Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 15

Tiphunzilapo Ciyani pa Zozizwitsa za Yesu?

Tiphunzilapo Ciyani pa Zozizwitsa za Yesu?

“Anayenda-yenda m’dziko, n’kumacita zabwino ndi kucilitsa.”—MAC. 10:38.

NYIMBO 13 Khristu ni Citsanzo Cathu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. Fotokozani cinapangitsa kuti Yesu acite cozizwitsa coyamba.

 GANIZILANI zinacitika kumapeto kwa caka ca 29 C.E, Yesu atangoyamba utumiki wake. Iye na mayi ake Mariya, komanso ena mwa ophunzila ake anaitanidwa kuphwando lacikwati ku Kana, kumudzi wokhala kumpoto kwa mzinda wa Nazareti, kwawo kwa Yesu. Mariya anali kumvana kwambili na banja lakucimuna komanso lakucikazi, ndipo zioneka kuti anali kuthandizila kusamalila obwela ku cikwatiwo. Koma phwando lili mkati, panabuka vuto limene likananyazitsa mabanja onse aŵili, kuphatikizapo ongokwatilanawo—vinyo unatha. b Mwina obwela ku cikwatico anali oculuka kuposa amene anali kuyembekezela. Mwamsanga Mariya anapita kwa mwana wake n’kumuuza kuti: “Vinyo waathela.” (Yoh. 2:1-3) Kodi Yesu anacita ciyani? Anacita cozizwitsa. Anasandutsa madzi kukhala “vinyo wabwino.”—Yoh. 2:9, 10.

2-3. (a) Kodi Yesu anaziseŵenzetsa bwanji mphamvu zake zocita zozizwitsa? (b) Kodi kuŵelenga zozizwitsa za Yesu kungatipindulile motani?

2 Yesu anacita zozizwitsa zina zambili pa utumiki wake. c Anagwilitsa nchito mphamvu zake zocita zozizwitsa pothandiza anthu masauzande. Mwacitsanzo, pa zozizwitsa ziŵili zokha, Yesu anadyetsa amuna 5,000. Ndipo panthawi ina anadyetsanso amuna 4,000. N’kutheka kuti onse amene anadyetsedwa anali anthu oposa 27,000 tikaphatikizapo akazi komanso ana amene analipo. (Mat. 14:15-21; 15:32-38) Pa zocitika zonse ziŵili, Yesu anacilitsanso anthu ambili odwala. (Mat. 14:14; 15:30, 31) Ganizilani mmene makamu a anthuwo anakondwela atacilitsidwa kapena kudyetsedwa na Yesu mozizwitsa!

3 Masiku ano, tingaphunzilepo zambili pa zozizwitsa za Yesu. M’nkhani ino, tikambilane maphunzilo olimbitsa cikhulupililo amene tingatengepo pa zozizwitsa zimenezo. Kenako tikambilane mmene tingatengele citsanzo ca Yesu pa kudzicepetsa na cifundo cimene anaonetsa pocita zozizwitsa.

ZIMENE TIPHUNZILAPO ZOKHUDZA YEHOVA NA YESU

4. Kodi zozizwitsa za Yesu zimatiphunzitsa za ndani?

4 Zozizwitsa za Yesu zimatipatsa maphunzilo olimbitsa cikhulupililo okhudza iye na Atate wake. Ndipo Gwelo lenileni kunacokela mphamvu ya zozizwitsazo, anali Yehova. Machitidwe 10:38 imatiuza kuti: “Mulungu anamudzoza [Yesu] ndi mzimu woyela ndi mphamvu. Ndiponso kuti popeza Mulungu anali naye, anayenda-yenda m’dziko, n’kumacita zabwino ndi kucilitsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.” Komanso kumbukilani kuti zonse zimene Yesu anakamba na kucita, kuphatikizapo zozizwitsa, zinaonetsa bwino maganizo a Atate wake na mmene iwo amamvela. (Yoh. 14:9) Tiyeni tione maphunzilo atatu amene tingatengepo pa zozizwitsa za Yesu.

5. N’ciyani cinalimbikitsa Yesu kucita zozizwitsa? (Mateyu 20:30-34)

5 Coyamba, Yesu na Atate wake amatikonda kwambili. Ali pa dziko lapansi, Yesu anaonetsa kuzama kwa cikondi cake pa anthu. Anatelo mwa kugwilitsa nchito mphamvu zake zocita zozizwitsa pothandiza nazo anthu ovutika. Panthawi ina, amuna aŵili akhungu anam’condolela kuti awathandize. (Ŵelengani Mateyu 20:30-34.) Onani kuti Yesu “atagwidwa ndi cifundo,” anawacilitsa. Palembali, mawu Acigiriki amene anamasulidwa kuti ‘kugwidwa ndi cifundo’ amatanthauza kukhudzika mtima kwambili. Cifundo cacikuluci, cimenenso ni njila ina yoonetsela cikondi, cinapangitsa Yesu kudyetsa anjala komanso kucilitsa munthu wolemala. (Mat. 15:32; Maliko 1:41) Tingakhale na cidalilo kuti Yehova, Mulungu “wacifundo cacikulu,” na Mwana wake amatikonda ngako, ndipo zimawapweteka mtima akamationa tikuvutika. (Luka 1:78; 1 Pet. 5:7) Iwo ayenela kuti ni ofunitsitsa kwambili kucotsa mavuto onse amene amavutitsa mtundu wa anthu!

6. Kodi Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zocita ciyani?

6 Caciŵili, Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zocotsapo mavuto onse a anthu. Mwa zozizwitsa zake, Yesu anaonetsa kuti ali na mphamvu zocotsapo mavuto onse omwe pa ife tokha sitingathe kuwacotsapo. Mwacitsanzo, iye ali na mphamvu zotimasula ku zonse zotibweletsela mavuto—ucimo, matenda, na imfa. (Mat. 9:1-6; Aroma 5:12, 18, 19) Zozizwitsa zake zinaonetsa kuti angathe kucilitsa “matenda amtundu uliwonse,” ngakhale kuukitsa akufa. (Mat. 4:23; Yoh. 11:43, 44) Cina, ali na mphamvu zolamulila mphepo zoopsa komanso kumasula anthu ku mizimu yoipa. (Maliko 4:37-39; Luka 8:2) N’zolimbikitsa zedi kudziŵa kuti Yehova anapatsa Mwana wake mphamvu zimenezi!

7-8. (a) Kodi zozizwitsa za Yesu zimatitsimikizila ciyani? (b) Kodi n’cozizwitsa citi cimene muyembekezela mwacidwi m’dziko latsopano?

7 Cacitatu, tingakhale na cidalilo conse kuti Ufumu wa Mulungu udzabweletsadi madalitso kutsogoloku. Zozizwitsa zimene Yesu anacita monga munthu padziko lapansi, zitiphunzitsa kuti kutsogoloku adzacita zambili monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Tangoganizilani mmene umoyo udzakhalile pansi pa ulamulilo wa Khristu. Tidzakhala na thanzi langwilo, cifukwa adzacotsapo matenda alionse na ulemali ulionse, zimene zimavutitsa anthu. (Yes. 33:24; 35:5, 6; Chiv. 21:3, 4) Sikudzakhalanso njala kapena kuvutitsidwa na matsoka azacilengedwe. (Yes. 25:6; Maliko 4:41) Tidzakondwela kwambili kulandila okondedwa athu kucokela “m’manda acikumbutso.” (Yoh. 5:28, 29) Kodi n’cozizwitsa citi cimene muyembekezela mwacidwi m’dziko latsopano?

8 Pocita zozizwitsa, Yesu anaonetsa kwambili kudzicepetsa na cifundo—makhalidwe amene tiyenela kutengela. Tiyeni tikambilane zitsanzo ziŵili. Tiyamba na cocitika ca phwando la ku Kana.

KUTENGAPO PHUNZILO PA KUDZICEPETSA KWAKE

9. Kodi Yesu anacita ciyani paphwando lacikwati? (Yohane 2:6-10)

9 Ŵelengani Yohane 2:6-10. Vinyo atatha ku phwando lacikwati, kodi unali udindo wa Yesu kucitapo kanthu? Ayi. Panalibe ulosi ulionse wonena kuti Yesu adzapanga vinyo mozizwitsa. Koma tangoganizani mmene mungamvelele ngati zakumwa zozizilitsa kukhosi zatha pa cikwati canu. Yesu ayenela kuti anamvela cifundo banjalo, maka-maka mkwati na mkwatibwi, ndipo sanafune kuti iwo acite manyazi. Conco monga takambila kale kuciyambi, iye anacita cozizwitsa. Anasandutsa madzi kukhala vinyo wabwino kwambili wokwana malita ngati 390. Mwina iye anapanga vinyo wambili conco kuti wotsala akam’gwilitse nchito m’tsogolo, kapena kumugulitsa kumene kuti akathandize ongokwatilanawo kupeza ndalama. Banja latsopanolo liyenela kuti linayamikila kwambili thandizolo!

ITengelani citsanzo ca Yesu mwa kupewa kudzitama pa zimene mwakwanitsa kucita (Onani ndime 10-11) e

10. Kodi mu Yohane caputala 2 muli mfundo zina ziti zofunika? (Onaninso cithunzi.)

10 Ganizilani mfundo zina zofunika zopezeka mu Yohane caputala 2. Kodi mwaona kuti si Yesu anadzaza mbiyazo na madzi? Posafuna kuti anthu aike maganizo pa iye, anauza amene anali kutumikila kuti adzaze mbiyazo na madzi. (vesi 6 na 7) Ndipo Yesu atasandutsa madziwo kukhala vinyo, sanapeleke yekha vinyo wina kwa woyang’anila phwandolo kuti akaulaŵe. M’malo mwake anauza otumikilawo kucita zimenezo. (vesi 8) Yesu sanatenge cikho ca vinyo n’kucikweza m’mwamba kutsogolo kwa alendo obwela kucikwati, n’kukamba modzitama kuti, ‘Uyu ndiye vinyo amene ine napanga, mulaŵeni!’

11. Tiphunzilapo ciyani pa cozizwitsa ca Yesu?

11 Kodi tiphunzilapo ciyani pa cozizwitsa ca Yesu cosandutsa madzi kukhala vinyo? Kukhala odzicepetsa. Yesu sanadzitame pa cozizwitsaco ayi. Ndipo sanadzitamepo pa zonse zimene anali kucita. M’malo mwake, nthawi zonse anali kudzicepetsa mwa kupeleka ulemu na ulemelelo kwa Atate wake. (Yoh. 5:19, 30; 8:28) Tikatengela citsanzo ca Yesu mwa kukhala odzicepetsa, sitidzadzitama pa zilizonse tingakwanitse kucita. Pa zilizonse zimene takwanitsa kucita mu utumiki wathu kwa Yehova, tisadzitame ayi, koma tidzitamandile kuti Mulungu wathu ni wabwino, ndipo tili na mwayi wom’tumikila. (Yer. 9:23, 24) Tizim’patsa ulemelelo wake. Ndi iko komwe, n’ciyani cabwino cimene tingakwanitse kucita popanda thandizo la Yehova?—1 Akor. 1:26-31.

12. Ni njila inanso iti imene tingatengele citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa? Fotokozani citsanzo.

12 Onani njila ina imene tingatengele citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa. Ganizilani cocitika ici: Mkulu wathela nthawi yoculuka pothandiza mtumiki wothandiza wacinyamata kukonzekela nkhani yake yoyamba ya anthu onse. Cotulukapo cake n’cakuti m’bale wacinyamatayo wakamba nkhani yolimbikitsa, ndipo mpingo wonse wapindula nayo. Pambuyo pa msonkhanowo, wina wafikila mkulu uja n’kumuuza kuti: ‘M’bale Uje wakamba nkhani yotentha kwambili, si conco?’ Kodi mkuluyo ayenela kukamba kuti: ‘Inde, koma n’nacita kuthelapo nthawi yoculuka kum’thandiza kuti aikambe bwino conco’? Kapena ayenela kudzicepetsa mwa kukamba kuti: ‘Inde, waikambadi bwino. Namunyadila kwambili’? Ngati tikhala odzicepetsa, sitidzafuna kudzipezela ulemu pa zabwino zimene tacitila ena. Timakhutila kudziŵa kuti Yehova amaona komanso amayamikila zimene timacita. (Yelekezelani na Mateyu 6:2-4; Aheb. 13:16) Ndithudi, timakondweletsa Yehova tikamatengela Yesu poonetsa kudzicepetsa.—1 Pet. 5:6.

KUTENGAPO PHUNZILO PA CIFUNDO CAKE

13. Kodi Yesu anaona ciyani atayandikila mzinda wa Naini? Nanga anacitapo ciyani? (Luka 7:11-15)

13 Ŵelengani Luka 7:11-15. Ganizilani zinacitika mu 31 C.E. Yesu anapita ku Galileya ku mzinda wa Naini. Mzindawo unali pafupi na Sunemu, kumene mneneli Elisa anaukitsa mwana wa mkazi wina zaka pafupi-fupi 900 kumbuyoko. (2 Maf. 4:32-37) Yesu atayandikila pacipata ca mzindawo, anaona anthu akutuluka mumzindawo atanyamula malilo. Malilo amenewa anali oŵaŵa kwambili, cifukwa mwana mmodzi yekhayo wa mkazi wamasiye anamwalila. Koma mayi wacisoniyo sanali yekha, khamu lalikulu la anthu la mumzindawo linali naye. Yesu anaimitsa gululo na kucitila mayi wolilayo cinacake capadela—anaukitsa mwana wake! Aka kanali koyamba Yesu kuukitsa munthu, pa ziukitso zitatu zimene anacita zochulidwa mwacindunji m’mabuku a Uthenga Wabwino.

Tengelani citsanzo ca Yesu mwa kuonetsa cifundo ofedwa (Onani ndime 14-16)

14. Kodi mu Luka caputala 2 muli mfundo zina ziti zofunika? (Onaninso cithunzi.)

14 Ganizilani mfundo zina zofunika zopezeka mu Luka caputala 7. Kodi mwaona kuti Yesu ‘ataona’ mayi wacisoniyo, ‘anamumvela cifundo’? (Vesi 13) Conco, zimene iye anaona—mwina kulila kwa mayiyo akuyenda moyang’ana mtembo wa mwana wake wamwamuna—zinapangitsa Yesu kumumvela cifundo. Yesu sanangomumvela cifundo mayiyo, koma anaonetsanso cifundoco mwa zimene anacita. Anakamba na mayiyo, ndipo mosakayikila analankhula naye mokoma mtima pomuuza kuti: “Tontholani mayi.” Kenako anacitapo kanthu pofuna kuthandiza mayiyo. Anaukitsa mwana wamwamunayo na ‘kum’peleka kwa mayi ake.’—Vesi 14, na 15.

15. Tiphunzilapo ciyani pa cozizwitsa ca Yesu?

15 Kodi tingaphunzile ciyani pa cozizwitsa ca Yesu coukitsa mwana wa mkazi wamasiye? Tiphunzilapo kuti tiyenela kuonetsa cifundo kwa acisoni ca imfa. Tidziŵa kuti sitingaukitse akufa monga anacitila Yesu. Koma mofanana na Yesu, tingaonetse ofedwa cifundo pokhala chelu kuona mmene tingawathandizile. Tingawaonetse cifundo cathu mwa kukamba kapena kucita zimene tingathe kuti tiwathandize na kuwatonthoza. d (Miy. 17:17; 2 Akor. 1:3, 4; 1 Pet. 3:8) Ngakhale mawu ocepa kapena kucita zinthu zina zazing’ono, kungathandize kwambili.

16. Monga tikuonela pa cithunzi, kodi muphunzilapo ciyani pa cocitika ca mayi wina amene anatayikilidwa mwana wake mu imfa?

16 Ganizilani cocitika ici. Zaka zingapo kumbuyoku, nyimbo ikuimbidwa pa msonkhano wa mpingo, mlongo anaona mayi wina akulila. Nyimboyo inali kukamba za kuuka kwa akufa, ndipo mayiyo caposacedwa anali atatayikilidwa mwana wake wamkazi mu imfa. Mlongoyo atazindikila zimenezo, anapita panali mayiyo n’kumukumbatila, ndipo anaimbila pamodzi nyimbo yonseyo. Patapita nthawi mayiyo anati: “N’naona kuti abale na alongo anga amanikonda.” Anayamikila kwambili kuti anapita ku msonkhanowo. Iye anati: “Ku Nyumba ya Ufumu n’kumene kuli thandizo.” Ndife otsimikiza kuti Yehova amaona, ndiponso amayamikila ngakhale zocepa zimene timacita, poonetsa cifundo kwa ofedwa ‘osweka mtima.’—Sal. 34:18.

PULOGILAMU YOPINDULITSA YOPHUNZILA BAIBO

17. Kodi taphunzilanji m’nkhani ino?

17 Mungapindule kwambili kuphunzila zozizwitsa za Yesu zochulidwa m’mabuku a Uthenga Wabwino. Zimatiphunzitsa kuti Yehova na Yesu amatikonda ngako, komanso kuti Yesu ali na mphamvu zothetsa mavuto onse a anthu. Zimatithandizanso kukhala na cikhulupililo conse kuti Ufumu wa Mulungu udzabweletsadi madalitso olonjezedwawo posacedwa. Pomwe tiŵelenga zocitikazo, tingasinkhesinkhe mmene tingatengele makhalidwe a Yesu. Bwanji osakonza pulogilamu ya phunzilo la inu mwini, kapena ya Kulambila kwa pa Banja kuti muphunzile zozizwitsa zina za Yesu? Pezani maphunzilo amene mutengapo, ndiyeno uzankoni ena zimene mwaphunzilazo. Tangoganizilani makambilano olimbikitsa amene mungakhale nawo!—Aroma 1:11, 12.

18. M’nkhani yotsatila tidzakambilana ciyani?

18 Kumapeto kwa utumiki wake Yesu anaukitsanso munthu. Ciukitsoco cinali cothela pa ziukitso zake zitatu zochulidwa m’Baibo. Koma ciukitsoco cinali cosiyanako, cifukwa amene anamwalila anali bwenzi lake la pamtima, ndipo anamuukitsa pambuyo pokhala m’manda masiku anayi. Kodi tiphunzilapo ciyani pa cozizwitsa cimeneco? Nanga tingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu pa ciyembekezo ca kuuka kwa akufa? Nkhani yotsatila idzayankha mafunso amenewa.

NYIMBO 20 Munapeleka Mwana Wanu Wokondeka

a Yesu anakhalitsa bata cimphepo camphamvu, kucilitsa odwala, na kuukitsa akufa. N’zokondweletsa kwambili kuŵelenga zokhudza zozizwitsa zimene Yesu anacita! Zozizwitsazo zinalembedwa m’Baibo kuti zitiphunzitse osati kungotisangalatsa. M’nkhani ino, tikambilane zina mwa zozizwitsazo, kuti tilimbitse cikhulupililo cathu pa zimene tiphunzilapo zokhudza Yehova na Yesu. Ndipo pa zozizwitsazo, tidzazindikilanso makhalidwe aumulungu amene tiyenela kukhala nawo.

b Katswili wina wa Baibo anati: “M’nthawi za anthu ochulidwa m’Baibo, kuceleza unali udindo wapadela. Ndipo munthu akaitanila ena kunyumba kwake sanali kungofunika kukonza cakudya cokwanila basi. Kuti munthu aonetse kuceleza kweni-kweni, maka-maka pa cikwati, anali kufunika kukonza cakudya ca mwana alilenji.”

c Mabuku a Uthenga Wabwino, amafotokoza zocitika zokhudza zozizwitsa za Yesu zoposa 30. Kuwonjezela apo, nthawi zina zozizwitsa zingapo zimaphatikizidwa m’cocitika cimodzi. Mwacitsanzo, panthawi ina “anthu onse a mumzinda” wina wake anapita kwa iye ndipo “anacilitsa ambili amene anali kudwala.”—Maliko 1:32-34.

d Mungapeze malingalilo ena okuthandizani kudziŵa zimene mungakambe kapena kucita kuti mutonthoze acisoni kaamba ka imfa, mu Nsanja ya Olonda ya Chichewa ya November 1, 2010. Nkhani yake ni yakuti “Muzitonthoza Anthu Amene Aferedwa, Ngati Mmene Yesu Anachitira.”

e MAWU OFOTOKOZELA CITHUNZI: Yesu waimilila capatali, pamene mkwati na mkwatibwi komanso obwela kucikwati akusangalala na vinyo.