kutipatsa mphamvu.—1 Pet. 5:10.

14. Kodi lemba la 2 Akorinto 12:9, 10 lingatithandize bwanji tikakumana na mavuto?

14 Paulo anakumana na mavuto ambili. Anthu ena anali kumunyoza na kum’zunza, ndipo nthawi zina anali kukhala wofooka. Kuwonjezela apo, anali kuvutika na “munga m’thupi.” (2 Akor. 12:7) Iye sanaone mavutowo monga cifukwa colekela kutumikila Yehova. Koma anawaona monga mpata woonetsela kuti anali kudalila Yehova. (Ŵelengani 2 Akorinto 12:9, 10.) Ndipo cifukwa coona zinthu mwa njila imeneyi, Yehova anamuthandiza kupilila mavuto ake onse.

15. Tikatengela citsanzo ca Paulo, kodi tidzakhala na mwayi wotani?

15 Nafenso anthu ena angatinyoze kapena kutizunza cifukwa ca cikhulupililo cathu. N’kuthekanso kuti tikudwala kapena timakhala wolema kwambili. Ngati titengela citsanzo ca Paulo, tingakhale na mwayi wothandizidwa mwacikondi na Yehova.

16. Kodi mungakwanitse kucita ciani ngakhale kuti mwina muli na thanzi lofooka?

16 Kodi ndimwe wodwala kwambili kapena wolemala moti simukwanitsa kuyenda? Kodi mumamvela miyendo kuphwanya kapena muli na vuto la kusaona bwino? Ngati n’conco, kodi mungakwanitse kuthamanga pamodzi na acinyamata athanzi? Inde, mungakwanitse! Okalamba ambili komanso odwala akuthamanga pa njila yopita ku moyo. Iwo sakwanitsa kucita izi mwa mphamvu zawo cabe. Koma amapeza mphamvu kwa Yehova mwa kumvetsela misonkhano yacikhristu yojambulidwa, kulumikiza misonkhano pa foni, kapena kucita daunilodi misonkhano pa JW streaming. Ndipo amagwila nchito yopanga ophunzila mwa kulalikila madokotala, manesi, komanso acibululu.

17. Kodi Yehova amawaona bwanji anthu a thanzi lofooka?

17 Ngati simukwanitsa kucita zonse zimene mumafuna potumikila Yehova, musataye mtima n’kuyamba kuganiza kuti simungathe kuthamanga pa njila yopita ku moyo. Yehova amakukondani cifukwa cakuti mumam’khulupilila, ndiponso cifukwa ca zonse zimene mwakhala mukucita pomutumikila. Lomba m’pamene mufunika kwambili thandizo lake, ndipo iye sadzakusiyani. (Sal. 9:10) Koma adzakuyandikilani kwambili. Onani zimene mlongo wina amene amadwala-dwala anakamba. Anati: “Cifukwa codwala-dwala, nthawi zambili sinikhala na mwayi wouzako ena coonadi. Koma nimadziŵa kuti zocepa zimene nimacita zimam’kondweletsa Yehova, ndipo kudziŵa zimenezi kumanipatsa cimwemwe.” Mukalefuka cifukwa ca mavuto, muzikumbukila kuti simuli mwekha. Muzikumbukila citsanzo ca mtumwi Paulo, komanso mawu olimbikitsa amene anakamba akuti: “Ndimasangalala ndi kufooka, . . . Pakuti pamene ndili wofooka, m’pamene ndimakhala wamphamvu.”—2 Akor. 12:10.

18. Kodi ena amene akuthamanga pa njila yopita ku moyo amakumana na vuto lalikulu liti?

18 Pali vuto lina limene anthu ena othamanga pa njila yopita ku moyo amakumana nalo. Amalimbana na zovuta zimene anthu ena sangazione kapena kuzimvetsetsa. Mwacitsanzo, ena ali na matenda ovutika maganizo kapena amakhala na nkhawa yopambanitsa. Koma kodi n’cifukwa ciani vuto limeneli limakhala losautsa kwambili kwa atumiki a Yehova amenewa? Cabwino, ganizilani izi: Ngati munthu wathyoka dzanja kapena mwendo, aliyense amaona vutolo, ndipo angadzipeleke kum’thandiza. Koma ngati munthu ali na matenda a maganizo kapena nkhawa yopambanitsa, nthawi zina amaoneka monga alibe vuto lililonse. Olo n’telo, vuto lawo limakhaladi leni-leni monga la munthu wothyoka dzanja kapena mwendo. Koma popeza ena saliona vutolo, sangawathandize kapena kuwaonetsa cikondi cimene afunikila.

19. Kodi tiphunzilapo ciani pa citsanzo ca Mefiboseti?

19 Ngati muona kuti anthu ena samvetsetsa vuto limene muli nalo, mungalimbikitsidwe na citsanzo ca Mefiboseti. (2 Sam. 4:4) Iye anali wolemala, ndiponso Mfumu Davide anamukayikila moti anamucitila zinthu mopanda cilungamo. Mefiboseti sanalakwe ciliconse kuti akumane na mavuto amenewa. Ngakhale n’conco, iye sanakhumudwe na zimenezi. Koma anayamikila zabwino zimene zinamucitikila pa umoyo. Anayamikilanso zabwino zimene Davide anamucitila kumbuyoko. (2 Sam. 9:6-10) Conco, pamene Davide anamuweluza mopanda cilungamo, Mefiboseti sanasumike maganizo ake pa zinthu zopanda cilungamo zimenezo. Sanalole zinthu zimenezo kum’khumudwitsa. Komanso sanaimbe mlandu Yehova cifukwa ca zimene Davide anacita. Koma anaganizila kwambili zimene akanacita pocilikiza Davide, mfumu yoikidwa na Yehova. (2 Sam. 16:1-4; 19:24-30) Yehova anaonetsetsa kuti citsanzo cabwino ca Mefiboseti calembedwa m’Baibo kuti ife tiphunzilepo kanthu.—Aroma 15:4.

20. Kodi nkhawa imawakhudza bwanji abale na alongo ena? Koma kodi sayenela kukayikila za ciani?

20 Cifukwa cokhala na nkhawa yaikulu, abale na alongo ena amacita mantha kwambili, ndiponso amacita manyazi akakhala pa gulu. Ngakhale kuti cimawavuta kukhala pa gulu, amayesetsabe kupezeka pa misonkhano yampingo, yadela, komanso yacigawo. Iwo samasuka kukamba ndi anthu amene sawadziŵa. Olo n’telo, amayesetsa kulankhula ndi anthu mu ulaliki. Ngati muli na vuto laconco, dziŵani kuti simuli mwekha. Pali ambili amene ali na vuto limeneli. Dziŵani kuti Yehova amakondwela na khama limene mumaonetsa pomutumikila na mtima wonse. Kupitiliza kwanu kum’tumikila ni umboni wakuti iye akukudalitsani ndiponso akukupatsani mphamvu. * (Afil. 4:6, 7; 1 Pet. 5:7) Ngati mupitiliza kutumikila Yehova olo kuti muli na mavuto amene amakulepheletsani kucita zambili, musakayikile kuti iye amakondwela na zimene mumacita.

21. Mwa thandizo la Yehova, kodi tonse tidzakwanitsa kucita ciani?

21 N’zokondweletsa kudziŵa kuti pali kusiyana pakati pa mpikisano wothamanga weni-weni, na mpikisano umene Paulo anakamba. Pampikisano wothamanga weni-weni wochulidwa m’Baibo, munthu mmodzi yekha ndiye anali kulandila mphoto. Mosiyana na izi, munthu aliyense amene amapilila mokhulupilika poyenda pa njila yacoonadi, adzalandila mphoto ya moyo wosatha. (Yoh. 3:16) Komanso, pampikisano wothamanga weni-weni, othamanga onse anali kufunika kukhala athanzi labwino kuti apambane. Mosiyana na othamanga amenewo, ambili a ife sitili na thanzi labwino, koma tikuthamangabe mopilila pa mpikisano wokalandila moyo. (2 Akor. 4:16) Mwa thandizo la Yehova, tonse tidzathamanga pa mpikisano umenewu mpaka ku mapeto!

NYIMBO 144 Yang’ana pa Mphoto

^ ndime 5 Masiku ano, atumiki ambili a Yehova amakumana na mavuto obwela cifukwa ca ukalamba. Ena akudwala matenda ofooketsa thupi. Ndipo tonsefe nthawi zina timakhala olema. Conco, nkhani ya kuthamanga pa mpikisano ingaoneke yovuta kwambili. M’nkhani ino, tikambilana mmene tonsefe tingathamangile mopilila. Tikambilananso zimene tingacite kuti tipambane pa mpikisano wokalandila moyo umene mtumwi Paulo anakamba.

^ ndime 6 Onani nkhani yakuti “Baibulo Limasintha Anthu,” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2013.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Kugwila nchito yolalikila mwakhama kumathandiza m’bale wokalambayu kuyenda pa njila ya coonadi.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Tingapunthwitse ena ngati tiwaumiliza kumwa moŵa wambili, kapena ngati ife timamwa kwambili.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale wodwala kwambili ali pa bedi m’cipatala, koma akupitilizabe kuthamanga pa mpikisano wauzimu mwa kulalikila ogwila nchito m’cipatala.