Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu

Mfundo Yothandiza Pa Kuŵelenga Kwanu

Kodi mumapindula nako kufotokozela vesi la m’Baibo kopezeka mu Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova?

Kufotokozela kumeneku kungakuthandizeni kukumba mozamilapo m’Mawu a Mulungu. Kumaphatikizapo kufotokoza mmene zinthu zinalili pamene nkhaniyo inali kulembedwa, cifukwa cake inalembedwa, amene anawalembela, komanso tanthauzo la liwu kapena mawu ena ake.

Mungaseŵenzetse LAIBULALE YA PA INTANETI na JW Library® kuti muone malifalensi a pa vesi ya m’Baibo mwacindunji opezeka mu Buku Lofufuzila. Mungapeze malifalensi amenewa a Baibo iliyonse imene ikupezeka pa ma laibulale amenewa.

Pamene muŵelenga malifalensiwa, muzionanso madeti ake. Malifalensi atsopano amakhala pamwamba penipeni. M’munsi mwake muli malifalensi akale amene kamvedwe kake kanafotokozedwanso.

  • Malifalensi a mavesi a m’Baibo m’Buku Lofufuzila Nkhani alipo kale pa LAIBULALE YA PA INTANETI.

  • Kuti mupeze malifalensi a mavesi pa JW Library, ikani Buku Lofufuzila Nkhani pa cipangizo canu na kumaicita daunilodi nthawi zonse ikakonzedwanso. Mungacite zimenezi mwa kudiniza pocitila daunilodi pamwamba pa danga lakumanja la caputala ciliconse ca m’Baibo.