NKHANI YOPHUNZILA 17
Yehova Adzakuthandizani pa Zakugwa Mwadzidzidzi
“Masoka a munthu wolungama ndi oculuka, koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.”—SAL. 34:19.
NYIMBO 44 Pemphelo la Munthu Wovutika
ZIMENE TIKAMBILANE a
1. Kodi ndife otsimikiza za ciyani?
POKHALA anthu a Yehova, tidziŵa kuti iye amatikonda, komanso kuti amafuna kuti tikhale na umoyo wabwino koposa. (Aroma 8:35-39) Cina, ndife otsimikiza kuti mfundo za m’Baibo zimatipindulila nthawi zonse tikamazigwilitsa nchito. (Yes. 48:17, 18) Koma kodi tingacite ciyani tikakumana na mavuto adzidzidzi?
2. Kodi tingakumane na mavuto otani? Nanga mavutowo angatipangitse kudzifunsa mafunso ati?
2 Mavuto amagwela atumiki onse a Yehova. Mwacitsanzo, wa m’banja mwathu angatikhumudwitse. Mwina tingadwale matenda aakulu amene angatilepheletse kucita zambili mu utumiki wa Yehova. Kapena tingamavutike cifukwa ca tsoka la zacilengedwe. Kapenanso tingamazunzidwe cifukwa ca cikhulupililo cathu. Tikakumana na mavuto ngati awa, tingadzifunse kuti: ‘N’cifukwa ciyani izi zikunicitikila? Kodi n’nalakwanji? Kodi n’cifukwa cakuti Yehova sakusangalala nane?’ Kodi munayamba mwamvapo conco? Ngati n’telo, musataye mtima. Atumiki ambili a Yehova okhulupilika nawonso amvapo conco.—Sal. 22:1, 2; Hab. 1:2, 3.
3. Kodi tiphunzilapo ciyani pa Salimo 34:19?
3 Ŵelengani Salimo 34:19. Onani mfundo ziŵili izi zimene zili pa salimoli: (1) Anthu olungama amakumana na mavuto. (2) Yehova amatipulumutsa ku mavutowo. Kodi amatipulumutsa bwanji? Njila imodzi ni kutithandiza kuona umoyo moyenela m’dzikoli. N’zoona kuti Yehova anatilonjeza kuti tidzakhala acimwemwe pom’tumikila. Koma sanatiuze kuti palipano tidzakhala na umoyo wopanda mavuto. (Yes. 66:14) Iye amatilimbikitsa kuganizila za tsogolo lathu, pamene tidzasangalala na moyo kwamuyaya. (2 Akor. 4:16-18) Koma pakali pano, iye amatithandiza kuti tisaleke kum’tumikila.—Maliro 3:22-24.
4. Kodi tikambilane ciyani m’nkhani ino?
4 Tiyeni tsopano tikambilane zimene tiphunzilapo pa zitsanzo za alambili a Yehova okhulupilika ochulidwa m’Baibo, komanso amakono. Monga tionele, tingakumane na mavuto mosayembekezela. Koma tikam’dalila Yehova, sadzalephela kutithandiza. (Sal. 55:22) Pamene tikukambilana zitsanzozi, dzifunseni kuti: ‘N’kanakhala kuti ndine nakumana na mavutowa, kodi n’kanatani? Kodi zitsanzozi zilimbitsa bwanji cidalilo canga mwa Yehova? Nanga ningazigwilitse nchito motani pa umoyo wanga?’
ZITSANZO ZA ANTHU OCHULIDWA M’BAIBO
5. Ni zovuta ziti zimene Yakobo anakumana nazo kwa Labani? (Onani cithunzi pacikuto.)
5 Atumiki a Yehova ochulidwa m’Baibo anakumanapo na zovuta zimene sanaziyembekezele. Ganizilani citsanzo ca Yakobo. Atate ake anamuuza kuti apite akapeze mkazi pakati pa ana aakazi a Labani, wacibale wawo wolambila Mulungu. Ndipo anam’tsimikizila kuti Yehova adzam’dalitsa kwambili. (Gen. 28:1-4) Yakobo anacitadi zimenezo. Iye ananyamuka ulendo wocoka ku Kanani kupita kunyumba kwa Labani, amene anali na ana aŵili aakazi—Leya na Rakele. Yakobo anagwa m’cikondi na Rakele, mwana wamng’ono wa Labani. Ndipo anavomela kuseŵenzela Labani zaka 7 kuti akam’kwatile. (Gen. 29:18) Koma zinthu sizinayende mmene Yakobo anaganizila. Labani anam’cita cinyengo pom’patsa Leya mwana wake wamkulu. Pambuyo pa mlungu umodzi, Labani analola kuti Yakobo akwatile Rakele. Koma anamuuza kuti am’gwilile nchito zaka zinanso 7. (Gen. 29:25-27) Cina, Labani anali kumudyela masuku pamutu Yakobo pamene anali kum’gwilila nchito. Ndipo anam’cita zacinyengo zimenezo kwa zaka 20!—Gen. 31:41, 42.
6. Kodi Yakobo anapililanso mavuto ena ati?
6 Yakobo anapililanso mavuto ena. Iye anali na banja lalikulu, ndipo nthawi zina ana ake sanali kukhala mwamtendele. Anawo anafika pogulitsa mng’ono wawo Yosefe mu ukapolo. Cina, ana ake aŵili Simiyoni na Levi, ananyazitsa banja lawo, komanso anatonzetsa dzina la Mulungu. Kuwonjezela apo, Rakele mkazi wake wokondeka, anamwalila pobeleka mwana wawo waciŵili. Ndipo cifukwa ca njala yaikulu, Yakobo anakakamizika kusamukila kudziko la Iguputo muukalamba wake.—Gen. 34:30; 35:16-19; 37:28; 45:9-11, 28.
7. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anali kumuyanja Yakobo?
7 Mosasamala kanthu za mavuto onsewa, Yakobo sanataye cikhulupililo cake mwa Yehova na malonjezo Ake. Ndipo nayenso Yehova anaonetsa kuti anali kumuyanja Yakobo. Mwacitsanzo, olo kuti Labani anali kumudyela masuku pamutu, Yehova anam’dalitsa Yakobo kuthupi. Ndipo tangoganizilani cimwemwe na ciyamikilo cimene Yakobo anali naco kwa Yehova, ataonananso na mwana wake Yosefe, amene anali kuganiza kuti anafa kale-kale! Ubwenzi wolimba na Yehova ni umene unam’thandiza Yakobo kupilila mavuto onsewo. (Gen. 30:43; 32:9, 10; 46:28-30) Nafenso tikakhala pa ubwenzi wathithithi na Yehova, tidzakwanitsa kupilila mavuto adzidzidzi.
8. Kodi Mfumu Davide anafunitsitsa atacita ciyani?
8 Mfumu Davide sanacite zonse zimene anali kufuna potumikila Yehova. Mwacitsanzo, iye anali kufunitsitsa kumanga kacisi wa Mulungu wake. Conco, anauza mneneli Natani cokhumba cake cimeneci. Natani anamuuza kuti: “Citani ciliconse cimene cili mumtima mwanu, cifukwa Mulungu woona ali nanu.” (1 Mbiri 17:1, 2) Davide ayenela kuti anakondwela kwambili atamva zimenezo. Mwina nthawi yomweyo anayamba kukonzekela nchito yaikulu imeneyo.
9. Kodi Davide anatani atalandila uthenga wokwinyililitsa?
9 Koma posakhalitsa, mneneli wa Yehova anabwela na uthenga wokwinyililitsa. “Usiku umenewo,” Yehova anauza Natani kuti Davide sindiye adzamange kacisi, koma mmodzi wa ana ake. (1 Mbiri 17:3, 4, 11, 12) Kodi Davide anacita ciyani atalandila uthengawo? Anasintha colinga cake. Iye anaika maganizo ake pa kusonkhanitsa ndalama na zinthu zina zofunikila pomanga, kuti mwana wake Solomo adzazigwilitse nchito.—1 Mbiri 29:1-5.
10. Kodi Yehova anam’dalitsa bwanji Davide?
10 Yehova atangouza Davide kuti sindiye ati adzamange kacisi, anacita naye pangano. Iye analonjeza Davide kuti mmodzi mwa mbadwa zake adzalamulila kwamuyaya. (2 Sam. 7:16) Tangoganizilani mmene Davide adzakondwele m’dziko latsopano, podzaona kuti akusangalala na umoyo pansi pa Ulamulilo wa Yesu wa Zaka Cikwi! Inde, mfumu yocokela mu mzele wa banja lake. Nkhaniyi itiphunzitsa kuti ngakhale n’zosatheka kucitila Yehova zonse zimene tikufuna, Mulungu wathu angaticitile zinthu zina zabwino zimene sitinali kuyembekezela.
11. Kodi Akhristu oyambilila anadalitsidwa motani olo kuti Ufumu wa Mulungu sunabwele panthawi imene anali kuganizila? (Machitidwe 6:7)
11 Akhristu oyambilila anakumana na mavuto osayembekezela. Mwacitsanzo, iwo anali kulakalaka kubwela kwa Ufumu wa Mulungu. Koma sanali kudziŵa kuti udzabwela liti. (Mac. 1:6, 7) Kodi iwo anacita ciyani? Anapitiliza kugwila nchito yolalikila mokangalika. Ndipo uthenga wabwino utayamba kufalikila, kwa iwo unali umboni wosatsutsika wa dalitso la Yehova pa nchito yawo.—Ŵelengani Machitidwe 6:7.
12. Kodi Akhristu oyambilila anatani kutagwa njala?
12 Nthawi ina, kunagwa njala yaikulu “padziko lonse lapansi.” (Mac. 11:28) Akhristu oyambilila nawonso anakhudzidwa. Tangoganizilani mmene anavutikila cifukwa cosoŵa cakudya. Mosakayikila, mitu ya mabanja inada nkhawa mmene ingasamalile mabanja awo. Nanga bwanji acinyamata amene anali kufuna kuwonjezela utumiki wawo? Kodi n’kutheka kuti iwo anaganiza zokankhila kutsogolo zolinga zawozo? Mosasamala kanthu za mikhalidwe yovutayo, Akhristuwo sanalefuke. Iwo anapitiliza kulalikila m’njila iliyonse imene akanatha, ndipo anali okondwa kugaŵana zinthu zakuthupi na Akhristu anzawo ku Yudeya.—Mac. 11:29, 30.
13. Kodi Akhristu anadalitsidwa motani panthawi ya njala?
13 Kodi Akhristuwo anadalitsidwa bwanji panthawi ya njala? Aja amene analandila zosoŵa zawo zakuthupi, anadzionela okha thandizo la Yehova. (Mat. 6:31-33) Iwo ayenela anamva kuti amakondedwa kwambili na okhulupilila anzawo amene anapeleka thandizolo. Ndipo aja amene anacita copeleka kapena kutengako gawo pa nchito yopeleka thandizo, anapeza cimwemwe cimene cimabwela cifukwa copatsa. (Mac. 20:35) Yehova anawadalitsa onsewo pamene anali kuzolowela umoyo watsopano zinthu zitasintha.
14. N’ciyani cinacitikila Baranaba na mtumwi Paulo? Nanga panakhala zotulukapo zotani? (Machitidwe 14:21, 22)
14 Kambili, Akhristuwo anali kuzunzidwa mosayembekezela. Ganizilani zinacitikila Baranaba na mtumwi Paulo pamene anali kulalikila ku Lusitara. Poyamba, anthu omvetsela anawalandila na manja aŵili. Koma pambuyo pake otsutsa “anakopa anthuwo,” ndipo ena mwa anthu amodzimodziwo anaponya Paulo miyala, n’kumusiya thasa poganiza kuti wafa. (Mac. 14:19) Koma Baranaba na Paulo anapitiliza kulalikila kumadela ena. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Iwo anathandiza “anthu angapo kuti akhale ophunzila,” ndipo mawu awo na citsanzo cawo zinalimbikitsa Akhristu anzawo. (Ŵelengani Machitidwe 14:21, 22.) Ambili anapindula poona kuti Baranaba na Paulo sanagonje, olo kuti anazunzidwa mosayembekezela. Nafenso tikalimbikila pa nchito imene Yehova watipatsa, tidzadalitsidwa.
ZITSANZO ZAMAKONO
15. Kodi muphunzilapo ciyani pa citsanzo ca M’bale A. H. Macmillan?
15 Caka ca 1914 cisanafike, anthu a Yehova anali kuyembekezela zinazake. Citsanzo ni M’bale A. H. Macmillan. Mofanana na Mboni zina panthawiyo, M’bale Macmillan anaganiza kuti adzapita kumwamba posacedwa. M’nkhani imene anakamba mu September 1914 anati: “Mwina ino ndiyo nkhani yanga yothela.” Koma siinakhale yothela. Pambuyo pake, M’bale Macmillan anadzalemba kuti: “Mwina ena a ife tinadya mfulumila poganiza kuti tidzapita kumwamba nthawi yomweyo.” Anapitiliza kuti: “Cimene tiyenela kucita ni kukhalabe okangalika m’nchito ya Ambuye.” Ndipo n’zimene M’bale Macmillan anacitadi. Anakhala wokangalika mu ulaliki. Analinso na mwayi wolimbikitsa abale amene anali m’ndende cifukwa cokana kuloŵa usilikali. Ndipo nthawi zonse anali kupezeka ku misonkhano ya mpingo ngakhale muukalamba wake. Kodi M’bale Macmillan anapindula bwanji cifukwa cogwilitsa nchito bwino nthawi yake poyembekezela mphoto yake? Asanamwalile mu 1966, iye analemba kuti: “Cikhulupililo canga cikali colimba monga cinalili kale.” Ici ni citsanzo cabwino cimene tingatengele, maka-maka tikapilila mavuto kwa nthawi yaitali.—Aheb. 13:7.
16. Ni vuto losayembekezela liti limene m’bale Herbert Jennings na mkazi wake anakumana nalo? (Yakobo 4:14)
16 Atumiki ambili a Yehova amalimbana na matenda osayembekezela. Mwacitsanzo, m’mbili ya moyo wake, M’bale Herbert Jennings b anafotokoza kuti iye na mkazi wake anali kusangalala na utumiki waumishonale ku Ghana. Koma m’kupita kwa nthawi, mbaleyu anam’peza na matenda okhudza maganizo. Pogwila mawu Yakobo 4:14, M’bale Jennings anati kusintha kwa zinthu kumeneku kunali “‘maŵa’ limene sitinali kuliyembekezela.” (Ŵelengani.) Iye analemba kuti: “Tinangocivomeleza. Conco, tinacoka ku Ghana, n’kusiya mabwenzi athu ambili apamtima na kubwelela ku Canada [kukalandila cithandizo cacipatala].” Yehova anathandiza M’bale Jennings na mkazi wake kupitiliza kum’tumikila mokhulupilika, mosasamala kanthu za matendawo.
17. Kodi citsanzo ca M’bale Jennings cinawalimbikitsa bwanji Akhristu anzake?
17 Zimene M’bale Jennings anakamba m’mbili ya moyo wake, zinalimbikitsa kwambili anthu ena. Mlongo wina analemba kuti: “Sin’nakhudzikepo mtima conco n’taŵelenga nkhani imeneyi. . . . Poona kuti Mbale Jennings anacita kusiya utumiki kuti akasamalile matenda ake, n’nayamba kuona umoyo wanga moyenela.” Mofananamo, m’bale wina analemba kuti: “N’tatumikila monga mkulu kwa zaka 10, n’natula pansi udindowo cifukwa ca matenda ena ake a maganizo. N’nayamba kudziona wolephela zedi, moti kambili cinali kunivuta kuŵelenga nkhani zakuti ‘Mbili Yanga.’ . . . Koma n’nalimbikitsidwa ngako poona kuti Mbale Jennings sanabwelele m’mbuyo.” Izi zitikumbutsa kuti tikapilila mavuto adzidzidzi, tingalimbikitse ena. Ngakhale kuti umoyo sungayende mmene tinali kuyembekezela, tingakhalebe citsanzo cabwino pa kukhulupilika na kupilila.—1 Pet. 5:9.
18. Monga tionela m’citsanzo cili pa cithunzi, kodi muphunzilapo ciyani pa cocitika ca mlongo wina wamasiye ku Nigeria?
18 Matsoka monga mlili wa COVID-19 akhudza atumiki a Yehova ambili. Mwacitsanzo, mlongo wina wamasiye ku Nigeria anangotsala na cakudya komanso ndalama zocepa kwambili. Tsiku lina m’maŵa, mwana wake wamkazi anam’funsa kuti adzadya ciyani akaphika tumpunga tothela. Poyankha, mlongo wathuyo anauza mwana wakeyo kuti analibe ndalama kapena cakudya ciliconse. Anati adzatengela citsanzo ca mkazi wamasiye wa ku Zarefati. Adzangophika cakudya cawo cothelaco, na kuika cidalilo cawo conse mwa Yehova. (1 Maf. 17:8-16) Asanayambe kuganizila zimene adzadya masana tsikulo, analandila cakudya kwa alambili anzawo cogaŵilidwa kwa okhudzidwa na matsoka. Cakudya cimene analandila cinali cokwanila kudya milungu iŵili na kuposapo. Mlongoyo anati sanadziŵe kuti Yehova anali kumvetsela mwachelu zimene anali kuuza mwana wake. Ndithudi, tikam’dalila Yehova, mavuto osayembekezela amene tingakumane nawo angatipangitse kumuyandikila kwambili.—1 Pet. 5:6, 7.
19. Kodi m’bale Aleksey Yershov anapilila cizunzo cotani?
19 M’zaka zaposacedwa, abale na alongo athu ambili apilila mazunzo osayembekezela. Ganizilani za M’bale Aleksey Yershov wa ku Russia. Mu 1994, caka cimene iye anabatizika, atumiki a Yehova kumeneko anali na ufulu wa kulambila. Koma pambuyo pa zaka, zinthu ku Russia zinasintha. Mu 2020, apolisi anathyola nyumba ya M’bale Yershov na kuyamba kufufuza zinthu, ndipo katundu wake wambili analandidwa. Pambuyo pa miyezi ingapo, boma linam’peleka ku khoti pomuimba milandu. Ndipo coipa kwambili n’cakuti, maziko omuzengela mlandu anali mavidiyo ojambulidwa na munthu amene kwa caka na kuposapo anali kunamizila kukhala na cidwi cophunzila Baibo. Ati ciwembu cake ŵati!
20. Kodi M’bale Yershov analimbitsa bwanji ubale wake na Yehova?
20 Kodi panali zotulukapo zilizonse zabwino pa mazunzo amene M’bale Yershov anakumana nawo? Inde. Ubale wake na Yehova walimba kwambili. Iye anati: “Ine na mkazi wanga timapemphela pamodzi kaŵili-kaŵili. N’nazindikila kuti sinikanatha kupilila mazunzo amenewo popanda thandizo la Yehova.” Anawonjezela kuti: “Phunzilo la munthu mwini limanithandiza kuthana nazo zinthu zolefula. Nimasinkhasinkha zitsanzo za atumiki okhulupilika akale. Ndipo m’Baibo, muli zitsanzo zambili zoonetsa kufunika kokhala wosatekeseka, komanso wokhulupilila Yehova.”
21. Taphunzilanji m’nkhani ino?
21 Kodi taphunzilanji m’nkhani ino? Umoyo m’dongosolo lino la zinthu ni wosadalilika. Ngakhale n’telo, nthawi zonse Yehova amathandiza atumiki ake amene amam’dalila. Lemba la mfundo yaikulu ya nkhani ino likuti: “Masoka a munthu wolungama ndi oculuka, koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.” (Sal. 34:19) Conco, m’malo mongoganizila mavuto athu, tiyeni tipitilize kudalila mphamvu zopulumutsa za Yehova. Tikatelo, nafenso monga mtumwi Paulo, tingakambe kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afil. 4:13.
NYIMBO 38 Adzakulimbitsa
a Ngakhale kuti tingakumane na mavuto osayembekezela m’dzikoli, ndife otsimikiza kuti Yehova amathandiza alambili ake okhulupilika. Kodi Yehova anawathandiza bwanji atumiki ake akale? Nanga amatithandiza bwanji ife masiku ano? Kukambilana zitsanzo za m’Baibo komanso zamakono, kudzatipatsa cidalilo cakuti nafenso Yehova adzatithandiza tikam’dalila.
b Onani Nsanja ya Olonda ya Chichewa ya December 1, 2000, masa. 24-28.