Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 19

Tingalimbitse Motani Cikhulupililo Cathu pa Lonjezo la Yehova la Dziko Latsopano?

Tingalimbitse Motani Cikhulupililo Cathu pa Lonjezo la Yehova la Dziko Latsopano?

“Kodi [Yehova] ananenapo kanthu koma osacita?”—NUM. 23:19.

NYIMBO 142 Tigwilitsitse Ciyembekezo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1-2. Tiyenela kucita ciyani poyembekezela dziko latsopano?

 TIMALIYAMIKILA kwambili lonjezo la Yehova lakuti adzacotsa dongosolo loipali, n’kubweletsa dziko latsopano lolungama. (2 Pet. 3:13) Ngakhale kuti sitidziŵa nthawi yeniyeni pamene lonjezoli lidzakwanilitsidwa, zocitika padzikoli zikuonetsa kuti kwangotsala nthawi yocepa.—Mat. 24:32-34, 36; Mac. 1:7.

2 Koma pakali pano, tonsefe tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu pa lonjezo limeneli, kaya takhala nthawi yaitali motani m’coonadi. Cifukwa ciyani? Cifukwa ngakhale cikhulupililo colimba cikhoza kufooka. N’cifukwa cake mtumwi Paulo anati kusoŵa cikhulupililo ni “chimo limene limatikola mosavuta.” (Aheb. 12:1) Kuti cikhulupililo cathu cisafooke, nthawi zonse tizisanthula maumboni amene aonetsa kuti dziko latsopano lili pafupi kwambili.—Aheb. 11:1.

3. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?

3 M’nkhani ino, tikambilane njila zitatu zotithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu pa lonjezo la Yehova la dziko latsopano: (1) kusinkhasinkha za dipo, (2) kuganizila mphamvu za Yehova, komanso (3) kucita zinthu zauzimu. Kenaka, tikambilanenso mmene uthenga wa Yehova kwa Habakuku umalimbitsila cikhulupililo cathu masiku ano. Koma coyamba, tiyeni tikambilane mikhalidwe imene tingakumane nayo palipano, yofuna cikhulupililo colimba pa lonjezo la dziko latsopano.

MIKHALIDWE YOFUNA CIKHULUPILILO COLIMBA

4. Ni zisankho ziti zimene zimafuna cikhulupililo colimba?

4 Tsiku lililonse, timapanga zisankho zofuna cikhulupililo colimba. Mwacitsanzo, timapanga zisankho pa nkhani ya mabwenzi, zosangalatsa, maphunzilo, ukwati, kukhala na ŵana, komanso nchito yakuthupi. Tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zosankha zanga zimaonetsa kuti nimakhulupililadi kuti dongosolo lino n’losakhalitsa, ndipo posacedwapa lidzaloŵedwa m’malo na dziko latsopano la Mulungu? Kapena kodi nimacita zinthu monga anthu amene amaona kuti moyo uno ndiwo wokha umene ulipo?’ (Mat. 6:19, 20; Luka 12:16-21) Tikalimbitsa cikhulupililo cathu kuti dziko latsopano layandikila, tidzapanga zisankho zanzelu.

5-6. N’cifukwa ciyani timafunika cikhulupililo colimba pa mayeso? Fotokozani citsanzo.

5 Cina cimene cimafuna cikhulupililo colimba ni mayeso. Tingakumane na cizunzo, matenda okhalitsa, kapena mavuto ena amene angatilefule. Poyamba, tingakwanitse kuwapilila mavutowo. Koma mavuto ngati awa samatha msanga. Conco, tifunikila cikhulupililo colimba kuti tiwapilile, na kupitiliza kutumikila Yehova mwacimwemwe.—Aroma 12:12; 1 Pet. 1:6, 7.

6 Tikakhala pa mayeso, tingaone kuti dziko latsopano la Yehova silidzabwela. Kodi izi zitanthauza kuti cikhulupililo cathu n’cofooka? Osati kwenikweni. Ganizilani citsanzo ici. Ngati mvula yamvumbi yakhala ikugwa kwa milungu ingapo, zingaoneke monga dzuŵa silidzawalanso. Koma mvulayo imasiya kugwa, ndipo dzuŵa limawala. Mofananamo, tikalefuka kwambili, tingaone kuti dziko latsopano silidzabwela. Koma ngati cikhulupililo cathu n’colimba, timadziŵa kuti Mulungu adzakwanilitsa malonjezo ake. (Sal. 94:3, 14, 15; Aheb. 6:17-19) Tikakhala na cidalilo cotelo, tidzapitiliza kuika kulambila Yehova patsogolo.

7. Kodi tiyenela kupewa maganizo otani?

7 Mbali inanso imene imafuna cikhulupililo colimba, ni nchito yolalikila. Anthu ambili amene timalalikila, amaona kuti “uthenga wa bwino” wokamba za dziko latsopano la Mulungu ni nkhambakamwa cabe. (Mat. 24:14; Ezek. 33:32) Sitifuna kuti maganizo amenewa atiyambukile. Kuti tipewe zimenezi, tiyenela kulimbitsa cikhulupililo cathu. Tiyeni lomba tikambilane njila zitatu zotithandiza kucita zimenezi.

MUZISINKHASINKHA ZA DIPO

8-9. Kodi kusinkhasinkha dipo kungalimbitse bwanji cikhulupililo cathu?

8 Njila yoyamba imene tingalimbitsile cikhulupililo cathu, ni kusinkhasinkha za dipo. Dipo limatitsimikizila kuti malonjezo a Mulungu adzakwanitsidwa. Tikamasinkhasinkha mosamala cifukwa cake dipo linapelekedwa, komanso zimene Mulungu anadzimana, timalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti lonjezo la moyo wosatha m’dziko latsopano ndithu lidzakwanilitsidwa. N’cifukwa ciyani tikutelo?

9 Kodi kupeleka dipo kunaloŵetsamo ciyani? Yehova anatuma Mwana wake woyamba kubadwa komanso wokondeka, kuti acoke kumwamba n’kudzabadwa monga munthu wangwilo. Ali padziko lapansi, Yesu anapilila mazunzo a mtundu uliwonse. Ndipo anavutika mpaka kufa imfa yoŵaŵa. Umenewu unali mtengo waukulu cotani nanga umene Yehova analipila! Mulungu wathu wacikondi sakanalola Mwana wake kuvutika mpaka kufa, kuti tingokhala na umoyo wabwinopo palipano kwa nthawi yocepa. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Cifukwa analipila mtengo wokwela kwambili, Yehova adzaonetsetsa kuti lonjezo lake la moyo wamuyaya m’dziko latsopano lakwanilitsidwa.

MUZIGANIZILA MPHAMVU ZA YEHOVA

10. Malinga na Aefeso 3:20, kodi Yehova angathe kucita ciyani?

10 Njila yaciŵili yolimbitsila cikhulupililo cathu, ni kuganizila mphamvu za Yehova. Ali na mphamvu zokwanilitsa zonse zimene amalonjeza. N’zoona kuti zingaoneke zosatheka kukwanilitsa lonjezo la moyo wosatha m’dziko latsopano. Koma nthawi zambili Yehova amalonjeza zinthu zimene anthu sangakwanitse kucita. Ndi iko komwe, iye ni Mulungu Wamphamvuzonse. (Yobu 42:2; Maliko 10:27) Conco, mpake kuti amatilonjeza zinthu zodabwitsa!—Ŵelengani Aefeso 3:20.

11. Fotokozani zitsanzo za malonjezo a Mulungu amene anali kuoneka ngati osatheka. (Onani bokosi lakuti, “ Kukwanilitsidwa kwa Malonjezo Ooneka Ngati Osatheka.”)

11 Onani zina mwa zinthu zooneka ngati zosatheka zimene Yehova analonjeza anthu ake kalelo. Iye anauza Abulahamu na Sara kuti adzakhala na mwana mu ukalamba wawo. (Gen. 17:15-17) Anamuuzanso kuti mbadwa zake zidzapatsidwa dziko la Kanani. Kwa zaka zambili zimene Aisiraeli, amene anali mbadwa za Abulahamu, anali mu ukapolo ku Iguputo, lonjezo limeneli linaoneka ngati losatheka. Koma linakwanilitsidwa. Patapita nthawi, Yehova ananena kuti Elizabeti wacikalambile adzakhala na mwana. Iye anauzanso namwali Mariya kuti adzabeleka Mwana wa Mulungu. Izi zinali kudzakwanilitsa lonjezo limene Yehova anapanga m’munda wa Edeni zaka masauzande kumbuyoko.—Gen. 3:15.

12. Kodi Malemba a Yoswa 23:14 komanso Yesaya 55:10, 11, amatitsimikizila ciyani za mphamvu za Yehova?

12 Tikaona mmene Yehova anakwanilitsila malonjezo ake kumbuyoku, timalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti iye adzakwanilitsanso lonjezo lake la dziko latsopano. (Ŵelengani Yoswa 23:14; Yesaya 55:10, 11.) Izi zimatilimbikitsa kuthandiza ena kuti azindikile kuti dziko latsopano ni lenileni, osati maloto cabe. Ponena za kumwamba kwatsopano na dziko lapansi latsopano, Yehova iye mwini anati: “Mawu awa ndi odalilika ndi oona.”—Chiv. 21:1, 5.

MUZICITA ZAUZIMU NTHAWI ZONSE

MISONKHANO YA MPINGO

Kodi kucita zinthu zauzimu zimenezi kungalimbitse bwanji cikhulupililo canu? (Onani ndime 13)

13. Kodi misonkhano ya mpingo imalimbitsa motani cikhulupililo cathu? Fotokozani.

13 Njila yacitatu imene tingalimbitsile cikhulupililo cathu, ni kukhala okangalika na zinthu zauzimu. Mwacitsanzo, onani mmene timapindulila na misonkhano ya mpingo. Mlongo Anna, amene wacita zosiyana-siyana mu utumiki wanthawi zonse kwa zaka zambili anati: “Misonkhano imanithandiza kukhalabe na cikhulupililo colimba. Ngakhale kuti mlankhuli si mphunzitsi waluso kwenikweni, kapena sachulako mfundo zatsopano, nthawi zambili nimamvapo mfundo zimene zimanithandiza kumvetsa coonadi ca m’Baibo. Ndipo izi zimalimbitsa cikhulupililo canga.” b Mosakayikila, cikhulupililo cathu cimalimbanso tikamva ndemanga za abale na alongo athu pamisonkhano.—Aroma 1:11, 12; 10:17.

ULALIKI WAKUMUNDA

Kodi kucita zinthu zauzimu zimenezi kungalimbitse bwanji cikhulupililo canu? (Onani ndime 14)

14. Kodi ulaliki umalimbitsa bwanji cikhulupililo cathu?

14 Timalimbitsanso cikhulupililo cathu tikamatengamo mbali mu utumiki wakumunda. (Aheb. 10:23) Mlongo Barbara, amene watumikila Yehova kwa zaka zopitilila 70 anati: “Naona kuti nchito yolalikila imanilimbitsa cikhulupililo nthawi zonse. Nikamalankhula kwambili za malonjezo a Yehova okondweletsa, cikhulupililo canga cimalimbilako.”

PHUNZILO LA MUNTHU MWINI

Kodi kucita zinthu zauzimu zimenezi kungalimbitse bwanji cikhulupililo canu? (Onani ndime 15)

15. Kodi phunzilo la munthu mwini limalimbitsa bwanji cikhulupililo ca munthu? (Onaninso zithunzi.)

15 Cinanso cimene cimalimbitsa cikhulupililo cathu, ni phunzilo la munthu mwini. Mlongo wina dzina lake Susan, amaona kuti kucita phunzilo la munthu mwini n’kothandiza. Iye anati: “Pa Sondo, nimakonzekela Phunzilo la Nsanja ya Mlonda ya mlungu wotsatila. Pa Mande na Ciŵili, nimakonzekela msonkhano wa mkati mwa mlungu. Ndipo masiku otsalawo nimacita phunzilo la ine mwini.” Cifukwa cocita zauzimu zimenezi, mlongo Susan amalimbitsa cikhulupililo cake. Mlongo Irene, amene watumikila ku likulu kwa zaka zambili, waona kuti kuphunzila maulosi a m’Baibo kumalimbitsa cikhulupililo cake. Iye anati, “Nimacita cidwi kwambili kuona kuti maulosi onse a m’Baibo amakwanilitsika, kuphatikizapo mbali zake zing’ono-zing’ono.” c

“ADZAKWANILITSIDWA NDITHU”

16. Kodi zimene Yehova anatsimikizila Habakuku n’zothandiza motani kwa ife? (Aheberi 10:36, 37)

16 Atumiki ena a Yehova akhala akuyembekezela mapeto a dzikoli kwa nthawi yaitali. M’kaonedwe kaumunthu, zingaoneke ngati Mulungu akucedwa kukwanilitsa malonjezo ake. Yehova amadziŵa nkhawa za atumiki ake. N’cifukwa cake anatsimikizila mneneli Habakuku kuti: “Masomphenyawa akuyembekezela nthawi yake yoikidwilatu ndipo akuthamangila kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengeleza, uziwayembekezelabe cifukwa adzakwanilitsidwa ndithu. Iwo sadzacedwa.” (Hab. 2:3) Kodi ni Habakuku yekha amene analimbikitsidwa na citsimikizo ca Mulungu cimeneci? Kapena nafenso timalimbikitsidwa na mawu amenewa masiku ano? Mouzilidwa, mtumwi Paulo analunjikitsa mawu amenewo kwa Akhristu amene akuyembekezela dziko latsopano. (Ŵelengani Aheberi 10:36, 37.) Conco, ndife otsimikiza kuti lonjezo la Mulungu lakuti adzatipulumutsa ‘lidzakwanilitsidwa ndithu,’ ngakhale lingaoneke ngati likucedwa.

17. Kodi mlongo wina anauseŵenzetsa motani uphungu wa Yehova kwa Habakuku?

17 Akhristu ambili amatsatila uphungu wa Yehova wakuti akhale ‘oyembekezelabe.’ Ndipo ena acita zimenezi kwa zaka zambili. Mwacitsanzo, mlongo Louise anayamba kutumikila Yehova mu 1939. Iye anati: “Pa nthawiyo, n’nali kuganiza kuti Aramagedo idzabwela nisanamalize maphunzilo akusekondale. Koma zimenezo sizinacitike. M’kupita kwanthawi, n’naona kuti kuŵelenga nkhani za anthu ochulidwa m’Baibo monga Nowa, Abulahamu, Yosefe, komanso ena ambili n’kothandiza. Anthu amenewa anayembekezela kwa nthawi yaitali Yehova asanawafupe. Kukhalabe woyembekezela kwanithandiza ineyo komanso anthu ena kusakayikila kuti dziko latsopano lili pafupi.” Zoonadi, atumiki ambili a Yehova aciyambakale angavomeleze mfundo imeneyi.

18. Kodi kusinkhasinkha zacilengedwe kungalimbitse bwanji cikhulupililo cathu pa dziko latsopano likubwelelalo?

18 N’zoona kuti dziko latsopano lisanafikebe. Koma ganizilani zinthu zina zimene zilipo kale, monga nyenyezi, mitengo, nyama, komanso anthu anzanu. Palibe aliyense amene angakaikile kuti zinthuzi n’zenizeni, ngakhale kuti panthawi inayake kunalibe. Zilipo cifukwa Yehova anazilenga. (Gen. 1:1, 26, 27) Mofananamo, Mulungu wathu analonjeza kuti adzalenga dziko latsopano. Iye adzalikwanilitsadi lonjezo limeneli. Ndipo m’dziko latsopano, anthu adzasangalala na moyo wosatha ali na thanzi langwilo. Pa nthawi yoikika ya Mulungu, dziko latsopano lidzakhaladi lenileni.—Yes. 65:17; Chiv. 21:3, 4.

19. Kodi cikhulupililo canu mungacilimbitse motani?

19 Pakali pano, gwilitsani nchito mpata uliwonse muli nawo kuti mulimbitse cikhulupililo canu. Mungacite zimenezi mwa kukulitsa ciyamikilo canu pa dipo, kuganizila mphamvu za Yehova, komanso kucita zauzimu nthawi zonse. Mukatelo, mungakhale pakati pa anthu amene “mwa cikhulupililo ndi kuleza mtima, akulandila zinthu zimene Mulungu analonjeza monga colowa cawo.”—Aheb. 6:11, 12; Aroma 5:5.

NYIMBO 139 Yelekeza Uli M’dziko Latsopano

a Anthu ambili masiku ano salikhulupilila lonjezo la m’Baibo la dziko latsopano. Iwo amaona kuti ni maloto cabe. Komabe, ndife otsimikiza kuti malonjezo onse a Yehova adzakwanilitsidwa. Ngakhale n’conco, kuti cikhulupililo cathu cikhalebe camoyo, tiyenela kupitiliza kucilimbitsa. Motani? Nkhani ino ifotokoza.

b Maina ena asinthidwa.

c Nkhani zambili za maulosi a m’Baibo, mungazipeze mu Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, pansi pa kamutu kakuti “Maulosi.” Mwacitsanzo, onani nkhani yakuti “Kodi Ndani Amadziŵadi Zamtsogolo?” mu Nsanja ya Mlonda ya May 1,2014.