Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 17

Yehova Amakukondani Kwambili!

Yehova Amakukondani Kwambili!

“Yehova amasangalala ndi anthu ake.”—SAL. 149:4.

NYIMBO 108 Cikondi Cokhulupilika ca Mulungu

ZIMENE TIKAMBILANE *

Atate wathu wakumwamba “amasangalala” na aliyense wa ife (Onani ndime 1)

1. Kodi Yehova amaona ciani mwa anthu ake?

YEHOVA MULUNGU “amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Mfundo imeneyi ni yokondweletsa ngako! Yehova amaona makhalidwe athu abwino. Amaonanso zabwino zimene tingathe kucita, ndipo amatikokela kwa iye. Ngati tikhalabe okhulupilika kwa Mulungu, iyenso adzakhalabe nafe mpaka muyaya!—Yoh. 6:44.

2. N’cifukwa ciani ena cimawavuta kukhulupilila kuti Yehova amawakonda?

2 Ena angakambe kuti: ‘Nidziŵa kuti Yehova amakonda anthu ake monga gulu, koma kodi ningadziŵe bwanji kuti inenso panekha Yehova amaniŵelengela?’ N’ciani cingapangitse munthu kufunsa funso limeneli? Mlongo Oksana, * amene anacitilidwa zoipa kwambili ali mwana ananena kuti: “N’tabatizika n’nakondwela kwambili, ndipo n’nayamba upainiya. Koma pambuyo pa zaka 15, n’nayamba kuvutika kwambili maganizo cifukwa ca zoipa zimene zinanicitikila. Kaamba ka izi, n’nayamba kuona kuti Yehova sakunikondanso.” Mlongo mpainiya dzina lake Yua, amenenso anakumana na zovuta zambili ali mwana, anakamba kuti: “N’napatulila moyo wanga kwa Yehova cifukwa n’nali kufuna kum’kondweletsa. Ngakhale n’telo, pansi pa mtima n’nali wotsimikiza kuti iye sanganikonde.”

3. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

3 Mofanana na Akhristu okhulupilika amene tawachulawo, inunso Yehova mumam’konda kwambili. Koma mwina mumakayikila ngati iyenso amakukondani. N’cifukwa ciani kukhala wotsimikiza kuti iye amakukondani n’kofunika? Nanga cingakuthandizeni n’ciani mukamakhala na maganizo akuti Yehova sakukondani? Tiyeni tikambilane mayankho pa mafunso amenewa.

KUKAYIKILA KUTI YEHOVA AMATIKONDA N’KOOPSA

4. N’cifukwa ciani kukayikila kuti Yehova amatikonda n’koopsa?

4 Cikondi n’camphamvu kwambili. Ngati ndife otsimikiza kuti Yehova amatikonda na kuticilikiza, tidzalimbikitsidwa kum’tumikila na mtima wonse olo tikumane na mavuto mu umoyo. Koma ngati tikayikila kuti Mulungu amatikonda, ‘mphamvu zathu zidzakhala zocepa.’ (Miy. 24:10) Ndipo ngati talefuka n’kuyamba kukayikila cikondi ca Yehova pa ife, tingagonje mosavuta ku misampha ya Satana.—Aef. 6:16.

5. Kodi kukayikila za cikondi ca Mulungu kwawakhudza bwanji ena?

5 Akhristu ena okhulupilika masiku ano, afooka kuuzimu cifukwa cokhala na zikayiko. M’bale wina dzina lake James, amene ni mkulu anati: “Ngakhale kuti n’nali kutumikila pa Beteli ndipo n’nali kusangalala na ulaliki wanga mumpingo wa citundu cina, n’nali kukayikilabe ngati Yehova amayamikila kudzipeleka kwanga. Panthawi ina, n’nafika ngakhale pokayikila ngati Yehova amamvetsela mapemphelo anga.” Mlongo Eva, amenenso ali mu utumiki wanthawi zonse anakamba kuti: “N’naona kuti kukayikila kuti Yehova amatikonda n’koopsa, cifukwa kungatifooketse kuuzimu. Izi zimacepetsa njala yako yocita zauzimu, komanso cimwemwe cako potumikila Yehova cimacepa.” M’bale Michael, amene ni mpainiya wanthawi zonse komanso mkulu ananena kuti: “Ngati umakayikila kuti Mulungu amakukonda, umatengeka pang’ono-pang’ono n’kuyamba kutalikilana naye.”

6. Tifunika kucita ciani tikayamba kukayikila kuti Mulungu amatikonda?

6 Zitsanzo zimenezi zionetsa mmene kukayikila cikondi ca Yehova pa ife kungakhalile kovulaza mwauzimu. Koma kodi tiyenela kucita ciani tikayamba kukhala na maganizo okayikila cikondi ca Yehova pa ife? Tifunika kukaniza maganizo amenewo mwamsanga! Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kucotsa ‘maganizo osowetsa mtendele’ amenewo kuti mukhale na “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Sal. 139:23; Afil. 4:6, 7) Ndipo kumbukilani kuti simuli mwekha. Abale na alongo ena okhulupilika akulimbana na maganizo okhwethemula amenewo. Ngakhale atumiki a Yehova akale analimbana nawo maganizo otelo. Onani zimene tingaphunzile pa citsanzo ca mtumwi Paulo.

ZIMENE TIPHUNZILAPO PA CITSANZO CA PAULO

7. Kodi Paulo anakumana na mavuto otani?

7 Kodi nthawi zina mumamva kuti mwaculukidwa na maudindo, ndipo simungathe kuwasamalila onse? Ngati n’conco, ndiye kuti mungamumvetse Paulo. Iye anali na nkhawa osati pa mpingo umodzi cabe, koma “pa mipingo yonse.” (2 Akor. 11:23-28) Kodi muli na matenda okhalitsa amene amakulandani cimwemwe? Paulo anali kuvutika na “munga m’thupi,” umene uyenela kuti unali matenda ena ake, amene iye anali kufunitsitsa kuti athe. (2 Akor. 12:7-10) Kodi mumalefulidwa cifukwa ca zophophonya zanu? Ni mmene Paulo anali kumvelela nthawi zina. Iye anadzicha “munthu wovutika” cifukwa ca nkhondo yosalekeza yolimbana na zophophonya zake.—Aroma 7:21-24.

8. N’ciani cinathandiza Paulo kupilila mavuto ake?

8 Ngakhale kuti Paulo anakumana na mayeso komanso zolefula zosiyana-siyana, iye sanaleke kutumikila Yehova. N’ciani cinam’patsa mphamvu yocita zimenezo? Ngakhale kuti anali kudziŵa zophophonya zake, cikhulupililo cake pa dipo cinali cosagwedezeka. Anali kulidziŵanso lonjezo la Yesu lakuti ‘aliyense wokhulupilila Yesu adzakhala ndi moyo wosatha.’ (Yoh. 3:16; Aroma 6:23) Ndithudi, Paulo anali mmodzi wa anthu amene anakhulupililadi nsembe ya dipo. Iye anali wotsimikiza kuti Yehova ni wokonzeka kukhululukila ngakhale anthu amene anacita macimo aakulu, malinga ngati alapa.—Sal. 86:5.

9. Tiphunzilapo ciani pa mawu a Paulo a pa Agalatiya 2:20?

9 Paulo anakhulupililanso mphamvu ya cikondi ca Mulungu, cimene anaonetsa kupitila mwa Khristu. (Ŵelengani Agalatiya 2:20.) Onani mawu olimbikitsa amene ali kumapeto kwa vesiyi. Paulo anati: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca ine.” Paulo sanayikile malile cikondi ca Mulungu, mwa kunena kuti, ‘Nimamvetsa cifukwa cake Yehova amawakonda abale anga, koma ine sanganikonde.’ Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Roma kuti: “Pamene tinali ocimwa, Khristu anatifela.” (Aroma 5:8) Cikondi ca Mulungu cilibe malile!

10. Tiphunzilapo ciani pa Aroma 8:38, 39?

10 Ŵelengani Aroma 8:38, 39. Paulo anali kudziŵa kuti cikondi ca Mulungu n’camphamvu. Iye analemba kuti palibe cimene ‘cidzatilekanitsa ndi cikondi ca Mulungu.’ Paulo anali kudziŵa mmene Yehova anacitila zinthu moleza mtima na mtundu wa Aisiraeli. Anadziŵanso mmene Yehova anamuonetsela cifundo. M’mawu ena Paulo anali kukamba kuti, ‘Popeza Mulungu anatumiza Mwana wake kuti adzanifele ine, kodi nili na cifukwa ciliconse cokayikilila za cikondi cake.’—Aroma 8:32.

Cofunika kwa Yehova ni zimene timacita palipano komanso zimene tidzacita kutsogolo, osati zimene tinacita kumbuyoku (Onani ndime 11) *

11. Ngakhale kuti Paulo anacita macimo monga amene achulidwa pa 1 Timoteyo 1:12-15, n’cifukwa ciani anali wotsimikiza kuti Mulungu amam’konda?

11 Ŵelengani 1 Timoteyo 1:12-15. N’kutheka kuti nthawi zina Paulo anali kudziimba mlandu cifukwa ca zolakwa zimene anacita kumbuyoko. Ndipo n’zosadabwitsa kuti iye anakamba kuti anali munthu “wocimwa kwambili.” Akalibe kuphunzila coonadi, Paulo anali kuzunza Akhristu mu mzinda na mzinda, ndipo ena anali kuwaponya m’ndende na kuvomeleza kuti aphedwe. (Mac. 26:10, 11) Ganizilani cabe mmene Paulo akanamvelela kukumana na Mkhristu wacinyamata amene makolo ake anaphedwa cifukwa cakuti iye anavomeleza kuti iwo aphedwe. Paulo anadziimba mlandu pa zolakwa zake, koma anadziŵa kuti sakanatha kusintha zakumbuyo. Iye anavomeleza kuti Khristu anamufela, ndipo mwacidalilo analemba kuti: “Mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili monga ndililimu.” (1 Akor. 15:3, 10) Kodi tiphunzilapo ciani? Vomelezani kuti Khristu anakufelani na kukukonzelani njila kuti mukhale pa ubwenzi wolimba na Yehova. (Mac. 3:19) Cofunika kwa Yehova ni zimene timacita palipano, komanso zimene tidzacita kutsogolo, osati zolakwa zimene tinacita kumbuyoku, kaya panthawiyo tinali wa Mboni za Yehova kapena ayi.—Yes. 1:18.

12. Kodi mawu a pa 1 Yohane 3:19,20 angatithandize bwanji ngati timadziona kuti ndife osafunika kapena osakondedwa?

12 Mukaganizila zakuti Yesu anakufelani kuti aphimbe macimo anu, mwina mungakambe kuti, ‘Sindine woyenela kucitilidwa zimenezo.’ N’cifukwa ciani mungamvele conco? Cifukwa mtima wathu wopanda ungwilo ungatinamize, na kutipangitsa kudziona wosafunika kapena wosakondedwa. (Ŵelengani 1 Yohane 3:19, 20.) Panthawi ngati zimenezi tiyenela kukumbukila kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu.” Cikondi ca Atate wathu wakumwamba na cikhululuko cake n’zamphamvu kuposa maganizo otilefula amene tingakhale nawo m’mitima yathu. Tiyenela kukhulupilila mumtima mwathu kuti Yehova amatikondadi. Kuti ticite zimenezi tiyenela kuŵelenga Mawu ake kaŵili-kaŵili, kupemphela mosalekeza, na kuyanjana na anthu ake okhulupilika. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika?

MMENE KUŴELENGA BAIBO, PEMPHELO, NA MABWENZI OKHULUPILIKA ANGATITHANDIZILE

13. Kodi kuŵelenga Mawu a Mulungu kungatithandize bwanji? (Onaninso bokosi lakuti “ Mmene Mawu a Mulungu Amawathandizila.”)

13 Ŵelengani Mawu a Mulungu tsiku lililonse, ndipo mudzadziŵa makhalidwe abwino a Yehova. Mudzaona kuti amakukondani kwambili. Kusinkha-sinkha pa Mawu a Mulungu tsiku lililonse kungakuthandizeni kukhala woganiza bwino, “kuwongola zinthu” m’maganizo na mu mtima mwanu. (2 Tim. 3:16) M’bale wina dzina lake Kevin amene ni mkulu, amenenso amavutika na maganizo odziona kuti ni wosafunika anati: “Kuŵelenga Salimo 103 na kusinkha-sinkhapo palembali, kwanithandiza kuwongolela maganizo anga na kudziŵa mmene Yehova amanionela.” Mlongo Eva, amene tam’chula kuciyambi anati: “Nimatsiliza tsiku langa mwa kusinkha-sinkha pa zimene Yehova amaona kuti n’zofunika. Zimanipatsa mtendele wa mumtima na kulimbitsa cikhulupililo canga.”

14. Kodi pemphelo lingatithandize bwanji?

14 Pemphelani kaŵili-kaŵili. (1 Ates. 5:17) Ubwenzi wolimba na mnzathu umadalila pa kukambilana moona mtima nthawi zonse. N’cimodzimodzi na ubwenzi wathu na Yehova. Tikamafotokoza maganizo athu, mmene timvelela, na kumuuza nkhawa zathu m’pemphelo, timaonetsa kuti timam’dalila komanso kuti tidziŵa kuti iye amatikonda. (Sal. 94:17-19; 1 Yoh. 5:14, 15) Mlongo Yua, amene tam’gwila mawu kuciyambi ananena kuti: “Nikamapemphela sinimangochula mmene zinthu zayendela pa tsikulo. Nimam’masukila Yehova na kumuuza mmene nimvelela. Pang’ono-m’pang’ono, nafika poona Yehova monga Tate amene amakondadi ana ake, osati monga bwana wa pakampani.”—Onani bokosi lakuti “ Kodi Munaliŵelengapo?

15. Kodi Yehova waonetsa bwanji kuti amatikonda?

15 Muziyanjana na mabwenzi okhulupilika. Iwo ni mphatso yocokela kwa Yehova. (Yak. 1:17) Atate wathu wakumwamba waonetsa kuti amatikonda potipatsa banja lauzimu la abale na alongo, amene amationetsa ‘cikondi nthawi zonse.’ (Miy. 17:17) M’kalata yake yopita kwa Akolose, Paulo anachula Akhristu ena amene anamucilikiza. Ponena za iwo, iye anakamba kuti ‘anam’thandiza na kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:10, 11) Ngakhale Khristu Yesu anafunika thandizo, ndipo anayamikila cicilikizo cimene analandila kucokela kwa mabwenzi ake onse, angelo komanso anthu.—Luka 22:28, 43.

16. Kodi mabwenzi okhulupilika angatithandize bwanji kuyandikila Yehova?

16 Kodi mukupindula mokwanila na mphatso ya Yehova ya mabwenzi okhulupilika? Kuuzako mnzathu wokhwima nkhawa zathu sindiye kuti ndife ofooka. Cingakhale citetezo. Ganizilani zimene m’bale James amene tam’gwila mawu kumayambililo anakamba. Iye anati: “Kukhala pa ubwenzi wabwino na Akhristu okhwima kwanithandiza kwambili. Nikalefuka cifukwa ca maganizo olakwika, mabwenzi abwino amenewa amanimvetsela moleza mtima na kuniuza kuti amanikonda. Kupitila mwa iwo, nimaona kuti Yehova amanikonda na kunisamalila.” Kukamba zoona, kukhala pa ubwenzi wolimba na abale na alongo athu auzimu n’kofunika kwambili!

KHALANIBE M’CIKONDI CA YEHOVA

17-18. Kodi tiyenela kumvela ndani, ndipo cifukwa ciani?

17 Colinga ca Satana n’cakuti tileke kumenya nkhondo yocita zabwino. Amafuna kuti tiziganiza kuti Yehova satikonda, ndipo sitiyenela cipulumutso cake. Koma monga taonela, limeneli ni bodza lamkunkhuniza.

18 Yehova amakukondani. Ndimwe cuma camtengo wapatali m’maso mwake. Ngati mumumvela, ‘mudzakhalabe m’cikondi cake’ mpaka muyaya monga zilili kwa Yesu. (Yoh. 15:10) Conco, musamvele Satana kapena mtima wanu ukayamba kukusulizani. M’malomwake, mvelani Yehova amene amaona zabwino mwa aliyense wa ife. Khalani wotsimikiza kuti iye “amasangalala ndi anthu ake,” kuphatikizapo imwe!

NYIMBO 141 Moyo ni Cozizwitsa

^ ndime 5 Abale na alongo athu ena cimawavuta kukhulupilila kuti Yehova amawakonda. M’nkhani ino, tikambilane cifukwa cake tingakhale otsimikiza kuti Yehova amakonda aliyense wa ife payekha. Tikambilanenso mmene tingagonjetsele zikayiko zilizonse zimene tingakhale nazo zokhudza cikondi cake pa ife.

^ ndime 2 Maina ena asinthidwa.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Paulo asanakhale Mkhristu, anaponya Akhristu ambili m’ndende. Koma atayamikila zimene Yesu anam’citila, anasintha na kulimbikitsa abale ake auzimu, amene n’kutheka kuti ena anali acibale kwa anthu amene iye anawazunza.