Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mmene Tingathanilane Nazo Nkhawa

Mmene Tingathanilane Nazo Nkhawa

NKHAWA ili monga cinthu colema kwambili cimene cakhazikidwa pa mtima wathu. (Miy. 12:25) Kodi munayamba mwakhalapo na cinkhawa cokupsinjani na kukuthetsani nzelu? Kodi zimafika poti simungathenso kupilila nkhawa zotelozo? Ngati n’conco, simuli nokha. Ambili a ife tikusamalila odwala, tataikilidwa munthu amene timakonda mu imfa, takumana na matsoka a zacilengedwe, kapena tikukumana na mavuto ena amene angatithetse mphamvu na kutikhwethemula m’maganizo. Nanga tingacite ciyani kuti tithane nazo nkhawa zotelozo? a

Tingaphunzile mocitila nazo nkhawa, mwa kuphunzila citsanzo ca Mfumu Davide. Iye anakumana na mikhalidwe yovuta, ndipo nthawi zina anali kufuna kumupha. (1 Sam. 17:34, 35; 18:10, 11) Kodi Davide analimbana nazo bwanji nkhawa zake? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?

MMENE DAVIDE ANACITILA NAZO NKHAWA ZAKE

Davide anakumana na mayeso angapo pa nthawi imodzi. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinam’citikila pamene anali kuthaŵa Mfumu Sauli, imene inali kufuna kumupha. Davide na asilikali ake atabwelako ku nkhondo, anasokonezeka kupeza kuti adani aba katundu wawo, atentha nyumba zawo, komanso atengela mabanja awo ku ukapolo. Kodi Davide anacita ciyani? “[Iye] ndi anthu amene anali naye anayamba kulila mofuula mpaka kulefuka osathanso kulila.” Cina cinaonjezela nkhawa yake, n’cakuti anthu ake amene anali kuwadalila, anali “kukambilana zom’ponya miyala.” (1 Sam. 30:1-6) Apa Davide anayang’anizana na mavuto atatu akulu-akulu panthawi imodzi: Banja lake linali pa ciwopsezo, anthu ake anali kufuna kumupha, komanso Mfumu Sauli anali akali kumuthamangitsa. Tangoganizilani nkhawa yaikulu imene Davide anali nayo!

Kodi Davide anacita ciyani ataona zimenezo? Nthawi yomweyo, “[iye] anadzilimbitsa mwa Yehova Mulungu wake.” Kodi anacita bwanji zimenezi? Anali na cizolowezi copemphela kwa Yehova kuti amuthandize, na kusinkhasinkha mmene anam’thandizila kumbuyoko. (1 Sam. 17:37; Sal. 18:2, 6) Iye anaona kuti ayenela kufunsila kwa Yehova. Conco, anafunsila kwa Yehova zimene ayenela kucita. Atalandila malangizo kwa Yehova, Davide anawagwilitsila nchito nthawi yomweyo. Izi zinapangitsa kuti Yehova adalitse iye na anthu ake, ndipo iwo analanditsa mabanja awo na katundu wawo kwa adani. (1 Sam. 30:7-9, 18, 19) Kodi mwaziona zinthu zitatu zimene Davide anacita? Iye anapemphela kwa Yehova, anasinkhasinkha mmene anam’thandizila m’mbuyomo, komanso anaseŵenzetsa malangizo a Yehova. Kodi tingatengele bwanji citsanzo cake? Tiyeni tione njila zitatu izi.

TENGELANI CITSANZO CA DAVIDE MUKAKHALA NA NKHAWA

1. Pemphelani. Nthawi zonse tikakhala na nkhawa, tizipempha Yehova kuti atithandize na kutipatsa nzelu. Nthawi zina m’pofunika kucedwamo m’pemphelo kuti tithe kumukhuthulila Mulungu za mu mtima mwathu. Koma nthawi zina tingangopeleka pemphelo lacidule la mumtima, malinga na mikhalidwe. Nthawi zonse tikayang’ana kwa Yehova kuti atithandize, timaonetsa kuti timam’dalila monga anacitila Davide. Iye anati: “Yehova ndiye thanthwe langa, malo anga acitetezo ndiponso Wopeleka cipulumutso kwa ine. Mulungu wanga ndiye thanthwe langa. Ine ndidzathaŵila kwa iye.” (Sal. 18:2) Kodi pemphelo limathandizadi? Mlongo wina dzina lake Kahlia, amene ni mpainiya anati: “Nikapemphela, nimakhala na mtendele wamaganizo. Pemphelo limanithandiza kuona zinthu mmene Yehova amazionela, komanso kumukhulupilila kwambili.” Kukamba zoona, pemphelo ni mphatso yocokela kwa Yehova imene imatithandiza kuthana na nkhawa.

2. Sinkhasinkhani. Mukakumbukila zimene mwapitamo pa umoyo, kodi mungaganizileko mayeso amene munakwanitsa kuwapilila cifukwa ca thandizo la Yehova? Tikaganizila mmene iye anatithandizila, komanso mmene anathandizila atumiki ake kumbuyoko, timakhala na mtendele wamaganizo, ndipo cidalilo cathu mwa iye cimalimbilako. (Sal. 18:17-19) Mkulu wina dzina lake Josua anati: “Nili na mndandanda wa mayankho ku mapemphelo anga. Izi zimanithandiza kukumbukila nthawi pamene n’napempha Yehova cina cake mwacindunji, ndipo iye ananipatsa cinthuco.” Inde, tikamasinkhasinkha mmene Yehova wakhala akutithandizila, timapeza mphamvu yolimbana na nkhawa.

3. Seŵenzetsani malangizo. Tisanasankhe zimene tidzacita, coyamba tiyenela kufufuza m’Mawu a Mulungu mmene muli citsogozo codalilika. (Sal. 19:7, 11) Ambili apeza kuti akafufuza lemba, amafika polimvetsa bwino mmene angaligwilitsile nchito pa umoyo wawo. Mkulu wina dzina lake Jarrod anakamba kuti: “Kufufuza kumanithandiza kumvetsa mbali zonse za lemba, na kuona zimene Yehova afuna kuti nicite. Izi zimanifika pamtima, komanso zimanilimbikitsa kuseŵenzetsa malangizowo.” Tikamafufuza malangizo a Yehova m’Malemba na kuwaseŵenzetsa, tidzakwanitsa kuthana nazo nkhawa zathu.

YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI KUTI MUPAMBANE

Davide anadziŵa kuti, kuti alimbane na nkhawa zake, anafunikila thandizo la Yehova. Iye anayamikila kwambili thandizolo moti analemba kuti: “Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwele khoma. Mulungu woona ndiye amandilimbitsa.” (Sal. 18:29, 32) Tingamaone mavuto athu ngati khoma lalitali. Koma na thandizo la Yehova, tingapilile mavutowo okhala ngati khoma. Zoonadi, tikamapemphela kwa Yehova, kusinkhasinkha zimene wakhala akuticitila, komanso kutsatila malangizo ake, tidzakhala na cidalilo cakuti iye adzatipatsa mphamvu na nzelu zofunikila kuti tipambane polimbana na nkhawa zathu.

a Munthu amene ali na nkhawa yopambanitsa angafunike cithandizo ca adokotala.