Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YOPHUNZILA 18

Tizilimbikitsana pa Misonkhano ya Mpingo

Tizilimbikitsana pa Misonkhano ya Mpingo

“Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane.”—AHEB. 10:24, 25.

NYIMBO 88 N’dziŵitseni Njila Zanu

ZIMENE TIKAMBILANE a

1. N’cifukwa ciyani timapelekapo ndemanga pa misonkhano?

 N’CIFUKWA ciyani timapezeka kumisonkhano ya mpingo? Cifukwa cacikulu ni kutamanda Yehova. (Sal. 26:12; 111:1) Timapezekanso kumisonkhano kuti tilimbikitsane m’nthawi zino zovuta. (1 Ates. 5:11) Tikakweza dzanja na kupelekapo ndemanga, timakwanilitsa zolinga ziŵili zimenezi.

2. Ni mbali ziti zimene zimatipatsa mwayi woyankhapo pamisonkhano?

2 Mlungu uliwonse, timakhala na mwayi wopelekapo ndemanga pa misonkhano yathu. Mwacitsanzo, timapelekapo ndemanga pa Phunzilo ya Nsanja ya Mlonda kumapeto kwa mlungu. Komanso pa misonkhano ya mkati mwa mlungu, timapelekapo ndemanga pa Kufufuza Cuma Cauzimu, Phunzilo la Baibo la Mpingo, na mbali zina zokambilana.

3. N’ciyani cingatimange pofuna kupelekapo ndemanga? Nanga Aheberi 10:24, 25 ingatithandize bwanji?

3 Tonsefe timafuna kutamanda Yehova, na kulimbikitsa alambili anzathu. Koma pali zinthu zimene zingatimange pofuna kupeleka ndemanga. Tingamadodome, kapena tingamafunitsitse kuyankhapo kangapo, koma sitikupatsidwa mwayi mmene tikufunila. N’ciyani cingatithandize pambali zimenezi? Timapeza yankho m’kalata imene mtumwi Paulo analembela Aheberi. Iye anafotokoza kuti tikasonkhana pamodzi, colinga cathu cizikhala ‘kulimbikitsana.’ (Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.) Tikadziŵa kuti ndemanga yathu idzalimbitsa cikhulupililo ca ena, sitidzadodoma kukweza dzanja kuti tiyankhepo, ngakhale itakhala yaifupi. Ndipo ngati sitinapatsidwe mwayi woyankhapo kangapo, tizikhalabe okondwela kuti ena akhala na mpata wopelekapo ndemanga zawo.—1 Pet. 3:8.

4. Ni mfundo zitatu ziti zimene tikambilane m’nkhani ino?

4 M’nkhani ino, coyamba tikambilane mmene tingalimbikitsilane popeleka ndemanga mumpingo waung’ono. Kenaka, tikambilane mmene tingalimbikitsilane popeleka ndemanga mumpingo waukulu. Ndipo cothela, tikambilane mmene tingakonzele ndemanga zathu kuti zizikhala zolimbikitsadi.

TIZILIMBIKITSANA MUMPINGO WAUNG’ONO

5. Kodi tingalimbikitsane bwanji mumpingo waung’ono?

5 Mumpingo waung’ono kapena kagulu, opelekapo ndemanga amakhala ocepa. Nthawi zina wotsogoza amayembekeza kwa masekondi kuti wina m’gulu akweze dzanja. Msonkhanowo ungaoneke wogwetsa ulesi, ndipo sungakhale wolimbikitsa kwenikweni. Kodi mungacite ciyani? Muzikweza dzanja pafupi-pafupi. Mwakutelo, mungalimbikitse ena kutengako mbali kaŵili-kaŵili.

6-7. Kodi tingacepetse bwanji mantha opelekapo ndemanga?

6 Koma bwanji ngati mumacita mantha kupelekapo ndemanga? Ambili amamva conco. Komabe, kuti muzilimbikitsa kwambili abale na alongo anu, pezani njila zimene zingakuthandizeni kucepetsa mantha opelekapo ndemanga. Kodi mungacite bwanji zimenezo?

7 Mungapindule kwambili kuŵelenganso mfundo zothandiza m’magazini a Nsanja ya Mlonda aposacedwa. b Mwacitsanzo, muzikonzekela bwino. (Miy. 21:5) Mukaimvetsa bwino nkhani imene mudzaphunzila, cidzakhala cosavuta kukapelekapo ndemanga pamsonkhano. Cina, mayankho anu azikhala aafupi. (Miy. 15:23; 17:27) Yankho lanu likakhala lalifupi simudzadodoma kwambili. Yankho lalifupi, mwina lokhala na ciganizo cimodzi kapena ziŵili, limakhala losavuta kwa abale na alongo kulimvetsa, kupambana yankho lamtatakuya lokhala na mfundo zambili. Mukapeleka ndemanga yaifupi m’mawu anu-anu, zidzaonetsa kuti munakonzekela bwino, komanso kuti munaimvetsa bwino nkhaniyo.

8. Kodi kuyesetsa kwathu Yehova amakuona bwanji?

8 Bwanji ngati mwayesa kutsatila malingalilo amenewa, koma mukucitabe mantha kupelekapo ndemanga kaŵili kapena kuposapo? Dziŵani kuti Yehova amayamikila kwambili kuyesetsa kwanu. (Luka 21: 1-4) Iye satipempha kucita zimene sitingakwanitse. (Afil. 4:5) Conco, dziŵani zimene mungathe kucita, dziikileni colinga cocita zimenezo, ndipo pemphelani kuti mukhale wodekha. Colingaco cingakhale kukapeleka ndemanga imodzi yaifupi.

TIZILIMBIKITSANA MUMPINGO WAUKULU

9. N’cifukwa ninji cingakhale covuta kupelekapo ndemanga mumpingo waukulu?

9 Ngati mumpingo mwanu muli ofalitsa ambili, cingakhalenso covuta kupelekapo ndemanga. Mwina abale na alongo amene amakweza manja kuti apelekepo ndemanga amakhala oculuka, moti nthawi zambili simupatsidwa mwayi wopelekapo ndemanga. Mwacitsanzo, mlongo Danielle amakonda kupelekapo ndemanga pa misonkhano. c Amaona kuti kupeleka ndemanga ni mbali ya kulambila, njila yolimbikitsila ena, komanso yokhomeleza mfundo za coonadi ca m’Baibo mumtima mwake. Koma atasamukila ku mpingo waukulu, analibe mwayi wopeleka ndemanga kaŵili-kaŵili. Ndipo nthawi zina msonkhano unali kuthelamo osapelekapo ndemanga. Iye anati: “N’nakhumudwa kwambili. N’namva monga kuti naphonya mwayi wamtengo wapatali. Izi zikamacitika mobweleza-bweleza, umayamba kudzifunsa ngati wotsogozayo akucitila dala.”

10. Kodi tingawonjezele bwanji mwayi wopelekapo ndemanga?

10 Kodi inunso munamvapo mmene mlongo Danielle anamvela? Ngati n’conco, mungaganize zongoleka kupelekapo ndemanga, n’kumangomvetsela msonkhano. Koma conde musaleke. Kodi muyenela kucita ciyani? Muzikonzekela ndemanga zingapo pa msonkhano uliwonse. Ngati sanakupatseni mwayi wopeleka ndemanga kumayambililo kwa msonkhano, mudzakhalabe na mipata ina yopelekapo ndemanga pamene msonkhanowo ukupitiliza. Mukamakonzekela Nsanja ya Mlonda, muziganizila mmene ndime iliyonse ikugwilizanila na mfundo yaikulu ya nkhaniyo. Mukatelo, mudzakhala na ndemanga zabwino zimene mungapeleke pa phunzilo lonselo. Kuwonjezela apo, mungakonzekele kukapeleka ndemanga pa ndime zokamba pa ziphunzitso zozama za m’Baibo zovuta kuzifotokoza. (1 Akor. 2:10) Cifukwa ciyani? Cifukwa ni anthu ocepa angakweze manja kuti apeleke ndemanga. Nanga bwanji ngati mwayesa kutsatila malingalilo amenewa pa misonkhano ingapo, koma sanakupatsenibe mwayi wopeleka ndemanga? Zikatelo, msonkhano usanayambe muuzeni wotsogoza, ndime imene mwakonzekela kupeleka ndemanga.

11. Kodi Afilipi 2:4 imatilimbikitsa kucita ciyani?

11 Ŵelengani Afilipi 2:4. Mouzilidwa na mzimu woyela, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti aziganizila zofuna za ena. Kodi tingatsatile motani uphungu umenewu pa misonkhano? Mwa kukumbukila kuti nawonso abale na alongo athu amafuna kupelekapo ndemanga.

Monga mmene mumapatsila ena mpata wokambapo mukamaceza, patsani ena mwayi wopelekapo ndemanga pamisonkhano (Onani ndime 12)

12. Kodi njila yabwino koposa yolimbikitsila ena pamisonkhano ni iti? (Onaninso cithunzi.)

12 Ganizilani izi. Mukamaceza na mabwenzi anu, kodi mungamalankhule kwambili moti anzanuwo n’kusoŵa mpata wakuti alankhulepo? Ayi simungatelo. Mumafuna kuti nawonso azilankhulapo. Mofananamo, pamisonkhano tiyenela kusiyilako ena mpata wopelekapo ndemanga. Ndipo njila yabwino koposa yolimbikitsila abale na alongo athu, ni kuwapatsa mpata woonetsa cikhulupililo cawo. (1 Akor. 10:24) Tiyeni tione mmene tingacitile zimenezi.

13. Kodi tingacite ciyani kuti ambili m’gulu azikhala na mpata wopelekapo ndemanga?

13 Coyamba, ndemanga zathu zizikhala zazifupi, kuti ena azikhalanso na mpata wopelekapo ndemanga. Akulu na ofalitsa ena acidziŵitso ayenela kukhala citsanzo. Ngakhale popeleka ndemanga yaifupi, pewani kukamba mfundo zambili. Musacite kukombelatu mfundo zonse m’ndime, moti ena n’kusoŵa ndemanga yopelekapo. Mwacitsanzo, m’ndime ino mwachulidwa mfundo ziŵili—ndemanga zathu zizikhala zazifupi, komanso kupewa kukamba mfundo zambili. Ngati mukhale woyamba kupeleka ndemanga m’ndime ino, bwanji osangopeleka ndemanga pa mfundo imodzi?

Ni panthawi iti pomwe tingakweze dzanja pamsonkhano? (Onani ndime 14) f

14. Ni khalidwe liti lingatithandize kudziŵa kuti tipelekepo kangati ndemanga? (Onaninso cithunzi.)

14 Khalani wozindikila kuona kuti muyankhapo kangati. Tikamakweza dzanja pafupi-pafupi, wotsogoza angamakakamizike kutilata kaŵili-kaŵili, ngakhale pamene ena sanapelekeko ndemanga. Izi zingalefule ena kuti asamakweze manja.—Mlal. 3:7.

15. (a) Ngati sitinapatsidwe mwayi wopelekapo ndemanga, tipewe ciyani? (b) Kodi otsogoza angaonetse bwanji kuti amaganizila aliyense? (Onani bokosi lakuti, “ Ngati Mukutsogoza.”)

15 Ngati ofalitsa ambili akukweza manja, sitingayankhe kaŵili-kaŵili mmene tingafunile. Nthawi zina, wotsogoza sangatilate n’komwe. Zimenezi zingatilefuleko, koma tisakhumudwe.—Mlal. 7:9.

16. Kodi amene apelekapo ndemanga pa msonkhano tingawalimbikitse bwanji?

16 Ngati simukuyankhapo kaŵili-kaŵili mmene mukufunila, mvetselani mwachelu pamene ena akupeleka ndemanga, ndipo ayamikileni pambuyo pa msonkhano. Kuwayamikila kudzawalimbikitsa monga mmene mukanawalimbikitsila na ndemanga zanu. (Miy. 10:21) Kuyamikila ena ni njila inanso yolimbikitsila abale na alongo.

NJILA ZINA ZOLIMBIKITSILANA

17. (a) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukonzekela ndemanga malinga na msinkhu wawo? (b) Monga tinaonela mu vidiyo, ni masitepe anayi ati amene tingatenge pokonzekela ndemanga? (Onaninso mawu am’munsi.)

17 Ni njila zinanso ziti zimene tingalimbikitsilane pa misonkhano? Ngati ndinu kholo, thandizani ana anu kukonzekela ndemanga malinga na msinkhu wawo. (Mat. 21:16) Nthawi zina, timakambilana nkhani zikulu-zikulu monga zokhudza mavuto a m’banja kapena ciyelo ca mpingo. Koma pamakhalabe ndime imodzi kapena ziŵili zimene ana angapelekepo ndemanga. Cina, fotokozelani ana anu kuti si nthawi zonse pomwe angapatsidwe mwayi woyankhapo akakweza dzanja. Kucita izi kudzawathandiza kuti asamakhumudwe mwayi woyankhapo ukapatsidwa kwa ena.—1 Tim. 6:18. d

18. Kodi tingapewe bwanji kukopela cidwi ca ena pa ife tikamapeleka ndemanga? (Miyambo 27:2)

18 Tonsefe tingakonzekele ndemanga zogwila mtima zimene zimalemekeza Yehova, na kulimbikitsa Akhristu anzathu. (Miy. 25:11) Ngakhale kuti nthawi zina tingafunike kufotokoza mwacidule zocitika pa umoyo wathu, tiyenela kupewa kukamba kwambili za ife eni. (Ŵelengani Miyambo 27:2; 2 Akor. 10:18) M’malo mwake, tiziika kwambili maganizo athu pa Yehova, Mawu ake, komanso anthu ake. (Chiv. 4:11) Koma ngati funso la ndimeyo ikulunjika mwacindunji kwa aliyense payekha-payekha, m’poyenela kufotokoza zimenezo. Citsanzo ca funso lotelo cili m’ndime yotsatila.

19. (a) Kodi padzakhala zotulukapo zotani tikamaganizila onse m’gulu? (Aroma 1:11, 12) (b) Kodi n’ciyani cimakukondweletsani pa nkhani yopeleka ndemanga pamisonkhano?

19 Kweni-kweni, palibe malamulo okhwima pa kapelekedwe ka ndemanga. Cofunika n’cakuti kutengapo mbali kwathu kuzikhala kolimbikitsa ena. Motani? Mumpingo waung’ono, tingacite izi mwa kupelekapo ndemanga kangapo. Mumpingo waukulu, tingacite izi mwa kukhala okhutila na mipata yocepa yopeleka ndemanga imene tingakhale nayo, na kusangalala kuti tapelekanso mpata kwa ena wopelekapo ndemanga. Tikamaika zofuna za ena patsogolo pa misonkhano ya mpingo, tonsefe ‘tidzalimbikitsana.’—Ŵelengani Aroma 1:11, 12.

NYIMBO 93 Dalitsani Misonkhano Yathu

a Tikamapeleka ndemanga pa misonkhano ya mpingo, timalimbikitsana wina na mnzake. Ngakhale n’telo, ena amadodoma kupelekapo ndemanga. Koma ena amasangalala kupelekapo ndemanga, ndipo amafuna kuti azipatsidwa mwayi woyankhapo woculukilapo. Pa mbali ziŵilizi, kodi tingaonetse bwanji kuti timaganizila ena, kotelo kuti tonse tilimbikitsidwe? Nanga tingacite ciyani kuti ndemanga zathu zizilimbikitsa abale na alongo pa cikondi na nchito zabwino? Tikambilane zimenezi m’nkhani ino.

b Malingalilo ena othandiza mungawapeze mu Nsanja ya Mlonda ya January 2019, masa. 8-13, komanso ya Chichewa ya September 1, 2003 masa. 19-22.

c Dzina lasinthidwa.

d Onelelani vidiyo yakuti, Khala Bwenzi la Yehova—Konzekela Yankho Lako pa jw.org.

e Onani Nsanja ya Olonda ya Chichewa ya July 15, 2013, tsa. 32; komanso ya September 1, 2003, masa. 21-22.

f MAWU OFOTOKOZELA: Mumpingo waukulu, m’bale amene wapelekapo kale ndemanga akupatsa ena mpata kuti nawonso ayankhepo.