Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 16

“Mlongo Wako Adzauka”!

“Mlongo Wako Adzauka”!

‘Yesu anauza Mariya kuti: ‘Mlongo wako adzauka.’’—YOH. 11:23.

NYIMBO 151 Adzaitana

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Kodi wacicepele wina anaonetsa bwanji kuti amakhulupililadi kuti akufa adzauka?

 WACICEPELE wina dzina lake Matthew ali na matenda aakulu. Kaamba ka ici, wacitidwapo maopaleshoni ambili. Ali na zaka 7, iye pamodzi na a m’banja lake anali kuonelela JW Broadcasting®. Cakumapeto kwa pulogilamuyo, iwo anaonelela vidiyo ya nyimbo yoonetsa mmene zidzakhalile panthawi ya ciukitso, kulandilanso okondedwa amene anamwalila. b Pambuyo pa pulogilamuyo, Matthew anapita kwa makolo ake na kuwagwila manja. Kenako anawauza kuti: “Amama, atate, mwaona? olo nife nidzauka paciukitso. Munganiyembekezele, osada nkhawa.” Makolowo ayenela kuti anakondwela kwambili kudziŵa kuti mwana wawo ali na cikhulupililo camphamvu kuti akufa adzauka.

2-3. N’cifukwa ciyani kumaganizila lonjezo la m’Baibo la kuuka kwa akufa n’kwabwino?

2 Tonsefe tingacite bwino nthawi na nthawi kumaganizila lonjezo la m’Baibo la kuuka kwa akufa. (Yoh. 5:28, 29) Cifukwa ninji? Cifukwa sitidziŵa pamene tidzadwala mwakayakaya, kapena kutaikilidwa munthu amene timam’konda mu imfa. (Mlal. 9:11; Yak. 4:13, 14) Ciyembekezo cathu ca kuuka cingatithandize kupilila mavuto otelo. (1 Ates. 4:13) Malemba amatitsimikizila kuti Atate wathu wakumwamba amatidziŵa bwino ndipo amatikonda kwambili. (Luka 12:7) Pa cifukwa cimeneci, iye adzatha kutilenganso na umunthu wathu, komanso zonse zimene ubongo wathu unasunga. Cifukwa cotikonda kwambili, Yehova watipatsa mwayi wodzakhala na moyo kwamuyaya. Ndipo ngati tingafe, iye adzatiukitsa!

3 M’nkhani ino, coyamba tikambilane cifukwa cake tingakhulupililedi lonjezo la kuuka kwa akufa. Kenako, tikambilane nkhani ya m’Baibo yolimbitsa cikhulupililo. M’nkhaniyo muli mawu akuti, “mlongo wako adzauka,” amene ni mawu a pa lemba la mutu wa nkhani yathu. (Yoh. 11:23) Cothela, tikambilane zimene tingacite kuti tizikhulupilila kwambili kuti akufa adzauka.

CIFUKWA CAKE TINGAKHULUPILILEDI LONJEZO LAKUTI AKUFA ADZAUKA

4. Kuti tikhulupilile lonjezo, tiyenelanso kukhulupilila ciyani? Fotokozani citsanzo.

4 Kuti tikhulupilile lonjezo, tiyenela kukhulupililanso kuti wolonjezayo ali na cifuno komanso mphamvu zokwanilitsila lonjezolo. Tiyelekeze kuti nyumba yanu yawonongeka na cimphepo camkuntho. Mnzanu akukulonjezani kuti, ‘Nidzakuthandiza kumanganso nyumba yako.’ Akulankhula moona mtima ndithu, ndipo inunso mwakhulupilila kuti akufunadi kukuthandizani. Ngati mnzanuyo ni katswili pa nchitoyo, ndipo zipangizo zofunikila ali nazo, mudzakhulupililadi kuti adzakuthandizani. Nanga bwanji za lonjezo la Mulungu lodzaukitsa akufa? Kodi iye alidi na cifuno komanso mphamvu zokwanilitsila lonjezolo?

5-6. N’cifukwa ciyani tili otsimikiza kuti Yehova ali na cifuno coukitsa akufa?

5 Kodi Yehova alidi na cifuno coukitsa akufa? Indedi. Iye anauzila olemba Baibo ambili kulemba lonjezo lake lakuti kutsogoloku adzaukitsa akufa. (Yes. 26:19; Hos. 13:14; Chiv. 20:11-13) Ndipo Yehova akalonjeza, nthawi zonse amakwanilitsa lonjezo lake. (Yos. 23:14) Yehova ni wofunitsitsa kuukitsa akufa. N’cifukwa ciyani tikutelo?

6 Ganizilani mawu a Yobu. Iye anali wotsimikiza kuti ngakhale atafa, Yehova adzalakalaka kumuonanso. (Yobu 14:14, 15) Yehova amalakalakanso kuukitsa alambili ake onse amene anamwalila. Amafunitsitsa kudzawaukitsa kuti akakhale na moyo wathanzi komanso wacimwemwe. Nanga bwanji za mabiliyoni amene anamwalila asanakhale na mwayi wophunzila coonadi cokhudza Yehova? Mulungu wathu wacikondi amafuna kuwaukitsa nawonso. (Mac. 24:15) Amafuna kuti akawapatse mwayi wokhala mabwenzi ake, komanso kuti akakhale na moyo kwamuyaya padziko lapansi. (Yoh. 3:16) N’zoonekelatu kuti Yehova alidi na cifuno codzaukitsa akufa.

7-8. N’cifukwa ninji tiyenela kukhala otsimikiza kuti Yehova ali na mphamvu zoukitsa akufa?

7 Kodi Yehova alinso na mphamvu zoukitsa akufa? Mosapeneka konse! Iye ni ‘Wamphamvuzonse.’ (Chiv. 1:8) Conco, ali na mphamvu zacikwanekwane zogonjetsa mdani aliyense kuphatikizapo imfa. (1 Akor. 15:26) Kudziŵa zimenezi kumatilimbikitsa na kutitonthoza. Ganizilani zinacitikila mlongo Emma Arnold. Panthawi ya Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse, iye na banja lake anakumana na mavuto aakulu amene anayesa cikhulupililo cawo. Potonthoza mwana wake wamkazi za okondedwa awo amene anafa m’ndende zacibalo za Nazi, mlongo Emma anati: “Ngati imfa ingapitilize kusunga anthufe mu ukapolo wake, ndiye kuti ingakhale yamphamvu kuposa Mulungu, si conco?” Mfundo ni yakuti palibe ciliconse camphamvu kuposa Yehova! Mulungu wamphamvuzonse amene analenga moyo, akhozanso kuubwezeletsa kwa amene anamwalila.

8 Cina cimene timadziŵila kuti Mulungu akhoza kuukitsa akufa n’cakuti iye amakumbukila cina ciliconse. Amachula dzina la nyenyenyezi iliyonse. (Yes. 40:26) Conco, amakumbukilanso amene anamwalila. (Yobu 14:13; Luka 20:37, 38) Angakumbukile mosavuta ngakhale zinthu zing’ono-zing’ono zokhudza amene iye adzawaukitsa, monga maonekedwe na umunthu wawo, zinawacitikila mu umoyo, komanso zimene zinali m’maganizo mwawo.

9. N’cifukwa ninji mumakhulupilila lonjezo la Yehova lakuti akufa adzauka?

9 Mwacionekele, tingalikhulupilile lonjezo la Yehova lakuti kutsogolo akufa adzauka, cifukwa tidziŵa kuti ali na cifuno komanso mphamvu zotha kukwanilitsa lonjezolo. Cifukwa cina cokhulupilila lonjezo la Mulungu la ciukitso n’cakuti Yehova kumbuyoku anaukitsapo anthu ena. M’nthawi za anthu a m’Baibo, Mulungu anapatsa Yesu komanso amuna ena mphamvu zoukitsa akufa. Tsopano tiyeni tikambilane ciukitso ca mu Yohane caputala 11, cimodzi mwa ziukitso zimene Yesu anacita.

BWENZI LOKONDEKA LA YESU LIMWALILA

10. N’ciyani cinacitika Yesu akulalikila kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano, nanga anacita ciyani? (Yohane 11:1-3)

10 Ŵelengani Yohane 11:1-3. Ganizilani zinacitika m’mudzi wa Betaniya cakumapeto kwa caka ca 32 C.E. M’mudziwo munali mabwenzi apamtima a Yesu—Lazaro, komanso alongo ake aŵili, Mariya na Marita. (Luka 10:38-42) Koma Lazaro atadwala, alongo akewo anada nkhawa. Zitatelo, iwo anatumiza uthenga wa matenda kwa Yesu. Panthawiyo, iye anali kutsidya kwa mtsinje wa Yorodano, pamtunda woyenda pansi masiku aŵili kucokela ku Betaniya. (Yoh. 10:40) N’zacisoni kuti wopeleka uthengayo atatsala pang’ono kufika kwa Yesu, Lazaro anamwalila. Ngakhale kuti Yesu anadziŵa kuti bwenzi lake lamwalila, anakhalabe kumene anali kwa masiku enanso aŵili. Pambuyo pake m’pamene anapanga ulendo wopita ku Betaniya. Conco Yesu podzafika ku Betaniya, n’kuti patapita masiku anayi cimwalileni Lazaro. Yesu anacita cina cake cimene cinapindulila mabwenzi ake, comwenso cinatamanditsa Mulungu.—Yoh. 11:4, 6, 11, 17.

11. Kodi pa cocitikaci tiphunzilapo ciyani ponena za mabwenzi?

11 Pankhaniyi tiphunzilapo mmene mabwenzi ayenela kucitila. Ganizilani izi: Uthenga umene Mariya na Marita anatumiza kwa Yesu sunali wom’pempha kuti apite ku Betaniya ayi. Anangotumiza uthenga wa matenda wakuti bwenzi lake likudwala. (Yoh. 11:3) Lazaro atamwalila, Yesu akanatha kumuukitsa ali kutali komweko. Koma m’malo mwake, Yesu anapita ku Betaniya kukakhala na mabwenzi ake, Mariya na Marita. Kodi muli na bwenzi limene lingakuthandizeni mosacita kupempha? Ngati muli nalo, mumalidalila kuti lidzakuthandizani mukadzakumana na “mavuto.” (Miy. 17:17) Mofanana na Yesu, tiyeni tikhale bwenzi lotelo kwa ena! Tsopano tibwelele ku nkhani ija, tione zotsatila zinacitika.

12. Kodi Yesu anam’lonjeza ciyani Marita? Nanga n’cifukwa ciyani analikhulupilila lonjezo limenelo? (Yohane 11:23-26)

12 Ŵelengani Yohane 11:23-26. Marita atadziŵa kuti Yesu watsala pang’ono kufika ku Betaniya, anathamanga kukam’cingamila. Atakumana naye anamuuza kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalila.” (Yoh. 11:21) Zoonadi, Yesu akanam’cilitsa Lazaro. Koma Yesu afuna kucita cina cake capadela coposa pamenepo. Iye anamulonjeza kuti: “Mlongo wako adzauka.” Anapatsanso Marita cifukwa cina cokhulupilila lonjezo lake. Iye anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” Inde, Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zoukitsa akufa. Kumbuyoko, iye anaukitsa kamtsikana komwe kanamwalila cakumene. Ndipo panthawi inanso, anaukitsa mnyamata amene mwacionekele anali atamwalila tsiku lomwelo. (Luka 7:11-15; 8:49-55) Koma kodi akanakwanitsanso kuukitsa munthu amene anagona m’manda masiku anayi, ndipo thupi lake litayamba kuwola?

“LAZARO, TULUKA!”

Yesu anawamvela cifundo kwambili mabwenzi ake amene anafeledwa (Onani ndime 13-14)

13. Malinga na Yohane 11:32-35, kodi Yesu anacita ciyani ataona Mariya na anthu ena akulila? (Onaninso cithunzi.)

13 Ŵelengani Yohane 11:32-35. Ganizilani zinacitika pambuyo pake. Mariya, mlongo wa Lazaro, anapita kukakumana na Yesu. Iye anabweleza zimene m’bale wake ananena kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalila.” Iye pamodzi na anthu ena amene anali naye, anali na cisoni cacikulu. Yesu atawaona na kuwamva akulila, anagwidwa cisoni kwambili. Powamvela cifundo mabwenzi ake, anagwetsa misozi. Anamvetsa mmene cimaŵaŵila munthu akatayikilidwa wokondedwa wake mu imfa. Iye anafunitsitsa kucotsapo cimene cinawapangitsa kugwetsa misozi!

14. Tingaphunzile ciyani zokhudza Yehova pa zimene Yesu anacita ataona Mariya akulila?

14 Zimene Yesu anacita ataona Mariya akulila, zitiphunzitsa kuti Yehova ni Mulungu wacifundo cacikulu. Tikutelo cifukwa ciyani? Monga tinaonela m’nkhani yapita, Yesu amatengela kwambili maganizo a Atate wake na mmene amamvela. (Yoh. 12:45) Yesu analila cifukwa anawamvela cifundo kwambili mabwenzi ake amene anafeledwa. Conco, timadziŵa kuti Yehova nayenso amatimvela cifundo kwambili tikafeledwa. (Sal. 56:8) Izi zimakupangitsani kufuna kumuyandikila Mulungu wathu wacifundo, si telo kodi?

Yesu anaonetsa kuti ali na mphamvu zoukitsa akufa (Onani ndime 15-16)

15. Mogwilizana na Yohane 11:41-44, n’ciyani cinacitika kumanda a Lazaro? (Onaninso cithunzi.)

15 Ŵelengani Yohane 11:41-44. Yesu atafika pamanda a Lazaro, anapempha kuti cimwala cimene anatsekela pamandapo cicotsedwe. Koma Marita anakamba kuti pofika nthawiyo thupi la Lazaro liyenela kuti linayamba kununkha. Yesu poyankha anati: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupilila udzaona ulemelelo wa Mulungu?” (Yoh. 11:39, 40) Kenako Yesu anayang’ana kumwamba na kupemphela pamaso pa onse. Anacita izi kuti apeleke ulemelelo wonse kwa Yehova pa zotsatila zimene anacita. Ndiyeno Yesu anafuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Pomwepo Lazaro anatuluka m’mandamo! Yesu anacita zomwe ena anaona kuti n’zosatheka.

16. Kodi nkhani ya mu Yohane caputala 11 imalimbitsa bwanji cikhulupililo cathu cakuti akufa adzauka?

16 Nkhani yopezeka mu Yohane caputala 11 imalimbitsa cikhulupililo cathu pa ciyembekezo cakuti akufa adzauka. Motani? Kumbukilani lonjezo la Yesu kwa Marita lakuti: “Mlongo wako adzauka.” (Yoh. 11:23) Mofanana na Atate wake, Yesu ali na cifuno komanso mphamvu zokwanilitsa lonjezolo. Kukhetsa kwake misozi kunaonetsa kuti amafunitsitsa kudzacotsapo imfa na cisoni cimene timakhala naco. Lazaro atatuluka m’manda, Yesu anapelekanso umboni wina wakuti ali na mphamvu zoukitsa akufa. Komanso, ganizilani zimene Yesu anakumbutsa Marita. Anati: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupilila udzaona ulemelelo wa Mulungu?” (Yoh. 11:40) Tili na zifukwa zomveka zokhulupilila kuti lonjezo la Mulungu la ciukitso lidzakwanilitsidwadi. Koma tingacite ciyani kuti ciyembekezoco cikhale ceniceni kwa ife?

KUTI CIYEMBEKEZO CA CIUKITSO CIKHALE CENICENI KWA IFE

17. Tizikumbukila ciyani tikamaŵelenga ziukitso za m’Baibo?

17 Ŵelengani na kusinkhasinkha ziukitso zakalelo. Baibo imafotokoza ziukitso 8 za anthu amene anaukitsidwa padziko lapansi. c Bwanji osakonza zakuti mukaŵelenge nkhani zimenezi mofatsa? Pamene mukutelo, kumbukilani kuti anthuwo anali ngati ife tomwe—amuna, akazi, komanso ana. Ganizilani mmene cocitika ciliconse cionetsela kuti Mulungu ali na cifuno komanso mphamvu zoukitsa akufa. Koposa zonse, sinkhasinkhani za kuuka kwa Yesu kumene n’kofunika kwambili. Kumbukilani kuti mboni zoona na maso zofika m’mahandiledi zinatsimikizila za kuuka kwa Yesu. Kudziŵa izi kumayala maziko olimba a cikhulupililo cathu.—1 Akor. 15:3-6, 20-22.

18. Mungacite ciyani kuti muzigwilitsa nchito bwino nyimbo zathu zokamba za ciyembekezo ca kuuka? (Onaninso mawu am’munsi.)

18 Gwilitsani nchito bwino “nyimbo zauzimu” zokamba za ciyembekezo ca kuuka. d (Aef. 5:19) Nyimbo zimenezi zimatithandiza kuona ciyembekezo ca ciukitso kukhala ceniceni, komanso zimalimbitsa cikhulupililo cathu pa ciyembekezo cabwino kwambili cimeneci. Muzizimvetsela na kuziyeseza kuti muziziimba bwino. Kambilanani mawu a nyimbozo pa kulambila kwanu kwa pabanja. Loŵezani mawu a nyimbozo na kuwasunga mumtima na m’maganizo. Ndiyeno mukadzakumana na mayeso oika moyo wanu pa ciwopsezo, kapena kutaikidwa wokondedwa wanu mu imfa, mzimu wa Yehova udzakuthandizani kukumbukila nyimbozi. Nyimbozi zidzakutonthozani na kukupatsani mphamvu.

19. Kodi tingayelekeze zotani m’maganizo zokhudza kuuka? (Onani kabokosi kakuti “ Kodi Mudzawafunsa Ciyani?”)

19 Muziyelekeza m’maganizo mwanu. Yehova anatipatsa luso lotha kuyelekeza kuti tili m’dziko latsopano. Mlongo wina anati: “Nimapatula nthawi yoculuka kuyelekeza kuti nili m’dziko lapatsono, moti zimakhala ngati nikumva kafungo kabwino ka maluŵa amene akuphuka m’Paradaiso.” Ganizilani mmene zidzakhalile kukambilana na amuna komanso akazi acikhulupililo ochulidwa m’Baibo. Kodi ndani amene mufunitsitsa kudzakambilana naye? Nanga mudzam’funsa mafunso otani? Ganizilaninso mmene zidzakhalile kuonananso na okondedwa anu amene anamwalila. Ganizilani makambilano oyamba amene mudzakhale nawo, kukumbatilana, komanso kugwetsa misozi yacisangalalo.

20. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciyani?

20 Timaliyamikila cotani nanga lonjezo la Yehova la ciukitso! Ndife otsimikiza kuti lonjezoli lidzakwanilitsidwa ndithu, cifukwa Yehova ali na cifuno komanso mphamvu zolikwanilitsa. Tiyeni tipitilizebe kulimbitsa cikhulupililo cathu m’ciyembekezo cabwino kwambili cimeneci. Mwa kucita izi, tidzamuyandikila kwambili Mulungu, amene mwanjila ina akulonjeza aliyense wa ife kuti, ‘Okondedwa anu adzauka!’

NYIMBO 147 Lonjezo la Moyo Wamuyaya

a Ngati munthu amene mumam’konda anamwalila, mosakayikila lonjezo lakuti akufa adzauka limakutonthozani kwambili. Koma kodi mungawafotokozele motani ena cifukwa cake mumakhulupilila lonjezolo? Nanga mungalimbitse bwanji cikhulupililo canu pa ciyembekezo cakuti akufa adzauka? Colinga ca nkhani ino ni kuthandiza tonsefe kulimbitsa cikhulupililo cathu pa ciyembekezo ca kuuka kwa akufa.

c Onani bokosi lakuti “Anthu 8 Otchulidwa M’baibulo Amene Anaukitsidwa,” mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2015 tsa. 4.

d Onani nyimbo zotsatilazi m’buku lakuti ‘Imbani Mokweza ndi Mosangalala’ kwa Yehova:Yelekeza Uli M’dziko Latsopano” (Nyimbo 139), “Yang’ana pa Mphoto” (Nyimbo 144), “Adzaitana” (Nyimbo 151). Onaninso pa jw.org nyimbo zopekedwa koyamba zakuti “Dziko Latsopano Ili Pafupi Kwambili,” “Dziko Latsopano Likubwelalo,” komanso yakuti “Bwelani M’dzaone.”