Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 14

‘Tsatilani Mapazi Ake Mosamala Kwambili’

‘Tsatilani Mapazi Ake Mosamala Kwambili’

“Khristu anavutika cifukwa ca inu, ndipo anakusiyilani citsanzo kuti mutsatile mapazi ake mosamala kwambili.”—1 PET. 2:21.

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE *

Yesu anatisiyila mapazi kuti tiziwatsatila mosamala kwambili (Onani ndime 1-2)

1-2. Kodi zingatheke bwanji kutsatila mapazi a Yesu? Fotokozani citsanzo.

YELEKEZANI kuti muli pagulu la anthu amene akuyenda m’cipululu coopsa ca mcenga. Ndiyeno munthu wodziŵa bwino cipululuco akukutsogolelani. Pamene akuyenda, akusiya mapazi ake kumbuyo mu mcenga. Kenako, muona kuti wokutsogolelani uja waleka kuoneka. Koma simukuda nkhawa, cifukwa imwe na anzanu amene mukuyenda nawo mukutha kutsatila bwino-bwino mapazi amene iye wakusiyilani.

2 Monga Akhristu oona, m’mawu ena tingati tikuyenda m’cipululu coopsa cimene ni dziko loipali. Koma nkhani yabwino ni yakuti Yehova anapeleka wotitsogolela wangwilo, Mwana wake Yesu Khristu, amene tingatsatile mapazi ake mosamala kwambili. (1 Pet. 2:21) Malinga na buku lina lofotokozela Baibo, Petulo pa lembali anayelekezela Yesu na wotsogolela paulendo. Monga wotsogolela paulendo amene akusiya mapazi kumbuyo, Yesu anatisiyila mapazi ake amene tingatsatile. Tiyeni tikambilane mafunso atatu okamba za kutsatila mapazi ake: Kodi kutsatila mapazi a Yesu kutanthauza ciani? N’cifukwa ciani tiyenela kutsatila mapazi ake? Nanga tingawatsatile motani?

KODI KUTSATILA MAPAZI A YESU KUTANTHAUZA CIANI?

3. Kodi kutsatila mapazi a munthu kutanthauza ciani?

3 Kodi kutsatila mapazi a munthu wina wake kutanthauza ciani? Mu Baibo, mawu akuti ‘kuyenda’ komanso “mapazi” nthawi zina amatanthauza zocita za munthu mu umoyo wake. (Gen. 6:9; Miy. 4:26, BL) Citsanzo cimene munthu amapeleka cingayelekezedwe na mapazi amene munthu amasiya kumbuyo akamayenda. Conco, kutsatila mapazi a munthu kumatanthauza kutsatila citsanzo cake, kapena kuti kutengela zocita zake.

4. Kodi kutsatila mapazi a Yesu kumatanthauza ciani?

4 Nanga kutsatila mapazi a Yesu kumatanthauza ciani? Mwacidule, kumatanthauza kutengela citsanzo cake. Pa lemba la mutu wa nkhani ino, Petulo anakamba maka-maka za citsanzo cabwino cimene Yesu anapeleka pankhani ya kupilila mavuto. Komabe, pali njila zina zambili za mmene tingatengele citsanzo ca Yesu. (1 Pet. 2:18-25) Kukamba zoona, umoyo wonse wa Yesu—kutanthauza zonse zimene anakamba na kucita, ni citsanzo kwa ife cimene tiyenela kutsatila.

5. Kodi zingathekedi anthu opanga ungwilo kutsatila citsanzo ca Yesu cangwilo? Fotokozani.

5 Popeza ndife anthu opanda ungwilo, kodi tingakwanitsedi kutsatila citsanzo ca Yesu? Inde tingakwanitse. Kumbukilani kuti Petulo akutilimbikitsa ‘kutsatila mapazi a Yesu mosamala kwambili’ osati mwangwilo. Ngati titsatila mapazi ake mosamala kwambili, kucita zonse zimene tingathe monga anthu opanda ungwilo, tidzalabadila mawu a mtumwi Yohane akuti: ‘Pitilizani kuyenda mmene Yesu anayendela.’—1 Yoh. 2:6.

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUTSATILA MAPAZI A YESU?

6-7. N’cifukwa ciani tingakambe kuti kutsatila mapazi a Yesu kungatithandize kuyandikila kwambili Yehova?

6 Kutsatila mapazi a Yesu kudzatiyandikilitsa kwa Yehova. N’cifukwa ciani takamba zimenezi? Coyamba, Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca mmene tingakhalile na umoyo wokondweletsa Mulungu. (Yoh. 8:29) Conco, tikamatsatila mapazi a Yesu tidzakondweletsa Yehova. Ndipo tingakhale otsimikiza kuti Atate wathu wakumwamba adzayandikila kwa anthu amene amayesetsa kukhala naye paubwenzi.—Yak. 4:8.

7 Cifukwa caciŵili n’cakuti Yesu anatengela citsanzo ca Atate wake mwangwilo. Ndiye cifukwa cake Yesu mwiniwakeyo anati: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Conco, pamene titengela makhalidwe a Yesu a mmene anacitila zinthu na ena, mwacitsanzo mmene anaonetsela cifundo kwa munthu wakhate, komanso kwa mzimayi wodwala matenda aakulu, ndiponso kwa anthu otayikidwa okondedwa awo mu imfa, timatengelanso citsanzo ca Yehova. (Maliko 1:40, 41; 5:25-34; Yoh. 11:33-35) Tikamatengela kwambili citsanzo ca Yehova, timakhala naye paubwenzi wolimba kwambili.

8. Fotokozani cifukwa cake kutsatila mapazi a Yesu kudzatithandiza ‘kugonjetsa’ dziko.

8 Kutsatila mapazi a Yesu kumatithandiza kusatangwanika na dziko loipali. Usiku womaliza kukhala na moyo padziko lapansi, Yesu anatha kukamba kuti: “Ndaligonjetsa dziko ine.” (Yoh. 16:33) Cimene anatanthauza n’cakuti iye anakana kusonkhezeledwa na maganizo, zolinga, komanso zocita za anthu a m’dzikoli. Yesu sanaiŵale cifukwa cimene anatumidwila padziko lapansi—kudzayeletsa dzina la Yehova. Nanga bwanji ife? M’dzikoli, muli zinthu zambili zimene zingaticeutse. Koma ngati nafenso monga Yesu tisumika maganizo pa kucita cifunilo ca Yehova, ‘tidzaligonjetsa’ dziko.—1 Yoh. 5:5.

9. Kodi tifunika kucita ciani kuti tipitilizebe kuyenda panjila ya kumoyo wosatha?

9 Kutsatila mapazi a Yesu kumatsogolela ku moyo wosatha. Pamene mnyamata wina wacuma anafunsa Yesu zimene anafunika kucita kuti akapeze moyo wamuyaya, Yesu anamuyankha kuti: ‘Bwela ukhale wotsatila wanga.’ (Mat. 19:16-21) Kwa Ayuda ena amene sanakhulupilile kuti iye ni Khristu, Yesu anati: “Nkhosa zanga . . . zimanditsatila. Ndidzazipatsa moyo wosatha.” (Yoh. 10:24-29) Kwa Nikodemo, mmodzi wa oweluza m’Khoti Yapamwamba ya Ayuda, amene anacita cidwi na ziphunzitso za Yesu, Yesu anakamba kuti “aliyense wokhulupilila iye” anali kudzakhala “ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Timaonetsa cikhulupililo cathu mwa Yesu, mwa kucita zimene iye anaphunzitsa kupitila m’mawu na zocita zake. Ngati ticita zimenezo, tidzapitilizabe kuyenda panjila ya kumoyo wosatha.—Mat. 7:14.

TINGACITE CIANI KUTI TITSATILE MAPAZI A YESU MOSAMALA KWAMBILI?

10. Kodi “kudziŵa” bwino Yesu kuphatikizapo ciani? (Yohane 17:3)

10 Tisanayambe kutsatila mapazi a Yesu mosamala, tifunika kumudziŵa. (Ŵelengani Yohane 17:3.) “Kudziŵa” Yesu si cocitika ca kamodzi cabe ayi, kumafuna kupitiliza. Tifunika kupitiliza kum’dziŵa bwino—kuphunzila makhalidwe ake, kaganizidwe kake, komanso mfundo zake. Kaya takhala m’coonadi kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenela kupitilizabe “kudziŵa” Yehova na Mwana wake.

11. Kodi m’Mauthenga Abwino anayi muli zotani?

11 Pofuna kutithandiza kum’dziŵa bwino Mwana wake, Yehova anaikamonso mabuku a Uthenga Wabwino anayi m’Mawu ake. Mabuku anayi amenewo, amafotokoza umoyo wa Yesu na utumiki wake. Mabukuwo amatiuza zimene Yesu anakamba, kutionetsa zimene anacita komanso mmene anali kumvelela. Amatithandizanso ‘kuganizila mozama’ citsanzo ca Yesu. (Aheb. 12:3) Conco, tingati m’mabuku amenewa muli mapazi amene Yesu anasiya kumbuyo. Conco, mwa kuphunzila Mauthenga Abwino amenewa, tingapitilizebe kum’dziŵa bwino Yesu. Cotulukapo cake n’cakuti tingatsatile mapazi ake mosamala kwambili.

12. Kodi tingacite ciani kuti tizipindula mokwanila na mabuku a Uthenga Wabwino?

12 Kuti tipindule mokwanila na Mauthenga Abwino amenewa sitiyenela kumangoyaŵelenga cabe ayi. Tifunika kupatula nthawi yowaphunzila mosamala komanso kuwasinkha-sinkha mozama. (Yelekezelani na Yoswa 1:8.) Tiyeni tikambilane njila ziŵili zimene zingatithandize kusinkha-sinkha pa mabuku a Uthenga Wabwino amenewo, komanso mmene tingaseŵenzetsele zimene tiŵelengamo.

13. Kodi mungacite ciani kuti nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zizikhala zeni-zeni kwa imwe?

13 Njila yoyamba, muzitha kuona m’maganizo mwanu zocitika za m’mabuku a Uthenga Wabwino ngati kuti zikucitika lelo. Yelekezani m’maganizo kuti mukuona, kumvela, na kukhudzika na zimene zinali kucitika. Kuti muthe kucita zimenezi, fufuzani m’zofalitsa za gulu la Yehova. Pendani zocitika zochulidwa m’nkhani imene mukuŵelengayo, za pambuyo kapena za patsogolo pankhaniyo. Fufuzani nkhani zina zounikila pa anthu na malo ochulidwa m’nkhaniyo. Ŵelenganinso nkhani yofananayo m’buku lina la Uthenga Wabwino. Nthawi zina, wolemba Uthenga Wabwino wina angafotokoze zinthu zina zocititsa cidwi zimene wina sanazifotokoze.

14-15. Kodi tingacite ciani kuti tiziseŵenzetsa zimene taphunzila m’nkhani zofotokoza umoyo wa Yesu?

14 Njila yaciŵili, seŵenzetsani mu umoyo wanu zimene mwaphunzila m’buku la Uthenga Wabwino. (Yoh. 13:17) Pambuyo poŵelenga mosamala nkhani ina yake m’buku la Uthenga Wabwino, dzifunseni kuti: ‘Kodi ni phunzilo lanji limene ningatengepo m’nkhaniyi limene ningaseŵenzetse mu umoyo wanga? Ningaseŵenzetse bwanji nkhaniyi kuti nithandize wina wake?’ Yesani kuganizila munthu wina wake, ndiyeno panthawi yoyenelela, mwacikondi komanso mosamala muuzenkoni zimene munaphunzila.

15 Tiyeni tione citsanzo ca mmene tingaseŵenzetsele njila ziŵili zimenezi. Tidzakambilana nkhani ya mkazi wamasiye wosauka, amene Yesu anaona m’kacisi.

MKAZI WAMASIYE WOSAUKA M’KACISI

16. Fotokozani cocitika ca pa Maliko 12:41.

16 Yelekezani kuti nkhaniyi mukuiona m’maganizo mwanu. (Ŵelengani Maliko 12:41.) Yelekezani cocitika ici. Ni pa Nisani 11, mu 33 C.E., ndipo mlungu umodzi usanathe Yesu adzaphedwa. Yesu wathela nthawi yambili pa tsikuli akuphunzitsa m’kacisi. Ndipo atsogoleli acipembedzo akhala akumutsutsa kwambili. Poyamba ena anam’funsa za kumene anacotsa ulamulilo wake. Ndipo ena anayesa kum’kola pom’panikiza na mafunso. (Maliko 11:27-33; 12:13-34) Apa lomba Yesu wapita ku malo ena ake m’kacisimo. Malowo ayenela kuti anali kuchedwa Bwalo la Azimayi. Pamalopo, Yesu anali kutha kuona tumabokosi toponyamo ndalama m’mbali mwa cipupa ca malowo. Kenako akukhala pansi na kupenyelela anthu akuponyamo zopeleka zawo, akuona anthu olemela ambili akuponyamo makobili oculuka. Mwina ali pafupi ndithu moti akumva kulila kwa ndalamazo pamene zikugwela m’tumabokosimo.

17. Kodi mkazi wamasiye wosauka wochulidwa pa Maliko 12:42 anacita ciani?

17 Ŵelengani Maliko 12:42. Kanthawi pang’ono, pakufika mzimayi amene akukopa cidwi ca Yesu. Mkaziyo ni “wamasiye wosauka.” (Luka 21:2) Umoyo ni wovuta kwambili kwa iye. Ndipo cioneka kuti zimamuvuta kupeza zofunikila pa umoyo. Ngakhale n’telo, iye akupita pa kabokosi koponyamo zopeleka. Ndipo mosadzionetsela aponyamo tumakoboli tocepa kwambili tuŵili, tumene mwina situnamveke n’komwe pogwela m’coponyamoco. Koma Yesu wadziŵa ndalama zimene mzimayiyo waponyamo. Iye waponyamo tumakobili tuŵili tochedwa tumaleputa, tocepetsetsa pa ndalama zonse. Inde, tosakwana ngakhale kugula mpheta imodzi, imodzi mwa mbalame zocepa kwambili zimene zimagulitsidwa monga cakudya.

18. Malinga na Maliko 12:43, 44, kodi Yesu anakamba ciani ponena za copeleka ca mkazi wamasiye?

18 Ŵelengani Maliko 12:43, 44. Yesu wakondwela kwambili na mkazi wamasiye ameneyu. Conco aitana ophunzila ake na kuwaonetsa mkazi wamasiyeyu. Ndiyeno akuwauza kuti: “Mkazi wamasiye wosaukayu waponya zoculuka kuposa onse.” Kenako afotokoza kuti: “Cifukwa onsewo [maka-maka anthu olemela] aponya zimene atapa pa zoculuka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zocilikizila moyo wake.” Pamene mkazi wamasiye wokhulupilika ameneyu anapeleka ndalama yake yothela patsikulo, anaika moyo wake m’manja mwa Yehova kuti adzam’samalila.—Sal. 26:3.

Mofanana na Yesu, yamikilani ena pa zimene amakwanitsa kucita potumikila Yehova (Onani ndime 19-20) *

19. Ni phunzilo lofunika liti limene tingatengepo pa mawu a Yesu okamba za mkazi wamasiye wosauka?

19 Tengam’poni maphunzilo pa nkhani imeneyi. Dzifunseni kuti, ‘Kodi niphunzilapo ciani pa mawu a Yesu okamba za mkazi wamasiye wosauka?’ Ganizilani za mkazi wamasiye uja. Mosakayikila, iye anali kulaka-laka kupeleka zambili kwa Yehova. Komabe anacita zimene akanakwanitsa. Anapatsa Yehova zonse zimene akanatha kupeleka. Ndipo Yesu anadziŵa kuti copeleka ca mkazi wamasiyeyo cinali ca mtengo wapatali m’maso mwa Atate wake. Apa pali phunzilo lofunika kwambili kwa ife. Yehova amakondwela tikam’patsa zonse zimene tingathe, kutanthauza kum’tumikila na mtima wathu wonse komanso moyo wathu wonse. (Mateyu 22:37; Akolose 3:23) Yehova amakondwela akamaona kuti tikucita zonse zimene tingathe! Mfundo imeneyi igwila nchito pa kuculuka kwa nthawi na mphamvu zimene timaseŵenzetsa pa kulambila kwathu, kuphatikizapo pankhani ya ulaliki na misonkhano.

20. Kodi mungaseŵenzetse bwanji phunzilo la m’nkhani ya mkazi wamasiye? Fotokozani citsanzo.

20 Kodi mungaseŵenzetse bwanji phunzilo limene mwatengapo pankhani ya mkazi wamasiye? Yesani kuganizila anthu amene angalimbikitsidwe mukawatsimikizila kuti Yehova amakondwela na kuyesetsa kwawo pom’tumikila. Mwacitsanzo, kodi mudziŵako mlongo wacikulile aliyense amene amavutika maganizo, kapena kudziona kuti ni wakutha nchito, cifukwa cakuti thanzi lake silimulola kucita zimene anali kukwanitsa kale mu utumiki? Kapena mungaganizile za m’bale amene akudwala matenda okhalitsa komanso opweteka, ndipo amalefuka akaganizila zakuti amalephela kupezeka ku misonkhano yonse ku Nyumba ya Ufumu? Thandizani anthu otelo mwa kukamba mawu “olimbikitsa.” (Aef. 4:29) Auzenkoni phunzilo lolimbikitsa limene munatengapo pankhani ya mkazi wamasiye wosauka. Mawu anu olimbikitsa angawatsimikizile kuti Yehova amakondwela akamam’patsa zonse zimene angathe. (Miy. 15:23; 1 Ates. 5:11) Mukamayamikila ena pa zimene amakwanitsa kucita potumikila Yehova olo zioneke zocepa bwanji ndiye kuti mukutsatila mapazi a Yesu mosamala kwambili.

21. Kodi mwatsimikiza mtima kuti mudzacita ciani?

21 Ha! Ndife oyamikila cotani nanga kuti nkhani za m’mabuku a Uthenga Wabwino zili na mfundo zambili zokhudza umoyo wa Yesu, zimene zimatithandiza kutengela citsanzo cake na kutsatila mapazi ake mosamala kwambili. Bwanji osakonza zakuti muziphunzila mabuku a Uthenga Wabwino pa phunzilo lanu laumwini kapena pa Kulambila kwa Pabanja? Tisaiŵale kuti, kuti tipindule na zimene tikuphunzila, tiyenela kumaona zocitikazo m’maganizo mwathu, na kuseŵenzetsa zimene taphunzilazo mu umoyo wathu. Kuwonjezela pa kutengela citsanzo ca Yesu pa zimene anacita, tiyenela kumvetsela zimene anakamba. M’nkhani yotsatila tidzakambilana zimene tingaphunzilepo pa mawu a Yesu othela amene anakamba anasanamwalile.

NYIMBO 15 Tamandani Woyamba Kubadwa wa Yehova

^ ndime 5 Monga Akhristu oona, tifunika ‘kutsatila mapazi a Yesu mosamala kwambili.’ Kodi Yesu anatisiyila “mapazi” otani amene tifunika kutsatila? Nkhani ino iyankha funso limeneli. Ifotokozanso cifukwa cake tiyenela kutsatila mapazi ake mosamala kwambili, na mmene tingacitile zimenezi.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Pambuyo posinkha-sinkha zimene Yesu anakamba ponena za mkazi wamasiye wosauka, mlongo akuyamikila mlongo wina wacikulile pa utumiki wake umene amacita na mtima wonse.