Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 18

Mmene Mungadziikile Zolinga Zauzimu na Kuzikwanilitsa

Mmene Mungadziikile Zolinga Zauzimu na Kuzikwanilitsa

“Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Dzipeleke pa zinthu zimenezi kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo.”—1 TIM. 4:15.

NYIMBO 84 Kudzipeleka na Mtima Wonse

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi tingadziikile zolinga zauzimu ziti?

 POKHALA Akhristu oona, timam’konda ngako Yehova. Timafuna kum’patsa zabwino koposa. Koma kuti ticite zimenezo, tiyenela kudziikila zolinga zauzimu, monga kukulitsa makhalidwe acikhristu, kuphunzila maluso othandiza, komanso kupeza mipata yotumikila ena. b

2. N’cifukwa ciyani tiyenela kudziikila zolinga zauzimu na kuyesetsa kuzikwanilitsa?

2 N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala ofunitsitsa kupita patsogolo kuuzimu? Cifukwa cacikulu n’cakuti timafuna kukondweletsa Atate wathu wacikondi wakumwamba. Yehova amakondwela akaona kuti tikuseŵenzetsa maluso athu mokwanila pom’tumikila. Cina, timafuna kupita patsogolo kuti tizithandiza kwambili abale na alongo athu. (1 Ates. 4:9, 10) Kaya takhala m’coonadi kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tisaleke kupitabe patsogolo kuuzimu. Tiyeni tione mmene tingacitile zimenezi.

3. Malinga na 1 Timoteyo 4:12-16, kodi mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteyo kucita ciyani?

3 Pamene mtumwi Paulo analembela Timoteyo kalata yoyamba, Timoteyo anali kale mkulu wacidziŵitso. Ngakhale n’conco, Paulo anamulimbikitsa kupitabe patsogolo kuuzimu. (Ŵelengani 1 Timoteyo 4:12-16.) Mukaganizila mawu a Paulo, mudzaona kuti iye anali kufuna kuti Timoteyo apite patsogolo m’mbali ziŵili izi: Yoyamba, kukulitsa makhalidwe acikhristu monga cikondi, cikhulupililo, na khalidwe loyela. Yaciŵili, kunola luso lake la kuŵelenga pamaso pa anthu, kulimbikitsa ena, komanso kuphunzitsa. Pamene tikuganizila citsanzo ca Timoteyo, tiyeni tikambilane mmene kudziikila zolinga zimene tingakwanilitse, kungatithandizile kupita patsogolo kuuzimu. Tikambilanenso mmene tingawonjezele utumiki wathu.

KULITSANI MAKHALIDWE ACIKHRISTU

4. Malinga n’kunena kwa Afilipi 2:19-22, n’ciyani cinapangitsa Timoteyo kukhala wofunika kwambili kwa Yehova?

4 N’ciyani cinapangitsa Timoteyo kukhala mtumiki wofunika kwambili kwa Yehova? Ni makhalidwe ake acikhristu osililika. (Ŵelengani Afilipi 2:19-22.) Malinga na zimene Paulo anakamba ponena za Timoteyo, tingathe kuona kuti iye anali wodzicepetsa, wokhulupilika, wakhama, komanso wodalilika. Iye anali kuwakonda abale ake, ndipo anali kusamala kwambili za iwo. Pa cifukwa cimeneci, Paulo anali kum’konda ngako Timoteyo, ndipo sanazengeleze kum’patsa mautumiki ovuta pom’dalila. (1 Akor. 4:17) Mofananamo, Yehova adzatikonda tikamakulitsa makhalidwe amene iye amakonda, ndipo tidzakhala dalitso lalikulu mu mpingo.—Sal. 25:9; 138:6.

Onani khalidwe lacikhristu limene mufuna kulikulitsa (Onani ndime 5-6)

5. (a) Kodi mungadziikile bwanji colinga cokulitsa khalidwe lacikhristu? (b) Malinga na cithunzici, kodi mlongo wacitsikana akucita ciyani pofuna kukwanilitsa colinga cake cocitila ena cifundo?

5 Onani khalidwe limene mufuna kulikulitsa. Pemphelani na kuganizila mbali ya umunthu wanu imene muyenela kuwongolela. Ndiyeno, onani khalidwe limodzi limene mufuna kuwongolela. Mwacitsanzo, kodi mungadziikile colinga cakuti muzionetsa kwambili cifundo, kapena kukulitsa mzimu wothandiza alambili anzanu? Kodi mufuna kukulitsa khalidwe lobweletsa mtendele kapena kukhululukila ena? Mungacite bwino kupempha mnzanu wapamtima kuti akuuzeni mbali zimene mufunika kuwongolela.—Miy. 27:6.

6. Kodi mungacite ciyani kuti mukwanilitse colinga canu cokulitsa khalidwe lina lake?

6 Yesetsani kukwanilitsa colinga canu. Mungacite bwanji zimenezi? Njila imodzi ni kuŵelenga mozama za khalidwe limene mufuna kukulitsa. Tinene kuti mufuna kuti muzikhululukila ena kwambili. Mungayambe mwa kuŵelenga na kusinkhasinkha zitsanzo za m’Baibo za anthu amene anakhululukila ena na mtima wonse, komanso aja amene sanakhululuke. Ganizilani citsanzo ca Yesu. Iye anali kukhululuka na mtima wonse. (Luka 7:47, 48) Analinso kunyalanyaza zolakwa za ena, na kuona zabwino mwa iwo. Mosiyana na iye, Afarisi anali ‘kuona ena onse ngati opanda pake.’ (Luka 18:9) Pambuyo poganizila zitsanzo zimenezi dzifunseni kuti: ‘Kodi nimaona ciyani mwa ena? Kodi nimayang’ana pa makhalidwe awo ati?’ Ngati cimakuvutani kukhululukila wina, yesani kulemba makhalidwe ake onse abwino. Kenako, dzifunseni kuti: Kodi Yesu amamuona bwanji munthuyu? Kodi angamukhululukile?’ Kucita izi kudzatithandiza kuwongolela maganizo athu. Poyamba, tingayesetse kukhululukila amene anatikhumudwitsa, koma movutikila. Koma tikalimbikila kucita zimenezo, m’kupita kwa nthawi tidzakhala ofunitsitsa kukhululuka.

PHUNZILANI MALUSO OTHANDIZA

Dzipelekeni kuti muphunzile mosamalila Nyumba yanu ya Ufumu (Onani ndim 7) e

7. Malinga na Miyambo 22:29, ni m’njila zina ziti zimene Yehova amaseŵenzetsela anchito aluso?

7 Colinga cina cimene mungadziikile ni kuphunzila maluso. Ganizilani kuculuka kwa anthu amene akufunika kuti amange nyumba za Beteli, Mabwalo a Misonkhano, na Nyumba za Ufumu. Ambili mwa anthu amenewa, amaphunzila maluso akamagwila nchito na abale na alongo amene ni amisili pa nchito zomanga. Malinga na cithunzi, abale na alongo akuphunzila maluso owathandiza kusamalila Mabwalo a Misonkhano na Nyumba za Ufumu. Mwa njila zimenezi komanso njila zina, Yehova Mulungu, “Mfumu yamuyaya,” na Yesu Khristu, “Mfumu ya . . . mafumu,” akukwanilitsa zinthu zambili kupitila mwa anchito aluso amenewo. (1 Tim. 1:17; 6:15; ŵelengani Miyambo 22:29.) Timafuna kugwila nchito molimbika poseŵenzetsa maluso athu kuti tilemekeze Yehova, osati kudzifunila ulemelelo.—Yoh. 8:54.

8. Kodi mungacite ciyani kuti mudziikile colinga cophunzila maluso?

8 Sankhani luso limene mufuna kuphunzila. Kodi mufuna kuphunzila luso liti? Funsilani kwa akulu mu mpingo mwanu kapena woyang’anila dela za luso limene aona kuti mungaphunzile. Mwacitsanzo, ngati iwo anena kuti muyenela kukulitsa luso lokamba nkhani komanso la kuphunzitsa, apempheni kuti akuuzeni mwacindunji mbali imene mufunika kugwililapo nchito. Kenako, yesetsani kuti muwongolele. Kodi mungacite bwanji zimenezi?

9. Kodi mungacite ciyani kuti mukwanilitse colinga canu conola luso la kuphunzitsa?

9 Yesetsani kukwanilitsa colinga canu. Tiyelekeze kuti mufuna kunola luso lanu la kuphunzitsa. Mungaŵelenge mosamala malangizo a m’bulosha yakuti Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa. Mukapatsidwa mbali ya ophunzila pa msonkhano wa mkati mwa mlungu, pemphani m’bale waluso kuti akumvetseleni pamene muyeseza nkhani yanu, n’colinga coti akuuzeni mbali zofunika kuwongolela. Muzikonzekela kukali nthawi kuti anthu aone kuti mumacita khama, komanso kuti ndinu odalilika.—Miy. 21:5; 2 Akor. 8:22.

10. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene tingapitile patsogolo pa luso limene tifuna kukulitsa.

10 Bwanji ngati cimakuvutani kukulitsa luso lina lake? Musataye mtima. M’bale wina dzina lake Garry, anali kulephela kuŵelenga bwino. Iye amakumbukila mmene anacitila manyazi atayesa kuŵelenga pa misonkhano ya mpingo. Koma anapitiliza kunola luso lake. Iye anati cifukwa ca maphunzilo amene analandila, tsopano amakwanitsa kukamba bwino nkhani pa misonkhano ya mpingo, yadela, komanso yacigawo.

11. Mofanana na Timoteyo, n’ciyani cidzatithandiza kusenza maudindo owonjezela?

11 Kodi Timoteyo anakhala mlankhuli wabwino kapenanso mphunzitsi waluso? Baibo siikamba. Koma codziŵika n’cakuti anafika pomacita bwino kwambili mu utumiki wake, potsatila malangizo a Paulo. (2 Tim. 3:10) Mofananamo, tikakulitsa maluso athu, tidzakwanitsa kusenza maudindo ena owonjezela.

MUZIFUNA-FUNA MIPATA YOTUMIKILA ENA

12. Kodi mwapindula bwanji na mautumiki a ena?

12 Tonsefe timapindula na mautumiki a ena. Mwacitsanzo, tikakhala m’cipatala, timayamikila ngako akulu a m’Makomiti Okambilana na Azacipatala kapena a M’tumagulu Toyendela Odwala akabwela kudzationa. Tikakumana na vuto lothetsa nzelu, timayamikila kwambili akulu acikondi akamapatula nthawi kuti atimvetsele na kutilimbikitsa. Tikafuna wopita naye kuphunzilo la Baibo, timayamikila ngati mpainiya waluso wadzipeleka kupita nafe, na kupelekapo malingalilo othandiza. Abale na alongo onsewa amakondwela kutithandiza. Nafenso tingakhale acimwemwe tikadzipeleka kutumikila abale athu. Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) Ngati mufuna kuwonjezela utumiki wanu mwa njila zimenezi kapena m’njila zina, n’ciyani cingakuthandizeni kukwanilitsa zolinga zanu?

13. Podziikila colinga ca inu mwini, kodi muyenela kukumbukila ciyani?

13 Pewani kudziikila zolinga zacisawawa. Mwacitsanzo, mungaganize kuti, ‘Nifuna kucita zambili mu mpingo.’ Koma cingakhale covuta kudziŵa mmene mungakwanilitsile zolingazo, komanso ngati mwazikwanilitsa. Conco, dziikileni colinga codziŵika bwino. Ndipo mungalembe colingaco na mmene mudzacikwanilitsila.

14. N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala okonzeka kusintha tikadziikila zolinga?

14 Cina, tizikhala okonzeka kusintha tikadziikila zolinga. Cifukwa ciyani? Cifukwa tilibe mphamvu yoletsa mikhalidwe pa umoyo kusintha. Ganizilani izi: Mtumwi Paulo anathandiza kukhazikitsa mpingo watsopano mu mzinda wa Atesalonika. Ndipo mosakaikila, colinga cake cinali cakuti akhalebe mu mzindawo pofuna kuthandiza Akhristu atsopano. Koma adani ake anam’kakamiza kucoka mu mzindawo. (Mac. 17:1-5, 10) Paulo akanaumililabe kukhala kumeneko, akanaika miyoyo ya abale ake pa ciopsezo. Mikhalidwe itasintha, iyenso anasintha. Ndipo atacoka sanaleke kuwathandiza abalewo. Patapita nthawi, anatuma Timoteyo kuti akasamalile zosoŵa za kuuzimu za Akhristu atsopano ku Tesalonika. (1 Ates. 3:1-3) Atesalonika anakondwela kwambili poona kuti Timoteyo wadzipeleka kutumikila kumene kunali kufunika thandizo lake.

15. Kodi zakugwa mwadzidzidzi zingatilepheletse kucita ciyani? Fotokozani citsanzo.

15 Tingatengepo phunzilo pa zimene zinacitikila Paulo ku Tesalonika. Tingadziikile colinga cauzimu, koma cifukwa ca zakugwa mwadzidzidzi tingalephele kukwanilitsa colingaco. (Mlal. 9:11) Ngati umu ni mmene zilili kwa imwe, dziikileni colinga cina cimene mungakwanilitse. Izi n’zimene Ted na mkazi wake Hiedi anacita. Cifukwa ca kudwala anacoka pa Beteli. Koma cifukwa cokonda Yehova, iwo anapeza njila zina zowonjezela utumiki wawo. Coyamba, anakhala apainiya a nthawi zonse. M’kupita kwa nthawi, anaikidwa kukhala apainiya apadela, ndipo Ted anamuphunzitsa kukhala woyang’anila dela wogwilizila. Zaka zitasintha kuti munthu atumikilebe monga wadela, iye na mkazi wake anaona kuti sadzapitilizabe kutumikila m’dela cifukwa anali atakula. Olo kuti zinawakhwethemula maganizo, anaona kuti akhoza kutumikilabe Yehova m’njila zina. Ted anati: “Tinaphunzila kuti sitiyenela kusumika maganizo athu pa utumiki umodzi.”

16. Kodi tiphunzilapo ciyani pa Agalatiya 6:4?

16 Kusintha kwa zinthu pa umoyo n’kosapeweka. Conco, tisamakhale na maganizo oona kuti timakhala ofunika kwambili kwa Yehova cifukwa ca mtundu wa utumiki umene tili nawo. Cina, tisamayelekezele utumiki wathu na utumiki wa anthu ŵena. Mlongo Hiedi anati: “Ukamadzilinganiza na anthu ŵena umakhala wopanda cimwemwe.” (Ŵelengani Agalatiya 6:4.) Conco, ni bwino kumayesa kupeza mipata yothandizila ena kutumikila Yehova. c

17. Kodi mungacite ciyani pali pano kuti mukayenelele mautumiki ena patsogolo?

17 Mudzakwanitsa kucita zambili potumikila Yehova mukakhala na umoyo wosalila zambili, komanso mukamapewa nkhongole zosafunikila. Dziikileni zolinga zing’ono-zing’ono zimene zidzakuthandizani kukwanilitsa zolinga zanu zikulu-zikulu. Mwacitsanzo, ngati colinga canu cacikulu ni kukhala mpainiya wa nthawi zonse, bwanji osacitako upainiya wothandiza wopitiliza? Ngati colinga canu ni kukhala mtumiki wothandiza, bwanji osamathela nthawi yoculuka mu ulaliki, komanso kumayendela odwala na okalamba mu mpingo wanu? Zimene mungaphunzile pali pano, zidzatsegula khomo la mautumiki enanso m’tsogolo. Conco, yesetsani kucita zimene mungathe pa utumiki ulionse umene mungapatsidwe.—Aroma 12:11.

Dziikileni colinga cimene muona kuti mungacikwanilitse (Onani ndime 18) f

18. Monga tikuonela pacithunzi, kodi muphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Beverley?

18 Kudziikila zolinga zauzimu na kuzikwanilitsa kulibe msinkhu. Onani citsanzo ici ca mlongo wina wa zaka 75 dzina lake Beverley. Iye anali na matenda aakulu amene anali kumulepheletsa kuyenda. Koma anali kufunitsitsa kutengako mbali mokwanila pa kampeni yoitanila anthu ku Cikumbutso. Conco, anadziikila zolinga. Mlongo Beverley anakondwela ngako atakwanilitsa colinga cake cotengako mbali pa kampeniyo. Khama lake linalimbikitsa ena kukhala okangalika mu ulaliki. Yehova amayamikila utumiki umene abale na alongo okalamba amacita, olo kuti mikhalidwe siwalola kucita zambili.—Sal. 71:17, 18.

19. N’zolinga zauzimu ziti zimene tingadziikile?

19 Dziikileni zolinga zimene muona kuti mungakwanilitse. Kulitsani makhalidwe amene adzapangitsa kuti Yehova akukondeni. Komanso, phunzilani maluso amene angapangitse kuti Mulungu akugwilitsileni nchito kwambili kudzela m’gulu lake. Yesani kupeza mipata yotumikila abale na alongo anu mokwanila. d Monga Timoteyo, Yehova adzakuthandizani kuti ‘anthu onse aone kuti mukupita patsogolo.’—1 Tim. 4:15.

NYIMBO 38 Adzakulimbitsa

a Timoteyo anali mlaliki waluso wa uthenga wabwino. Ngakhale n’conco, mtumwi Paulo anamulimbikitsa kupitabe patsogolo kuuzimu. Cifukwa cotsatila malangizo a Paulo amenewo, iye anacita zambili potumikila Yehova, ndiponso anakhala wothandiza kwambili kwa abale na alongo ake. Mofanana na Timoteyo, kodi mumafunitsitsa kucita zambili potumikila Yehova komanso okhulupilila anzanu? Sitikaikila. Ni zolinga ziti zimene zingakuthandizeni kucita zimenezo? Nanga mungacite ciyani kuti mudziikile zolingazo na kuzikwanilitsa?

b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Zolinga zauzimu, ni zilizonse zimene timayesetsa kucita mwakhama kuti tizikwanilitse, n’colinga cakuti ticite zambili potumikila Yehova na kum’kondweletsa.

c Onani nkhani yakuti “Kutumikila Kumalo Osoŵa,” m’buku la Gulu Lolinganizidwa Kucita Cifunilo ca Yehova, mutu 10, ndime 6-9.

d Onani phunzilo 60 lakuti, “Pitanibe Patsogolo,” m’buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

e MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: M’bale akuphunzitsa alongo aŵili nchito yokonza zinthu zowonongeka, ndipo pambuyo pake, iwo akuseŵenzetsa maluso amene aphunzila.

f MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo amene sacoka panyumba akuitanila anthu ku Cikumbutso mwa kucita ulaliki wa pafoni.