Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 17

Inu Anakubala—Phunzilani ku Citsanzo ca Yunike

Inu Anakubala—Phunzilani ku Citsanzo ca Yunike

“Usasiye malamulo a mayi ako, pakuti [ali] ngati nkhata ya maluŵa yokongola pamutu pako, ndi mkanda wokongola m’khosi mwako.”—MIY. 1:8, 9.

NYIMBO 137 Azimayi Okhulupilika, Alongo Athu

ZIMENE TIKAMBILANE a

Yunike mayi ake a Timoteyo, na a Loisi ambuye ake ni okondwa komanso onyadila pamene akupenyelela ubatizo wa Timoteyo (Onani ndime 1)

1-2. (a) Kodi Yunike anali ndani? Nanga anakumana na zovuta zotani monga nakubala? (b) Fotokozani cithunzi ca pacikuto.

 NGAKHALE kuti Baibo siifotokoza za ubatizo wa Timoteyo, tingathe kuonabe m’maganizo mwathu cimwemwe codzaza tsaya cimene mayi ake, Yunike, anali naco pa tsikulo. (Miy. 23:25) Muoneni m’maganizo mwanu nakubala ameneyu, ali wonyadila pamene mwana wake Timoteyo waimilila m’madzi. Akumwetulila pamene a Loisi, ambuye ake a Timoteyo, ataimilila pafupi naye. Yunike akuika manja pamtima pamene Timoteyo akumila m’madzi. Kenako, akugwetsa misozi ya cisangalalo pamene mwana wake Timoteyo akuvuuka m’madzi nkhope yake ili mwee na cisangalalo. Olo kuti inali nchito yovuta, Yunike wakwanilitsa colinga cake cophunzitsa Timoteyo kukonda Yehova na Mwana wake Yesu Khristu. Kodi iye anagonjetsa mavuto otani kuti akwanilitse colingaci?

2 Timoteyo anakulila m’banja la makolo osiyana zipembedzo. Ndiponso, atate ake anali Mgiriki, pamene amayi ake komanso ambuye ake aakazi anali Ayuda. (Mac. 16:1) Mwacionekele, Timoteyo anali wacicepele pamene Yunike na Loisi anakhala Akhristu. Koma atate ake sanakhale Mkhristu. Kodi Timoteyo anasankha cipembedzo citi? N’kutheka kuti iye anali pa msinkhu wotha kupanga yekha zisankho. Kodi anasankha cipembedzo ca atate ake? Kodi anamamatila miyambo ya Ayuda imene anaphunzila ali mwana? Kapena kodi anasankha kukhala wotsatila wa Yesu Khristu?

3. Malinga na Miyambo 1:8, 9, kodi Yehova amaiona bwanji nchito imene amayi amagwila pothandiza ana awo kukhala mabwenzi ake?

3 Mofananamo, anakubala amene ni Akhristu amakonda mabanja awo. Coposa zonse, iwo amafuna kuthandiza ana awo kukhala pa ubwenzi wolimba na Yehova. Ndipo Mulungu amayamikila kuyesetsa kwawo. (Ŵelengani Miyambo 1:8, 9.) Yehova wacilikiza amayi ambili kuthandiza ana awo kuphunzila Baibo.

4. Kodi anakubala amakumana na zovuta zotani masiku ano?

4 Mwacibadwa, nthawi zina mayi amadela nkhawa ngati ana ake adzasankha kutumikila Yehova monga anacitila Timoteyo. Makolo amadziŵa mavuto amene ana awo amakumana nawo m’dzikoli la Satana. (1 Pet. 5:8) Cina, alongo ambili amavutika kulela ana awo popanda mwamuna, kapena mwamuna angakhale naye koma salambila Yehova. Mwacitsanzo, mlongo wina dzina lake Christine b anati: “Mwamuna wanga anali tate wabwino komanso anali kusamalila bwino banja lathu. Koma sanali kufuna olo pang’ono kuti niziphunzitsa ana athu kuti akhale Mboni za Yehova. N’nalila kwa zaka poganizila mmene ningathandizile ana athu kuyamba kulambila Yehova.”

5. Tikambilane ciyani m’nkhani ino?

5 Ngati ndimwe nakubala, monga Mkhristu mungakwanitse kuthandiza ana anu kukonda Yehova na kum’tumikila monga anacitila Yunike. M’nkhani ino, tikambilane mmene mungatengele citsanzo cake pophunzitsa ana anu mwa zokamba zanu na zocita zanu. Tionenso mmene Yehova adzakuthandizilani.

PHUNZITSANI ANA ANU MWA ZOKAMBA ZANU

6. Malinga n’kunena kwa 2 Timoteyo 3:14, 15, kodi Timoteyo anakhala bwanji Mkhristu?

6 Pamene Timoteyo anali wacicepele, amayi ake anayesetsa kum’phunzitsa “malemba oyela,” malinga na kamvedwe ka Ayuda panthawiyo. Koma Yunike anali na cidziŵitso cocepa cifukwa sanali kudziŵa ciliconse ponena za Yesu Khristu panthawiyo. Ngakhale n’conco, zimene Timoteyo anaphunzila m’Malemba zinam’patsa maziko abwino amene anam’thandiza kukhala Mkhristu. Koma kodi anakhaladi Mkhristu? Pokhala wacinyamata, iye anali na ufulu wosankha kaya kukhala Mkhristu kapena ayi. Mosakayikila, Timoteyo ‘anakhulupilila’ coonadi conena za Yesu cifukwa ca kuyesa-yesa kwa amayi ake. (Ŵelengani 2 Timoteyo 3:14, 15.) Yunike anakondwela kwambili kuti anakwanitsa kuphunzitsa mwana wake za Yehova. Iye anacitadi monga mwa dzina lake, limene limatanthauza “kugonjetsa.”

7. Kodi Yunike akanathandiza bwanji mwana wake kupitabe patsogolo pambuyo pa ubatizo?

7 Timoteyo atabatizika, anakwanilitsa colinga cake cacikulu. Koma Yunike sanaleke kudela nkhawa za mwana wake. Kodi mwana wakeyo adzasankha kucita ciyani pa umoyo wake? Kodi adzasankha anthu a makhalidwe oipa kukhala anzake? Kodi adzapita kusukulu ku Atene na kuyamba kukhulupilila ziphunzitso za anthu zacikunja? Kodi adzatayila nthawi yake komanso mphamvu zake pogwila nchito molimbika kuti alemele? Yunike sakanapangila Timoteyo cisankho, koma akanamuthandiza kusankha mwanzelu. Motani? Mwa kucita khama kum’phunzitsa kukonda Yehova, komanso kuyamikila Yesu. Makolo amene mnzawo wa mu ukwati si Mboni, si ndiwo okha amene amakumana na zovuta pothandiza ana awo kukonda Yehova. Ngakhale makolo amene onse ni Mboni, cingakhale covuta kwa iwo kufika ana awo pamtima kuti akhale atumiki a Yehova okhulupilika. Kodi makolo angaphunzilepo ciyani pa citsanzo ca Yunike?

8. Kodi mlongo angathandize bwanji mwamuna wake amene ni Mboni kusamalila zosoŵa zauzimu za ana awo?

8 Muziphunzila Baibo na ana anu. Inu alongo, ngati mwamuna wanu ali m’coonadi, Yehova amafuna kuti muzimuthandiza kusamalila zosoŵa zauzimu za ana anu. Njila imodzi imene mungacitile zimenezi, ni kucilikiza makonzedwe a kulambila kwa pabanja. Muzikamba zabwino zokhudza makonzedwewo, komanso muziganizila zimene mungacite kuti kulambilako kuzikhala kokondweletsa. Mwina mungathandize mwamuna wanu kukonzekela kukacitila pamodzi mbali ina yake yapadela ya m’Baibo. Cina, ngati ana anu ena afika pa msinkhu woyenela kuwatsogoza phunzilo m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, mungalinganize na mwamuna wanu kuti mupeleke thandizo lofunikilalo.

9. Kodi nakubala amene mwamuna wake si Mboni angapeze kuti thandizo?

9 Alongo ena ndiwo amaphunzitsa Baibo ana awo cifukwa akulela okha ana, kapena mwamuna wawo si Mboni. Ngati umu ni mmene zilili kwa inu, musamade nkhawa kwambili. Yehova adzakuthandizani. Gwilitsilani nchito zida zophunzitsila zogwila mtima zimene wakupatsani kupitila m’gulu lake, pophunzila na ana anu. Bwanji osafunsilako maganizo kwa makolo aciyambakale kuti akuuzenkoni moseŵenzetsela zida zimenezi pa kulambila kwa pabanja? c (Miy. 11:14) Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kugwilitsila nchito mafunso oyenelela, kuti mudziŵe zimene ana anu akuganiza, komanso mmene akumvelela. (Miy. 20:5) Funso losavuta monga lakuti, ‘Kodi vuto lalikulu limene umakumana nalo kusukulu ni liti?’ lingatsogolele ku makambilano opindulitsa.

10. Ni m’njila ina iti imene mungathandizile ana anu kuphunzila za Yehova?

10 Muzisakila mipata yophunzitsa ana anu za Yehova. Muzikamba za Yehova, na zinthu zabwino zimene wakucitilani. (Deut. 6:6, 7; Yes. 63:7) Kucita izi n’kofunika kwambili maka-maka ngati simumaphunzila nthawi zonse na ana anu panyumba. Christine, amene tam’chula kumayambililo anati: “Nthawi yokambilana zauzimu na ana ŵanga inali yocepa kwambili. Conco, mpata ukapezeka n’nali kutengelapo mwayi. Tikapita kokayenda kapena tikakwela bwato, n’nali kukambilana na ana ŵanga zacilengedwe ca Yehova cokongola, komanso zinthu zambili zauzimu. N’taona kuti ana ŵanga asinkhuka, n’nawalimbikitsa kuti aziŵelenga Baibo paokha.” Kuwonjezela apo, muzikamba zabwino zokhudza gulu la Yehova komanso abale na alongo anu. Pewani kupeza zifukwa akulu. Zimene mumakamba zokhudza iwo, zingalimbikitse ana anu kumapempha thandizo kwa iwo kapena ayi.

11. Mogwilizana na Yakobo 3:18, n’cifukwa ciyani kulimbikitsa mtendele panyumba n’kofunika?

11 Muzilimbikitsa mtendele panyumba. Nthawi zonse muzionetsa cikondi kwa mwamuna wanu komanso ana anu. Muzikamba naye mokoma mtima komanso mwaulemu, ndipo phunzitsani ana anu kucita cimodzi-modzi. Mukatelo, cidzakhala cosavuta kwa iwo kuphunzila za Yehova. (Ŵelengani Yakobo 3:18.) Ganizilani citsanzo ici ca Jozsef, amene ni mpainiya wapadela ku Romania. Pamene iye anali kukula, atate ake anali kuletsa iye, amayi ake, na azibale ake kutumikila Yehova. Jozsef anati: “Amayi anali kuyesetsa kukhazikitsa mtendele panyumba. Atate akakwiya kwambili, m’pamenenso amayi anali kukhala wodekha kwambili. Amayi akaona kuti zikutivuta kulemekeza atate na kuwamvela, anali kuŵelenga nafe Aefeso 6:1-3. Kenako, anali kutiuuza makhalidwe abwino a Atate, na kutithandiza kumvetsa cifukwa cake tiyenela kuwakonda. Mwa kutelo, iwo anathandiza kwambili kuti m’banja mwathu mukhale mtendele.”

PHUNZITSANI ANA ANU MWA ZOCITA ZANU

12. Malinga n’kunena kwa 2 Timoteyo 1:5, kodi citsanzo ca Yunike cinamuthandiza bwanji Timoteyo?

12 Ŵelengani 2 Timoteyo 1:5. Yunike anali citsanzo cabwino kwa Timoteyo. Iye ayenela kuti anaphunzitsa mwana wake kuti cikhulupililo ceniceni cimaonekela m’zocita. (Yak. 2:26) Mosakaikila, Timoteyo anaona kuti amayi ake anali kucita zinthu mosonkhezeledwa na cikondi cawo cacikulu pa Yehova. Anaonanso kuti amayi ake anali acimwemwe cifukwa cotumikila Yehova. Kodi citsanzo ca Yunike cinamulimbikitsa bwanji Timoteyo? Monga anakambila Paulo, Timoteyo anali na cikhulupililo monga ca amayi ake. Izi sizinacitike mwangozi. Anali kuona citsanzo cabwino ca amayi ake, ndipo izi zinamulimbikitsa kutengela citsanzoco. Mofananamo, alongo ambili athandiza a m’banja mwawo kutumikila Yehova “osati ndi mawu.” (1 Pet. 3:1, 2) Inunso mungacite cimodzi-modzi. Motani?

13. N’cifukwa ciyani nakubala ayenela kuika ubale wake na Yehova patsogolo?

13 Muziika ubale wanu na Yehova patsogolo. (Deut. 6:5, 6) Mofanana na anakubala ambili, inunso m’madzimana zambili. Mumadzimana nthawi yanu, ndalama, kugona, komanso zinthu zina kuti musamalile zofunikila zakuthupi za ana anu. Koma simuyenela kutangwanika kwambili kusamalila zofunikilazo, cakuti n’kusoŵa nthawi yolimbitsa ubale wanu na Yehova. Muzipatula nthawi yopemphela panokha, yoŵelenga Baibo, komanso yosonkhana. Mukatelo, mudzakhala olimba kuuzimu, komanso mudzakhala citsanzo cabwino ku banja lanu ndiponso kwa anthu ena.

14-15. Kodi mwaphunzila ciyani pa citsanzo ca Leanne, Maria, komanso João?

14 Ganizilani zitsanzo zocepa izi za acicepele amene anaphunzila kukonda Yehova na kum’khulupilila cifukwa coona citsanzo ca amayi awo. Leanne, mwana wa Christine, anati: “Tinali kuphunzila mwakabisila. Amayi sanali kuphonya misonkhano. Citsanzo cawo na cikhulupililo cawo, zinatithandiza kukhala na cikhulupililo colimba. Tinadziŵa kuti ici cinali coonadi tisanayambe n’komwe kupezeka ku misonkhano.”

15 Maria, amene atate ake nthawi zina anali kulanga banja lonse likapita ku misonkhano anati: “Amayi ni mlongo wolimba mtima kwambili. Nili mwana, nthawi zina n’nali kukana kucita zina zake poopa zimene ena angakambe. Koma poona kulimba mtima kwawo, komanso kuika kwawo Yehova patsogolo nthawi zonse, kunanithandiza kugonjetsa mantha oopa anthu.” João, amene atate ake anali kuletsa kuti banja lawo lisamakambilane zauzimu pa nyumba, anati: “Mwina cinanifika pa mtima kwambili n’cakuti amayi anali okonzeka kutaya ciliconse, kupatulapo cikondi cawo pa Yehova, n’colinga cakuti akondweletse atate.”

16. Kodi ena angacite ciyani poona citsanzo cabwino ca amayi?

16 Inu anakubala, muzikumbukila kuti citsanzo canu cingalimbikitse ena. Motani? Ganizilani mmene citsanzo ca Yunike cinakhudzila mtumwi Paulo. Iye anazindikila kuti cikhulupililo ca Timoteyo copanda cinyengo, “cinayamba kukhazikika mwa . . . Yunike.” (2 Tim. 1:5) Ni liti pamene Paulo anaona cikhulupililo ca Yunike koyamba? N’kutheka kuti panali pa ulendo wake woyamba waumishonale. Iye anakumana na Loisi na Yunike ku Lusitara, ndipo ayenela kuti ndiye anawathandiza kukhala Akhristu. (Mac. 14:4-18) Ganizilani izi: Pamene Paulo analembela Timoteyo patapita zaka ngati 15, iye anali akali kukumbukilabe nchito za cikhulupililo za Yunike, ndipo anati citsanzo cake n’cofunika kutengela. N’zacidziŵikile kuti citsanzo cake cinalimbikitsa kwambili Paulo, komanso mwina ngakhale Akhristu ena oyambilila. Ngati mukulela nokha ana kapena ngati mnzanu wa m’cikwati si Mboni, dziŵani kuti citsanzo canu ca cikhulupililo cimalimbikitsa ena.

Kuthandiza mwana kupita patsogolo kuuzimu kumatenga nthawi. Koma musagwe mphwayi (Onani ndime 17)

17. Kodi muyenela kucita ciyani ngati mwana wanu sakulabadila zimene mukum’phunzitsa?

17 Bwanji ngati mwaona kuti ana anu sakulabadila zimene mukuwaphunzitsa? Kumbukilani kuti kuphunzitsa mwana kumatenga nthawi. Malinga n’zimene tikuona pa cithunzipo, tikabyala mbewu, nthawi zina tingakaikile ngati mbewuyo idzakula na kubala zipatso. Ngakhale sitingadziŵiletu motsimikiza kuti mtengo udzabaladi zipatso, timapitiliza kuuthilila kuti ukule bwino. (Maliko 4:26-29) Mofananamo, pokhala nakubala, nthawi zina mungakaikile ngati mukuwafika pa mtima ana anu. Simungadziŵiletu zisankho zimene ana anu adzapanga. Koma mukapitiliza kucita zotheka kuti muwaphunzitse, mudzawapatsa mpata wabwino kwambili wakuti akule kuuzimu.—Miy. 22:6.

DALILANI THANDIZO LA YEHOVA

18. Kodi Yehova angawathandize bwanji ana anu kukula kuuzimu?

18 Kuyambila kale-kale, Yehova wakhala akuthandiza acicepele ambili kukhala mabwenzi ake. (Sal. 22:9, 10) Iye angathandizenso ana anu kukula kuuzimu, ngati n’zimene iwo akufuna. (1 Akor. 3:6, 7) Ngakhale kuti ana anu sakutumikila Yehova na mtima wonse, iye adzapitilizabe kuwayang’anila mwacikondi. (Sal. 11:4) Iwo akaonetsa kuti ali na “maganizo abwino,” iye ni wokonzeka kuwathandiza kuti akhale mabwenzi ake. (Mac. 13:48; 2 Mbiri 16:9) Angakuthandizeni kukamba zoyenela pa nthawi imene ana anu akufunikila kumva zimenezo. (Miy. 15:23) Kapena angalimbikitse m’bale kapena mlongo mu mpingo mwanu kuwaonetsa cidwi. Ngakhale ana anu atakula, Yehova adzawathandiza kukumbukila zimene munawaphunzitsa ali acicepele. (Yoh. 14:26) Mukapitiliza kuphunzitsa ana anu mwa mawu na citsanzo canu, Yehova adzakufupani.

19. N’cifukwa ciyani simuyenela kukaikila kuti Yehova adzakuyanjani?

19 Yehova amakukondani, osati kwenikweni cifukwa ca zisankho zimene ana anu amapanga. Iye amakukondani maka-maka cifukwa inunso mumam’konda. Ngati mukulela nokha ana, Yehova analonjeza kuti adzakhala Atate wa ana anu komanso Mtetezi wanu. (Sal. 68:5) Simungakakamize ana anu kusankha kutumikila Yehova. Koma mukapitiliza kudalila thandizo lake na kuyesetsa kucita zimene mungathe, iye adzakuyanjani.

NYIMBO 134 Ana ni Mphatso Zimene Mulungu Amaikiza kwa Makolo

a Nkhani ino ifotokoza mmene anakubala amene ni Akhristu angapindulile na citsanzo ca Yunike, mayi ake a Timoteyo, ndiponso mmene angathandizile ana awo kudziŵa Yehova na kum’konda.

b Maina ena asinthidwa.

c Mwacitsanzo, onani phunzilo 50 m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, komanso nkhani yakuti, “Njira Zopangira Kulambira kwa Pabanja Kapena Kuphunzira Baibulo Patokha,” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2011, masa. 6-7.