Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga
Mkhristu akasudzula mkazi wake popanda maziko a m’Malemba, kapena kuti popanda cifukwa ca m’Malemba, kenako n’kukwatilana na mkazi wina, kodi mpingo uyenela kuuona bwanji ukwati wakalewo komanso watsopanowo?
Ngati mwamuna wasudzula mkazi wake mwa njila imeneyi na kukwatilanso mkazi wina, mpingo uyenela kuona ukwati wakalewo kuti unatha, ndiponso ukwati watsopanowo ayenela kuuona kuti ni wovomelezeka. Kuti timvetse cifukwa cake tafika pa mfundo imeneyi, tiyeni tionenso zimene Yesu anakamba ponena za cisudzulo na kukwatilanso.
Pa Mateyu 19:9, Yesu anafotokoza maziko amodzi okha a m’Malemba amene munthu angathetsele ukwati. Iye anati: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatila wina wacita cigololo, kupatulapo ngati wamusiya cifukwa ca dama.” Pa mawu a Yesu amenewa, tiphunzilapo zinthu ziŵili, (1) cigololo ndico maziko okha a m’Malemba othetsela ukwati mwa cisudzulo, ndipo (2) mwamuna amene wasudzula mkazi wake popanda maziko a m’Malemba amenewa na kukwatilanso mkazi wina, wacita cigololo. a
Kodi Yesu anatanthauza kuti mwamuna amene wacita cigololo na kusudzula mkazi wake, ni womasuka mwa Malemba kukwatilanso? Osati kwenikweni. Pakacitika cigololo, mnzake wa mu ukwati wosalakwayo ali na ufulu wosankha kukhululukila mwamuna wake kapena kum’kana. Ndipo akam’kana, na kukasudzulana kukhoti, onse aŵili amakhala omasuka kukwatilanso.
Kumbali ina, wosalakwayo angafunitsitse kusunga ukwati wawo, kutanthauza kuti ni wokonzeka kukhululukila mwamuna wake. Koma bwanji ngati mwamuna amene wacita cigololo akukana cikhululuko ca mkazi wake, kenako n’kukam’sudzula mkazi wakeyo mwalamulo, kapena kuti kukhoti? Popeza mkaziyo anali wokonzeka kukhululuka kuti asunge ukwati wawo, koma mwamuna wake n’kukana, mwa Malemba mwamunayo si womasuka kuti akwatilenso. Akakwatilabe mkazi wina mosemphana na Malemba, ndiye kuti wacitanso cigololo cina. Zikatelo, akulu adzapanganso komiti yaciweluzo kuti asamalile mlanduwo.—1 Akor. 5:1, 2; 6:9, 10.
Mwamuna amene si womasuka mwa Malemba akakwatilanso, kodi mpingo uyenela kuuona motani ukwati wakale komanso watsopanowo? Kodi ukwati wakalewo ukalipobe mwa Malemba? Kodi mkazi wolakwilidwayo akali nalo danga losankha kukhululukila mwamuna wake wakaleyo kapena kum’kana? Kodi ukwati watsopanowo uyenela kuonedwa kuti ni wacigololo?
Kumbuyoku, mpingo unali kuona ukwati watsopano wotelo kukhala wacigololo malinga ngati wolakwilidwayo ali moyo, sanakwatilenso, komanso sanacite ciwelewele. Komabe, Yesu sanachulepo za wa mu ukwati wolakwilidwa pokamba za cisudzulo na kukwatilanso. M’malo mwake, iye anafotokoza kuti mwamuna amene wasudzula mkazi wake popanda maziko a m’Malemba na kukwatila mkazi wina, ameneyo wacita cigololo. Zikakhala
conco, ndiye kuti cisudzulo limodzi na kukwatilanso, zimene Yesu anaonetsa kuti ndico cigololo comwe, zimathetsa ukwati.“Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatila wina wacita cigololo, kupatulapo ngati wamusiya cifukwa ca dama.”—Mat. 19:9.
Ukwati ukatha cifukwa ca cisudzulo limodzi na kukwatilanso, n’zosathekanso kwa wolakwilidwayo kuti akhululukile mnzakeyo kapena kum’kana. Zikatelo, wosalakwayo wamasuka pa udindo wovuta wopanga cisankho ca kukhululuka kapena kum’kana mnzakeyo. Kuwonjezela apo, mpingo uyenela kuona ukwati watsopanowo kukhala wovomelezeka, kaya wolakwilidwayo amwalile kapena asamwalile, akwatilenso kapena asakwatilenso, acite ciwelewele kapena asacite ciwelewele. b
M’cocitika cimene tayelekezela, mwamuna anacita cigololo ndipo zinawafikitsa ku cisudzulo. Koma bwanji mwamunayo akanakhala kuti sanacite cigololo, koma n’kusudzulabe mkazi wake na kukwatilanso wina? Kapena bwanji ngati mwamunayo akalibe kusudzula mkazi wake sanacite ciwelewele, koma n’kudzacita ciwelewele pambuyo pa cisudzulo, kenako n’kukwatilanso, ngakhale kuti mkazi wake ni wofunitsitsabe kum’khululukila? Pa zitsanzo zonsezi, cisudzulo limodzi na kukwatilanso, zimene ndico cigololo, zimathetsa ukwati. Mwa ici, ukwati watsopanowo umakhala wovomelezeka mwalamulo. Monga inakambila Nsanja ya Olonda ya November 15, 1979 tsamba 32, “iye tsopano waloŵa mu ukwati watsopano. Conco, sangangouthetsa wamba-wamba n’kubwelelananso na mnzake wakale. Ukwati wa poyambawo unatha mwa cisudzulo, cigololo, na kukwatilanso.”
Ngakhale n’conco, kamvedwe katsopano kameneka sikapeputsa kupatulika kwa ukwati kapena kucepetsa chimo la cigololo. Mwamuna amene wasudzula mkazi wake popanda cifukwa ca m’Malemba na kukwatilanso, pamene sali womasuka mwa Malemba kutelo, komiti yaciwelulo idzasamalila mlandu wake wa cigololo. (Ngati mkazi amene wakwatilayo ni Mkhristu, nayenso komiti yaciweluzo idzasamalila mlandu wake wa cigololo.) Ngakhale kuti ukwati watsopanowu suyenela kuonedwa kuti ni wacigololo, mwamunayo sangayenelele utumiki wapadela uliwonse mu mpingo kwa zaka zambili, kufikila atakonzanso mbili yake na kucotselatu citonzo cimene anabweletsa pa iye mwini pa zimene anacitazo. Kuti akulu amuganizile pa utumiki uliwonse, ayenela kuona bwino mmene zinthu zilili kwa mkazi wake wakale amene mwamunayo anam’citila cinyengo, komanso umoyo wa ana amene mwina anangowatayilila.—Mal. 2:14-16.
Poona mavuto aakulu obwela cifukwa ca kusudzulana popanda maziko a m’Malemba na kukwatilanso, Akhristu ayenela kukhalabe anzelu polemekeza ukwati monga cinthu copatulika, mmenenso Yehova amauonela.—Mlal. 5:4, 5; Aheb. 13:4.
a Kungoti mfundoyi imveke mosavuta, tizichula mwamuna pa mbali ya wocita cigololo, ndipo mkazi pa mbali ya wa mu ukwati wosalakwa. Komabe, malinga na Maliko 10:11, 12, Yesu anaonetsa bwino kuti uphungu wake pa nkhani imeneyi ukupita kwa amuna komanso akazi cimodzimodzi.
b Mfundoyi ikusintha kamvedwe kathu kakumbuyoku, kakuti ukwati wotelowo uyenela kuonedwa kuti ni wacigololo kufikila wolakwilidwayo atamwalila, atakwatilanso, kapena atacita ciwelewele.